Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MFUNDO ZA M’BAIBULO N’ZOTHANDIZABE MASIKU ANO?

Mfundo Zake N’zothandiza Nthawi Zonse—Kuchita Zinthu Mwachilungamo

Mfundo Zake N’zothandiza Nthawi Zonse—Kuchita Zinthu Mwachilungamo

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Ndani amene angakhale mlendo m’chihema [cha Mulungu]? . . . Ndi amene akuyenda mosalakwitsa zinthu, amene amachita chilungamo, ndi kulankhula zoona mumtima mwake.”Salimo 15:1, 2.

UBWINO WOCHITA ZINTHU MWACHILUNGAMO: Anthu ambiri amadziwa kufunika kochita zinthu mwachilungamo ndi mokhulupirika. Koma mpata ukapezeka n’kuona kuti akhoza kupeza phindu ndipo sagwidwa, ambiri amachita zachinyengo. Choncho, kuti munthu apewe chinyengo, zingadalire mmene mtima wake ulili.

Raquel, yemwe ankagwira ntchito yogula zinthu za kampani yawo, anati: “Anthu ena ogulitsa zinthu ankandikopa kuti ndizichita zachinyengo. Ankandiuza kuti ndikawagula iwowo, azitigulitsa motchipa katundu wawo ndipo ndalama zomwe achotserazo, zizikhala zanga. Koma ndinkakumbukira kuti Baibulo limati tiyenera kuchita zinthu mwachilungamo ndipo ndinkakana. Abwana anga atamva zimenezi, anayamba kundikhulupirira kwambiri.”

Raquel akanavomera kuchita zachinyengo, bwenzi akupeza ndalama, koma khalidwe limeneli silikanamufikitsa patali. Mukuganiza kuti chikanachitika n’chiyani abwana ake akanadziwa kuti akuchita zachinyengo? Kodi sakanamuchotsa ntchito? Nanga zimenezi sizikanapangitsa kuti avutike kupeza ntchito ina? Raquel anaganizira mfundo zonsezi ndipo anaona kuipa kochita zinthu mwachinyengo. Koma chofunika kwambiri, anaona kuti kuchita zimenezi kumuipitsira mbiri komanso kukwiyitsa Yehova. Lemba la Miyambo 22:1 limati: “Ndi bwino kusankha dzina labwino kusiyana ndi chuma chochuluka. Kulemekezedwa kuli bwino kuposa siliva ndi golide.”

Jessie ankadziwika kuti ndi wokhulupirika pa ntchito

Jessie nayenso ankachita zinthu mokhulupirika kuntchito kwawo. Zimenezi zinapangitsa kuti akhale ndi mbiri yabwino ndipo abwana ake ankamudalira. Choncho, anamukweza pa ntchito komanso anamupatsa ufulu wambiri. Izi zinachititsa kuti azikhala ndi nthawi yochita zinthu zosiyanasiyana ndi banja lake komanso yochita zinthu zauzimu.

Mabwana ena akamafuna antchito, amapita kwa anthu omwe amadziwika kuti ndi okhulupirika. Mwachitsanzo ku Philippines, bwana wa kampani ina analembera ofesi ya Mboni za Yehova n’kuwauza kuti auze a Mboni kuti afunsire ntchito ku kampani yawo. Iye ananena kuti a Mboni za Yehova ndi “olimbikira ntchito, okhulupirika komanso odzipereka pa ntchito.” Komabe timadziwa kuti zimenezi zimatheka chifukwa choti Yehova amatiphunzitsa kuti ‘tizidana ndi choipa ndi kukonda chabwino.’—Amosi 5:15.