MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | BANJA
Zimene Mungachite Kuti Musamagwire Ntchito Pamene Simuli Kuntchito
Chifukwa cha zipangizo zamakono, a bwana anu, ogwira nawo ntchito, kapena makasitomala anu, angamayembekezere kuti muzigwira ntchito tsiku lililonse pa nthawi iliyonse. Koma zimenezi zingachititse kuti zikhale zovuta kuti musiyanitse ntchito yanu ndi zinthu zina zofunika kwambiri, kuphatikizapo banja lanu.
Zimene muyenera kudziwa
Zipangizo zamakono zingakuchititseni kuti muzigwira ntchito pa nthawi yomwe mukuyenera kumachita zinthu ndi banja lanu. Choncho foni, imelo, kapena meseji iliyonse yokhudza ntchito imene mungalandire pamene simuli kuntchito, ingakuchititseni kuganiza kuti kufunika kugwira ntchito.
“Zikuoneka kuti masiku ano n’zosatheka kuti munthu ufike pakhomo kuchokera kuntchito n’kuchita zinthu ndi banja lako, chifukwa umalandirabe maimelo komanso mafoni a kuntchito ndipo susamalanso za banja lako.”—Jeanette.
Kuti muzipeza nthawi yogwira ntchito komanso yochita zinthu ndi banja lanu, muyenera kuchitapo kanthu. Ngati simungakhale ndi dongosolo lochitira zinthu, ntchito yanu ikhoza kusokoneza banja lanu.
“Nthawi zambiri mwamuna kapena mkazi wako ndi amene amakhala woyamba kumunyalanyaza chifukwa umaganiza kuti, ‘Andimvetsa komanso andikhululukira. Ndicheza nayebe nthawi ina.’”—Holly.
Mfundo zothandiza kuti muzipeza nthawi yogwira ntchito komanso yochita zinthu zina
Muziona kuti banja lanu ndi lofunika kwambiri. Baibulo limanena kuti: “Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” (Mateyu 19:6) Ngati simungalole kuti munthu akulekanitseni ndi mwamuna kapena mkazi wanu, kodi mungalole kuti ntchito ikulekanitseni?
“Makasitomala ena amaona kuti chifukwa choti amakulipira, ndiye kuti uyenera kupezeka nthawi iliyonse imene akukufuna. Poganizira kuti banja langa ndi lofunika kwambiri, ndimawauza kuti sindipezeka pa nthawi yomwe sindikugwira ntchito, ndipo kuti ndiwadziwitsa mwansanga ndikayamba kugwira.”—Mark.
Dzifunseni kuti, ‘Kodi zochita zanga zimasonyeza kuti banja langa ndi lofunika kwambiri kuposa ntchito yanga?’
Muzikana ntchito ngati mukufunika kutero. Baibulo limanena kuti: “Nzeru zimakhala ndi anthu odzichepetsa.” (Miyambo 11:2) Kudzichepetsa kungakuthandizeni kuona kuti zingakhale bwino ngati mutakana kapena kupatsa anthu ena ntchito zina.
“Ndine pulambala, ndiye ngati munthu wina akufuna ndikamugwirire ntchito msangamsanga, amayamba kuda nkhawa. Ngati sindingathe kugwira ntchitoyo pa nthawi imene akufuna, ndimamuuza za munthu wina yemwe angagwire ntchitoyo.”—Christopher.
Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndine wokonzeka kukana ntchito yowonjezera ngati kuvomera ntchitoyo kungachititse mwamuna kapena mkazi wanga kuona kuti akunyalanyazidwa? Kodi mwamuna kapena mkazi wanga akuonanso choncho?’
Muzipeza nthawi yochita zinthu limodzi. Baibulo limanena kuti: “Chilichonse chili ndi nthawi yake.” (Mlaliki 3:1) Pamene muli wotanganidwa kwambiri ndi ntchito, m’pamene mukufunika kupeza nthawi yochita zinthu ndi mwamuna kapena mkazi wanu.
“Nthawi zambiri pamene tili otanganidwa kwambiri, timagwirizana kuti tichitire zinthu limodzi, kaya ndi kudya limodzi chakudya chamadzulo kapena kukayenda m’mbali mwa nyanja kumene sitingasokonezedwe.”—Deborah.
Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimakonza nthawi imene ndingachite zinthu ndi mwamuna kapena mkazi wanga popanda kusokonezedwa? Kodi mwamuna kapena mkazi wanga angayankhe bwanji?’
Muzithimitsa zipangizo zanu zamakono. Baibulo limanena kuti: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.” (Afilipi 1:10) Kodi nthawi zina mungamathimitse zipangizo zanu zamakono kuti musamasokonezedwe ndi mameseji kapena mafoni a kuntchito kwanu?
“Ndimayesetsa kuti ndisagwirenso ntchito ikakwana nthawi imene ndinasankha. Nthawiyo ikakwana, ndimatchera foni yanga m’njira yoti ndisalandirenso mauthenga.”—Jeremy.
Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimaona kuti foni yanga iyenera kukhala yoyatsa nthawi zonse kupangira ngati abwana anga kapena kasitomala angandifune? Kodi mwamuna kapena mkazi wanga angayankhe bwanji?’
Muzikhala wololera. Baibulo limanena kuti: “Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.” (Afilipi 4:5) Kunena zoona, nthawi zina ntchito ikhoza kukhudza banja lanu. Mwachitsanzo, mwina ntchito imene mwamuna kapena mkazi wanu amagwira imafuna kuti iye azipezekabe pa nthawi yomwe si ya ntchito. Musamayembekezere zambiri kwa mwamuna kapena mkazi wanuyo kuposa zimene angakwanitse.
“Mwamuna wanga amapanga bizinesi yaing’ono, ndipo nthawi zambiri amafunika kuchita zinthu zina zamwadzidzidzi pambuyo poweruka. Nthawi zina zimenezi sizindisangalatsa, koma sindidandaula kwambiri chifukwa choti timakhala ndi nthawi yambiri yochitira zinthu limodzi.”—Beverly.
Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimasonyeza kumuganizira mwamuna kapena mkazi wanga ngati ali ndi ntchito yambiri, posayembekezera zambiri kwa iye? Kodi mwamuna kapena mkazi wanga angayankhe bwanji?’
Mafunso othandiza pokambirana
Choyamba, aliyense wa inu angapeze mayankho a mafunso otsatirawa payekha. Kenako kambiranani mayankho anuwo pamodzi.
Kodi mwamuna kapena mkazi wanu anadandaulapo kuti mumagwira ntchito pamene muli pakhomo? Ngati ndi choncho, kodi mukuona kuti zimenezi ndi zoona?
Kodi ndi zinthu ziti zimene mukuona kuti mukufunika kusintha kuti muzitha kugwira ntchito komanso kuchita zinthu zina?
Kodi munayamba mwaganizapo kuti mwamuna kapena mkazi wanu amagwira ntchito pa nthawi yoti si ya ntchito? Ngati ndi choncho, kodi mungakumbukire nthawi imene anachita zimenezi?
Kodi mungakonde kuti mwamuna kapena mkazi wanu asinthe zinthu ziti pa nkhani yoonetsetsa kuti ntchito sikusokoneza mbali zina za moyo wanu?