Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MFUNDO ZA M’BAIBULO N’ZOTHANDIZABE MASIKU ANO?

Mfundo Zake N’zothandiza Nthawi Zonse—Chikondi

Mfundo Zake N’zothandiza Nthawi Zonse—Chikondi

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Valani chikondi, pakuti chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.”Akolose 3:14.

UBWINO WOSONYEZA CHIKONDI: Chikondi chimene chimatchulidwa m’Baibulo kawirikawiri, si chikondi cha pakati pa mwamuna ndi mkazi. Koma ndi chikondi chomwe timasonyeza chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo. Munthu amene ali ndi chikondichi amakhala ndi makhalidwe monga, chifundo, kukhululuka, kudzichepetsa, kukhulupirika, kukoma mtima, kufatsa ndi kuleza mtima. (Mika 6:8; Akolose 3:12, 13) Chikondi chimene chimakhalapo pakati pa mwamuna ndi mkazi chikhoza kuzirala mkupita kwa nthawi. Koma chikondi chomwe timasonyeza chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo, sichitha.

Brenda, yemwe wakhala m’banja kwa zaka pafupifupi 30 anati: “Anthu akangokwatirana kumene amaona kuti akukondana kwambiri. Koma akakhala m’banja zaka zambiri, amaona kuti m’pamene akukondana kwambiri kuposa poyamba paja.”

Sam, yemwe wakhala m’banja kwa zaka zoposa 12 anati: “Ine ndi mkazi wanga timaona kuti malangizo a m’Baibulo ndi othandiza komanso si ovuta kuwatsatira. Zimenezi zimatichititsa chidwi kwambiri. Ndimaona kuti ndikamatsatira malangizo a m’Baibulo zinthu zimandiyendera bwino. Komabe nthawi zina ndikatopa, ndikakhala kuti ndili ndi nkhawa kapena ndikhala kuti ndikungoganizira za ineyo, ndimalephera kutsatira malangizo a m’Baibulo. Zikatere ndimapempha Yehova kuti andithandize. Kenako ndimamusonyeza mkazi wanga kuti ndimamukonda, basi n’kuiwala nkhaniyo.”

“Nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha ntchito zake”

Yesu Khristu anati “nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha ntchito zake.” (Mateyu 11:19) Zimene takambiranazi ndi umboni woti Baibulo lili ndi malangizo othandiza pa nkhani zosiyanasiyana. Zimene limaphunzitsa komanso mfundo zake n’zothandiza kwambiri ndipo sizitha ntchito. Zimagwira ntchito kwa anthu a zikhalidwe komanso mayiko osiyanasiyana. Zimenezi zimachita kusonyezeratu kuti nzeru zomwe zili m’Baibulo n’zochokera kwa Yehova Mulungu, yemwe ndi Mlengi wathu. Koma Baibulo lingamuthandize munthu pokhapokha ngati akutsatira mfundo zake, osati kungoliwerenga basi. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Talawani ndipo muona kuti Yehova ndi wabwino.” (Salimo 34:8) Tikukulimbikitsani kuti nanunso muyambe kutsatira mfundo za m’Baibulo kuti muone mmene zingakuthandizireni.