Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Maliko 8:1-38

  • Yesu adyetsa anthu 4,000 (1-9)

  • Apempha cizindikilo (10-13)

  • Zofufumitsa za Afarisi ndi za Herode (14-21)

  • Munthu wakhungu acilitsidwa ku Betsaida (22-26)

  • Petulo azindikila Khristu (27-30)

  • Yesu anenelatu za imfa yake (31-33)

  • Zimene ophunzila oona a Yesu amacita (34-38)

8  M’masiku amenewo, khamu lalikulu la anthu linasonkhananso, koma linalibe cakudya. Conco Yesu anaitana ophunzila ake n’kuwauza kuti: 2  “Ndikuwamvela cifundo anthuwa cifukwa akhala nane masiku atatu, ndipo alibe cakudya. 3  Ndikawauza kuti azipita kwao ndi njala,* akomoka m’njila, ndipo ena mwa iwo kwao n’kutali kwambili.” 4  Koma ophunzila ake anamuyankha kuti: “Kodi munthu angapeze kuti cakudya cokwanila anthu onsewa kumalo opanda anthu ngati kuno?” 5  Pamenepo iye anawafunsa kuti: “Muli ndi mitanda ingati ya mkate?” Iwo anati: “Tili nayo 7.” 6  Ndiyeno anauza anthuwo kuti akhale pansi. Kenako anatenga mitanda 7 ija ya mkate n’kuyamika, pambuyo pake anainyema-nyema n’kuyamba kupatsa ophunzila ake kuti aigawile kwa anthuwo. Ndipo iwo anaipeleka kwa anthuwo. 7  Analinso ndi tunsomba tocepa, ndipo atatudalitsa anauzanso ophunzila ake kuti atugawile kwa anthuwo. 8  Conco anadya n’kukhuta, ndipo anasonkhanitsa zotsala zokwana matadza* 7 akulu-akulu. 9  Amene anadya analipo amuna pafupifupi 4,000. Kenako anauza anthuwo kuti azipita. 10  Nthawi yomweyo iye anakwela bwato pamodzi ndi ophunzila ake n’kupita ku cigao ca Dalamanuta. 11  Kumeneko, Afarisi anabwela n’kuyamba kukangana naye. Iwo anali kumuumiliza kuti awaonetse cizindikilo cocokela kumwamba pofuna kumuyesa. 12  Conco pomva cisoni iye anafuza mwamphamvu n’kunena kuti: “N’cifukwa ciani m’badwo uwu ukufuna-funa cizindikilo? Ndithu ndikukuuzani, m’badwo uwu sudzapatsidwa cizindikilo ciliconse.” 13  Atakamba zimenezi, anawasiya n’kukwelanso bwato kupita ku tsidya lina la nyanja. 14  Koma ophunzilawo anaiwala kunyamula mkate, ndipo analibe cakudya ciliconse m’bwatomo kupatulapo mtanda umodzi wa mkate. 15  Ndipo iye anawacenjeza mosapita m’mbali kuti: “Khalani maso ndipo samalani ndi zofufumitsa za Afarisi komanso zofufumitsa za Herode.” 16  Conco iwo anayamba kukangana pa nkhani yakuti sananyamule mkate. 17  Yesu atadziwa zimenezi, anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciani mukukangana zakuti mulibe mkate? Kodi mpaka pano simukuzindikila ndi kumvetsa tanthauzo lake? Kodi mitima yanu ikali yosazindikila? 18  ‘Ngakhale kuti maso muli nao, kodi simukuona, komanso ngakhale kuti matu muli nao kodi simukumva?’ Simukukumbukila kodi 19  zimene zinacitika pamene n’nanyema-nyema mitanda isanu ya mkate n’kupatsa amuna 5,000? Kodi zotsala zimene munasonkhanitsa zinakwana matadza angati?” Iwo anayankha kuti: “Matadza 12.” 20  “Nanga pamene n’nanyema-nyema mitanda 7 ya mkate n’kupatsa amuna 4,000, kodi zotsala zimene munasonkhanitsa zinadzala matadza* angati akulu-akulu?” Iwo anamuyankha kuti: “Matadza 7.” 21  Pamenepo iye anawafunsa kuti: “Ndiye kodi simukumvetsabe?” 22  Tsopano anafika ku Betsaida. Kumeneko anthu anamubweletsela munthu wakhungu, ndipo anamucondelela kuti amukhudze munthuyo. 23  Iye anagwila dzanja la munthu wakhunguyo n’kupita naye kunja kwa mudzi. Ndiye atamuthila mata m’maso, anaika manja ake pa iye n’kunena kuti: “Kodi ukuona ciliconse?” 24  Munthuyo anayang’ana kumwamba n’kunena kuti: “Ndikuona anthu, koma akuoneka monga mitengo imene ikuyenda.” 25  Iye anagwilanso m’maso mwa munthuyo, ndipo anayamba kuona bwino-bwino. Maso ake anatseguka moti anayamba kuona ciliconse bwino-bwino. 26  Basi anamuuza kuti azipita kunyumba, ndipo anati: “Usalowe m’mudzimu.” 27  Tsopano Yesu ndi ophunzila ake ananyamuka kupita ku midzi ya Kaisareya wa ku Filipi. Ali m’njila, anayamba kufunsa ophunzilawo kuti: “Kodi anthu amati ndine ndani?” 28  Iwo anamuyankha kuti: “Amati ndinu Yohane M’batizi, koma ena amati ndinu Eliya. Ndipo enanso amati ndinu mmodzi wa aneneli.” 29  Ndiyeno anafunsa ophunzilawo kuti: “Nanga inu mumati ndine ndani?” Petulo anamuyankha kuti: “Ndinu Khristu.” 30  Pamenepo anawalamula mwamphamvu kuti asauze aliyense za iye. 31  Komanso anayamba kuwaphunzitsa kuti Mwana wa munthu ayenela kukumana ndi masautso ambili ndiponso kukanidwa ndi akulu, ansembe aakulu, komanso alembi, kenako adzaphedwa. Ndipo pambuyo pa masiku atatu adzaukitsidwa. 32  Ndithudi, iye anali kukamba zimenezi poyela. Koma Petulo anamutengela pambali n’kuyamba kumudzudzula. 33  Atamva izi anaceuka n’kuyang’ana ophunzila ake. Kenako anadzudzula Petulo kuti: “Pita kumbuyo kwanga Satana! Ndiwe copunthwitsa kwa ine, cifukwa zimene ukuganiza si maganizo a Mulungu koma maganizo a anthu.” 34  Ndiyeno anauza khamu la anthu pamodzi ndi ophunzila ake kuti abwele kwa iye. Kenako anawauza kuti: “Ngati munthu akufuna kunditsatila adzikane yekha, ndipo anyamule mtengo wake wozunzikilapo* n’kupitiliza kunditsatila. 35  Pakuti aliyense wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya, koma aliyense wotaya moyo wake cifukwa ca ine komanso cifukwa ca uthenga wabwino, adzaupeza. 36  Kunena zoona, kodi pali phindu lanji munthu atapeza zinthu zonse za m’dzikoli, koma n’kutaya moyo wake? 37  Kapena kodi munthu angapeleke ciani cosinthanitsa ndi moyo wake? 38  Pakuti aliyense wocita manyazi ndi ine komanso ndi mau anga mu m’badwo wacigololo* ndiponso wocimwawu, Mwana wa munthu adzacitanso naye manyazi akadzabwela mu ulemelelo wa Atate wake pamodzi ndi angelo oyela.”

Mau a m'Munsi

^ Kapena kuti, “kwao asanadye.”
^ Kapena kuti, “matadza onyamulilamo zinthu.”
^ Kapena kuti, “matadza onyamulilamo zinthu.”
^ Kapena kuti, “wosakhulupilika.”