Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mulungu Azikutsogolerani M’zinthu Zonse

Mulungu Azikutsogolerani M’zinthu Zonse

 Mulungu Azikutsogolerani M’zinthu Zonse

“Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu ku nthawi za nthawi: Adzatitsogolera kufikira imfa.”​—SAL. 48:14.

1, 2. Kodi ndi chifukwa chiyani tiyenera kudalira Yehova kutitsogolera osati nzeru zathu, ndipo tikambirana mafunso otani?

NDI zosavuta kudzinyenga mwa kuganiza kuti zinthu zopanda pake kapena zoipa ndi zabwinobwino. (Miy. 12:11) Tikamalakalaka kuchita zinthu zimene Mkhristu sayenera kuchita, nthawi zambiri mtima wathu umatipatsa zifukwa zooneka ngati zabwino zakuti tichite zimene tikulakalakazo. (Yer. 17:5, 9) Ndiye chifukwa chake wamasalmo mwanzeru anapemphera kwa Yehova kuti: “Tumizirani kuunika kwanu ndi choonadi chanu zinditsogolere.” (Sal. 43:3) Iye sanadalire nzeru zake zokhala ndi malire, koma anadalira Yehova ndipo anachita bwino chifukwa kulibenso wina amene akanamutsogolera bwino. Mofanana ndi wamasalmo, ifenso tiyenera kudalira Mulungu kuti azititsogolera.

2 Koma kodi ndi chifukwa chiyani tiyenera kudalira Yehova kutitsogolera kuposa wina aliyense? Kodi ndi liti pamene timafunika kutsogoleredwa ndi iye? Kodi tiyenera kukhala ndi makhalidwe otani kuti iye atitsogolere, ndipo kodi Yehova amagwiritsa ntchito chiyani potitsogolera masiku ano? Mafunso ofunika kwambiri amenewa ayankhidwa mu nkhani ino.

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kudalira Yehova Kutitsogolera?

3-5. Tchulani zifukwa zimene zimatipatsa chidaliro chonse chakuti Yehova angatitsogolere.

3 Yehova ndi Atate wathu wakumwamba.  (1 Akor. 8:6) Amatidziwa bwino aliyense payekha ndipo amaona zimene zili mu mtima mwathu. (1 Sam. 16:7; Miy. 21:2) Mfumu Davide inauza Mulungu kuti: “Inu mudziwa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga, muzindikira lingaliro langa muli kutali. Pakuti asanafike mawu pa lilime langa, taonani, Yehova, muwadziwa onse.” (Sal. 139:2, 4) Popeza kuti Yehova amatidziwa bwino choncho, kodi tingakayikirenso zakuti amadziwanso zinthu zimene zingakhale zabwino kwa ife? Pajanso Yehova ndi wanzeru zonse. Amaona zonse, amaona zinthu zimene anthu sangaone, ndipo amadziwa mapeto ake a zinthu, ngakhale zinthuzo zisanayambe kuchitika. (Yes. 46:9-11; Aroma 11:33) Iye ndi “Mulungu wanzeru yekhayo.”​—Aroma 16:27.

4 Ndiponso, Yehova amatikonda ndipo amatifunira zabwino. (Yoh. 3:16; 1 Yoh. 4:8) Iye ndi Mulungu wachikondi, ndipo amatipatsa zinthu mowolowa manja. Wophunzira Yakobe analemba kuti: “Mphatso iliyonse yabwino ndi mtulo uliwonse wangwiro zimachokera kumwamba, pakuti zimatsika kuchokera kwa Atate wa zounika zonse zakuthambo.” (Yak. 1:17) Anthu amene amafuna kuti Mulungu aziwatsogolera amapindula kwambiri chifukwa iye ali ndi mtima wopatsa.

5 Chinanso, Yehova ndi wamphamvuyonse. Pankhani imeneyi, wamasalmo anati: “Iye amene akhala pansi m’ngaka yake ya Wam’mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse. Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndim’khulupirira.” (Sal. 91:1, 2) Ife tikamatsatira pamene Yehova akutitsogolera, timakhala tikuthawira kwa Mulungu amene salephera. Ngakhale tikumane ndi chitsutso, Yehova amatithandiza. Iye sangatigwiritse mwala. (Sal. 71:4, 5; Werengani Miyambo 3:19-26.) Zoonadi, Yehova amadziwa zinthu zimene zingakhale zabwino kwa ife, amatifunira zabwino ndipo ali ndi mphamvu yotipatsa zinthu zabwino. Kungakhale kupusa kwambiri ngati tikana kutsogoleredwa ndi iye. Koma kodi ndi liti pamene timafunika kutsogoleredwa?

Kodi Ndi Liti Pamene Timafunika Kutsogoleredwa?

6, 7. Kodi ndi liti pamene timafunika kutsogoleredwa ndi Yehova?

6 Kunena chilungamo, timafunikira Mulungu kutitsogolera pamoyo wathu wonse, kuyambira tili ana mpaka kukalamba. Wamasalmo anati: “Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu ku nthawi za nthawi: Adzatitsogolera kufikira imfa.” (Sal. 48:14) Mofanana ndi wamasalmo, Akhristu anzeru sasiya kuyang’ana kwa Mulungu kuti awatsogolere.

7 Koma pamakhala nthawi zina pamene timafunikira thandizo kwambiri. Mwachitsanzo, timakumana ndi masautso monga chizunzo, matenda aakulu, kapena kuchotsedwa ntchito. (Sal. 69:16, 17) Tikakumana ndi mavuto oterewa, zimakhala bwino kuyang’ana kwa Yehova, tili ndi chikhulupiriro chakuti iye adzatipatsa mphamvu kuti tipirire ndipo adzatithandiza kusankha zochita mwanzeru. (Werengani Salmo 102:17.) Timafunikanso kuthandizidwa pa zinthu zina. Mwachitsanzo, tikamauza anzathu za uthenga wabwino wa Ufumu, timafunika kutsogoleredwa ndi  Yehova kuti ulaliki wathuwo ukhale wogwira mtima. Ndipo nthawi iliyonse imene tifunikira kupanga chosankha, kaya ndi pa zosangalatsa, kavalidwe ndi kudzikongoletsa, mabwenzi, ntchito yolembedwa, maphunziro kapena china chilichonse, sitingachite mwanzeru pokhapokha ngati tatsatira malangizo a Yehova. Kunena zoona, palibe nthawi imene tinganene kuti sitifunikira kutsogoleredwa.

Si Nzeru Kukana Kutsogoleredwa ndi Mulungu

8. Kodi Hava anasonyeza chiyani mwa kudya chipatso choletsedwa?

8 Tisaiwale kuti timafunika kutsatira malangizo a Yehova mwa kufuna kwathu. Mulungu satikakamiza ngati sitikufuna kutsogoleredwa ndi iye. Munthu woyamba amene anakana kutsogoleredwa ndi Yehova anali Hava, ndipo zimene anachitazo zimasonyeza kuti ngati munthu sanasankhe bwino, pamakhala mavuto. Ganiziraninso kukula kwa nkhani imeneyi. Hava anadya chipatso choletsedwa chifukwa anafuna ‘kukhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.’ (Gen. 3:5) Mwa kuchita zimenezi, iye anafuna kulanda udindo wa Mulungu. Anafuna kuti azichita kusankha yekha zabwino ndi zoipa m’malo motsatira malangizo a Yehova. Choncho, anakana ulamuliro wa Yehova. Sanafune kuti wina aliyense azimuuza zochita. Nayenso mwamuna wake Adamu, anatsatira njira yachipanduko imeneyi.​—Aroma 5:12.

9. Kodi tikamakana malangizo a Yehova timakhala tikusonyeza chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani kutero kuli kupanda nzeru?

9 Ngati ifenso masiku ano sitikutsatira malangizo a Yehova, ndiye kuti tikukana ulamuliro wake. Mwachitsanzo, taganizirani za munthu amene ali ndi chizolowezi choonera zinthu zolaula. Ngati munthuyo ali mu mpingo wachikhristu, ndiye kuti amadziwa malangizo a Yehova pankhani imeneyi. Zinthu zonyansa siziyenera kutchulidwa n’komwe. Ndiyeno kuli bwanji kuziyang’ana mwachidwi zinthuzo, mtima uli dyokodyoko? (Aef. 5:3) Mwa kunyalanyaza malangizo a Yehova, munthuyo amakhala akukana ulamuliro ndi umutu wa Yehovayo. (1 Akor. 11:3) Kuchita zimenezi ndi kupanda nzeru, chifukwa Yeremiya anati, “sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.”​—Yer. 10:23.

10. Kodi ndi chifukwa chiyani tiyenera kusamala ndi mmene timagwiritsira ntchito ufulu wathu wosankha?

10 Anthu ena sangagwirizane ndi mawu a Yeremiya. Iwo angaganize kuti popeza Yehova anatipatsa ufulu wosankha, sangatiimbe mlandu ndi mmene taugwiritsira ntchito ufuluwo. Koma musaiwale kuti ufulu wosankha ndi mphatso komanso udindo. Timayankha mlandu kwa Mulungu pazinthu zomwe timasankha kunena ndi kuchita. (Aroma 14:10) Yesu anati: “Pakamwa pamalankhula zosefukira mu mtima.” Iye anatinso: “Maganizo oipa, za kupha anthu, za chigololo, za dama, za umbala, maumboni onama, zonyoza Mulungu zimachokera mu mtima.” (Mat. 12:34; 15:19) Choncho, zimene timanena ndi kuchita zimasonyeza zimene zili mu mtima wathu. Zimasonyeza kuti ndife munthu wamtundu wanji kwenikweni. N’chifukwa chake Mkhristu wanzeru amafuna kuti Yehova azimutsogolera m’zinthu zonse. Zikatero, Yehova amaona munthuyo kukhala ‘woongoka mtima’ ndipo ‘amamuchitira chokoma.’​—Sal. 125:4.

11. Kodi zimene zinachitikira Aisiraeli zikutiphunzitsa chiyani?

11 Kumbukirani zimene zinachitikira Aisiraeli. Iwo akasankha mwanzeru ndi kumvera malamulo a Yehova, iye anali kuwateteza. (Yos. 24:15, 21, 31) Koma nthawi zambiri, iwo sanagwiritse ntchito bwino ufulu wawo. M’nthawi ya Yeremiya, Yehova anati za iwo: ‘Sanamvera, sanatchera khutu, koma anayenda m’upo ndi m’kuuma kwa mtima wawo woipa, nabwerera cham’mbuyo osayenda m’tsogolo.’ (Yer. 7:24-26) Zimenezitu zinali zomvetsa chisoni. Ifeyo tisalole kuuma  mtima kapena zilakolako zathu kutilepheretsa kutsatira malangizo a Yehova ndi kuyamba kuyendera nzeru zathu, mpaka ‘kumabwerera cham’mbuyo m’malo mopita m’tsogolo.’

Kodi Chimafunika Ndi Chiyani Kuti Tizitsatira Uphungu wa Mulungu?

12, 13. (a) Kodi ndi khalidwe liti limene limatilimbikitsa kutsatira malangizo a Yehova? (b) N’chifukwa chiyani chikhulupiriro chili chofunika kwambiri?

12 Chikondi chathu pa Yehova chimatilimbikitsa kutsatira malangizo ake. (1 Yoh. 5:3) Paulo anatchula chinthu china chimenenso timafunikira, ponena kuti: “Tikuyenda mwa chikhulupiriro, osati mwa zooneka ndi maso.” (2 Akor. 5:6, 7) Kodi ndi chifukwa chiyani chikhulupiriro chili chofunika? Yehova amatitsogolera “m’mabande a chilungamo,” koma mabande kapena kuti njira zimenezo sizitipatsa chuma kapena mwayi wotchuka m’dzikoli. (Sal. 23:3) Pachifukwa chimenechi, maso athu a chikhulupiriro amafunika kukhala pa madalitso auzimu osayerekezereka amene timapeza tikamatumikira Yehova. (Werengani 2 Akorinto 4:17, 18.) Ndiponso chikhulupiriro chimatithandiza kuti tizikhala okhutira ndi zinthu zochepa zimene tili nazo.​—1 Tim. 6:8.

13 Yesu anasonyeza kuti kulambira koona kumafuna kudzimana, ndipo kudzimana kumafuna chikhulupiriro. (Luka 9:23, 24) Ena mwa anthu amene amalambira Yehova mokhulupirika akhala odzimana kwambiri ndipo apirira umphawi, kuponderezedwa, tsankho ngakhale kuzunzidwa kumene. (2 Akor. 11:23-27; Chiv. 3:8-10) Chikhulupiriro cholimba ndi chimene chawathandiza kukhalabe osangalala popirira mavutowo. (Yak. 1:2, 3) Chikhulupiriro cholimba chimatithandiza ifenso kukhala ndi chidaliro chonse kuti kutsogoleredwa ndi Yehova ndi chinthu chabwino kwambiri nthawi zonse. Ndiponso iye akamatitsogolera, timapindula nthawi zonse. Ife sitikayika ngakhale pang’ono kuti anthu amene amapirira mokhulupirika adzalandira mphoto yabwino kwambiri. Ndipo mavuto akanthawi amene amakumana nawo si kanthu powayerekeza ndi mphotoyo.​—Aheb. 11:6.

14. Kodi n’chifukwa chiyani Hagara anafunika kudzichepetsa?

14 Kutsogoleredwa ndi Yehova kumafunanso kudzichepetsa. Mwachitsanzo, ganizirani nkhani ya Hagara, mdzakazi wa Sara. Sara atakhala wosabereka kwa nthawi yaitali, anapereka Hagara kwa Abulahamu, ndipo Hagara anakhala ndi pathupi pa Abulahamu. Kenako, Hagara uja anayamba kudzikuza ndi kumanyoza Sara, mbuye wake wosaberekayo. Mapeto ake, Sara “anam’sautsa iye,” ndipo Hagara anathawa. Mngelo wa Yehova atakumana ndi Hagara, anamuuza kuti: “Bwera kwa wakuka wako, udzichepetse wekha pamanja pake.” (Gen. 16:2, 6, 8, 9) Mwina Hagara akanakonda malangizo osiyana ndi amenewa. Koma kuti achite zimene mngelo anamuuza, anafunika kusiya mtima wake wodzikuza. Ndipo anadzichepetsadi ndi kuchita zimene mngelo ananena. Atatero, mwana wake Ismayeli anabadwa ali wotetezeka m’mahema a atate wake.

15. Kodi ndi pankhani ziti pamene ife masiku ano tingafunike kudzichepetsa kuti titsatire malangizo a Yehova?

15 Ifenso tingafunike kudzichepetsa kuti titsatire malangizo a Yehova. Mwachitsanzo, enafe tingafunike kusintha maganizo ndi kuvomereza kuti zosangalatsa zimene timakonda sizikondweretsa Yehova. Zingachitike kuti Mkhristu walakwira mnzake ndipo afunika kupepesa. Kapena angalakwitse chinthu chinachake ndipo afunika avomereze. Koma nanga bwanji ngati wina wachita  tchimo lalikulu? Amafunika adzichepetse ndi kuulula tchimolo kwa akulu. Munthu angafike mpaka pochotsedwa mu mpingo. Kuti abwezeretsedwe, amafunika adzichepetse, alape ndi kutembenuka. Pazochitika izi ndi zina ngati zimenezi, mawu a pa Miyambo 29:23 amakhala olimbikitsa. Amati: “Kudzikuza kwa munthu kudzam’chepetsa; koma wokhala ndi mtima wodzichepetsa adzalemekezedwa.”

Kodi Yehova Amatitsogolera Bwanji?

16, 17. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tipindule kwambiri ndi Baibulo, limene Mulungu akuligwiritsa ntchito potitsogolera?

16 Njira yaikulu imene Mulungu amagwiritsa ntchito potitsogolera ndi Mawu ake ouziridwa, Baibulo. (Werengani 2 Timoteyo 3:16, 17.) Kuti tipindule kwambiri ndi Mawu a Mulungu, si bwino kuti tizidikira kuti tikumane kaye ndi mavuto ndiye kenako kumafufuza malangizo a m’Malemba. M’malo mwake, tiyenera kukhala ndi chizolowezi chowerenga Baibulo tsiku ndi tsiku. (Sal. 1:1-3) Tikamatero, timadziwa bwino zimene mawu ouziridwawa amanena. Timayamba kuganiza ngati mmene Mulungu amaganizira, ndipo timakhala okonzeka kulimbana ndi mavuto ngakhale osayembekezereka.

17 Ndiponso, timafunika kusinkhasinkha zimene tikuwerenga m’Malemba ndi kupemphera mogwirizana ndi zimenezo. Posinkhasinkha malemba a m’Baibulo, timayesetsa kuona mmene mfundo zake zingatithandizire pa nkhani zosiyanasiyana. (1 Tim. 4:15) Tikakumana ndi mavuto aakulu, timapemphera kwa Yehova kuti atithandize kupeza malangizo amene tikufunikira. Mzimu wa Yehova umatithandiza kukumbukira mfundo za m’Malemba zomwe tawerenga m’Baibulo kapena m’mabuku olifotokoza.​—Werengani Salmo 25:4, 5.

18. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji gulu la abale achikhristu potitsogolera?

18 Gulu lathu la abale achikhristu ndi chinthu chinanso chofunika kwambiri chimene Yehova amagwiritsa ntchito potitsogolera. Mbali yofunika kwambiri ya gulu limeneli ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” limodzi ndi Bungwe Lolamulira limene limaimira kapoloyo. Bungweli limatulutsa chakudya chauzimu nthawi zonse. Chakudyachi ndi mabuku ndi mapulogalamu a misonkhano ya mpingo ndiponso misonkhano ikuluikulu. (Mat. 24:45-47; yerekezerani ndi Machitidwe 15:6, 22-31.) M’gulu limeneli la abale achikhristu, mulinso anthu okhwima mwauzimu, makamaka akulu, amene ndi oyenerera kuthandiza munthu aliyense payekha ndi kupereka uphungu wa m’Malemba. (Yes. 32:1) M’mabanja achikhristu, achinyamata alinso ndi kumene angapeze malangizo odalirika. Iwo amalimbikitsidwa nthawi zonse kudalira makolo awo kuti aziwatsogolera, chifukwa Mulungu anapatsa makolowo udindo wochita zimenezi.​—Aef. 6:1-3.

19. Kodi timapeza madalitso otani chifukwa chotsogoleredwa ndi Yehova nthawi zonse?

19 Zoonadi, Yehova amatitsogolera m’njira zosiyanasiyana, ndipo ndi bwino kuzigwiritsa ntchito njira zimenezi kuti tipindule nazo kwambiri. Pofotokoza za nthawi imene Aisiraeli anali okhulupirika, Mfumu Davide inati: “Makolo athu anakhulupirira Inu: Anakhulupirira, ndipo munawalanditsa. Anafuula kwa Inu, napulumutsidwa: Anakhulupira Inu, ndipo sanachita manyazi.” (Sal. 22:3-5) Ngati tikhulupirira ndi kutsatira malangizo a Yehova, ifenso ‘sitidzachita manyazi.’ Chiyembekezo chathu sichidzapita pachabe. ‘Tikamapereka njira yathu kwa Yehova,’ m’malo modalira nzeru zathu, tidzapeza madalitso ambiri ngakhale panopa. (Sal. 37:5) Ndipo tikapitiriza kuchita zimenezi mokhulupirika, madalitso amenewo sadzatha. Mfumu Davide inati: “Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake [“okhulupirika ake,” NW]: Asungika kosatha . . . Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”​—Sal. 37:28, 29.

Kodi Mungafotokoze?

• N’chifukwa chiyani timadalira Yehova kutitsogolera?

• Kodi tikakana kutsogoleredwa ndi Yehova, timasonyeza chiyani?

• Kodi ndi pankhani ziti zimene Mkhristu angafunike kudzichepetsa?

• Kodi Yehova masiku ano amagwiritsa ntchito chiyani potitsogolera?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 8]

Kodi mumadalira Yehova m’zinthu zonse pamoyo wanu?

[Chithunzi patsamba 9]

Hava anakana ulamuliro wa Yehova

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi Hagara anafunika chiyani kuti atsatire malangizo a mngelo?