Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Akakhala Wosakhulupirika

Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Akakhala Wosakhulupirika

Maria, yemwe amakhala ku Spain, anati: “Mwamuna wanga atandiuza kuti akufuna kundisiya kuti akakwatire kamtsikana, zinandipweteka kwambiri mumtima moti ndinkaona kuti bola kungofa. Ndinkaona kuti si chilungamo, makamaka ndikaganizira zinthu zambirimbiri zimene ndinamuchitira.”

Bill, yemwenso amakhala ku Spain, anati: “Mkazi wanga atandithawa, ndinkangoona ngati mbali ina ya thupi langa yafa. Ndinkaona kuti maloto ndi mapulani athu onse athera pompo. Nthawi zina ndinkaona ngati ndasiya kuda nazo nkhawa, koma pakangotha masiku angapo ndinkayambiranso kuda nkhawa kwambiri.”

ZIMAKHALA zowawa kwambiri, mkazi kapena mwamuna akachita zinthu zosakhulupirika m’banja. N’zoona kuti amuna kapena akazi ena amasankha kukhululukira mnzawoyo ngati wapepesa ndipo amayesetsa kuti ayambirenso kumakhala bwinobwino. * Koma kaya banjalo likhalapobe kapena ayi, wolakwiridwayo amamva ululu woopsa mumtima mwake. Ndiye kodi n’chiyani chingawathandize anthu oterewa kupirira?

MAVESI AMENE ANGAKUTHANDIZENI

Ngakhale kuti zimakhala zowawa mkazi kapena mwamuna akakhala wosakhulupirika, anthu ambiri amene zoterezi zawachitikirapo aona kuti Mawu a Mulungu amathandiza kwambiri. Mawu a Mulungu awathandiza kudziwa kuti Yehova amaona kulira kwawo ndipo nayenso amamva ululu.​—Malaki 2:13-16.

“Malingaliro osautsa atandichulukira mumtima mwanga, Mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.”​Salimo 94:19.

Bill ananena kuti: “Nditawerenga vesi limeneli, ndinkamva ngati Yehova akunditonthoza mokoma mtima ngati mmene bambo wachikondi amachitira.”

“Munthu wokhulupirika, mudzamuchitira mokhulupirika.”​Salimo 18:25.

Carmen, amene mwamuna wake anakhala wosakhulupirika kwa miyezi ingapo, anati: “Mwamuna wanga sankakhulupirika. Koma ndinkakhulupirira kuti Yehova akhalabe wokhulupirika kwa ine ndipo sandikhumudwitsa.”

“Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero . . . zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.”​Afilipi 4:6, 7.

Sasha ananena kuti: “Lemba limeneli ndinkaliwerenga mobwerezabwereza. Ndinkati ndikapemphera, Mulungu ankandipatsa mtendere wamumtima.”

Anthu onse amene tawatchula munkhaniyi, pa nthawi ina ankaona kuti palibenso chifukwa chokhalira ndi moyo. Koma anadalira Yehova ndipo mfundo za m’Baibulo zinawalimbikitsa. Bill anati: “Pamene zinkaoneka ngati palibenso chomwe chikuyenda, chikhulupiriro ndi chimene chinandithandiza. Zinali ngati ndikuyenda ‘m’chigwa cha mdima wandiweyani,’ koma Yehova anali nane.”​—Salimo 23:4.

^ ndime 4 Nkhani zofotokoza ngati munthu angasankhe kukhululukira kapenanso kusakhululukira mkazi kapena mwamuna wake, zikupezeka mu Galamukani! ya May 8, 1999, yamutu wakuti, “Pamene Mwamuna Kapena Mkazi Akhala Wosakhulupirika.”