Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Banja

Banja

Kodi ukwati ndi mgwirizano woti ukhoza kungotha mwachisawawa?

“Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”—Mateyu 19:6.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Mulungu amaona kuti ukwati si chinthu choti chingathe mwachisawawa. Ukwati ndi mgwirizano wopatulika wapakati pa mwamuna ndi mkazi. Baibulo limanena kuti: “Kuyambira pa chiyambi pa chilengedwe, ‘Mulungu anawalenga mwamuna ndi mkazi. Pa chifukwa chimenechi, mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi’ . . . Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” *Maliko 10:6-9; Genesis 2:24.

Mawu akuti, “chimene Mulungu wachimanga pamodzi,” sakutanthauza kuti Mulungu amasankhiratu munthu amene aliyense adzakwatirane naye. M’malomwake, Baibulo likusonyeza kuti Mlengi wathu ndi amene anayambitsa banja, ndipo zimenezi zikusonyeza kuti banja ndi chinthu chapadera chosayenera kuchiona mopepuka. Anthu okwatirana omwe amaona banja lawo mwanjira imeneyi, amalemekeza banja lawo komanso amadziwa kuti siliyenera kutha. Zimenezi zimawathandiza kuti azichita zinthu zomwe zingachititse kuti banja lawo liziyenda bwino. Banja lawo likhoza kumayenda bwino kwambiri ngati atamatsatira mfundo za m’Baibulo pokwaniritsa udindo wawo monga mwamuna ndi mkazi wake.

 Kodi udindo wa mwamuna ndi wotani?

“Mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake.”Aefeso 5:23.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kuti banja liziyenda bwino, mmodzi ayenera kukhala patsogolo posankha zochita. Baibulo limanena kuti mwamuna ndi amene ali ndi udindo umenewu. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti mwamuna asamakambirane kaye ndi mkazi wake kapena akhale wankhanza. Sayeneranso kupewa udindo wake, zomwe zingachititse kuti mkazi wake asamamulemekeze komanso zingachititse kuti mkazi azichulukiridwa chifukwa chochita zonse yekha. M’malomwake, Mulungu amafuna kuti mwamuna azichita khama posamalira mkazi wake ndiponso kuti azimulemekeza monga mnzake wapamtima. (1 Timoteyo 5:8; 1 Petulo 3:7) Lemba la Aefeso 5:28 limanena kuti “amuna akonde akazi awo monga matupi awo.”

Mwamuna amene amakondadi mkazi wake amayamikira luso komanso nzeru zimene mkaziyo ali nazo ndipo samanyalanyaza maganizo amene mkazi wake wapereka, makamaka pa nkhani zomwe zingakhudze banja lawo. Sayenera kukakamira maganizo ake chifukwa choti iyeyo ndiye mutu wa banja. Abulahamu atakana kutsatira malangizo othandiza a mkazi wake, Yehova Mulungu anamuuza kuti: “Mvera mawu ake.” (Genesis 21:9-12) Modzichepetsa, Abulahamu anamvera zimenezi ndipo banja lawo linayamba kukhala mwamtendere komanso mogwirizana, ndipo Mulungu anawadalitsa.

Kodi udindo wa mkazi ndi wotani?

“Akazi, muzigonjera amuna anu.”1 Petulo 3:1.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Asanalenge mkazi wa munthu woyambirira, Mulungu anati: “Si bwino kuti munthu akhale yekha. Ndimupangira womuthandiza, monga mnzake womuyenerera.” (Genesis 2:18) Mawu amene anamasuliridwa kuti womuyenerera amasonyeza kuti mkazi amathandiza mwamuna kukhala woyenerera bwino kukwaniritsa udindo wake. Choncho, Mulungu sanalenge mkazi kuti akhale wofanana ndi mwamuna kapena kuti azipikisana naye, koma kuti azimuthandiza monga mnzake. Ngati atamathandizana, akhoza kukwaniritsa udindo umene Mulungu anawapatsa, womwe ndi wobereka ana n’kudzaza dziko lapansi.Genesis 1:28.

Mulungu anapatsa mkazi thupi komanso maganizo omwe angamuthandize kukwaniritsa bwinobwino udindo wake. Ngati atagwiritsa ntchito mwanzeru zinthu zimenezi, akhoza kuthandiza kuti banja lawo likhale losangalala ndiponso angachititse kuti mwamuna wake azikhala wokhutira komanso aziona kuti ndi wotetezeka. Mulungu amaona kuti mkazi wotere ndi woyenera kutamandidwa. *Miyambo 31:28, 31.

^ ndime 5 Baibulo limavomereza kuti banja lingathe ngati mmodzi m’banjamo wachita chigololo.Mateyu 19:9.

^ ndime 14 Anthu okwatira akhoza kupeza mfundo zothandiza mabanja awo m’nkhani za mutu wakuti “Mfundo Zothandiza Mabanja” zomwe zimatuluka mu Galamukani!