Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | MWAMUNA NDI MKAZI WAKE

Zimene Mungachite Ngati Mumakonda Zosiyana

Zimene Mungachite Ngati Mumakonda Zosiyana

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Tiyerekeze kuti inuyo mumakonda mpira, pomwe mnzanuyo amakonda kuwerenga. Mumakonda kuchita zinthu mwadongosolo pamene mnzanuyo ndi wopanda dongosolo. Kapenanso mumakonda kucheza ndi anthu, pomwe mnzanuyo si kwenikweni.

Mwina zimenezi zingakuchititseni kuganiza kuti, ‘Ndikanadziwa kuti ndife osiyana chonchi, sindikanakwatirana ndi munthu ameneyu. N’chifukwa chiyani sindinaone zimenezi tili pa chibwenzi?’

N’kutheka kuti muli pa chibwenzi munkaona ndithu kuti ndinu osiyana. Koma mwina chifukwa choti chikondi chinali chitakusokonezani, munkaona kuti limeneli si vuto kwenikweni. Choncho, vuto limeneli likhoza kutha ngati mutakhala ndi maganizo amene munali nawo pamene munali pa chibwenzi. Ndiyeno nkhaniyi ikuthandizani kuchita zimenezi. Koma choyamba, tiyeni tikambirane zinthu zina zokhudza vutoli.

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

Kusiyana kwina kumayambitsa mavuto. Dziwani kuti cholinga chachikulu chimene anthu amakhalira pa chibwenzi n’choti adziwane bwino n’kuona ngati angadzakwanitse kukhala limodzi kwa moyo wawo wonse. Choncho anthu ena akaona kuti amakonda zinthu zosiyana kwambiri, amathetsa chibwenzi chawo. Amachita zimenezi chifukwa amadziwa kuti akalowa m’banja akhoza kudzakumana ndi mavuto. Koma akaona kuti amasiyana pa zinthu zing’onozing’ono, amakwatiranabe chifukwa amadziwa kuti anthu amene anakulira kosiyana sangakonde zofanana.

Pamakhalabe zina zimene okwatirana amasiyana. Musaganize kuti ngati mumasiyana zinthu zina ndi mwamuna kapena mkazi wanu ndiye kuti banja lanu silili bwino. Nthawi zina mukhoza kusiyana pa zinthu ngati izi:

Zimene mumakonda. Mkazi wina, dzina lake Anna * anati: “Sindikonda zopita kwinakwake kukayenda. Koma mwamuna wanga amakonda kupondaponda. Amatha kuyenda maulendo ataliatali wapansi komanso amakonda kukwera mapiri ndipo wakhala akuchita zimenezi kuyambira ali mwana.”

Zimene munazolowera kuchita. Mwamuna wina dzina lake Brian anati: “Mkazi wanga amakonda kugona usiku kwambiri ndipo amadzuka m’mawa kwambiri, mwina cha m’ma 5 koloko. Koma ineyo ndikapanda kugona mokwanira, sizimandiyendera.”

Makhalidwe. Mwina inuyo simukonda zoyankhulayankhula, pomwe mnzanuyo amamasuka ndi aliyense. Mwamuna wina dzina lake David anati: “Ndinakulira m’banja lomwe sitinkakonda kunena mavuto athu. Koma banja limene mkazi wanga anakulira linali la anthu omasuka moti ankangokambirana chilichonse.”

Nthawi zina kusiyana zochita n’kothandiza. Mkazi wina dzina lake Helena anati: “Ndimaona kuti zimene ndimakonda ndi zabwino. Koma ndimadziwanso kuti zimene mwamuna wanga amakonda ndi zabwinonso, moti nanenso ndimatha kuyamba kuzikonda.”

ZIMENE MUNGACHITE

Muziyesa kuchita nawo zimene mnzanuyo amakonda. Mwamuna wina dzina lake Adam anati: “Mkazi wanga Karen sakonda mpira. Komabe, kangapo konse takhala tikupita limodzi kokaonera mpira. Amakonda kupita ku miziyamu ya zithunzi ndipo nanenso ndimam’perekeza. Timaona limodzi zithunzi mpaka pamene atopere. N’zoona kuti sindimakonda zithunzi kwenikweni. Komabe panopa ndayamba kuzitsata ndipo ndimachita zimenezi chifukwa ndimamukonda kwambiri mkazi wanga.”—Lemba lothandiza: 1 Akorinto 10:24.

Muzidziwa kuti pali zinthu zinanso zabwino. Muyenera kudziwa kuti zimene mwamuna kapena mkazi wanu amakonda n’zabwinonso ngakhale kuti n’zosiyana ndi zanu. Mwamuna wina dzina lake Alex anati: “Poyamba ndinkaona kuti zimene ineyo ndimakonda ndiye zabwino kwambiri. Moti munthu wina akamakonda zosiyana ndi zanga, ndinkamuona kuti ndi wotsalira kwambiri. Koma nditakwatira ndinasintha maganizo. Ndinayamba kuona kuti zimene mkazi wanga amakonda ndi zabwino kuposa mmene ndimaganizira.—Lemba lothandiza: 1 Petulo 5:5.

Musafulumire kuganiza kuti munasankha molakwika. Monga taonera kumayambiriro kwa nkhaniyi, anthu okwatirana sangafanane pa chilichonse. Choncho musafulumire kumanga mfundo yoti simunasankhe bwino chifukwa choti mumakonda zosiyana. Buku lina limati: “Anthu ena amakonda kunena kuti, ‘Ndinasankha mosaganiza bwino.’ Koma si bwino kufulumira kuganiza choncho. Chifukwa ngakhale mumakonda zosiyana, n’zotheka kumakondanabe.” (The Case Against Divorce) Choncho zinthu zikhoza kumayendabe bwino m’banja lanu ngati mutapitiriza “kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake.”—Akolose 3:13.

Tayesani kuchita izi: Lembani zimene mumakonda komanso zimene mnzanuyo amakonda. Kenako yerekezerani zimene mumakondazo ndi za mnzanuyo, n’kuona ngati pali zimene mumagwirizana. Mungadabwe kuona kuti simumasiyana zinthu zambiri. Mukadziwa zimene mumasiyana, mungaone zimene mukufunika kuyesetsa kuphunzira. Mwamuna wina dzina lake Kenneth anati: “Ndimasangalala kwambiri mkazi wanga akamachita nawo zimene ine ndimakonda. Ndimadziwa kuti nayenso amasangalala ndikachita chimodzimodzi. Ngakhale mkazi wangayo akamachita zinthu zimene sindikonda kwenikweni, ndimasangalalabe ndikaona kuti akusangalala.”—Lemba lothandiza: Afilipi 4:5.

^ ndime 10 Tasintha mayina ena m’nkhaniyi.