Pitani ku nkhani yake

Kodi Maulosi Onena za Mesiya Amatsimikizira Kuti Yesu Analidi Mesiya?

Kodi Maulosi Onena za Mesiya Amatsimikizira Kuti Yesu Analidi Mesiya?

Yankho la m’Baibulo

Inde. Yesu ali padzikoli anakwaniritsa maulosi ambiri onena za “Mesiya Mtsogoleri” amenenso adzakhale “Mpulumutsi wa dziko.” (Danieli 9:25; 1 Yohane 4:14) Ndipotu ngakhale atamwalira n’kuukitsidwa, Yesu anapitirizabe kukwaniritsa maulosi onena za Mesiya.​—Salimo 110:1; Machitidwe 2:34-36.

 Kodi dzina lakuti “Mesiya” limatanthauza chiyani?

Mawu Achiheberi akuti Ma·shiʹach kapena kuti Mesiya omwenso ndi ofanana ndi mawu Achigiriki akuti Khri·stos kapena kuti Khristu, amatanthauza kuti “Wodzozedwa.” Choncho dzina lakuti, “Yesu Khristu” limatanthauza kuti “Yesu ndi Wodzozedwa,” kapena kuti “Yesu ndi Mesiya.”

Kale, nthawi zambiri munthu akamaikidwa pa udindo winawake wapadera, ankamuthira mafuta pamutu posonyeza kuti wadzozedwa. (Levitiko 8:12; 1 Samueli 16:13) Mulungu anadzoza Yesu kuti akhale Mesiya ndipo udindo umenewu ndi waukulu kwambiri. (Machitidwe 2:36) Komabe Mulungu sanadzoze Yesu ndi mafuta enieni, koma anamudzoza ndi mzimu woyera.​—Mateyu 3:16.

 Kodi maulosi onena za Mesiya anakwaniritsidwa ndi anthu angapo?

Ayi. Monga mmene zimakhalira kuti chidindo cha chala sichingaimire anthu awiri, maulosi a m’Baibulo onena za Mesiya ankafunika kukwaniritsidwa pa munthu m’modzi. Ndipo Baibulo linapereka chenjezo lakuti, “kudzafika onamizira kukhala Khristu ndi aneneri onyenga, ndipo adzachita zizindikiro zamphamvu ndiponso zodabwitsa, kuti ngati n’kotheka, adzasocheretse ngakhale osankhidwawo.”​—Mateyu 24:24.

 Kodi Mesiya adzaonekera m’tsogolo?

Ayi. Baibulo linaneneratu kuti Mesiya adzachokera m’banja la Mfumu Davide ya ku Isiraeli. (Salimo 89:3, 4) Komabe zikuoneka kuti mipukutu yakale ya Ayuda yofotokoza za mzere wa makolo mpaka kukafika pa Davide, inasowa ndipo n’kutheka kuti mipukutuyi inawonongedwa pa nthawi imene Aroma anabwera kudzagonjetsa Yerusalemu mu 70 C.E. * Kuchokera nthawi imeneyo palibe munthu winanso akananena kuti iyeyo ndi Mesiya wochokeradi m’banja lachifumu la Davide. Ngakhale zili choncho, m’nthawi ya Yesu mipukutuyo inalipo ndipo adani ake sakanatsutsa zomwe iye ananena kuti ndi wochokera m’banja la Davide.​—Mateyu 22:41-46.

 Kodi m’Baibulo muli maulosi angati onena za Mesiya?

N’zovuta kutchula kuti maulosi onena za Mesiya ndi ochuluka bwanji. Ndipo njira imene wina angagwiritse ntchito powerengera kuchuluka kwa maulosi, ikhoza kusiyana ndi imene wina angagwiritsenso ntchito, ngakhale pa nkhani zimene zikuonekeratu kuti zikufotokoza za Mesiya. Mwachitsanzo, nkhani ya pa Yesaya 53:2-7, imafotokoza za maulosi osiyanasiyana onena za Mesiya. Ena akhoza kuona mavesi onsewa ngati ulosi umodzi, pamene ena akhoza kuona mfundo iliyonse ngati ulosi pawokha.

 Ena a maulosi onena za Mesiya omwe anakwaniritsidwa pa Yesu

Ulosi

Umapezeka pa

Kukwaniritsidwa kwake

Mbewu ya Abulahamu

Genesis 22:17, 18

Mateyu 1:1

Mbadwa ya Isaki yemwe anali mwana wa Abulahamu

Genesis 17:19

Mateyu 1:2

Adzabadwira mu mtundu wa Chiyuda

Genesis 49:10

Mateyu 1:1, 3

Adzabadwira mumzere wa banja lachifumu la Mfumu Davide

Yesaya 9:7

Mateyu 1:1

Adzabadwa kwa namwali

Yesaya 7:14

Mateyu 1:18, 22, 23

Adzabadwira ku Betelehemu

Mika 5:2

Mateyu 2:1, 5, 6

Adzapatsidwa dzina lakuti Emanueli *

Yesaya 7:14

Mateyu 1:21-23

Adzabadwira m’banja losauka

Yesaya 53:2

Luka 2:7

Ana aang’ono adzaphedwa iye akadzangobadwa

Yeremiya 31:15

Mateyu 2:16-18

Adzaitanidwa kuti achoke ku Iguputo

Hoseya 11:1

Mateyu 2:13-15

Adzatchedwa Mnazareti *

Yesaya 11:1

Mateyu 2:23

Mthenga adzatsogola kudzalengeza za iye

Malaki 3:1

Mateyu 11:7-10

Adzadzozedwa kukhala Mesiya mu 29 C.E *

Danieli 9:25

Mateyu 3:13-17

Mulungu adzatsimikizira kuti Yesu ndi Mwana wake

Salimo 2:7

Machitidwe 13:33, 34

Adzadzipereka kwambiri panyumba ya Mulungu

Salimo 69:9

Yohane 2:13-17

Adzalengeza uthenga wabwino

Yesaya 61:1

Luka 4:16-21

Adzalalikira ku Galileya ndipo anthu ambiri adzaona kuwala

Yesaya 9:1, 2

Mateyu 4:13-16

Adzachita zozizwitsa ngati Mose

Deuteronomo 18:15

Machitidwe 2:22

Adzalankhula Mawu ochokera kwa Mulungu ngati mmene anachitira Mose

Deuteronomo 18:18, 19

Yohane 12:49

Adzachiritsa anthu ambiri

Yesaya 53:4

Mateyu 8:16, 17

Sadzakhala wodzikonda

Yesaya 42:2

Mateyu 12:17, 19

Adzachitira chifundo anthu ovutika

Yesaya 42:3

Mateyu 12:9-20; Maliko 6:34

Adzasonyeza chilungamo cha Mulungu

Yesaya 42:1, 4

Mateyu 12:17-20

Mlangizi wodabwitsa

Yesaya 9:6, 7

Yohane 6:68

Adzalengeza za dzina la Yehova

Salimo 22:22

Yohane 17:6

Adzagwiritsa ntchito mafanizo pophunzitsa

Salimo 78:2

Mateyu 13:34, 35

Mtsogoleri

Danieli 9:25

Mateyu 23:10

Anthu ambiri sadzamukhulupirira

Yesaya 53:1

Yohane 12:37, 38

Adzakhala mwala wopunthwitsa

Yesaya 8:14, 15

Mateyu 21:42-44

Anthu adzamukana

Salimo 118:22, 23

Machitidwe 4:10, 11

Anthu adzadana naye popanda chifukwa

Salimo 69:4

Yohane 15:24, 25

Adzalowa mu Yerusalemu mwaulemerero atakwera pabulu

Zekariya 9:9

Mateyu 21:4-9

Adzatamandidwa ndi ana

Salimo 8:2

Mateyu 21:15, 16

Adzabwera m’dzina la Yehova

Salimo 118:26

Yohane 12:12, 13

Adzaperekedwa ndi mnzake wapamtima

Salimo 41:9

Yohane 13:18

Adzaperekedwa ndi ndalama 30 zasiliva *

Zekariya 11:12, 13

Mateyu 26:14-16; 27:3-10

Anzake adzamuthawa

Zekariya 13:7

Mateyu 26:31, 56

Anthu adzamuperekera umboni wabodza

Salimo 35:11

Mateyu 26:59-61

Sadzayankha chilichonse kwa anthu omuimba mlandu

Yesaya 53:7

Mateyu 27:12-14

Adzamulavulira

Yesaya 50:6

Mateyu 26:67; 27:27, 30

Adzamenyedwa m’mutu

Mika 5:1

Maliko 15:19

Adzakwapulidwa

Yesaya 50:6

Yohane 19:1

Sadzabwezera anthu omumenya

Yesaya 50:6

Yohane 18:22, 23

Olamulira adzagwirizana kuti alimbane naye

Salimo 2:2

Luka 23:10-12

Adzamukhomerera manja ndi mapazi ake kumtengo

Salimo 22:16

Mateyu 27:35; Yohane 20:25

Anthu adzachitira mayere zovala zake

Salimo 22:18

Yohane 19:23, 24

Adzakhala ngati m’modzi wa anthu ochimwa

Yesaya 53:12

Mateyu 27:38

Adzanyozedwa ndi kumunenera zachipongwe

Salimo 22:7, 8

Mateyu 27:39-43

Adzavutika chifukwa cha anthu ochimwa

Yesaya 53:5, 6

1 Petulo 2:23-25

Adzakhala ngati wakanidwa ndi Mulungu

Salimo 22:1

Maliko 15:34

Adzapatsidwa vinyo wosakaniza ndi ndulu kuti amwe

Salimo 69:21

Mateyu 27:34

Adzamva ludzu asanamwalire

Salimo 22:15

Yohane 19:28, 29

Adzapereka mzimu wake kwa Mulungu

Salimo 31:5

Luka 23:46

Adzataya moyo wake

Yesaya 53:12

Maliko 15:37

Adzapereka dipo kuti achotse uchimo

Yesaya 53:12

Mateyu 20:28

Mafupa ake sadzathyoledwa

Salimo 34:20

Yohane 19:31-33, 36

Adzalasidwa

Zekariya 12:10

Yohane 19:33-35, 37

Adzaikidwa m’manda pamodzi ndi anthu olemera

Yesaya 53:9

Mateyu 27:57-60

Adzaukitsidwa kwa akufa

Salimo 16:10

Machitidwe 2:29-31

Womupereka adzalowedwa m’malo ndi munthu wina

Salimo 109:8

Machitidwe 1:15-20

Adzakhala kudzanja lamanja la Mulungu

Salimo 110:1

Machitidwe 2:34-36

^ ndime 15 Buku la McClintock and Strong’s Cyclopedia limanena kuti: “Sitikukayikira kuti kaundula wonena za anthu a mtundu wachiyuda komanso mabanja awo anasokonezekera pa nthawi imene Yerusalemu ankawonongedwa.”

^ ndime 40 Dzina lakuti Emanueli ndi la Chiheberi ndipo limatanthauza kuti “Mulungu Ali Nafe.” Dzinali limafotokoza bwino za udindo wa Yesu monga Mesiya. Kubwera kwake padzikoli komanso zimene anachita, zinasonyeza kuti Mulungu ali kumbali ya anthu omwe amamulambira.​—Luka 2:27-32; 7:12-16.

^ ndime 52 Mawu akuti “Mnazareti” anachokera ku mawu achiheberi akuti neʹtser, omwe amatanthauza “mphukira.”

^ ndime 58 Kuti mudziwe zambiri zokhudza maulosi a m’Baibulo kudzafika mu 29 C.E. chaka chomwe Mesiya anafika, werengani nkhani yakuti, “Mmene Ulosi wa Danieli Unasonyezera Nthawi Imene Mesiya Adzafike,” m’buku la kodi Baibulo limaphunzitsa Chiyani, patsamba 197—199. (mu kabuku ka Zimene Baibulo Limaphunzitsa, ndi patsamba 211-212 koma mutu wake ndi wina)

^ ndime 127 Ulosi umenewu uli m’buku la Zekariya ngakhale kuti Mateyu amene analemba nawo Baibulo ananena kuti ulosiwu unanenedwa “kudzera mwa mneneri Yeremiya.” (Mateyu 27:9) Zikuoneka kuti nthawi ina m’mbuyomo buku la Yeremiya, linkaikidwa koyambirira m’mabuku omwe ankadziwika kuti “Zolemba za Aneneri.” (Luka 24:44) Choncho n’kutheka kuti Mateyu ananena kuti ulosiwu uli m’buku la “Yeremiya” pofotokoza za mabuku onse a aneneriwo omwe ankaphatikizaponso buku la Zekariya.