Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Maliko 13:1-37

  • CIMALIZILO CA NTHAWI INO (1-37)

    • Nkhondo, zibvomezi, njala (8)

    • Uthenga wabwino udzalalikidwa (10)

    • Cisautso cacikulu (19)

    • Kubwela kwa Mwana wa munthu (26)

    • Fanizo la mtengo wa mkuyu (28-31)

    • Khalanibe maso (32-37)

13  Pamene Yesu anali kutuluka m’kacisi, mmodzi wa ophunzila ake anamuuza kuti: “Mphunzitsi, onani kukongola kwa miyalayi ndi nyumbazi!” 2  Koma Yesu anamufunsa kuti: “Kodi waziona nyumba zikulu-zikulu zokongolazi? Pano sipadzatsala mwala ulionse pamwamba pa unzake umene sudzagwetsedwa.” 3  Atakhala pansi m’Phili la Maolivi, moyang’ana kumene kunali kacisi, Petulo, Yakobo, Yohane, ndi Andireya anamufunsa mwamseli kuti: 4  “Tiuzeni, kodi zinthu zimenezi zidzacitika liti, nanga cizindikilo cakuti zinthu zonsezi zili pafupi kufika kumapeto cidzakhala ciani?” 5  Conco, Yesu anayamba kuwauza kuti: “Samalani kuti munthu asakusoceletseni. 6  Ambili adzabwela m’dzina langa n’kumanena kuti, ‘Khristu uja ndine,’ ndipo adzasoceletsa anthu ambili. 7  Ndiponso mukadzamva phokoso la nkhondo komanso malipoti a nkhondo, musadzacite mantha. Zimenezi ziyenela kucitika, koma mapeto adzakhala asanafikebe. 8  “Mtundu udzaukilana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana ndi ufumu wina. Kudzakhala zibvomezi m’malo osiyana-siyana, komanso kudzakhala njala. Zinthu zonsezi ndi ciyambi ca masautso.* 9  “Koma inu samalani. Anthu adzakupelekani ku makhoti aang’ono, ndipo adzakukwapulani m’masunagoge ndi kukupelekani kwa abwanamkubwa ndi mafumu cifukwa ca ine, kuti ukhale umboni kwa iwo. 10  Komanso uthenga wabwino uyenela kulalikidwa ku mitundu yonse coyamba. 11  Ndipo akakutengani kuti akakupelekeni, musade nkhawa kuti mukakamba ciani. Koma mukakambe zilizonse zimene mudzapatsidwa nthawi yomweyo, pakuti amene adzakamba si inuyo ai, koma mzimu woyela. 12  Komanso munthu adzapeleka m’bale wake kuti aphedwe, tate adzapeleka mwana wake, ndipo ana adzaukila makolo ao n’kuwapeleka kuti aphedwe. 13  Anthu onse adzakudani cifukwa ca dzina langa. Koma amene adzapilile* mpaka pa mapeto adzapulumuka. 14  “Koma mukadzaona cinthu conyansa cobweletsa cionongeko citaimilila pa malo amene siciyenela kuima (wowelenga adzazindikile), pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawila ku mapili. 15  Munthu amene adzakhale pa mtenje asadzatsike kapena kulowa m’nyumba mwake kuti akatenge cinthu ciliconse. 16  Ndipo munthu amene adzakhale ku munda, asadzabwelele ku zinthu zimene wasiya kumbuyo kuti akatenge cobvala cake cakunja. 17  Tsoka kwa akazi apathupi komanso oyamwitsa m’masiku amenewo! 18  Pitilizani kupemphela kuti zimenezi zisadzacitike m’nyengo yozizila, 19  cifukwa masiku amenewo kudzakhala cisautso cimene sicinacitikepo kucokela pa ciyambi ca cilengedwe cimene Mulungu analenga mpaka pa nthawiyo, ndipo sicidzacitikanso. 20  Kukamba zoona, Yehova* akanapanda kucepetsa masikuwo, palibe amene akanapulumuka. Koma cifukwa ca osankhidwa amene iye wawasankha, adzacepetsa masikuwo. 21  “Cotelo munthu akadzakuuzani kuti, ‘Onani! Khristu uja ali kuno,’ kapena kuti, ‘Onani! Ali uko,’ musakakhulupilile. 22  Pakuti kudzabwela anthu onamizila kukhala Khristu komanso aneneli abodza. Ndipo adzacita zizindikilo ndi zodabwitsa, kuti ngati n’kotheka, asoceletse osankhidwawo. 23  Conco samalani. Ine ndakuuzilantoni zinthu zonse. 24  “Koma m’masiku amenewo cisautsoco cikadzatha, dzuwa lidzacita mdima, ndipo mwezi sudzawala. 25  Komanso nyenyezi zidzagwa kucokela kumwamba, ndipo mphamvu zimene zili kumwamba zidzagwedezeka. 26  Ndiyeno iwo adzaona Mwana wa munthu akubwela m’mitambo, ali ndi mphamvu zazikulu komanso ulemelelo. 27  Kenako iye adzatumiza angelo ake ndipo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kucokela ku mphepo zinai, kucokela ku malekezelo a dziko mpaka ku malekezelo a kumwamba. 28  “Tsopano phunzilamponi kanthu pa fanizo ili la mtengo wa mkuyu. Mukangoona kuti nthambi yake yanthete yayamba kuphuka ndi kutulutsa masamba, mumadziwa kuti dzinja layandikila. 29  Mofananamo, inunso mukadzaona zinthu zimenezi zikucitika, mukadziwe kuti iye ali pafupi, pa khomo penipeni. 30  Ndithu ndikukuuzani, m’badwo uwu sudzatha wonse mpaka zinthu zonsezi zitacitika. 31  Kumwamba ndi dziko lapansi zidzacoka, koma mau anga sadzacoka ai. 32  “Ponena za tsikulo kapena ola lake, palibe amene adziwa, ngakhale angelo kumwamba kapena Mwanayo, koma Atate yekha basi. 33  Khalani maso, khalani chelu, cifukwa nthawi yoikika simukuidziwa. 34  Zili monga munthu amene anasiya nyumba yake n’kupita ku dziko lina, ndipo anapatsa akapolo ake ulamulilo. Aliyense anamupatsa nchito yake, komanso analamula mlonda wa pakhomo kuti akhalebe maso. 35  Conco khalanibe maso cifukwa simukudziwa nthawi imene mwininyumba adzabwela, kaya ndi madzulo, pakati pa usiku, m’matandakuca* kapena m’mamawa, 36  kuti iye akadzabwela modzidzimutsa, asadzakupezeni mutagona. 37  Koma zimene ndikukuuzani ndikuuza onse kuti: Khalanibe maso.”

Mau a m'Munsi

Kucokela ku Cigiriki, “ca zowawa za pobeleka.”
Kapena kuti, “wapilila.”
Kucokela ku Cigiriki, “usiku, tambala akulila.”