Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Ndi Mawu Ouziridwadi ndi Mulungu

Baibulo Ndi Mawu Ouziridwadi ndi Mulungu

KODI mtumwi Paulo ankatanthauza chiyani kwenikweni ponena kuti Baibulo ‘analiuzira ndi Mulungu’? (2 Timoteyo 3:16) Iye ankatanthauza kuti Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu wake woyera potsogolera anthu amene analemba Baibulo kuti alembe zinthu zokhazo zimene Mulunguyo ankafuna.

Mtumwi Petulo ananena kuti olemba Baibulo “analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.” (2 Petulo 1:21) N’chifukwa chakenso mtumwi Paulo ananena kuti mabuku a m’Baibulo ndi  “malemba opatulika amene angathe kukupatsa nzeru za mmene ungapezere chipulumutso kudzera m’chikhulupiriro chokhudza Khristu Yesu.”​—2 Timoteyo 3:15.

Anthu ambiri amatsutsiratu zoti Baibulo ndi mawu ochokera kwa Mulungu. Akatswiri amene amaphunzira Baibulo pofuna kulipezera zifukwa, nthawi zambiri amatsutsa monyoza zoti Baibulo limanena zoona zokhazokha. Ndipo Sir Charles Marston ananena kuti iwo amachita zimenezi “mosalemekeza ngakhale pang’ono nkhani zofotokozedwa m’Baibulo.” Ena amati Baibulo ndi “buku lakale la nthano basi.”

Ganizirani Umboni Umene Ulipo

Ndiyeno kodi tiyeneradi kukhulupirira Baibulo? M’pofunika kuganizira nkhaniyi mofatsa, chifukwa ngati Baibulo lilidi mawu ochokera kwa Mulungu, si chinthu chanzeru kulinyalanyaza, ndipotu ngati titatero sitingadzapeze moyo wosatha. Ngati mumaona kuti Baibulo ndi mawu a anthu osati a Mulungu, n’zovuta kulikhulupirira kuti lingakuthandizeni posankha zochita komanso polimbitsa chikhulupiriro chanu.​—1 Atesalonika 2:13.

Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti mudziwe ngati n’zoyenera kukhulupirira Baibulo kapena ayi? Choyamba taganizirani funso ili: Kodi mumatani kuti mudziwe ngati muyenera kukhulupirira munthu amene mwangokumana naye koyamba? Pa nkhani imeneyi, mungavomereze kuti n’zovuta kukhulupirira munthu amene simukum’dziwa kwenikweni. Koma mutam’dziwa bwino munthuyo kwakanthawi, m’pamene mumatha kudziwa ngati alidi woona mtima ndiponso wokhulupirika. Umu ndi mmenenso mungadziwire ngati n’zoyenera kukhulupirira Baibulo. Musafulumire kukhulupirira maganizo kapena mfundo za akatswiri ongofuna kuti anthu azikayikira Baibulo. Ganizirani mwachifatse umboni wotsimikizira zimene Baibulo limanena zakuti ndi buku ‘louziridwa ndi Mulungu.’

Nkhondo Ndi Anansi

Musafulumire kukayikira Baibulo poganizira kuti ngakhale anthu ena amene amanena kuti amalidziwa bwino amatsutsa zoti ndi Mawu a Mulungu ndiponso kuti limanena zoona. Buku lina  lotanthauzira mawu a m’Baibulo linanena kuti, masiku ano akatswiri ambiri a Baibulo “amanena kuti Malemba kwenikweni ndi nkhani zongolembedwa ndi anthu basi.” Iwo amatero ngakhale kuti amadzitcha Akhristu.​—New Dictionary of Theology.

Akatswiri ambiri ophunzira za mawu a Mulungu amanena kuti mabuku ena a m’Baibulo sanalembedwe ndi anthu amene anatchulidwa m’Baibulomo. Mwachitsanzo, ena amatsutsa zoti mneneri Yesaya ndiye analemba buku la Yesaya. Iwo amati buku la m’Baibulo limeneli linalembedwa patapita nthawi yaitali kuchokera pamene Yesayayo anamwalira. Katswiri wina, dzina lake Lowther Clarke, analemba kuti buku la Yesaya “linalembedwa ndi anthu ambiri amene anakhalako m’zaka zosiyanasiyana.” (Concise Bible Commentary) Komatu mfundo zoterezi zimasonyeza kuti anthuwa akunyalanyaza zimene Yesu Khristu ndi ophunzira ake ananena mobwerezabwereza, zosonyeza kuti mneneri Yesaya ndiye analemba bukuli.​—Mateyo 3:3; 15:7; Luka 4:17; Yohane 12:38-41; Aroma 9:27, 29.

Kuwonjezera pamenepa, akatswiri ofufuza za Baibulo, monga J. R. Dummelow, amati maulosi a m’buku la Daniele “kwenikweni ndi nkhani zimene zinalembedwa zinthuzo zitachitika kale, kungoti wolembayo anazilemba moti zizioneka ngati kuti anachita kulosera.” Ponena zimenezi akatswiriwa akunyalanyazanso umboni umene Yesu Khristu anapereka pa nkhaniyi. Yesu anachenjeza anthu kuti kudzabwera “chonyansa chosakaza, chonenedwa kudzera mwa mneneri Daniele, chitaimirira m’malo oyera.” (Mateyo 24:15) Ndiyeno kodi mukuganiza kuti ndi chinthu chanzeru kuti Mkhristu azikhulupirira zoti nayenso Yesu Khristu ankanena zinthu zabodza? Kodi zikanakhala zabodza, bwenzi Yesu Khristu atauza anthu kuti zimene Daniele analemba zinali ulosi? Ayi, Yesu sakanachita zimenezi.

Kodi Kudziwa Amene Analemba Baibulo Kuli ndi Phindu Lanji?

Mwina mungaganize kuti kudziwa amene analemba Baibulo kulibe phindu lililonse. Zimenezi si zoona, chifukwa kudziwa amene analemba Baibulo n’kofunika kwambiri. Tiyerekezere kuti pali wilo ya mnzanu amene anamwalira. Kodi mungamve bwanji mutazindikira kuti wiloyo siinalembedwe ndi mnzanuyo? Akatswiri akuuzani kuti wiloyo ndi yachinyengo chifukwa anzake ena a malemuyo analembamo zinthu zimene iwowo ankakhulupirira kuti ndi zimene malemuyo ankafuna. Kodi zimenezi sizingakuchititseni kukayikira wiloyo? Kodi mungakhulupirire kuti zimene zalembedwamo ndi zimenedi mnzanuyo ankafuna?

N’chimodzimodzinso ndi Baibulo. Moti n’zosadabwitsa kuti anthu ambiri, ngakhale amene amadzitcha Akhristu, amaona kuti palibe vuto ngati atapanda kutsatira zimene Baibulo limanena pa nkhani zosiyanasiyana, monga kukhala oona mtima ndi kupewa chiwerewere. Kodi simunayambe mwamvapo anthu akunyoza Baibulo ponena mawu ngati akuti, “Koma zimenezo ndi za m’Chipangano Chakale”? Ponena zimenezi iwo amasonyeza kuti Chipangano Chakale n’chosafunika kwenikweni. Ngakhale kuti iwo amaganiza choncho, mtumwi Paulo anatchula mabuku amenewa kuti “malemba opatulika” omwe “anawauzira ndi Mulungu.”

Koma mwina mungadzifunse kuti, “Nanga akatswiri a Baibulo onsewa amanena zabodza?” Ayi, sikuti onse amanena zabodza. Mwachitsanzo, pali akatswiri oona mtima amene athandiza kwambiri kuti tidziwe mipukutu yeniyeni ya Baibulo. Ndipo ndi zoona kuti anthu ena okopera Baibulo ankalakwitsa zinthu zina zing’onozing’ono pa  zaka zambirimbiri zimene anthu akhala akukopera mabuku a m’Baibulo. Komabe muzikumbukira mfundo iyi: Ndi zoona kuti pali zinthu zina zochepa zimene okopera Baibulo analakwitsa koma si zomveka kunena kuti zimenezi zikutanthauza kuti zonse za m’Baibulo ndi maganizo a anthu basi.

Pitirizani Kukhulupirira “Malemba Opatulika”

Paulo asananene kuti Baibulo analiuzira ndi Mulungu, anauza Timoteyo za phindu la Malemba ouziridwa amenewa. Iye anati: “M’masiku otsiriza, idzafika nthawi yovuta yoikika. Koma anthu oipa ndi onyenga adzaipiraipirabe, kusocheretsa ena ndi kusocheretsedwa.” (2 Timoteyo 3:1, 13) Ngakhale m’nthawi ya Paulo, panali anthu ooneka ngati ‘anzeru ndi ophunzira’ amene ankagwiritsa ntchito “mfundo zokopa” pofuna kusokoneza anthu ndi kufooketsa chikhulupiriro chawo mwa Yesu Khristu. (1 Akorinto 1:18, 19; Akolose 2:4, 8) N’chifukwa chake mtumwi Paulo analangiza Timoteyo kuti adziteteze kwa anthu amenewa. Anamuuza kuti ‘apitirize kutsatira zimene anaphunzira kuyambira pamene anali wakhanda zochokera m’malemba opatulika’ amene Mulungu anapereka.​—2 Timoteyo 3:14, 15.

Inunso mukufunika kuchita zimenezi “m’masiku otsiriza” ano. Musaganize kuti simungasocheretsedwe ndi anthu ochenjera amene nthawi zambiri amagwiritsa ntchito “mfundo zokopa.” Koma, mofanana ndi Akhristu am’nthawi ya atumwi, dzitetezeni. Mungachite zimenezi potsatira kwambiri zimene mumaphunzira m’Baibulo. Buku limeneli ndi mawu ouziridwadi ndi Mulungu.

Anthu a Mboni za Yehova ndi okonzeka kukuthandizani kuti muzikhulupirira kwambiri Baibulo. Iwo angakuthandizeni kupeza umboni wa mfundo zosiyanasiyana zokhudza Baibulo monga izi: Baibulo lakhala likuthandiza anthu kuyambira kalekale, ndi lolondola pa nkhani za sayansi, nkhani zake zonse ndi zogwirizana kuyambira m’buku la Genesis mpaka Chivumbulutso, komanso maulosi ake amakwaniritsidwa ndendende. Ngati mungakonde, lemberani kalata ofalitsa magaziniyi kuti mudziwe mfundo zimene zathandiza anthu oona mtima ambirimbiri kutsimikizira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu.