Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi Banja Ndi Limene Limapangitsa Munthu Kukhala Wosangalala?

Kodi Banja Ndi Limene Limapangitsa Munthu Kukhala Wosangalala?

Kodi Baibulo limaphunzitsa kuti, munthu sangakhale wosangalala pokhapokha atakhala pa banja? Kungoona mwachisawawa, munthu angaganize kuti Mawu a Mulungu amanena zimenezi. Kodi n’chifukwa chiyani tikutero?

Mogwirizana ndi zimene timawerenga m’buku la Genesis, Mulungu anaona kuti “si bwino” kuti munthu woyamba, Adamu apitirize kukhala yekha. Choncho Mulungu anam’pangira Hava kuti akhale “mnzake womuyenerera.” (Genesis 2:18) Lemba limeneli limapangitsa anthu ena kuganiza kuti munthu sangakhale wosangalala pokhapokha atakwatira kapena kukwatiwa. Komanso m’Baibulo muli nkhani zambiri zimene zimasonyeza kuti ukwati umabweretsa madalitso ambiri ndiponso umathandiza kuti munthu akhale wosangalala. Chitsanzo cha nkhani zoterezi, ndi nkhani ya Rute.

Komabe, kodi n’zoona kuti nkhani zimenezi zimatiphunzitsa kuti Akhristu masiku ano sangakhale osangalala pokhapokha atakhala pa banja n’kukhala ndi ana? Ayi si choncho. Munthu amene anali wosangalala kwambiri pa moyo wake anali Yesu Khristu. Komatu iye anakhala wosakwatira moyo wake onse. Yesu, yemwe anali wanzeru kuposa munthu aliyense, ankasonyezanso bwino makhalidwe a Yehova, yemwe ndi “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteyo 1:11; Yohane 14:9) Komanso Yesu anatchula zimene zingathandize munthu kukhala wosangalala m’dzikoli. (Mateyu 5:1-12) Koma pa zomwe anatchulazo, sanatchulepo ukwati.

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Baibulo limadzitsutsa pa nkhaniyi? Ayi. Tiyenera kuona ukwati mogwirizana ndi cholinga chimene Mulungu anali nacho poyambitsa ukwati. Mulungu anakonza zoti anthu okwatirana azisangalala, kukondana ndiponso kulimbikitsana. Komanso nthawi zina Mulungu amagwiritsa ntchito banja kuti akwaniritse zolinga zake. Mwachitsanzo, Mulungu anafuna kuti Adamu ndi Hava ‘aberekane, achuluke, adzaze dziko lapansi.’ (Genesis 1:28) Aliyense payekha sakanakwaniritsa cholinga cha Mulungu chimenechi. M’malomwake onse awiri anali ofunika kuti cholinga cha Mulunguchi chikwaniritsidwe.

Mofanana ndi zimenezi, pochita zinthu ndi Aisiraeli, Mulungu anagwiritsa ntchito banja kuti akwaniritse zolinga zake zapadera. Iye ankafuna kuti Aisiraeli achuluke kuti asamagonjetsedwe mosavuta ndi adani awo. Iye anafunanso kuti mtundu wa Yuda udzatulutse Mesiya amene adzapulumutse anthu okhulupirika, ku uchimo ndi imfa. (Genesis 49:10) Choncho azimayi achiisiraeli ankaona kuti ndi mwayi waukulu kukwatiwa n’kukhala ndi ana ndipo kukhala wosakwatiwa kapena wopanda ana ankakuona ngati chinthu chochititsa manyazi komanso chomvetsa chisoni.

Nanga bwanji masiku ano, pomwe m’dzikoli muli kale anthu ambiri? Kodi lamulo la Mulungu loti anthu ‘adzadze dziko lapansi’ limalimbikitsa Akhristu kuti azikwatira ndiponso kubereka ana? Ayi. (Mateyu 19:10-12) Chifukwa maulosi okhudza Mesiya anakwaniritsidwa kale choncho Mulungu alibenso cholinga choti mtundu winawake udzatulutse Mesiya. Ndiyeno kodi Akhristu ayenera kuona bwanji nkhani ya kukhala pa banja kapena kusakhala pa banja?

Kunena zoona, zonsezi ndi mphatso zochokera kwa Mulungu. Koma monga mukudziwira, mphatso imene ingakhale yoyenera kwa munthu wina ingakhale yosayenera kwa wina. Banja ndi dongosolo lochokera kwa Mulungu ndipo lingachititse anthu okwatirana kuti azikondana komanso kugwirizana. Komanso banja ndi malo abwino olerera ana. Komabe Baibulo limanenanso kuti anthu amene amakwatira adzakumana ndi “nsautso m’thupi mwawo” kutanthauza mavuto osiyanasiyana. Yehova saona kuti kusakhala pa banja ndi chinthu chochititsa manyazi kapena chomvetsa chisoni. M’malomwake, Mawu ake amasonyeza kuti kukhala wosakwatira kapena wosakwatiwa kuli ndi ubwino wake kuposa kukhala pa banja.—1 Akorinto 7:28, 32-35.

Choncho Baibulo silinena kuti munthu wapabanja amakhala wosangalala kwambiri kuposa munthu amene sali pa banja. Yehova, yemwe ndi amene anayambitsa ukwati, amafuna kuti atumiki ake, apabanja ndi amene sali pa banja omwe, azikhala osangalala.