ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Mesiya
Baibulo linalosera kuti Mesiya adzabwera padzikoli kudzapulumutsa anthu ku matenda, imfa ndi mavuto ena onse. Kodi Yesu Khristu ndiye Mesiyayo?
Kodi anthu akanadziwa bwanji Mesiya?
Ulosi wa m’Baibulo unanena kuti Mesiya kapena kuti Khristu adzakhala ndi maudindo awiri. Udindo woyamba unali woti adzaukwaniritsa ali munthu padziko lapansi. Udindo wachiwiri unali woti adzaukwaniritsa patapita nthawi yaitali kuchokera pamene anakwaniritsa woyambawo. * Choncho kuti anthu athe kumuzindikira, olemba Baibulo analosera zinthu zosiyanasiyana zokhudza moyo ndi utumiki wake. Ndipotu, cholinga chachikulu cha maulosi a m’Baibulo ndi ‘kuchitira umboni za Yesu.’—Chivumbulutso 19:10.
Zimene Yesu anachita ali padziko lapansi, zimasonyeza kuti akamadzalamulira padziko lonse adzachita zambiri
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Mesiya anali woti . . .
-
Adzabadwira ku banja la Mfumu Davide.—Yesaya 9:7; Luka 3:23-31. *
-
Adzabadwira m’tauni ya Betelehemu.—Mika 5:2; Luka 2:4-7.
-
Adzalengeza “uthenga wabwino” modzichepetsa.—Yesaya 61:1; Luka 4:43.
-
Adzanyozedwa ndi kuonedwa ngati munthu wopanda pake.—Yesaya 53:3; Mateyu 26:67, 68.
-
Adzagulitsidwa ndi ndalama 30 zasiliva.—Zekariya 11:12, 13; Mateyu 26:14, 15.
-
Adzakhala chete adani ake akamadzamuweruza kuti aphedwe.—Yesaya 53:6, 7; Mateyu 27:12-14.
-
Adzaphedwa ngati “mwanawankhosa” woperekedwa nsembe kuti achotse machimo a anthu n’cholinga choti Mulungu aziwaona kuti ndi olungama.—Yesaya 53:7; Yohane 1:29, 34, 36.
-
Adzaphedwa koma mafupa ake sadzathyoledwa.—Salimo 34:20; Yohane 19:33, 36.
-
Adzaikidwa m’manda a anthu olemera.—Yesaya 53:9; Mateyu 27:57-60.
-
Adzauka pa tsiku lachitatu.—Mateyu 16:21; 28:5-7.
Maulosi onsewa, komanso ena ambiri, anakwaniritsidwa pa Yesu. Iye anachiritsanso odwala ndi kuukitsa akufa. Zimenezi ndi umboni woti Yesu ndi Mesiya. Zimatithandizanso kukhulupirira kuti zimene Baibulo limalonjeza, zoti adzachitanso zomwezi padziko lonse, ndi zoona. (Luka 7:21-23; Chivumbulutso 21:3, 4) Yesu ataukitsidwa n’kupita kumwamba, anakhala ‘kudzanja lamanja’ la Mulungu. Ankayembekezera kuti ifike nthawi yoti adzakwaniritse udindo wake wachiwiri uja.—Salimo 110:1-6.
“Akadzafika Khristu, kodi adzachita zizindikiro zochuluka kuposa zimene munthu uyu wachita?”—Yohane 7:31.
Kodi Mesiya adzachita chiyani pomalizitsa ntchito yake?
Ayuda a m’nthawi ya Yesu ankayembekezera kuti Mesiya akadzabwera adzawamasula ku ulamuliro wa Aroma, adzabwezeretsa Ufumu kwa Aisiraeli ndipo adzakhala Mfumu yawo. (Machitidwe 1:6) Koma patapita nthawi, otsatira a Yesu omwe anali Ayuda anadziwa kuti Yesu adzamalizitsa udindo wake wachiwiri ali kumwamba monga Mfumu yopatsidwa mphamvu.—Mateyu 28:18.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Pokwaniritsa udindo wake wachiwiri Mesiya . . .
-
Adzakhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu womwe udzalamulire padziko lonse.—Danieli 7:13, 14; Chivumbulutso 11:15.
-
Adzadalitsa anthu onse amene amamukhulupirira.—Genesis 22:17, 18; Salimo 72:7, 8.
-
“Adzadabwitsa mitundu yambiri” ndi olamulira awo akamadzawononga onse amene amamutsutsa.—Yesaya 52:15; Chivumbulutso 19:19, 20.
-
Adzapulumutsa “khamu lalikulu” la anthu olungama pa chisautso chachikulu ndipo anthuwo adzakhala m’dziko lamtendere.—Chivumbulutso 7:9, 10, 13-17.
-
Iye pamodzi ndi Yehova Mulungu adzaukitsa anthu amene anamwalira kuti adzakhale m’Paradaiso padziko lapansi.—Luka 23:43; Yohane 5:21, 28, 29.
-
Adzaphunzitsa nzika za Ufumu wa Mulungu kuti zizikhala mwamtendere.—Yesaya 11:1, 2, 9, 10.
-
Adzachotsa uchimo womwe umapangitsa kuti anthufe tizidwala komanso kufa.—Yohane 1:29; Aroma 5:12.
-
Adzawononga ntchito zonse za Satana ndipo adzathandiza kuti anthu onse azilambira Yehova Mulungu mogwirizana.—1 Akorinto 15:25-28; 1 Yohane 3:8.
Yesu anakwaniritsa kale udindo wake woyamba monga Mesiya. M’tsogolomu adzakwaniritsanso udindo wake wachiwiri. Choncho tingachite bwino kuphunzira za Yesu kuti timudziwe bwino. Ndipotu iye anati: “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo.”—Yohane 14:6.
“M’masiku ake, wolungama adzaphuka, ndipo padzakhala mtendere wochuluka kwa nthawi yonse pamene mwezi udzakhalepo. Ndipo adzakhala ndi anthu omugonjera . . . kukafika kumalekezero a dziko lapansi.”—Salimo 72:7, 8.
^ ndime 5 Mawu akuti “Mesiya” ndiponso “Khristu” tanthauzo lake ndi limodzi. “Mesiya” ndi mawu ochokera ku Chiheberi pomwe “Khristu” ndi mawu ochokera ku Chigiriki.—Yohane 1:41.
^ ndime 7 Lemba loyamba likunena za ulosi ndipo lachiwiri likunena za kukwaniritsidwa kwake.