Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?

Kodi mfundo yaikulu yomwe imapezeka m’Baibulo ndi iti?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuphunzira Baibulo?

Werengani kuti mudziwe mfundo zofunika zokhudza Baibulo, lomwe ndi buku lotchuka kwambiri padziko lonse.

GAWO 1

Mlengi Anapatsa Anthu Paradaiso

Kodi Baibulo limati anthufe tinalengedwa bwanji? Kodi Mulungu anapatsa anthu awiri oyambirira malamulo otani?

GAWO 2

Anataya Mwayi Wokhala M’Paradaiso

Mulungu atapereka chilango kwa Adamu ndi Hava chifukwa cha kusamvera kwawo, kodi anatani kuti apatse anthu chiyembekezo?

GAWO 3

Anthu Anapulumuka Chigumula

kodi kuipa kunafalikira bwanji padziko lapansi? Kodi nowa anasonyeza bwanji kuti anali wokhulupirika?

GAWO 4

Mulungu Anachita Pangano ndi Abulahamu

N’chifukwa chiyani Abulahamu anasamukira ku Kanani? Kodi Mulungu anachita pangano lotani ndi Abulahamu?

GAWO 5

Mulungu Anadalitsa Abulahamu ndi Banja Lake

Kodi Mulungu anasonyeza chiyani pamene anauza Abulahamu kuti apereke nsembe mwana wake Isaki? Kodi Yakobo analosera chiyani asanamwalire?

GAWO 6

Yobu Anapitiriza Kutumikira Mulungu ndi Mtima Wosagawanika

Kodi buku la Yobu limasonyeza bwanji kuti n’zotheka munthu aliyense kusonyeza kuti Mulungu ndi amene ali woyenera kulamulira

GAWO 7

Mulungu Anapulumutsa Ana a Isiraeli

Kodi Mulungu anagwiritsa ntchito bwanji Mose kuti akapulumutse ana a Isiraeli ku ukapolo wa ku Iguputo? Kodi cholinga cha chikondwerero cha pasika chinali chiyani?

GAWO 8

Aisiraeli Analowa M’dziko la Kanani

Aisiraeli atalowa m’dziko la Kanani, n’chifukwa chiyani Mulungu sanawononge Rahabi ndi anthu a m’banja lake ku Yeriko?

GAWO 9

Aisiraeli Anapempha Kuti Akhale ndi Mfumu

Mulungu anasankha Sauli kuti akhale mfumu Aisiraeli atapempha kuti akhale ndi mfumu. N’chifukwa chiyani Mulungu anachotsa Sauli n’kuika Davide kuti akhale mfumu?

GAWO 10

Solomo Anali Mfumu Yanzeru

Kodi pali zitsanzo zotani zosonyeza kuti Solomo anali mfumu yanzeru? Kodi chinamuchitikira n’chiyani atasiya kutsatira malamulo a Mulungu?

GAWO 11

Nyimbo Zouziridwa Zomwe Ndi Zolimbikitsa Komanso Zamalangizo

Kodi ndi masalimo ati amene amasonyeza mmene Mulungu amathandizira komanso kulimbikitsa anthu amene amamukonda? Kodi mfumu inaulula chiyani m’Nyimbo ya Solomo?

GAWO 12

Nzeru Zochokera kwa Mulungu N’zothandiza pa Moyo

Onani mmene malangizo ochokera kwa Mulungu opezeka m’buku la Miyambo ndi Mlaliki angatithandizire pa moyo wathu komanso kuti tizikhulupirira kwambiri Mulungu.

GAWO 13

Mafumu Abwino Ndiponso Oipa

Kodi chinachitika n’chiyani kuti Aisiraeli agawikane n’kupanga maufumu awiri?

GAWO 14

Mulungu Ankalankhula Kudzera mwa Aneneri Ake

Kodi aneneri a Mulungu ankapereka mauthenga otani? Werengani mauthenga 4 amene ankafotokoza kwa anthu.

GAWO 15

Mneneri Amene Anali ku Ukapolo Anaona Masomphenya a Zimene Zidzachitike M’tsogolo

Kodi Danieli anauzidwa zinthu zotani zokhudza Mesiya ndi Ufumu wa Mulungu?

GAWO 16

Kufika kwa Mesiya

Kodi Yehova anagwiritsa ntchito bwanji angelo ndi Yohane M’batizi pofuna kuti anthu adziwe kuti Yesu ndi Mesiya? Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti Mwana wake ndi Mesiya?

GAWO 17

Yesu Ankaphunzitsa za Ufumu wa Mulungu

Kodi mfundo yaikulu yomwe Yesu ankaphunzitsa anthu inali yotani? Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti adzalamulira anthu mwachilungamo ndiponso mwachikondi?

GAWO 18

Yesu Ankachita Zozizwitsa

Kodi zozizwitsa za Yesu zinasonyeza kuti adzachita chiyani m’tsogolo pamene azidzalamulira dziko lapansi?

GAWO 19

Yesu Analosera Zinthu za M’tsogolo Zimene Zidzakhudze Dziko Lonse

Kodi chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu chomwe iye anauza ophunzira ake chimatanthauza chiyani?

GAWO 20

Yesu Khristu Anaphedwa

Kodi Yesu anayambitsa mwambo watsopano uti, atatsala pang’ono kuti akhomedwe pa mtengo?

GAWO 21

Yesu Anaukitsidwa

Kodi ophunzira a Yesu anadziwa bwanji kuti iye waukitsidwa ndi Mulungu?

GAWO 22

Atumwi Ankalalikira Mopanda Mantha

Kodi chinachitika n’chiyani pa chikondwerero cha Pentekosite? Kodi adani anachita chiyani ataona kuti ophunzira a Yesu akugwira ntchito yolalikira?

GAWO 23

Uthenga Wabwino Unafalikira

Kodi chinachitika n’chiyani Paulo atachiritsa munthu wolumala ku Lusitara? Kodi Paulo anakafika bwanji ku Roma?

GAWO 24

Paulo Analemba Makalata Opita Kumipingo

Kodi Paulo anapereka malangizo ati othandiza kuti mpingo uziyenda bwino? Kodi Paulo anafotokoza zotani zokhudza mbewu yolonjezedwa?

GAWO 25

Malangizo Okhudza Kukhala ndi Chikhulupiriro, Makhalidwe Abwino Ndiponso Chikondi

Kodi Mkhristu angasonyeze bwanji kuti ali ndi chikhulupiriro? Kodi munthu angasonyeze bwanji kuti amakondadi Mulungu?

GAWO 26

Dziko Lapansi Lidzakhalanso Paradaiso

Kodi buku la m’Baibulo la Chivumbulutso limamalizitsa bwanji pofotokoza uthenga wa m’Baibulo?

Onani Uthenga wa M’Baibulo Mwachidule

Kodi Yehova anachita zotani pofuna kuulula kuti Yesu ndi amene adzakhale Mesiya ndipo ndiye adzabwezeretse dzikoli kuti likhalenso paradaiso?

Nthawi Imene Zinthu Zosiyanasiyana Zinachitika

Tawerengani kuti mudziwe zinthu zotchulidwa m’Baibulo zomwe zinachitika kuyambira mu 4026 B.C.E. mpaka 100 C.E.