Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Mfundo za M’Baibulo N’zothandizabe Masiku Ano?

Kodi Mfundo za M’Baibulo N’zothandizabe Masiku Ano?

‘Ndinayamba kuona kuti ndine wosangalala kwambiri kuposa poyamba.’

HILTON ankakonda kwambiri masewera a nkhonya. Ali ndi zaka 7, anali katswiri wa masewerawa ndipo ankakondanso kuchita ndewu. Ali kusekondale, iye ndi anzake ankachita kuputa dala anthu n’cholinga choti amenyane nawo. Hilton anati: “Ndinkaba, kuonera zolaula, kuchitira akazi zachipongwe komanso kutukwana makolo anga. Chifukwa cha makhalidwe anga oipawa makolo anga ankaganiza kuti sindingasinthenso. Nditamaliza sukulu, ndinachoka panyumba.”

Patatha zaka 12, Hilton anabwereranso kwawo, koma makolo ake sanamuzindikire chifukwa anali atasintha kwambiri. Anali wodekha komanso waulemu. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti asinthe chonchi? Pa nthawi yomwe anachoka panyumba, anayamba kuganizira za kuipa kwa khalidwe lake. Anayambanso kuwerenga Baibulo kuti aone ngati lingamuthandize kusintha. Hilton anati: “Kuwerenga Baibulo kunandithandiza kudziwa kuti ndiyenera kusiya khalidwe langa. Komanso palemba la Aefeso 6:2, 3 ndinawerenga kuti ndiyenera kumalemekeza makolo anga, ndipo ndinayambadi kuchita zimenezi. Tsopano ndinayamba kuona kuti ndine wosangalala kwambiri kuposa poyamba. Makolo anganso anasangalala kwambiri ataona kuti ndasintha ndipo zinathandiza kuti asamadandaulenso ngati poyamba paja.”

Nkhani ya Hilton ikusonyeza kuti Baibulo lili ndi mphamvu yotha kusintha munthu ndipo mfundo zake n’zothandiza kwambiri. (Aheberi 4:12) Tiyeni tikambirane zina mwa mfundo zimenezi ndi kuona mmene zingatithandizire. Mfundo zake ndi kufunika kochita zinthu mwachilungamo, kusakwiya msanga, kukhulupirika m’banja komanso chikondi.