Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Maliko 3:1-35

  • Munthu wa dzanja lopuwala acilitsidwa (1-6)

  • Khamu lalikulu la anthu m’mbali mwa nyanja (7-12)

  • Atumwi 12 (13-19)

  • Kunyoza mzimu woyela (20-30)

  • Mai a Yesu ndi abale ake (31-35)

3  Pa nthawi inanso Yesu analowa m’sunagoge, ndipo m’sunagogemo munali munthu wina wopuwala* dzanja. 2  Conco Afarisi anali kumuyang’anitsitsa kuti aone ngati angacilitse munthuyo pa Sabata. Colinga cao cinali cakuti amuimbe mlandu. 3  Ndiyeno Yesu anauza munthu wopuwala* dzanjayo kuti: “Nyamuka bwela pakatipa.” 4  Kenako anawafunsa kuti: “Kodi cololeka n’citi pa Sabata, kucita cabwino kapena coipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha?” Koma iwo anangokhala cete. 5  Yesu anawayang’ana mokwiya ndipo anamva cisoni kwambili poona kuuma mitima kwao. Kenako anauza munthuyo kuti: “Tambasula dzanja lako.” Iye analitambasuladi, ndipo linakhala bwino. 6  Zitatelo Afarisiwo anatuluka, ndipo nthawi yomweyo anayamba kukambilana ndi acipani ca Herode zakuti amuphe. 7  Koma Yesu anacoka n’kupita ku nyanja pamodzi ndi ophunzila ake, ndipo khamu lalikulu la anthu ocokela ku Galileya komanso ku Yudeya linamutsatila. 8  Ngakhalenso anthu ambili ocokela ku Yerusalemu, ku Idumeya, ku tsidya lina la Yorodano komanso kumadela a Turo ndi Sidoni, anabwela kwa iye atamva zinthu zambili zimene anali kucita. 9  Ndipo iye anauza ophunzila ake kuti amubweletsele bwato laling’ono loti akwelemo kuti khamulo lisamupanikize. 10  Cifukwa cakuti anacilitsa anthu ambili, onse amene anali ndi matenda aakulu, anamuunjilila kuti angomukhudza. 11  Ngakhale mizimu yonyansa ikamuona inali kudzigwetsa pansi n’kupfuula kuti: “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.” 12  Koma mobweleza-bweleza iye anali kuilamula mwamphamvu kuti isamuulule. 13  Yesu anakwela m’phili n’kuitana anthu amene anali kuwafuna, ndipo iwo anapita kwa iye. 14  Ndiyeno anapanga* gulu la anthu 12, amenenso anawacha atumwi. Anthu amenewa anali oti aziyenda naye komanso kuti aziwatuma kukalalikila 15  ndi kuwapatsa mphamvu zotulutsa ziwanda. 16  Ndipo pa gulu la anthu 12 amenewo panali Simoni, amene anamupatsanso dzina lakuti Petulo, 17  Yakobo mwana wa Zebedayo ndi Yohane m’bale wake wa Yakobo (Awiliwa anawapatsanso dzina lakuti Bowanege, kutanthauza “Ana a Bingu”), 18  Andireya, Filipo, Batulomeyo, Mateyo, Thomasi, Yakobo mwana wa Alifeyo, Tadeyo, Simoni Kananiya,* 19  komanso Yudasi Isikariyoti amene pambuyo pake anapeleka Yesu. Ndiyeno iye atalowa m’nyumba, 20  khamu la anthu linasonkhananso, moti iwo sanathe ngakhale kudya cakudya. 21  Koma acibale ake atamva nkhaniyi, anapita kukamugwila, cifukwa anali kunena kuti: “Ameneyu wafuntha.” 22  Komanso, alembi amene anacokela ku Yerusalemu anali kunena kuti: “Ali ndi Belezebule* ndipo amatulutsa ziwanda ndi mphamvu za wolamulila ziwanda.” 23  Conco atawaitana anayamba kulankhula nao mwa mafanizo kuti: “Kodi Satana angatulutse bwanji Satana? 24  Ngati ufumu wagawikana, ufumuwo sukhalitsa; 25  ndipo ngati nyumba yagawikana, nyumbayo singalimbe. 26  Mofanana ndi zimenezi, ngati Satana wadziukila yekha, ndipo wagawikana, iye sangakhalitse koma amenewo adzakhala mapeto ake. 27  Kukamba zoona, palibe aliyense angalowe m’nyumba ya munthu wamphamvu kuti amubele katundu, asanayambe wam’manga munthu wamphamvuyo. Akamumanga m’pamene angathe kutenga zinthu m’nyumbamo. 28  Ndithu ndikukuuzani kuti, ana a anthu adzakhululukidwa zinthu zonse, kaya anacita macimo otani komanso kaya analankhula mau onyoza otani. 29  Koma aliyense wonyoza mzimu woyela sadzakhululukidwa kwamuyaya.” 30  Iye anakamba izi cifukwa iwo anali kumunena kuti: “Ali ndi mzimu wonyansa.” 31  Tsopano amai ake ndi abale ake anabwela n’kuimilila panja. Kenako anatuma winawake kuti akamuitane. 32  Panali khamu la anthu limene linakhala pansi momuzungulila, ndipo iwo anamuuza kuti: “Mai anu ndi abale anu ali panja ndipo akukufunani.” 33  Koma iye anawayankha kuti: “Kodi mai anga ndi abale anga ndani?” 34  Ndiyeno anayang’ana anthu amene anakhala pansi momuzungulila aja n’kunena kuti: “Ona! Awa ndio amai anga ndi abale anga! 35  Aliyense wocita cifunilo ca Mulungu ameneyo ndiye m’bale wanga, mlongo wanga, komanso mai anga.”

Mau a m'Munsi

^ Kapena kuti, “wolemala.”
^ Kapena kuti, “wolemala.”
^ Kapena kuti, “anasankha.”
^ Kapena kuti, “wokangalika.”
^ Dzina lina la Satana.