Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Maliko 2:1-28
2 Koma patapita masiku angapo, iye analowanso mu mzinda wa Kaperenao, ndipo anthu anamva kuti ali kunyumba.
2 Conco, anthu ambili anasonkhana m’nyumbamo, moti munalibiletu malo ngakhale pafupi ndi khomo. Kenako iye anayamba kuwauza uthenga wabwino.
3 Ndiyeno anthu anamubweletsela munthu wofa ziwalo, atanyamulidwa ndi amuna anai.
4 Koma iwo sanakwanitse kufikitsa munthuyo pomwe panali Yesu cifukwa ca kuculuka kwa anthu. Conco, anakasula mtenje pamwamba pa malo pomwe panali Yesu, n’kupanga cibowo. Kenako analowetselapo macila amene panagona munthu wofa ziwalo uja.
5 Yesu ataona cikhulupililo cao, anauza wofa ziwaloyo kuti: “Mwanawe, macimo ako akhululukidwa.”
6 Ena mwa alembi anali khale pomwepo, ndipo mu mtima anali kunena kuti:
7 “N’cifukwa ciani munthu uyu akulankhula conci? Akunyoza Mulungu. Ndaninso wina angakhululukile munthu macimo kupatulapo Mulungu?”
8 Koma mwa mzimu wake, nthawi yomweyo Yesu anazindikila zimene iwo anali kuganiza m’mitima yao. Conco anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciani mukuganiza zimenezi m’mitima yanu?
9 Kodi capafupi n’citi, kuuza munthu wofa ziwaloyu kuti, ‘Macimo ako akhululukidwa,’ kapena kukamba kuti, ‘Nyamuka, tenga macila ako uyambe kuyenda’?
10 Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali ndi mphamvu zokhululukila macimo pa dziko lapansi—” Iye anauza wofa ziwaloyo kuti:
11 “Ndikukuuza kuti, Nyamuka, nyamula macila akowa, pita ku nyumba kwanu.”
12 Pamenepo munthuyo ananyamuka, ndipo nthawi yomweyo ananyamula macila ake n’kuyamba kuyenda onse akuona. Conco anthu onsewo anadabwa kwambili, ndipo anatamanda Mulungu n’kumati: “Zotelezi sitinazionepo.”
13 Kenako iye anapitanso m’mbali mwa nyanja, ndipo khamu lonse la anthu linali kupitabe kwa iye. Ndiyeno anayamba kuwaphunzitsa.
14 Pamene iye anali kudutsa, anaona Levi mwana wa Alifeyo atakhala pansi mu ofesi yokhomelamo misonkho. Ndipo anamuuza kuti: “Khala wotsatila wanga.” Nthawi yomweyo iye ananyamuka ndi kumutsatila.
15 Patapita nthawi, Yesu anali kudya m’nyumba ya Levi, ndipo okhometsa misonkho ambili komanso ocimwa anali kudya naye pamodzi ndi ophunzila ake, cifukwa ambili mwa iwo anali kumutsatila.
16 Koma akalembela a Afarisi ataona kuti iye akudya ndi anthu ocimwa komanso okhometsa misonkho, anayamba kufunsa ophunzila ake kuti: “Kodi munthu ameneyu amadya ndi okhometsa misonkho komanso ocimwa?”
17 Yesu atamva zimenezi anawauza kuti: “Anthu olimba safunikila dokotala, koma odwala ndio amamufuna. Ine n’nabwela kudzaitana anthu ocimwa, osati olungama.”
18 Ophunzila a Yohane komanso Afarisi anali kusala kudya. Conco iwo anabwela kwa Yesu n’kumufunsa kuti: “N’cifukwa ciani ife ophunzila a Yohane komanso ophunzila a Afarisi timasala kudya, koma ophunzila anu sasala kudya?”
19 Yesu anawayankha kuti: “Mkwati akakhala pamodzi ndi anzake, anzakewo sasala kudya, amatelo kodi? Pa nthawi yonse imene mkwatiyo ali nao limodzi, iwo sangasale kudya.
20 Koma masiku adzafika pamene mkwatiyo adzacotsedwa pakati pao, ndipo pa tsikulo adzasala kudya.
21 Palibe munthu amene amasokelela cigamba ca nsalu yatsopano pa cobvala cakunja cakale. Akatelo, cigamba catsopanoco cimaguza cobvala cakaleco, ndipo pong’ambikapo pamakula kwambili.
22 Komanso palibe amene amathila vinyo watsopano m’matumba acikumba akale. Akatelo matumba a vinyowo amaphulika, ndipo vinyoyo amataika, matumbawo n’kuonongeka. Koma vinyo watsopano amamuthila m’matumba acikumba atsopano.”
23 Pamene iye anali kudutsa m’minda ya tiligu pa Sabata, ophunzila ake anayamba kubudula ngala za tiligu pamene anali kuyenda.
24 Conco Afarisi anamufunsa kuti: “Onani! N’cifukwa ciani akucita zosaloleka pa Sabata?”
25 Koma iye anawayankha kuti: “Kodi simunawelengepo zimene Davide anacita cakudya citamuthela, komanso pamene iye ndi amuna amene anali naye anamva njala?
26 Nkhani yokamba za Abiyatara wansembe wamkulu, imakamba kuti Davide analowa m’nyumba ya Mulungu n’kudya mkate wa cionetselo, ndipo mitanda ina ya mkatewo anapatsako ena mwa amuna amene anali naye. Koma mwalamulo, palibe amene anali kuloledwa kudya mkatewo kupatulapo ansembe.”
27 Kenako Yesu anawauza kuti: “Sabata linakhalapo cifukwa ca munthu, osati munthu kukhalapo cifukwa ca Sabata.
28 Conco Mwana wa munthu ndiye Mbuye wa Sabata.”

