Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Maliko 4:1-41
4 Yesu anayambanso kuphunzitsa m’mbali mwa nyanja, ndipo cikhamu ca anthu cinasonkhana pafupi ndi iye. Conco iye anakwela m’bwato n’kukhala m’bwatomo capatali pang’ono ndi anthuwo. Koma khamu lonse la anthulo linali m’mbali mwa nyanjayo.
2 Iye anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambili mwa mafanizo, ndipo powaphunzitsa anawauza kuti:
3 “Tamvelani! Munthu wina anapita kukafesa mbeu.
4 Pamene anali kufesa mbeuzo, zina zinagwela m’mbali mwa mseu, ndipo mbalame zinabwela n’kuzidya.
5 Zina zinagwela pa miyala pomwe panalibe dothi lokwanila, ndipo zinamela mwamsanga cifukwa nthaka inali yosazama.
6 Koma dzuwa litatentha zinawauka, ndipo zinafota cifukwa zinalibe mizu.
7 Mbeu zina zinagwela pa minga, ndipo mingazo zitakula zinalepheletsa mbeuzo kukula moti sizinabale cipatso ciliconse.
8 Koma mbeu zina zinagwela pa nthaka yabwino, ndipo zitamela n’kukula, zinayamba kubala zipatso. Mbeu zina zinabala zipatso 30, zina 60, ndipo zina 100.”
9 Kenako anaonjezela kuti: “Amene ali ndi matu akumva, amve.”
10 Tsopano pamene Yesu anali payekha, anthu amene anali naye komanso atumwi 12 aja anayamba kumufunsa za mafanizowo.
11 Iye anawauza kuti: “Inu mwapatsidwa mwai womvetsa cinsinsi copatulika ca Ufumu wa Mulungu. Koma kwa aja amene ali kunja zinthu zonse zimakambidwa mwa mafanizo,
12 kuti kuyang’ana aziyang’ana ndithu, koma osaona. Kumva azimva ndithu koma osamvetsa tanthauzo lake, komanso kuti asatembenuke n’kukhululukidwa.”
13 Anawauzanso kuti: “Ngati fanizoli simukulimvetsa, ndiye kodi mudzamvetsa bwanji mafanizo ena onse?
14 “Wofesa amafesa mau.
15 Cotelo mbeu zimene zimagwela m’mbali mwa mseu ndi mau amene amafesedwa mwa anthu omwe amati akangomva mauwo, Satana amabwela n’kucotsa mau amene afesedwa mwa iwo.
16 Mofananamo, mbeu zimene zafesedwa pa miyala ndi mau amene amafesedwa mwa anthu amene akangomva mauwo amawalandila mwacimwemwe.
17 Ngakhale n’telo, mauwo sazika mizu mwa iwo. Koma anthuwo amapitiliza kwa kanthawi. Ndiyeno cisautso kapena mazunzo akangobwela cifukwa ca mauwo, iwo amapunthwa.
18 Palinso mbeu zina zimene zimafesedwa pa minga. Mbeu zimenezi ndi anthu amene amamva mau,
19 koma nkhawa za nthawi ino* ndi cinyengo camphamvu ca cuma komanso kulakalaka zinthu zina zonse, zimalowa m’mitima yao ndi kulepheletsa mauwo kukula ndipo sabala zipatso.
20 Cothela, mbeu zimene zinafesedwa pa nthaka yabwino ndi anthu amene amamva mau ndi kuwalandila bwino, ndipo amabala zipatso wina 30, wina 60, ndiponso wina 100.”
21 Iye anawauzanso kuti: “Nyale saibwinikila ndi thadza* kapena kuiika kunsi kwa bedi, amatelo kodi? Kodi saiika pa coikapo nyale?
22 Pakuti palibe cobisika cimene sicidzaululika. Ndipo palibe cobisidwa mosamala kwambili cimene sicidzaonekela poyela.
23 Amene ali ndi matu akumva, amve.”
24 Anawauzanso kuti: “Mvetselani mosamala zimene mukumva. Muyeso umene mukupimila ena, inunso adzakupimilani womwewo. Inde adzakuonjezelani zoculuka.
25 Pakuti aliyense amene ali nazo adzapatsidwa zoculuka, koma aliyense amene alibe adzalandidwa ngakhale zimene ali nazo.”
26 Iye anapitiliza kukamba kuti: “Ufumu wa Mulungu uli monga mmene munthu amamwazila mbeu pa nthaka.
27 Iye amagona usiku ndipo kukaca amauka. Mbeuzo zimamela ndi kukula, koma iye sadziwa mmene izi zimacitikila.
28 Pang’ono-pang’ono, nthakayo payokha imabala zipatso. Umene umayamba ndi mmela, kenako ngala, pothela pake maso okhwima m’ngalamo.
29 Koma mbeuzo zikangoti zaca, iye amazimweta ndi cikwakwa cifukwa nthawi yokolola yakwana.”
30 Ndiyeno anapitiliza kuwauza kuti: “Kodi Ufumu wa Mulungu tingauyelekezele ndi ciani, kapena tingaufotokoze ndi fanizo lotani?
31 Uli ngati kanjele ka mpilu kamene pa nthawi yofesa kamakhala kakang’ono kwambili kuposa njele zonse pa dziko lapansi.
32 Koma kakafesedwa kamamela ndi kukula kwambili kuposa mbeu zina zonse za kudimba. Ndipo kamapanga nthambi zikulu-zikulu, moti mbalame za mumlengalenga zimapeza malo okhala mu mthunzi wake.”
33 Iye analankhula nao mogwilitsa nchito mafanizo ambili otelo malinga ndi zimene akanakwanitsa kumvetsa.
34 Ndithudi, sanalankhule nao popanda fanizo, koma kumbali iye anali kuwafotokozela zinthu zonse ophunzila ake.
35 Tsiku limenelo madzulo, iye anauza ophunzila ake kuti: “Tiyeni tiolokele ku tsidya lina la nyanja.”
36 Conco atauza khamu la anthulo kuti lizipita, ophunzilawo anamutenga n’kupita naye m’bwato, mmene analilimo. Pafupi ndi bwatolo, panalinso mabwato ena.
37 Ndiyeno kunayamba cimphepo camphamvu camkuntho, ndipo mafunde anali kuomba bwatolo moti linatsala pang’ono kumila.
38 Koma iye anali gone kumbuyo m’bwatomo atasamila pilo. Conco anamuutsa ndi kumufunsa kuti: “Mphunzitsi, kodi sizikukukhudzani kuti tikufa?”
39 Pamenepo ananyamuka n’kudzudzula mphepoyo, n’kuuza nyanjayo kuti: “Cete! Khala bata!” Mphepoyo inaleka, ndipo panakhala bata lalikulu.
40 Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciani mukucita mantha conci? Kodi mulibiletu cikhulupililo mpaka pano?”
41 Koma iwo anacita mantha kwambili, ndipo anayamba kufunsana kuti: “Kodi ameneyu ndani maka-maka? Ngakhale mphepo ndi nyanja zikumumvela!”

