Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Maliko 7:1-37

  • Kubvumbula miyambo ya anthu (1-13)

  • Zodetsa munthu zimacokela mu mtima (14-23)

  • Cikhulupililo ca mai wacisirofoinike (24-30)

  • Munthu wogontha acilitsidwa (31-37)

7  Tsopano Afarisi ndi alembi ena amene anacokela ku Yerusalemu anasonkhana kwa Yesu. 2  Ndipo iwo anaona ena mwa ophunzila ake akudya cakudya ndi manja odetsedwa, kapena kuti cosasamba m’manja.* 3  (Pakuti Afarisi ndi Ayuda onse sakudya cakudya asanasambe m’manja kufika mu kakonyokonyo.* Iwo amacita izi potsatila mwambo wa makolo ao akale. 4  Ndipo akacoka ku msika, sakudya cakudya asanasambe. Palinso miyambo ina yambili imene iwo analandila ndipo amaitsatila, monga mwambo wobviika makapu m’madzi, mitsuko, ndi ziwiya zakopa.) 5  Conco Afarisi ndi alembiwo anamufunsa kuti: “N’cifukwa ciani ophunzila anu sasunga miyambo ya makolo akale, koma amadya cakudya ndi manja odetsedwa?” 6  Iye anawauza kuti: “Yesaya analosela molondola za onyenga inu pamene analemba kuti, ‘Anthu awa amandilemekeza ndi milomo yao cabe, koma mitima yao ili kutali ndi ine. 7  Iwo amandipembedza pacabe cifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu monga ziphunzitso za Mulungu.’ 8  Mumanyalanyaza malamulo a Mulungu n’kumamatila miyambo ya anthu.” 9  Kuonjezela apo, iye anawauza kuti: “Mocenjela mumakankhila pambali malamulo a Mulungu kuti musunge miyambo yanu. 10  Mwacitsanzo, Mose anati, ‘Uzilemekeza atate ako ndi amai ako,’ komanso anati, ‘Aliyense wonyoza atate ake kapena amai ake ayenela kuphedwa.’ 11  Koma inu mumati, ‘Ngati munthu wauza atate ake kapena amai ake kuti: “Ciliconse cimene ndili naco, cimene ndikanakuthandizani naco, ndi khobani (kutanthauza mphatso yoyenela kupelekedwa kwa Mulungu),”’ 12  simumulola kucitila atate ake kapena amai ake ciliconse. 13  Mwa kutelo, mwapangitsa mau a Mulungu kukhala opanda phindu cifukwa ca miyambo yanu imene munaipeleka kwa anthu. Ndipo mumacita zinthu zambili zotelezi.” 14  Conco ataitananso gulu la anthuwo anawauza kuti: “Ndimvetseleni nonsenu, ndipo mumvetsetse tanthauzo lake. 15  Palibe ciliconse cocokela kunja kwa munthu cimene cikalowa m’thupi lake cingamudetse. Koma zinthu zimene zimatuluka mwa munthu n’zimene zimamudetsa.” 16 * —— 17  Ndiyeno atalowa m’nyumba inayake kutali ndi gulu la anthulo, ophunzila ake anayamba kumufunsa za fanizo lija. 18  Conco anawafunsa kuti: “Kodi inunso simukumvetsa ngati anthu aja? Kodi simukudziwa kuti palibe ciliconse cocokela kunja kwa munthu cimene cikalowa m’thupi mwake cingamudetse? 19  Pakuti sicilowa mu mtima mwake koma m’mimba, ndipo cimakatuluka ku cimbudzi.” Mwa kukamba zimenezi, Yesu anagamula kuti zakudya zonse n’zoyela. 20  Anakambanso kuti: “Cotuluka mwa munthu n’cimene cimamudetsa. 21  Pakuti mkati, mumtima mwa anthu, ndi mmene mumatuluka maganizo oipa monga zaciwelewele,* zakuba, zakupha anthu, 22  zacigololo, dyela, kucita zoipa, cinyengo, khalidwe lopanda manyazi,* diso lakaduka, manyozo, kudzikuza, ndi kucita zinthu mopanda nzelu. 23  Zinthu zoipa zonsezi zimacokela mumtima mwa munthu ndipo zimamudetsa.” 24  Iye anacoka kumeneko n’kupita ku cigao ca Turo ndi Sidoni. Ali kumeneko, analowa m’nyumba inayake, ndipo sanafune kuti munthu aliyense adziwe kuti ali kumeneko. Koma anthu anadziwabe. 25  Nthawi yomweyo mai wina amene mwana wake wamng’ono wamkazi anagwidwa ndi mzimu wonyansa anamva za iye, ndipo anabwela n’kugwada kumapazi ake. 26  Maiyu anali Mgiriki wacisirofoinike.* Iye anapempha Yesu mobweleza-bweleza kuti atulutse ciwanda mwa mwana wakeyo. 27  Koma Yesu anamuuza kuti: “Ana ayenela kukhuta coyamba, cifukwa n’kosayenela kutenga cakudya ca ana n’kuponyela tuagalu.” 28  Koma maiyo anayankha kuti: “N’zoona mbuyanga, koma ngakhale tuagalu tumene tuli pansi pa thebulo tumadya nyenyeswa za anawo.” 29  Pamenepo Yesu anauza maiyo kuti: “Cifukwa ca zimene wakambazi, pita. Ciwanda cija catuluka mwa mwana wako.” 30  Conco maiyo anapita ku nyumba kwake, ndipo anapeza mwana wamng’ono uja ali gone pabedi ciwanda cija citatuluka. 31  Pamene Yesu anali kubwelela kucokela ku dela la Turo kupita ku Nyanja ya Galileya anapitila m’dela la Sidoni komanso m’cigao ca Dekapole.* 32  Kumeneko, anthu anamubweletsela munthu wogontha komanso wosalankhula, ndipo anamucondelela kuti aike dzanja lake pa iye. 33  Ndiyeno anatengela munthuyo pambali capatali ndi gulu la anthulo. Kenako anapisa zala zake m’matu a munthuyo, ndipo atalabvula mata anakhudza lilime la munthuyo. 34  Ndiyeno atayang’ana kumwamba, anafuza mwamphamvu n’kunena kuti: “Efata,” kutanthauza, “Tseguka.” 35  Atakamba izi, matu ake anatseguka ndipo bvuto lake losalankhula linatha, moti anayamba kulankhula bwino-bwino. 36  Ndiyeno anawalamula kuti asauze aliyense zimene zinacitikazo. Koma amati akawalamula mwamphamvu, m’pamenenso anthuwo anali kufalitsa kwambili nkhaniyo. 37  Inde, iwo anazizwa kosaneneka ndipo anakamba kuti: “Wacita zonse bwino-bwino. Akucititsa ngakhale ogontha kumva, ndi osalankhula kulankhula!”

Mau a m'Munsi

^ Kutanthauza kusayeletsedwa motsatila mwambo.
^ Ena amati, “kasukusuku.”
^ Mau a pa vesiyi amapezeka m’ma Baibo ena, koma sapezeka m’mipukutu yosiyana-siyana yodalilika yamakedzana ya Cigiriki. Onani Zakumapeto A3.
^ M’Cigiriki, por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mau Ena.
^ M’Cigiriki, a·sel′gei·a. Onani Matanthauzo a Mau Ena.
^ Cioneka kuti maiyu anabadwila ku Foinike.
^ Kapena kuti, “Cigao ca Mizinda 10.”