Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | MWAMUNA NDI MKAZI WAKE

Mungatani Kuti Mukwaniritse Lonjezo Lanu?

Mungatani Kuti Mukwaniritse Lonjezo Lanu?

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Pa tsiku lomwe munakwatirana, munalonjezana kuti mudzakhala limodzi mpaka imfa. Munalonjezananso kuti mudzakhala limodzi pa mtendere ndi pa mavuto pomwe.

Koma panopa, mukukumana ndi mavuto osiyanasiyana m’banja lanu. Izi zingapangitse kuti muyambe kudzifunsa kuti, ‘Kodi n’zotheka kukhalabe ndi munthu ameneyu mpaka imfa?’

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

Lonjezo lanu loti mudzakhala limodzi mpaka imfa tingaliyerekeze ndi nangula, ndipo limathandiza kuti banja lanu likhale lolimba

Lonjezo lomwe munapanga lingathandize kuti banja lanu likhale lolimba. Anthu ambiri amaona kuti si bwino kulonjeza kuti adzakhala limodzi ndi mkazi kapena mwamuna wawo mpaka kalekale. Ena amaona kuti kuchita zimenezi kuli ngati kulowa m’goli loti sangathe kuchokamonso. Koma zimenezi si zoona. Lonjezo lanu loti mudzakhala limodzi mpaka imfa tingaliyerekeze ndi nangula, ndipo limathandiza kuti banja lanu likhale lolimba. Mkazi wina dzina lake Megan anati: “Ubwino wa lonjezo limeneli ndi woti mukayambana, simukhala ndi nkhawa kuti banja litha. Zili choncho chifukwa mumadziwa kuti munalonjezana kuti mudzakhala limodzi mpaka kalekale.” * Kudziwa kuti banja lanu silingathe, kumathandiza kuti mukakumana ndi mavuto muyesetse kupeza njira yowathetsera.—Onani bokosi lakuti, “Yesetsani Kuti Musalekane.”

Mfundo yofunika kwambiri ndi yakuti: Ngati mukukumana ndi mavuto a m’banja, musayambe kuganiza kuti munalakwitsa kulonjeza kuti mudzakhala limodzi mpaka kalekale. M’malomwake, muziyesetsa kuchita zinthu zogwirizana ndi lonjezo lanu. Koma kodi mungachite bwanji zimenezi?

ZIMENE MUNGACHITE

Musamaone ngati kukhalabe ndi mwamuna kapena mkazi wanu kukukupherani ufulu. Kodi mukamva mawu akuti, “Kukhala limodzi mpaka imfa,” mumaganiza chiyani? Kodi mumaganiza kuti muli m’goli loti simungathe kutulukamo, kapena mumaona kuti ndinu wotetezeka? Pakakhala mavuto, kodi mumaganiza kuti njira yabwino ndi kungothetsa banja? Kuganiza kuti kuthetsa banja ndi njira yabwino yothetsera mavuto, kungakulepheretseni kuchita zinthu zogwirizana ndi lonjezo lanu. M’malomwake muziona kuti banja lanu ndi lofunika ndipo muyenera kukhala ndi mwamuna kapena mkazi wanu mpaka imfa.—Lemba lothandiza: Mateyu 19:6.

Ganizirani banja lomwe munakulira. Nthawi zina, mungamaone kuti n’zosatheka kukhala limodzi ndi mwamuna kapena mkazi wanu mpaka imfa, chifukwa chotengera zochita za makolo anu. Mkazi wina, dzina lake Lea anati: “Makolo anga anasiyana ndili mwana. Ndimada nkhawa kuti mwina zimenezi zingapangitse kuti nanenso ndiziona kuti pakakhala mavuto, ndi bwino kungothetsa banja.” Dziwani kuti ngakhale anthu amene banja la makolo awo linatha, akhoza kukhala ndi banja lolimba.—Lemba lothandiza: Agalatiya 6:4, 5.

Ganizirani mmene mumalankhulira. Mukakangana ndi mwamuna kapena mkazi wanu, muzipewa kulankhula mawu omwe pambuyo pake munganong’oneze nawo bondo. Mawu ake ndi monga akuti: “Banja limeneli lingotha basi” kapena “Ndipeza wina wabwino.” Zimenezi sizingathandize kuti mupeze njira yothetsera vutolo koma zingangopangitsa kuti mkanganowo ukule ndipo zingasokoneze banja lanu. Choncho m’malo molankhulana mawu opweteka, ndi bwino kunena mawu monga akuti, “Popeza tonse takwiya, bwanji nkhaniyi tiisiye kaye ndipo nthawi ina tipeze njira yothetsera vutoli.”—Lemba lothandiza: Miyambo 12:18.

Muzisonyeza kuti mumakonda mwamuna kapena mkazi wanu. Ngati n’zotheka, mungachite bwino kuika chithunzi cha mkazi kapena mwamuna wanu padesiki yanu kuntchito. Mukamacheza ndi anzanu musamanyoze mwamuna kapena mkazi wanu. Mungachitenso bwino kumayesetsa kuimbirana foni tsiku lililonse, mukakhala kuntchito kapena malo ena. Polankhula muzikonda kunena kuti “ife,” “ine ndi mkazi wanga” kapena “ine ndi mwamuna wanga.” Zimenezi zingachititse kuti anthu azidziwa kuti muli pa banja ndiponso zingakuthandizeni inuyo kukhalabe wokhulupirika kwa mnzanuyo.

Muzitengera chitsanzo cha mabanja achitsanzo chabwino. Muzitengera chitsanzo cha mabanja omwe akakumana ndi mavuto, amawathetsa n’kumakondanabe. Mungachite bwino kucheza nawo n’kuwafunsa funso lakuti, “Kodi mumaona kuti muli m’goli loti simungathe kuchokamo chifukwa choti munalonjezana kuti mudzakhala limodzi mpaka imfa, Kapena zimenezi zimakupangitsani kuona kuti ndinu wotetezeka?” Kuchita zimenezi n’kothandiza chifukwa Baibulo limati: “Chitsulo chimanola chitsulo chinzake. Momwemonso munthu amanola munthu mnzake.” (Miyambo 27:17) Choncho kucheza ndi mabanja achitsanzo chabwino kungakuthandizeni kuti mukwaniritse lonjezo lanu loti mudzakhala limodzi mpaka imfa.

^ ndime 7 Baibulo limati munthu akhoza kuthetsa ukwati pokhapokha ngati mnzakeyo wachita chigololo. Onani nkhani yakuti, “Zimene Baibulo Limanena—Chigololo” patsamba 12.