Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MFUNDO ZA M’BAIBULO N’ZOTHANDIZABE MASIKU ANO?

Mfundo Zake N’zothandiza Nthawi Zonse—Kusakwiya Msanga

Mfundo Zake N’zothandiza Nthawi Zonse—Kusakwiya Msanga

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Wopusa amatulutsa mkwiyo wake wonse, koma wanzeru amakhala wodekha mpaka pamapeto.”Miyambo 29:11.

“Ndimaona kuti ndinapulumuka lokumbakumba”

UBWINO WOSAKWIYA MSANGA: Titati titchule ubwino wosakwiya msanga, dzuwa likhoza kulowa. Koma ubwino wina ndi woti, munthu wosakwiya msanga amakhala ndi thanzi labwino. Baibulo limati: “Mtima wodekha ndiwo moyo wa munthu.” Limanenanso kuti: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa.” (Miyambo 14:30; 17:22) Akatswiri ambiri anapeza kuti anthu amene amakwiya pafupipafupi amakhala pa ngozi yoti angathe kudwala matenda osiyanasiyana, makamaka matenda a mtima. Komatu kusakwiya msanga sikumangothandiza munthu kukhala ndi thanzi labwino. Kumathandizanso kuti azikhala bwino ndi anthu.

Mwachitsanzo Cassius, yemwe ali ndi zaka za m’ma 30 anati: “Poyamba ndinali munthu wovuta ndipo sindinkachedwa kupsa mtima. Sindinkati ndamenyana liti ndi anthu. Komabe pansi pa mtima ndinkadziona kuti ndine munthu wachabechabe. Koma nditayamba kutsatira mfundo za m’Baibulo ndinasintha kwambiri ndipo ndinayamba kuugwira mtima. Ndinkayesetsanso kukhala wodzichepetsa komanso wokhululuka. Ndikanapanda kusintha, mwina bwenzi pano ndili kundende kapena bwenzi nditafa. Kunena zoona ndimaona kuti ndinapulumuka lokumbakumba.”

Cassius anayamba kukhululuka komanso kuugwira mtima, ena akamuputa