Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Limaloleza Kuthetsa Ukwati?

Kodi Baibulo Limaloleza Kuthetsa Ukwati?

Yankho la m’Baibulo

 Baibulo limaloleza kuthetsa ukwati. Komabe, Yesu anatchula chifukwa chimodzi chokha chovomerezeka chimene chingachititse kuti banja lithe. Iye anati: “Aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatira wina wachita chigololo, kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha dama [kugonana ndi munthu amene si mkazi kapena mwamuna wake].”—Mateyu 19:9.

 Mulungu amadana ndi anthu amene amathetsa banja lawo mwachinyengo. Iye adzalanga munthu aliyense amene amasiya mwachinyengo mkazi kapena mwamuna wake n’cholinga choti apezenso munthu wina woti akwatirane naye.—Malaki 2:13-16; Maliko 10:9.