Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | BANJA

Ana Akakula N’kuchoka Pakhomo

Ana Akakula N’kuchoka Pakhomo

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Nthawi zambiri makolo amavutika kwambiri ana awo akakula n’kuchoka pakhomo. Zimenezi zimachititsa kuti azidzimva ngati ndi alendo. Mlangizi wina wa mabanja dzina lake M. Gary Neuman anati: “Ndimalangiza amuna ndi akazi ambiri amene zimawavuta kuti azimasukirana ana awo akachoka pakhomo. Makolo ambiri pa nthawiyi amasowa nkhani zoti azicheza kapena kukambirana.” *

Kodi zimene tafotokozazi zikufanana ndi zomwe zachitikira banja lanu? Ngati ndi choncho, mungathe kukonza zinthu kuti ziyambirenso kuyenda bwino. Komabe choyamba muyenera kuganizira zimene mukuona kuti ndi zomwe zayambitsa kuti inuyo ndi mwamuna kapena mkazi wanu muzivutika kumasukirana.

ZIMENE ZIMACHITITSA

Makolo amakhala akuganizira kwambiri za ana awo. Makolo ambiri amakonda ana awo moti amaika zofuna za anawo pamalo oyamba kuposa zimene mwamuna kapena mkazi wawo akufuna. Zotsatira zake n’zakuti amangoyesetsa kukwaniritsa udindo wawo monga makolo koma amalephera kuchita zinthu zina limodzi ngati mwamuna ndi mkazi wake. Ndipo zimenezi zimaonekera kwambiri ana akachoka pakhomopo. Mayi wina wazaka 59 anati: “Pa nthawi imene tinkakhala limodzi ndi ana athu, tinkachita zinthu limodzi ngati banja. Koma anawo atachoka, ine ndi mwamuna wanga tinkachita zinthu zosiyana kwambiri.” Nthawi ina mayiyu anauza mwamuna wake kuti: “Aliyense azingopanga zoti zimuthandize basi.”

Mabanja ambiri samakonzekera zoti adzachite ana akadzachoka. Buku lina linanena kuti, “M’mabanja ambiri ana akachoka, mwamuna ndi mkazi wake amangokhala ngati adziwana kumene.” Popeza mwamuna ndi mkazi wake amayamba kuona kuti akukonda zosiyana, aliyense amayamba kuchita zimene akufuna ndipo amangoonana ngati anthu amene akukhala nyumba imodzi basi.​—Empty Nesting.

Nkhani yosangalatsa ndi yakuti mukhoza kupewa mavuto amenewa n’kumasangalala ngakhale pa nthawi imene ana anu achoka pakhomo. Baibulo lingakuthandizeni pa nkhaniyi. Tiyeni tione.

ZIMENE MUNGACHITE

Muzivomereza kuti zinthu zasintha. Ponena za ana amene akukula, Baibulo limati: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake.” (Genesis 2:24) Choncho monga makolo, cholinga chanu chimakhala kuphunzitsa komanso kuthandiza ana anuwo kuti adzathe kuima pawokha akadzakula. Kuganizira zimenezi kungakuthandizeni kuti muzinyadira ana anu akachoka pakhomo.​—Lemba lothandiza: Maliko 10:7.

Sikuti zikatere ndiye kuti musiya kukhala makolo a ana anuwo ayi. Koma tsopano udindo wanu ndi wongowathandiza osati kuwauza zochita. Izi zingakuthandizeni kuti muzigwirizana kwambiri ndi anawo ndipo pa nthawi imeneyi m’pamenenso mungasonyeze kuti mumakonda kwambiri mwamuna kapena mkazi wanu. *​—Lemba lothandiza: Mateyu 19:6.

Muzikambirana ndi mwamuna kapena mkazi wanu zimene zikukudetsani nkhawa. Muziuza mwamuna kapena mkazi wanu mmene mukumvera chifukwa cha kusinthaku. Ndipo kaya ndinu mwamuna kapena mkazi muzimvetsera moleza mtima mnzanuyo akamakuuzani mmene zikumukhudzira. N’zoona kuti zingatenge nthawi kuti muyambirenso kuchitira zinthu limodzi ngati kale, koma kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri.​—Lemba lothandiza: 1 Akorinto 13:4.

Muzipeza zinthu zatsopano zimene mungamachitire limodzi. Muzikambirana zolinga komanso zosangalatsa zomwe mukufuna kuchitira limodzi monga banja. Ndipotu popeza kuti munalerapo ana, muyenera kuti muli ndi nzeru zothandiza kwambiri. Ndiye mungachite bwino kugwiritsira ntchito nzeruzo pothandiza mabanja ena amene akuleranso ana.​—Lemba lothandiza: Yobu 12:12.

Muzikumbukira mmene munkakonderana poyamba. Muzikumbukira makhalidwe abwino a mnzanuyo amene munakopeka nawo. Muziganiziranso kumene mwachoka ndiponso mavuto amene mwakhala mukuwapirira limodzi monga banja. Mukatero mudzaona kuti nthawi imene zinthu zasinthayi ndi yosangalatsa. Banja lanu lingathe kukhala labwino kwambiri ndipo mungayambirenso kukondana ngati mmene munkachitira poyamba.

^ ndime 4 Kuchokera m’buku lakuti Emotional Infidelity.

^ ndime 12 Ngati mukulerabe ana, musamaiwale kuti ndinu “thupi limodzi” ndi mwamuna kapena mkazi wanu. (Maliko 10:8) Nawonso ana amamva kuti ndi otetezeka akaona kuti makolo awo amakondana kwambiri.