Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yamikani Yehova Ndipo Adzakudalitsani

Yamikani Yehova Ndipo Adzakudalitsani

“Yamikani Yehova, chifukwa iye ndi wabwino.”—SAL. 106:1.

1. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira Yehova?

TIYENERA kuyamikira Yehova chifukwa chakuti amatipatsa “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro.” (Yak. 1:17) Iye ndi M’busa wachikondi ndipo amatipatsa zinthu zonse zofunikira. (Sal. 23:1-3) Yehova amakhala “pothawira pathu ndi mphamvu yathu,” makamaka tikakumana ndi mavuto. (Sal. 46:1) Choncho pali zifukwa zambiri zotichititsa kumuyamikira ngati mmene anachitira wamasalimo amene analemba kuti: “Yamikani Yehova, chifukwa iye ndi wabwino. Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.”—Sal. 106:1.

Lemba la chaka cha 2015: “Yamikani Yehova, chifukwa iye ndi wabwino.”—Salimo 106:1

2, 3. (a) Kodi chingachitike n’chiyani tikayamba kukhala ndi mtima wosayamikira? (b) Kodi tikambirana mafunso ati m’nkhaniyi?

2 N’chifukwa chiyani ndi bwino kukambirana nkhani yoyamikira? Baibulo linaneneratu kuti anthu adzakhala osayamika m’masiku otsiriza ano. (2 Tim. 3:2) Ambiri sayamikira madalitso amene ali nawo. Mwina n’chifukwa chakuti amalonda amawalimbikitsa kuti azifuna zambiri ndiponso asamakhutire ndi zimene ali nazo. Ifenso tikhoza kuyamba mtima wosayamikawu. Tikhoza kukhala ngati Aisiraeli amene sankayamikira ubwenzi wawo ndi Yehova komanso sankayamikira madalitso amene anapatsidwa.—Sal. 106:7, 11-13.

3 Kodi n’chiyani chingachitike tikakumana ndi mavuto? Tikhoza kusokonezeka kwambiri n’kuiwala madalitso athu. (Sal. 116:3) Ndiyeno kodi tingatani kuti tikhalebe ndi mtima woyamikira? Nanga n’chiyani chingatithandize kukhalabe osangalala tikakumana ndi mavuto? M’nkhaniyi tipeza mayankho a mafunso amenewa.

‘INU YEHOVA, MWATICHITIRA ZINTHU ZAMBIRI’

4. Kodi tingatani kuti tikhalebe ndi mtima woyamikira?

4 Kodi tingatani kuti tikhalebe ndi mtima woyamikira? Tiyenera kuganizira madalitso amene Yehova watipatsa komanso mmene amatisonyezera chikondi. Wamasalimo anachita zimenezi ndipo anakhudzidwa kwambiri mumtima ndi zinthu zonse zabwino zimene Yehova anachita.—Werengani Salimo 40:5; 107:43.

5. Kodi tingaphunzire chiyani kwa mtumwi Paulo pa nkhani yokhala oyamikira?

5 Tingaphunzire zambiri kwa mtumwi Paulo pa nkhani yoyamikirayi. Iye ayenera kuti ankaganizira kwambiri madalitso ake. Tikutero chifukwa chakuti ankayamikira Yehova kuchokera pansi pa mtima. Paulo ankadziwa kuti kale anali munthu “wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake ndiponso wachipongwe.” Choncho ankayamikira kuti Mulungu ndiponso Khristu anamuchitira chifundo n’kumupatsa utumiki. (Werengani 1 Timoteyo 1:12-14.) Paulo ankayamikiranso Akhristu anzake chifukwa anali ndi makhalidwe abwino komanso ankatumikira Yehova mokhulupirika. Iye ankathokoza Yehova chifukwa cha zimenezi. (Afil. 1:3-5, 7; 1 Ates. 1:2, 3) Paulo akakumana ndi mavuto n’kuthandizidwa ndi Akhristu anzake, ankathokoza Yehova. (Mac. 28:15; 2 Akor. 7:5-7) N’chifukwa chake analimbikitsa Akhristu m’kalata yake kuti: “Sonyezani kuti ndinu oyamikira. . . . Pitirizani kuphunzitsana ndi kulangizana mwa masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu, ndi nyimbo zauzimu zogwira mtima.”—Akol. 3:15-17.

TIZIGANIZIRA MADALITSO ATHU NDIPONSO TIZIPEMPHERA

6. Kodi ndi madalitso ati ochokera kwa Yehova amene inuyo mumayamikira?

6 Kodi tingatsanzire bwanji Paulo pa nkhani yoyamikira? Nafenso tiyenera kuganizira zimene Yehova watichitira. (Sal. 116:12) Kodi mungayankhe bwanji munthu atakufunsani kuti: ‘Ndi madalitso ati ochokera kwa Yehova amene mumayamikira?’ Kodi mungatchule ubwenzi wamtengo wapatali umene muli nawo ndi Yehova? Kapena mungatchule mwayi wokhululukidwa machimo chifukwa chokhulupirira nsembe ya Khristu? Kodi mwina mungatchule abale ndi alongo amene anakuthandizani pa nthawi ya mavuto? N’zosachita kufunsa kuti ena anganene za mwamuna wawo, mkazi wawo kapena ana awo. Kuganizira madalitso ngati amenewa kungatilimbikitse kuti tiziyamikira Atate wathu wachikondi tsiku lililonse.—Werengani Salimo 92:1, 2.

7. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira Mulungu m’mapemphero athu? (b) Kodi kuyamikira Mulungu m’mapemphero athu kungatithandize bwanji?

7 Kuganizira kwambiri madalitso amene tili nawo kungatilimbikitse kuti tizipemphera kwa Yehova n’kumamuthokoza. (Sal. 95:2; 100:4, 5) N’zoona kuti anthu ambiri amangopemphera akafuna kupempha zinazake. Koma ife timadziwa kuti Yehova amasangalala tikamamuyamikira chifukwa cha zimene tili nazo. M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za mapemphero oyamikira amene anthu ena anapereka. Ena mwa anthuwa ndi Hana ndiponso Hezekiya. (1 Sam. 2:1-10; Yes. 38:9-20) Choncho, tiyenera kutsanzira atumiki okhulupirikawa amene anali ndi mtima woyamikira. Tizipemphera kwa Yehova poyamikira madalitso amene tili nawo. (1 Ates. 5:17, 18) Tikamatero, tidzakhala osangalala ndipo ubwenzi wathu ndi iye udzakhala wolimba.—Yak. 4:8.

Kodi ndi madalitso ati ochokera kwa Yehova amene mumayamikira? (Onani ndime 6 ndi 7)

8. Kodi n’chiyani chingatichititse kusiya kuyamikira zinthu zimene Yehova watichitira?

8 Tiyenera kusamala kuti tisasiye kuyamikira zinthu zabwino zimene Yehova amatichitira. Tikutero chifukwa chakuti anthu ochimwafe sitichedwa kuyamba mtima wosayamika. Tinatengera mtima umenewu kwa Adamu ndi Hava. Iwo anapatsidwa malo okongola kwambiri kuti azikhalamo. Anapatsidwanso chilichonse chofunika ndipo anali ndi mwayi wokhala ndi moyo wosatha. (Gen. 1:28) Koma sanayamikire madalitsowa. Mtima wofuna zonse unawatayitsa zonsezi. (Gen. 3:6, 7, 17-19) Popeza tili m’dziko la anthu osayamika, nafenso tikhoza kuiwala zimene Yehova watichitira. Tikhoza kuyamba kuona kuti ubwenzi wathu ndi iye ndi wosafunika. Tingasiyenso kuyamikira mwayi wokhala m’gulu la abale padziko lonse. Tikhozanso kumangoganizira kwambiri zinthu za m’dzikoli, zimene zikupita posachedwapa. (1 Yoh. 2:15-17) Kuti tisayambe kuchita zimenezi, tiyenera kuganizira madalitso amene tili nawo komanso kuyamikira Yehova chifukwa chotilola kukhala m’gulu lake.—Werengani Salimo 27:4.

TIKAKUMANA NDI MAVUTO

9. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira madalitso athu tikakumana ndi mavuto?

9 Mtima woyamikira ungatithandize kupirira tikakumana ndi mavuto aakulu. Tingavutike kwambiri tikakumana ndi mavuto monga matenda aakulu, imfa ya mnzathu, tsoka la chilengedwe mwinanso kusakhulupirika kwa mwamuna kapena mkazi wathu. Kuganizira madalitso athu kungatilimbikitse tikakumana ndi zinthu ngati zimenezi. Tiyeni tione zitsanzo pa nkhaniyi.

10. Kodi mtima woyamikira madalitso unathandiza bwanji mlongo wina?

10 Mpainiya wina ku United States, dzina lake Irina, * anali pa banja ndi m’bale amene anali mkulu. Koma m’baleyo anakhala wosakhulupirika ndipo anamusiya. N’chiyani chinathandiza Irina kuti azitumikirabe Yehova mokhulupirika atatsala ndi ana ake? Iye anati: “Ndikuyamikira kwambiri kuti Yehova amandiganizira ndiponso amandisamalira. Tsiku lililonse ndimaganizira zinthu zabwino zimene wandichitira. Ndimaona kuti ndi mwayi waukulu kudziwidwa komanso kukondedwa ndi Atate wathu wakumwamba. Ndikudziwa kuti sadzandisiya.” Irina wakumana ndi mavuto aakulu koma amakhalabe wosangalala. Izi zimamuthandiza komanso zimalimbikitsa anthu ena.

11. Kodi n’chiyani chinathandiza mlongo wina kuti apirire matenda aakulu?

11 Mlongo wina wa ku Asia, dzina lake Kyung-sook, anachita upainiya limodzi ndi mwamuna wake kwa zaka zoposa 20. Ndiyeno mosayembekezereka anapezeka ndi khansa ya m’mapapo n’kuuzidwa kuti amwalira pasanathe miyezi itatu kapena 6. Iye ndi mwamuna wake anali atakumana ndi mavuto osiyanasiyana koma sankayembezera kuti angadwale choncho. Mlongoyu anati: “Ndinakhudzidwa kwambiri nditamva za matendawa. Ndinkachita mantha kwambiri ndipo ndinkaona kuti chabwino palibe.” Kodi n’chiyani chamuthandiza? Iye anati: “Tsiku lililonse ndisanagone ndimapita pamalo andekha n’kupemphera mokweza. Ndimayamikira zinthu zabwino 5 zimene zandichitikira tsikulo. Zimenezi zimandikhazika mtima m’malo ndipo zimandilimbikitsa kuchita zinthu zosonyeza kuti ndimakonda Yehova.” Ananenanso kuti: “Ndazindikira kuti Yehova amatithandiza tikakumana ndi mavuto. Ndimaonanso kuti madalitso amene tili nawo ndi ambiri poyerekezera ndi mavuto athu.”

Sheryl ndi mchimwene wake John, yemwe anapulumukanso (Onani ndime 13)

12. N’chiyani chinathandiza Jason pamene mkazi wake anamwalira?

12 Chitsanzo china ndi Jason amene amatumikira ku ofesi ya nthambi ina ku Africa. Iye wakhala mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka zoposa 30. Jason anati: “Mkazi wanga anamwalira zaka 7 zapitazo ndipo zimandipwetekabe kwambiri mumtima. Ndimakhumudwa kwambiri ndikaganizira zimene anakumana nazo chifukwa cha matenda a khansa.” N’chiyani chimathandiza Jason? Iye anati: “Pa nthawi ina ndinkaganizira zinthu zosangalatsa zimene ndinkachita ndi mkazi wanga ndipo nthawi yomweyo ndinapemphera kwa Yehova pomuthokoza chifukwa chokumbukira zimenezo. Ndinayamba kupeza mtendere mumtima ndipo kuyambira nthawi imeneyo ndakhala ndikuthokoza Yehova pokumbukira zinthu zosangalatsazi. Mtima woyamikira wandithandiza kukhala wosangalala. Zimandipwetekabe mumtima kuti mkazi wanga anamwalira. Koma ndimayamikira Yehova chifukwa chakuti ndinali ndi banja labwino komanso chifukwa choti ndinkakhala ndi munthu wokonda kwambiri Yehova. Zimenezi zimandithandiza kwambiri.”

“Ndimayamikira kuti Mulungu wanga ndi Yehova.”—Sheryl

13. N’chiyani chinathandiza Sheryl pamene abale ake ambiri anafa?

13 Chakumapeto kwa chaka cha 2013, ku Philippines kunachitika chimphepo choopsa. M’banja lina munafa bambo, mayi ndi ana atatu. Mwana wina wa m’banjali dzina lake Sheryl anapulumuka ndipo pa nthawiyo anali ndi zaka 13. Iye anati: “Nyumba yathu ndi katundu yense zinawonongeka ndipo abale anga ambiri anafa.” Kodi n’chiyani chinathandiza Sheryl pa nthawiyi? Iye ali ndi mtima woyamikira ndipo amaganizira kwambiri madalitso ake. Anati: “Ndinaona zonse zimene abale ndi alongo anachita pothandiza anthu amene anakhudzidwa ndi tsokali. Ndinazindikiranso kuti abale padziko lonse akundipempherera.” Ananenanso kuti: “Ndimayamikira kuti Mulungu wanga ndi Yehova. Nthawi zonse amatipatsa zinthu zimene tikufunikira.” Zonsezi zikusonyeza kuti kuganizira madalitso athu kumathandiza kuti tisamade nkhawa kwambiri. Mtima woyamikira ungatithandize kuti tisafooke ngakhale titakumana ndi mavuto oopsa.—Aef. 5:20; werengani Afilipi 4:6, 7.

“INE NDIDZAKONDWERABE MWA YEHOVA”

14. Tchulani zinthu zosangalatsa zimene tikuyembekezera. (Onani chithunzi patsamba 8.)

14 Kuyambira kale, anthu a Yehova akhala akusangalala kwambiri akamaganizira madalitso awo. Mwachitsanzo, Aisiraeli atangopulumutsidwa kwa Farao ndi asilikali ake pa Nyanja Yofiira, anasangalala ndipo anaimba nyimbo zotamanda ndiponso zothokoza Mulungu. (Eks. 15:1-21) Nafenso timasangalala kwambiri tikamaganizira zoti posachedwapa tidzapulumutsidwa ndipo mavuto athu onse adzatheratu. (Sal. 37:9-11; Yes. 25:8; 33:24) Tidzasangalala kwambiri Yehova akadzawononga adani ake n’kutilola kuti tikhale m’dziko latsopano lamtendere komanso lachilungamo. Kunena zoona, pa nthawiyo tidzathokoza kwambiri Yehova.—Chiv. 20:1-3; 21:3, 4.

15. Kodi inuyo mukufunitsitsa kuchita chiyani m’chaka chonse cha 2015?

15 M’chaka cha 2015, tikuyembekezeranso madalitso ambiri ochokera kwa Yehova. N’zoona kuti tikhoza kukumananso ndi mavuto ena. Koma kaya tikumana ndi zotani, chomwe tikudziwa n’chakuti Yehova sadzatisiya. (Deut. 31:8; Sal. 9:9, 10) Iye adzatipatsa zonse zofunikira kuti tizimutumikira mokhulupirika. Choncho tiyeni tikhale ndi maganizo ngati a Habakuku amene ananena kuti: “Ngakhale mkuyu usaphukire maluwa, mtengo wa mpesa usabale zipatso, mtengo wa maolivi ulephere kubala zipatso, munda wa m’mphepete mwa phiri usatulutse chakudya, nkhosa ndi ng’ombe zithemo m’khola, ine ndidzakondwerabe mwa Yehova ndipo ndidzasangalala mwa Mulungu wachipulumutso changa.” (Hab. 3:17, 18) Tiyeni tipitirize kuganizira madalitso amene Yehova watipatsa n’kumatsatira lemba la chaka cha 2015 lakuti: “Yamikani Yehova, chifukwa iye ndi wabwino.”—Sal. 106:1.

^ ndime 10 Tasintha mayina ena m’nkhaniyi.