Pitani ku nkhani yake

Kodi Nkhani Zimene Zili M’Baibulo Ndi Nzeru za Anthu?

Kodi Nkhani Zimene Zili M’Baibulo Ndi Nzeru za Anthu?

Yankho la m’Baibulo

 M’Baibulo, lomwenso limadziwika kuti Malemba Opatulika, muli mawu ambiri a nzeru. Komabe, taonani mfundo yochititsa chidwi iyi imene ili m’Baibulo: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu.” (2 Timoteyo 3:16) Pali maumboni ambiri otsimikiza kuti mawuwa ndi oona. Mwachitsanzo, taonani mfundo zotsatirazi:

  •   Palibe munthu amene anaperekapo umboni woona wosonyeza kuti mbiri inayake yotchulidwa m’Baibulo ndi yolakwika.

  •   Anthu amene anauziridwa kulemba Baibulo anali oona mtima ndipo analemba zinthu mosabisa. Zinthu zonse zimene analemba zimasonyezeratu kuti n’zoona.

  •   Nkhani zonse za m’Baibulo zili ndi mfundo imodzi. Mfundo yake ndi yakuti: Mulungu yekha ndiye woyenerera kulamulira anthu komanso kuti kudzera mu Ufumu wake wakumwamba, adzachita chifuniro chake.

  •   Ngakhale kuti Baibulo linalembedwa zaka masauzande ambiri zapitazo, nkhani zimene linanena zokhudza sayansi ndi zolondolabe mpaka pano mosiyana ndi nkhani zina zimene anthu ambiri ankakhulupirira pa nthawiyo.

  •   Zimene anthu olemba mbiri yakale analemba zikusonyeza kuti maulosi a m’Baibulo akukwaniritsidwa.