Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mofanana ndi anthu awiri oyendetsa ndege, mwamuna ndi mkazi amafunika kukhala ndi zolinga zofanana

 MWAMUNA NDI MKAZI WAKE

2: Kuchita Zinthu Mogwirizana

2: Kuchita Zinthu Mogwirizana

ZIMENE ZIMACHITIKA

Mwamuna ndi mkazi wake akamachita zinthu mogwirizana, amakhala ngati anthu awiri oyendetsa ndege omwe ali ndi cholinga chimodzi. Ngakhale akakumana ndi mavuto, mwamuna kapena mkazi saganizira zayekha koma zomwe onse awiri angachite.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Chotero salinso awiri, koma thupi limodzi.”​—Mateyu 19:6.

A Christopher ananena kuti: “Mutu umodzi suzenza denga. Choncho kuti zinthu ziziyenda bwino m’banja, mwamuna ndi mkazi amafunika kuchitira zinthu limodzi.”

N’CHIFUKWA CHIYANI KUGANIZIRA NKHANIYI N’KOFUNIKA?

Banja likakumana ndi mavuto, mwamuna ndi mkazi omwe sachita zinthu mogwirizana amayamba kulimbana, m’malo mopeza njira yothetsera vutolo. Nkhani yaing’ono imakula mpaka kufika poipa kwambiri.

Alexandra ananena kuti: “Kuchita zinthu mogwirizana n’kofunika kwambiri m’banja. Zikanakhala kuti ine ndi mwamuna wanga, aliyense amangochita zake, tikanangokhala ngati anthu awiri okhala nyumba imodzi basi. Moti sitikanathanso kumakambirana zinthu zofunika.”

ZIMENE MUNGACHITE

DZIFUNSENI KUTI

  • Kodi ndikapeza ndalama, ndimangoona kuti ndi za ine ndekha?

  • Kodi ndimaona kuti ndimapeza mtendere ndikakhala ndekha popanda mwamuna kapena mkazi wanga?

  • Kodi sindikonda kucheza ndi achibale a mwamuna kapena a mkazi wanga, ngakhale kuti iyeyo amagwirizana nawo kwambiri?

ZOTI MUKAMBIRANE

  • Kodi ndi zinthu ziti zomwe timachitira limodzi monga banja?

  • Kodi tingafunike kukonza zinthu ziti?

  • Kodi tingatani kuti tiziyesetsa kuchitira zinthu limodzi?

ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI

  • Tiyerekeze kuti mukusewera mpira m’matimu awiri osiyana. M’malo moti aliyense azisewera m’timu yake, kodi pali zimene mungachite kuti nonse muzisewera m’timu imodzi?

  • M’malo moganiza kuti, ‘nditani kuti timu yanga iwine,’ muzidzifunsa kuti, ‘titani kuti timu yathu iwine?’

A Ethan ananena kuti: “Musamalimbane ndi kuti mupeze amene akulakwitsa ndi amene akulondola. Zimenezi si zofunika. Chofunika kwambiri ndi kukhala mwamtendere komanso mogwirizana ndi mnzanuyo.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”​—Afilipi 2:3, 4.