Yankho la m’Baibulo

Anthu ambiri amauzidwa kuti sitingadziwe anthu amene analemba Baibulo. Koma Baibulo nthawi zambiri limanena mosapita m’mbali za anthu amene analemba nkhani zake. Mabuku ena a m’Baibulo amayamba ndi mawu monga akuti, “awa ndi mawu a Nehemiya,” “masomphenya amene Yesaya . . . anaona” ndiponso “Yehova analankhula kudzera mwa Yoweli.”—Nehemiya 1:1; Yesaya 1:1; Yoweli 1:1.

Anthu ambiri amene analemba Baibulo ananena kuti Yehova, Mulungu woona, ndi amene anawauza zomwe analembazo. Mwachitsanzo, aneneri amene analemba Malemba Achiheberi ananena maulendo oposa 300 kuti: “Yehova wanena kuti.” (Amosi 1:3; Mika 2:3; Nahumu 1:12) Anthu ena amene analemba nawo Baibulo, anauzidwa ndi angelo uthenga wochokera kwa Mulungu kuti alembe.—Zekariya 1:7, 9.

Baibulo linalembedwa ndi amuna pafupifupi 40 kwa zaka 1,600. Anthu ena anauziridwa kulemba mabuku angapo a m’Baibulo. Ndipotu m’Baibulo lonse muli mabuku 66. Mabuku 39 a m’Baibulo ndi a Malemba Achiheberi, omwe anthu ambiri amawatcha Chipangano Chakale. Mabuku 27 ndi a Malemba Achigiriki, omwe nthawi zambiri amatchedwa Chipangano Chatsopano.