Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Baibulo Langokhala Buku Labwino Basi?

Kodi Baibulo Langokhala Buku Labwino Basi?

Baibulo linalembedwa zaka pafupifupi 2,000 zapitazo. Kuyambira nthawi imeneyo, mabuku ena ambirimbiri akhala akulembedwa koma pano sapezekanso. Komatu si mmene ziliri ndi Baibulo. Tiyeni tione mfundo zotsatirazi.

  • Olamulira ambiri anayesetsa kuchita zinthu zoti Baibulo lisamafalitsidwenso, koma sizinatheke. Mwachitsanzo, buku lina linanena kuti m’zaka za m’ma 500 mpaka 1500, m’mayiko ena omwe amati ndi achikhristu, “munthu amene anali ndi Baibulo lachinenero cha anthu wamba kapena amene ankaliwerenga, ankamuona kuti ndi wampatuko ndiponso woukira boma.” (An Introduction to the Medieval Bible) Ndipotu anthu ena omwe ankamasulira Baibulo kapenanso amene ankalimbikitsa anthu kuliphunzira, anaika moyo wawo pangozi ndipo ena anaphedwa.

  • Komabe, padziko lonse palibenso buku lina limene limapezeka ndi anthu ambiri kuposa Baibulo. Tikutero chifukwa chakuti Mabaibulo pafupifupi 5 biliyoni kapena mabuku ake ena, asindikizidwa m’zinenero zoposa 2,800. Zimenezi ndi zosiyana kwambiri ndi mabuku ena monga olimbikitsa nzeru za anthu, a sayansi ndi ena ambiri chifukwa ndi anthu ochepa chabe amene amapezeka nawo ndipo pakapita nthawi anthu ambiri sawagwiritsanso ntchito.

  • Baibulo lathandiza kuti zinenero zina zisasinthe kwambiri. Mwachitsanzo, chinenero cha ku Germany chinatengera kwambiri Chijeremani cha m’Baibulo limene Martin Luther anamasulira. Anthu amati Baibulo la King James Version lomwe linatuluka koyamba “mwina ndi buku [la Chingelezi] limene lathandiza kwambiri kuti chinenerochi chisasinthe.”

  • Buku lina linanena kuti Baibulo “linathandiza kwambiri anthu a m’mayiko a ku Europe komanso North America osati pa nkhani za kupembedza zokha, komanso za chikhalidwe, luso losiyanasiyana, malamulo, ndale ndiponso zinthu zina zambiri.”—The Oxford Encyclopedia of the Books of the Bible.

Zimenezi ndi zitsanzo zochepa chabe zomwe zimasiyanitsa Baibulo ndi mabuku ena. Koma kodi n’chifukwa chiyani Baibulo limapezeka ndi anthu ambiri? Nanga n’chifukwa chiyani anthu analolera kuika moyo wawo pangozi chifukwa cha Baibulo? Zifukwa zina n’zakuti: Baibulo limathandiza anthu kukhala ndi makhalidwe abwino komanso kudziwa Mulungu molondola. Limawathandizanso kudziwa mmene mavuto anayambira. Chosangalatsa kwambiri n’chakuti limathandizanso kudziwa kuti mavutowa adzatha komanso limafotokoza mmene adzathere.

 Baibulo Limatithandiza Kukhala Ndi Makhalidwe Abwino Komanso Kudziwa Mulungu Molondola

Maphunziro ndi ofunika ndithu. Koma nyuzipepala ina inanena kuti, “Maphunziro . . . amene amachititsa munthu kupatsidwa mayina aulemu . . . sathandiza munthu kuti akhale ndi makhalidwe abwino.” (Ottawa Citizen) Ndipotu zimenezi n’zoona chifukwa kafukufuku wina amene bungwe lina linachita anasonyeza kuti anthu ambiri ophunzira kwambiri, kuphatikizaponso akuluakulu a bizinesi komanso a boma amakonda kuchita chinyengo, kunama, ndiponso kuba. Ndipo zimenezi “zimachititsa kuti anthu asamawakhulupirire.”

Koma Baibulo limatithandiza kwambiri pa nkhani za makhalidwe abwino komanso kuti tidziwe Mulungu. Limatithandizanso kuzindikira zinthu “zolungama, zowongoka, ndiponso njira yonse ya zinthu zabwino.” (Miyambo 2:9) Mwachitsanzo, bambo wina wazaka 23, dzina lake Stephen, nthawi ina anamangidwa ku Poland. Ali m’ndende anayamba kuphunzira Baibulo ndipo anayamba kutsatira zimene ankaphunzirazo. Iye ananena kuti: “Panopa ndikumvetsa bwino zimene amatanthauza akamati, ‘Uzilemekeza atate ako ndi amayi ako.’ Ndaphunziranso kumaugwira mtima makamaka ndikakwiya kwambiri.”—Aefeso 4:31; 6:2.

Stephen anasangalala kwambiri ndi mfundo ya pa Miyambo 19:11, yakuti: “Kuzindikira kumachititsa munthu kubweza mkwiyo wake, ndipo kunyalanyaza cholakwa kumam’chititsa kukhala wokongola.” Panopa akakumana ndi vuto linalake lalikulu amayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo n’kupeza njira yabwino yothetsera vutolo. Iye ananenanso kuti: “Ndaona kuti Baibulo ndi buku lomwe lili ndi malangizo abwino kwambiri.”

Chitsanzo china ndi Maria, yemwe ndi wa Mboni za Yehova. Tsiku lina iye ananyozedwa ndi mayi wina yemwe amadana ndi a Mboni, anthu ambiri akuona. Ngakhale kuti anamulalatira kwambiri, Maria sanabwezere ndipo anangopitiriza ulendo wake. Mayi wachipongweyo anachita manyazi kwambiri ndi zimene anachitazi  ndipo kenako anayamba kufunafuna a Mboni za Yehova. Patapita mwezi umodzi mayiyu anakumana ndi Maria ndipo anamukumbatira n’kumupepesa. Mayiyu anazindikira kuti Maria sanabwezere zachipongwe zija chifukwa cha zimene amakhulupirira. Zimenezi zinachititsa kuti iye ndi anthu 5 a m’banja lake, ayambe kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova.

Yesu ananena kuti nzeru imatsimikiziridwa ndi ntchito zake. (Luka 7:35) Choncho palibe amene angatsutse kuti mfundo za m’Baibulo n’zothandiza. Baibulo limatithandiza kukhala anthu abwino. Ndipo mfundo zake “zimapatsa nzeru munthu wosadziwa zinthu,” ‘zimasangalatsa mtima’ ndiponso zimathandiza anthu kukhala ndi makhalidwe abwino komanso kukonda Mulungu.—Salimo 19:7, 8.

Baibulo Limafotokoza Mmene Mavuto Anayambira

Anthu ofufuza akafuna kudziwa zambiri za mliri wa matenda enaake, amafufuza chimene chayambitsa mliriwo. Mofananamo, kuti timvetse chifukwa chake anthu amavutika, tiyenera kudziwa chomwe chinayambitsa mavutowo. Baibulo ndi lothandiza kwambiri chifukwa limatiuza mmene mavuto anayambira komanso mmene tinalengedwera.

Buku la Genesis limanena kuti mavuto a anthu anayamba pamene Adamu ndi Hava anakana kumvera Mulungu. Zimene anachitazi zinasonyeza kuti iwo anafuna kuti azisankha okha zabwino kapena zoipa m’malo modalira Mulungu yemwe anawalenga. (Genesis 3:1-7) N’zomvetsa chisoni kuti kungochokera nthawi imeneyo, anthu anayamba kukhala ndi mtima wosafuna kuuzidwa zochita. Zimenezi zinachititsa kuti anthu asakhale ndi ufulu weniweni, azikangana, aziponderezana ndiponso kuti makhalidwe aipe kwambiri. (Mlaliki 8:9) Izi zikugwirizana ndi zimene Baibulo limanena kuti: “Munthu . . . alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Koma n’zosangalatsa kuti mavuto onse atha posachedwapa.

 Baibulo Limanena Kuti Mavuto Adzatha

Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu amakonda anthu omwe amalemekeza ulamuliro komanso mfundo zake. Limatitsimikiziranso kuti Iye sadzalekerera anthu oipa kuti apitirize kubweretsa mavuto padzikoli ndipo limanena kuti, oipa “adzadya zipatso za njira yawo.” (Miyambo 1:30, 31) Koma limanenanso kuti “anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—Salimo 37:11.

“Chifuniro [cha Mulungu] n’chakuti anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.”—1 Timoteyo 2:3, 4.

Mulungu adzagwiritsa ntchito ‘Ufumu wake’ kuti akwaniritse zimene ankafuna zoti anthu azikhala mwamtendere padzikoli. (Luka 4:43) Ufumu umenewu udzakhala boma lolamulira dziko lonse ndipo udzasonyeza kuti Mulungu ndiye woyenera kulamulira anthu. M’pemphero lachitsanzo, Yesu anasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwambiri kuti zinthu ziziyenda bwino padzikoli. Iye anati: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike . . . pansi pano.”—Mateyu 6:10.

Mu Ufumu umenewu, anthu onse azidzachita zimene Mulungu akufuna podziwa kuti ndi Mlengi wawo komanso kuti ndiye woyenera kulamulira. Mavuto monga katangale, dyera, umphawi, kusankhana mitundu ndiponso nkhondo adzatha. Padziko lonse padzakhala boma limodzi, ndipo anthu onse azidzatsatira mfundo zofanana za makhalidwe abwino komanso azidzapembedza Mulungu m’njira yofanana.—Chivumbulutso 11:15.

 Kuti mudzakhale nawo m’dziko latsopanoli, muyenera kuphunzira zimene Mulungu amafuna. Lemba la 1 Timoteyo 2:3, 4 limati: “Chifuniro [cha Mulungu] n’chakuti anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” Muyenera kudziwa malamulo ndiponso mfundo zimene Ufumu wa Mulungu uzidzayendera. Zina mwa mfundo zimenezi ndi zomwe Yesu Khristu ananena pa ulaliki wa paphiri. (Mateyu, chaputala 5 mpaka 7) Mukamawerenga machaputala amenewa muziganizira mmene moyo udzakhalire munthu aliyense akamadzatsatira malangizo anzeru omwe Yesu anaperekawa.

Malinga ndi mfundo zimene zafotokozedwa m’nkhaniyi, kodi n’zodabwitsa kuti Baibulo lafalitsidwa kwambiri kuposa buku lina lililonse? Ayi. Tikutero chifukwa uthenga wake ndi wochokera kwa Mulungu. Ndipo zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu amafunitsitsa kuti anthu amitundu ndiponso zinenero zonse aphunzire za Iye n’kudzasangalala ndi madalitso amene Ufumu wake udzabweretse.—Machitidwe 10:34, 35.