Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Lolani Kuti Yehova Alimbitse Ndiponso Kuteteza Banja Lanu

Lolani Kuti Yehova Alimbitse Ndiponso Kuteteza Banja Lanu

“Yehova akapanda kulondera mzinda, alonda amakhala maso pachabe.”—SAL. 127:1b.

1, 2. (a) N’chiyani chinalepheretsa Aisiraeli 24,000 kulandira madalitso? (b) N’chifukwa chiyani nkhani imeneyi imatikhudza kwambiri?

AISIRAELI atangotsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, amuna ambiri anachita “chiwerewere ndi akazi a ku Mowabu.” Izi zinachititsa kuti anthu 24,000 aphedwe ndi Yehova. Ndiye tangoganizani. Aisiraeliwo atangotsala pang’ono kulandira madalitso awo, anakopeka ndi zoipa n’kuwonongedwa.—Num. 25:1-5, 9.

2 Nkhani imeneyi inalembedwa ‘kuti itichenjeze ifeyo amene mapeto a nthawi zino atifikira.’ (1 Akor. 10:6-11) Panopa tili kumapeto kwenikweni kwa “masiku otsiriza.” Posachedwapa tilowa m’dziko latsopano. (2 Tim. 3:1; 2 Pet. 3:13) Chomvetsa chisoni n’chakuti atumiki a Mulungu ena asiya kukhala tcheru. Iwo achita chiwerewere n’kukumana ndi mavuto oopsa. Ngati anthu oterewa salapa, akhoza kulephera kulandira madalitso osatha amene tikuyembekezera.

3. N’chifukwa chiyani anthu ayenera kutsatira malangizo a Yehova kuti ateteze banja lawo? (Onani chithunzi pamwambapa.)

3 Masiku ano, chiwerewere chili paliponse choncho anthu  ayenera kutsatira malangizo a Yehova kuti ateteze banja lawo. (Werengani Salimo 127:1.) Tiyeni tikambirane zimene anthu angachite kuti alimbitse mabanja awo. Tikambirana za kuteteza mtima, kulimbitsa ubwenzi ndi Mulungu, kuvala umunthu watsopano, kulankhulana bwino ndiponso kuganizira zofuna za mwamuna kapena mkazi wathu pa nkhani ya kugonana.

TETEZANI MTIMA WANU

4. N’chiyani chachititsa kuti Akhristu ena agwere mumsampha wa chiwerewere?

4 Kodi Mkhristu angagwere bwanji mumsampha wa chiwerewere? Nthawi zambiri amayamba ndi kuyang’ana zinthu zosayenera. Yesu anati: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.” (Mat. 5:27, 28; 2 Pet. 2:14) Akhristu ambiri achita tchimo chifukwa chakuti anayamba kuonera kapena kuwerenga zinthu zolaula. Ena amaonera zinthu zimenezi m’mafilimu, m’masewero, pa TV kapena pa Intaneti. Ena amapita kumadisiko kapena kumalo ena amene amagwiranagwirana.

5. N’chifukwa chiyani tiyenera kuteteza mtima wathu?

5 Ena amachita chiwerewere chifukwa choyamba kucheza ndi anthu olakwika. Anthu ambiri m’dzikoli ali ndi mtima wachiwerewere ndipo sadziletsa. Choncho popeza mtima wathu ndi wonyenga, n’zosavuta kuyamba kukopana ndi munthu amene sitili naye pa banja. (Werengani Yeremiya 17:9, 10.) Yesu anati: ‘Maganizo oipa, za kupha anthu, za chigololo, za dama zimachokera mumtima.’—Mat. 15:19.

6, 7. (a) Kodi mtima wonyenga ungachititse munthu kuchita zinthu ziti? (b) Kodi tingapewe bwanji kuchita zinthu zolakwika?

6 Anthu amene akukopana akhoza kuyamba kukambirana zinthu zimene ayenera kuuza mwamuna kapena mkazi wawo yekha. Kenako amayesetsa kupeza mpata woti azicheza. Amacheza kawirikawiri ndipo zimakhala ngati angokumana mwangozi. Akayamba kukondana kwambiri zimavuta kudziwa malire ochitira zinthu. Akapitiriza kuchita zimenezi amavutika kuti asiye ngakhale kuti pansi pa mtima amadziwa kuti n’zolakwika.—Miy. 7:21, 22.

7 Iwo amaiwala mfundo za Yehova n’kuyamba kugwirana manja, kusisitana kapena kuchita zinthu zina zoyenera anthu okwatirana okha. Iwo ‘amakopedwa ndi kukodwa m’chilakolako chawo.’ Ndiyeno chilakolakocho chikakula, amachita chiwerewere. (Yak. 1:14, 15) Zimenezi n’zomvetsa chisoni kwambiri. Anthu akhoza kupewa zonsezi ngati atalola Yehova kuwathandiza kuti aziona banja mmene iye amalionera. Koma kodi angachite bwanji zimenezi?

MUZILIMBITSA UBWENZI WANU NDI MULUNGU

8. Kodi ubwenzi ndi Yehova umathandiza bwanji kuti munthu asayambe khalidwe loipa?

8 Werengani Salimo 97:10. Ubwenzi ndi Yehova umathandiza kuti munthu asayambe khalidwe loipa. Tikamaphunzira makhalidwe abwino a Yehova, timayesetsanso ‘kumutsanzira monga ana ake okondedwa ndipo timayendabe m’chikondi.’ Tikatero timatha kupewa “dama ndi chonyansa chamtundu uliwonse.” (Aef. 5:1-4) Akhristu amayesetsa kuti ukwati wawo ukhale wolemekezeka  ndiponso wosaipitsidwa chifukwa amadziwa kuti “Mulungu adzaweruza adama ndi achigololo.”—Aheb. 13:4.

9. (a) Kodi Yosefe anatani atayesedwa ndi mkazi wa bwana wake? (b) Kodi tikuphunzirapo chiyani pa chitsanzo cha Yosefe?

9 Akhristu ena amayamba khalidwe loipa chifukwa chocheza ndi anzawo akuntchito pambuyo poweruka. Komatu munthu akhoza kuyesedwanso pa nthawi ya ntchito ngati mmene zinalili ndi Yosefe. Tsiku lililonse mkazi wa bwana wake ankamunyengerera. Tsiku lina “mkaziyo anam’gwira malaya mnyamatayo n’kumuuza kuti: ‘Ugone nane basi!’” Koma Yosefe anathawa. Kodi n’chiyani chinathandiza Yosefe pa nthawiyo? Iye sankafuna kusokoneza ubwenzi wake ndi Mulungu. Izi zinachititsa kuti achotsedwe ntchito n’kumangidwa pa mlandu womunamizira koma Yehova anamudalitsa. (Gen. 39:1-12; 41:38-43) Kaya tili kuntchito kapena kwatokha, tiyenera kupewa kuchita zinthu zimene zingatigwetsere mumsampha wa chiwerewere.

VALANI UMUNTHU WATSOPANO

10. Kodi umunthu watsopano ungatiteteze bwanji?

10 Anthu amene ali pa banja ayenera kuvala umunthu watsopano kuti banja lawo litetezeke. Tikutero chifukwa umunthuwu “unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndipo umatsatira zofunika pa chilungamo chenicheni ndi pa kukhulupirika.” (Aef. 4:24) Anthu amene amavala umunthu watsopanowu ‘amachititsa ziwalo za thupi lawo kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa, chilakolako cha kugonana, chikhumbo choipa ndi kusirira kwa nsanje.’ (Werengani Akolose 3:5, 6.) Mawu akuti ‘kuchititsa ziwalo kukhala zakufa’ amasonyeza kuti tiyenera kuchita zinthu mwamphamvu kwambiri kuti tilimbane ndi zilakolako zoipa. Tiyenera kupeweratu chilichonse chimene chingatichititse kulakalaka kugonana ndi munthu amene sitili naye pa banja. (Yobu 31:1) Tikamayesetsa kuchita zimene Mulungu amafuna, timayamba ‘kunyansidwa ndi choipa n’kugwiritsitsa chabwino.’—Aroma 12:2, 9.

11. Kodi umunthu watsopano ungateteze bwanji banja?

11 Munthu amene wavala umunthu watsopano amatsanzira makhalidwe a Yehova. (Akol. 3:10) Banja limakhala lotetezeka komanso limadalitsidwa ngati onse avala makhalidwe monga “chifundo chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima.” (Akol. 3:12) Banja lawo limakhalanso logwirizana ngati onse alola kuti ‘mtendere wa Khristu uzilamulira m’mitima yawo.’ (Akol. 3:15) Anthu amene ali pa banja akakhala achifundo, amafunitsitsa ‘kukhala patsogolo posonyezana ulemu.’—Aroma 12:10.

12. Kodi ndi makhalidwe ati amene mumaona kuti ndi ofunika m’banja?

12 M’bale wina dzina lake Sid anafunsidwa zimene zathandiza kuti banja lake likhale losangalala. Iye anayankha kuti: “Nthawi zonse takhala tikuyesetsa kusonyezana chikondi. Taonanso kuti kufatsa n’kofunika kwambiri.” Mkazi wake dzina lake Sonja akugwirizana ndi zimenezi ndipo ananenanso kuti: “Kukoma mtima n’kofunikanso. Timayesetsanso kukhala odzichepetsa ngakhale kuti zimativuta nthawi zina.”

 MUZILANKHULANA BWINO

13. Fotokozani zinthu zimene zingathandize kuti banja likhale lolimba.

13 Banja limakhala lolimba kwambiri ngati anthu amalankhulana mwaulemu. Zimakhala zomvetsa chisoni kuona anthu akulankhula mwaulemu kwa anthu osawadziwa kuposa mmene amachitira ndi mwamuna kapena mkazi wawo. Anthu m’banja akhoza kusokoneza ubwenzi wawo ngati polankhulana amasonyeza ‘kuwawidwa mtima, njiru, kupsa mtima, mkwiyo ndiponso ngati amalalata kapena kunena mawu achipongwe.’ (Aef. 4:31) Kuimbana mlandu kapena kunyozana kumasokonezanso banja. Choncho, mwamuna ndi mkazi ayenera kulankhulana mokoma mtima komanso mwachifundo kuti alimbitse ubwenzi wawo.—Aef. 4:32.

14. Kodi tiyenera kupewa chiyani kuti banja lathu likhale lolimba?

14 Baibulo limanena kuti pali “nthawi yokhala chete.” (Mlal. 3:7) Lembali silitanthauza kuti ngati pali vuto tizingokhala duu osalankhulana. Mkazi wina ku Germany anati: “Kukhala duu pa nthawi ngati imeneyi kumasokoneza mnzanu.” Koma ananenanso kuti: “N’zoona kuti kuugwira mtima pamene takhumudwa n’kovuta koma si bwino kungolankhulapo chilichonse chimene chabwera m’mutu mwathu. Zimene mungalankhulezo zikhoza kupweteka kwambiri mnzanuyo komanso kuwonjezera vutolo.” Ngati pali vuto, mwamuna ndi mkazi sayenera kusiya kulankhulana. Koma polankhulana, ayenera kupewa kukalipirana. Aziyesetsa kuthetsa msanga mavuto popanda kukangana. Akatero banja lawo lidzakhala lolimba.

15. Kodi kulankhulana bwino kungathandize bwanji m’banja?

15 Banja limalimbanso ngati mwamuna ndi mkazi amakambirana momasuka zimene zili mumtima mwawo. Tiyenera kusamala ndi zimene timalankhula komanso mmene timalankhulira. Choncho ngakhale  zinthu zitavuta kwambiri, tiyenera kusankha bwino mawu ndiponso kuwalankhula mwaulemu. Tikatero, mnzathuyo sadzavutika kutimvetsera. (Werengani Akolose 4:6.) Kulankhulana bwino kumathandiza kuti banja liziyenda bwino. Choncho nthawi zonse tizilankhula mawu ‘olimbikitsa amene angasangalatse’ mwamuna kapena mkazi wathu.—Aef. 4:29.

Kulankhulana bwino kumathandiza kuti banja likhale lolimba (Onani ndime 15)

MUZIGANIZIRA ZOFUNA ZA MWAMUNA KAPENA MKAZI WANU

16, 17. N’chifukwa chiyani aliyense ayenera kuganizira zofuna za mnzake m’banja?

16 Anthu angalimbitsenso banja lawo akamaganizira zofuna za mnzawo kuposa zofuna zawo. (Afil. 2:3, 4) Amuna ndi akazi ayenera kuganizira zimene mnzawo angafune pa nkhani yosonyezana chikondi komanso kugonana.—Werengani 1 Akorinto 7:3, 4.

17 Anthu ena safuna kuchita zinthu zina zosonyezana chikondi ndipo amuna ena amaganiza kuti mwamuna weniweni sachita zimenezi. Koma Baibulo limati: “Amuna, pitirizani kukhala ndi akazi anu mowadziwa bwino.” (1 Pet. 3:7) Amuna ayenera kukumbukira kuti kupereka mangawa kumatanthauza zambiri osati kungogonana. Mkazi akhoza kusangalala pogonana ngati mwamuna wake amamusonyeza chikondi nthawi zonse osati pa nthawi yogonana yokha. Anthu onse amakhala osangalala ngati amasonyezana chikondi ndiponso kuganizirana.

18. Kodi amuna ndi akazi angalimbitse bwanji banja lawo?

18 N’zoona kuti munthu amene wakhala wosakhulupirika m’banja amakhala wolakwa. Koma kusasonyezana chikondi m’banja kungachititse kuti wina afunefune munthu wina amene angamusonyeze chikondicho. (Miy. 5:18; Mlal. 9:9) N’chifukwa chake Baibulo limalimbikitsa anthu apabanja kuti: “Musamanane, kupatulapo ngati mwagwirizana kuimitsa kaye mangawawo kwa nthawi yodziwika . . . kuopera kuti Satana angapitirize kumakuyesani mukalephera kudzigwira.” (1 Akor. 7:5) Zingakhale zomvetsa chisoni kwambiri ngati anthu apabanja alola kuti ayesedwe ndi Satana chifukwa ‘cholephera kudzigwira’ ndipo wina n’kuchita chigololo. Koma banja lingakhale lolimba ngati aliyense amayesetsa kuti ‘asamafune zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina.’ Choncho ayenera kupereka mangawa posonyeza kuti amakonda kwambiri mnzake komanso amamuganizira.—1 Akor. 10:24.

PITIRIZANI KUTETEZA BANJA LANU

19. Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani? Perekani chifukwa.

19 Posachedwapa tilowa m’dziko latsopano. Choncho kukopeka ndi zilakolako zathu zoipa kungakhale koopsa kwambiri chifukwa tikhoza kukhala ngati Aisiraeli 24,000 amene anaphedwa kuchigwa cha Mowabu aja. Pambuyo pofotokoza nkhani imeneyi, Mawu a Mulungu amanena kuti: “Amene akuyesa kuti ali chilili asamale kuti asagwe.” (1 Akor. 10:12) Choncho tiyeni tikhalebe okhulupirika kwa Yehova komanso kwa mwamuna kapena mkazi wathu n’cholinga choti banja lathu likhale lolimba. (Mat. 19:5, 6) Panopa, tiyenera kuyesetsa kwambiri kuchita ‘chilichonse chotheka kuti Yehova adzatipeze opanda banga, opanda chilema ndiponso tili mu mtendere.’—2 Pet. 3:13, 14.