Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chikhulupiriro Chanu Chimakulimbikitsani Kuchitapo Kanthu?

Kodi Chikhulupiriro Chanu Chimakulimbikitsani Kuchitapo Kanthu?

Kodi Chikhulupiriro Chanu Chimakulimbikitsani Kuchitapo Kanthu?

KAPITAWO winawake wa asilikali anali wotsimikiza kuti Yesu angachiritse kapolo wake wodwala manjenje. Koma kapitawo ameneyu sanaitanire Yesu kunyumba kwake, mwinamwake chifukwa chodziona ngati wosayenera kapena chifukwa chakuti sanali Myuda. Mwalo mwake, kapitawoyu anatuma akuluakulu ena achiyuda kuti apite kwa Yesu kukamuuza kuti: “Ambuye, sindiyenera kuti mukalowe pansi pa chindwi langa iyayi; koma mungonena mawu, ndipo adzachiritsidwa mnyamata wanga.” Poona kuti kapitawo wa asilikaliyu akukhulupirira kuti Yesu angachiritse munthu ngakhale ali kutali, Yesu anauza khamu la anthu amene anali kumutsatira kuti: “Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mwa Israyeli, sindinapeza chikhulupiriro chotere.”​—Mateyu 8:5-10; Luka 7:1-10.

Zomwe zinachitikazi zingatithandize kuganizira mofatsa mfundo yofunika pa nkhani ya chikhulupiriro. Chikhulupiriro chenicheni chimaonekera m’zochita. Wolemba Baibulo Yakobo anafotokoza kuti: “Chikhulupiriro, chikapanda kukhala nazo ntchito, chikhala chakufa m’kati mwakemo.” (Yakobo 2:17) Tingamvetse bwino mfundo imeneyi titaona chitsanzo cha zomwe zinachitikadi chosonyeza zimene zingachitike ngati chikhulupiriro chilibe ntchito zake.

Mu 1513 B.C.E., mtundu wa Israyeli unapanga mgwirizano ndi Yehova Mulungu kudzera mu pangano la Chilamulo. Monga mkhala pakati wa pangano limeneli, Mose anauza ana a Israyeli Mawu a Mulungu akuti: “Ngati mudzamvera mawu anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani . . . mtundu wopatulika.” (Eksodo 19:3-6) Inde, kumvera kukanathandiza Aisrayeli kukhalabe opatulika.

Patapita zaka zambiri, Ayuda anayamba kuona kuphunzira Chilamulo kukhala kofunika kwambiri kuposa kugwiritsa ntchito mfundo zake. M’buku lake lakuti The Life and Times of Jesus the Messiah (Moyo ndi Nthawi za Yesu Mesiya), Alfred Edersheim analemba kuti: “[Arabi] kapena kuti ‘atsogoleri a zipembedzo’ anavomerezana kalekale kuti, kuphunzira n’kofunika kwambiri kuposa kuchitapo kanthu.”

N’zoona kuti Aisrayeli akale analamulidwa kuphunzira mwakhama zimene Mulungu amafuna. Mulungu mwini wake anati: “Mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.” (Deuteronomo 6:6, 7) Koma kodi Yehova anatanthauza kuti kuphunzira Chilamulo kukhale patsogolo pa kuchita mogwirizana ndi Chilamulocho? Tiyeni tione.

Kuphunzira Kwambiri

Mwinamwake kwa Aisrayeli zinali zomveka kuti kuphunzira Chilamulo kokha kunali kofunika kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti Ayuda ena ankakhulupirira kuti Mulungu amatha maola atatu tsiku lililonse akuphunzira Chilamulo. Mungamvetse chifukwa chake Ayuda ena ankaganiza kuti, ‘Ngati Mulungu amaphunzira Chilamulo nthawi zonse, zolengedwa zake za padziko lapansi zilekeranji kuchita chimodzimodzi mwakhama?’

Podzafika m’nthawi ya Yesu, maganizo a arabi anali atapotoka chifukwa chofufuza kwambiri ndi kutanthauzira Chilamulo. Yesu anati: “Alembi ndi Afarisi . . . amalankhula, koma samachita. Inde, amanga akatundu olemera ndi osautsa ponyamula, nawasenza pamapewa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi chala chawo.” (Mateyu 23:2-4) Atsogoleri achipembedzo amenewo ankasenzetsa anthu wamba katundu wolemera wa malamulo osawerengeka, koma iwowo mwachinyengo ankapeza njira zozembera malamulo amenewa. Komanso, anthu ophunzira kwambiriwo ‘ankasiya zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro.’​—Mateyu 23:16-24.

Ndipotu n’zodabwitsa kuti pofuna kudzionetsa ngati anthu achilungamo, alembi ndi Afarisi ankaswa Chilamulo chimene iwo ankati amachitsatira. Kutsutsana kwawo pa mawu ndi mfundo zing’onozing’ono za m’Chilamulo kwa zaka zambiri, sikunawathandize kuyandikira kwa Mulungu. Chifukwa cha zimenezi, iwo anapatuka pa Chilamulo monga mmene zimakhalira munthu akatsatira zimene mtumwi Paulo anazitcha kuti “zokamba zopanda pake,” “zotsutsana” komanso “chizindikiritso” kapena kuti nzeru zonama. (1 Timoteo 6:20, 21) Koma vuto lina lalikulu limene linabwera linali momwe kufufuza kwawo kosathako kunawakhudzira. Kufufuzaku sikunawathandize kukhala ndi chikhulupiriro chimene chikanawalimbikitsa kuchita zinthu zabwino.

Anthu Ophunzira, Koma Opanda Chikhulupiriro

Maganizo a atsogoleri achipembedzo achiyudawo anali osiyana kwambiri ndi a Mulungu. Aisrayeli atangotsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, Mose anawauza kuti: “Ikani mitima yanu pa mawu onse ndikuchitirani nawo mboni lero; kuti muuze ana anu asamalire kuwachita mawu onse a chilamulo ichi.” (Deuteronomo 32:46) Mwachionekere, anthu a Mulungu anafunika kuchita mawu a m’Chilamulo, osati kungophunzira Chilamulocho basi.

Koma mobwerezabwereza, mtundu wa Israyeli unachita mosakhulupirika kwa Yehova. M’malo mochita ntchito zabwino, ana a Israyeli ‘sanam’khulupirire, kapena kumvera mawu ake.’ (Deuteronomo 9:23; Oweruza 2:15, 16; 2 Mbiri 24:18, 19; Yeremiya 25:4-7) Pamapeto pake, Ayuda anachita chinthu choipitsitsa chosonyeza kusakhulupirika kwawo pamene anakana Yesu monga Mesiya. (Yohane 19:14-16) Chotero, Yehova Mulungu anakana Israyeli ndi kutembenukira kwa amitundu.​—Machitidwe 13:46.

Ndithudi, tiyenera kusamala kuti tisakodwe mu msampha umodzimodziwo. Tisaganize kuti tingalambire Mulungu mwa kuphunzira kwambiri koma opanda chikhulupiriro. M’mawu ena, sitiyenera kuphunzira Baibulo n’cholinga chongofuna kudziwa zinthu basi. Ziphunzitso zolondola ziyenera kutifika pamtima ndi kutilimbikitsa kuchita zinthu zopindulitsa pa moyo wathu. Kodi tingapindule chiyani ngati titaphunzira za ulimi wa ndiwo za kudimba koma osayesako kubzala mbewu n’kamodzi komwe? N’zoona kuti tingadziwe zambiri za mmene tingalimire ndi kusamalira dimba lathulo, koma sitingakolole kanthu. Mofananamo, anthu amene akuphunzira Baibulo kuti adziwe zimene Mulungu amafuna, ayenera kulola mbewu za choonadi kuwafika pamtima kuti ziphuke ndi kuwalimbikitsa kuchitapo kanthu.​—Mateyu 13:3-9, 19-23.

“Khalani Akuchita Mawu”

Mtumwi Paulo ananena kuti “chikhulupiriro chidza ndi mbiri,” kapena kuti zimene munthu wamva. (Aroma 10:17) Tikamva Mawu a Mulungu ndi kukhulupirira Mwana wake, Yesu Kristu, timakhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Inde, pakufunika zambiri osati kungonena chabe kuti, ‘Ndimakhulupirira Mulungu ndi Kristu.’

Yesu analimbikitsa otsatira ake kukhala ndi chikhulupiriro chimene chingawalimbikitse kuchitapo kanthu. Iye anati: “Mwa ichi alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale chipatso chambiri; ndipo mudzakhala akuphunzira anga.” (Yohane 15:8) Patapita nthawi, Yakobo, mbale wake wa Yesu, analemba kuti: “Khalani akuchita mawu, osati akumva okha.” (Yakobo 1:22) Koma kodi tingadziwe bwanji zoyenera kuchita? Mwa mawu ake komanso chitsanzo chake, Yesu anasonyeza zimene tiyenera kuchita kuti tikondweretse Mulungu.

Ali padziko lapansi, Yesu anagwira ntchito mwakhama popititsa patsogolo zinthu za Ufumu ndi kulemekeza dzina la Atate wake. (Yohane 17:4-8) Motani? Anthu ambiri angakumbukire zozizwitsa za Yesu, monga kuchiritsa odwala ndi olumala. Komabe, Uthenga wabwino wa Mateyu ukufotokoza momveka bwino njira yaikulu imene anachitira zimenezi, kuti: “Yesu anayendayenda m’mizinda yonse ndi m’midzi, namaphunzitsa m’masunagoge mwawo, nalalikira uthenga wabwino wa Ufumuwo.” N’zoonekeratu kuti utumiki wa Yesu sunali wongolankhula mwa apa ndi apo ndi mabwenzi kapena anthu ochepa amene anali kukumana nawo m’dera la kwawolo. Anayesetsa mwakhama, ndi kuchita zonse zotheka kuti ayendere anthu “m’Galileya monse.”​—Mateyu 4:23, 24; 9:35.

Yesu analamula otsatira ake kuti nawonso azigwira ntchito yopanga ophunzira. Inde, anawapatsa chitsanzo chabwino choti atsanzire. (1 Petro 2:21) Yesu anauza ophunzira ake okhulupirikawo kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.”​—Mateyu 28:19, 20.

Kunena zoona, ntchito yolalikira siyophweka. Yesu mwiniwakeyo anati: “Taonani, Ine ndituma inu ngati ana a nkhosa pakati pa mimbulu.” (Luka 10:3) Anthu akamatitsutsa, kawirikawiri timabwerera m’mbuyo popewa zowawa kapena nkhawa. Izi n’zimene zinachitika usiku umene Yesu anagwidwa. Atumwi anathawa chifukwa cha mantha. Nthawi ina usiku womwewo, Petro anakana katatu kuti sakum’dziwa Yesu.​—Mateyu 26:56, 69-75.

Komanso mungadabwe kumva kuti ngakhale mtumwi Paulo ananena kuti analalikira uthenga wabwino movutikira. Iye analembera mpingo wa ku Tesalonika kuti: “Tinalimba mtima mwa Mulungu wathu kulankhula kwa inu uthenga wabwino wa Mulungu movutikira kwambiri.”​—1 Atesalonika 2:1, 2, NW.

Paulo ndi atumwi anzake anatha kuchotsa mantha onse kuti auze ena za Ufumu wa Mulungu, ndipo inunso mungatero. Motani? Chofunika kwambiri ndi kudalira Yehova. Tikakhulupirira kwambiri Yehova, chikhulupiriro chimenecho chidzatilimbikitsa kuchitapo kanthu, ndipo tidzatha kuchita zofuna zake.​—Machitidwe 4:17-20; 5:18, 27-29.

Mudzalandira Mphoto Chifukwa cha Ntchito Yanu

Yehova akudziwa bwino lomwe kuti tikuyesetsa mwakhama kuti timutumikire. Mwachitsanzo, tikadwala kapena kutopa, iye amadziwa. Tikamadzikaikira amadziwanso. Nthawi zonse, Yehova amadziwa ngati tili pa mavuto a zachuma, kapena ngati zinthu sizikuyenda bwino chifukwa chodwala kapena kuvutika maganizo.​—2 Mbiri 16:9; 1 Petro 3:12.

Yehova amasangalala kwambiri, chikhulupiriro chathu chikatilimbikitsa kuchitapo kanthu, ngakhale kuti ndife opanda ungwiro komanso tikukumana ndi mavuto. Chikondi chimene Yehova ali nacho pa atumiki ake okhulupirika sichachiphamaso ayi, chifukwa chili ndi lonjezo. Mouziridwa ndi Mulungu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.”​—Ahebri 6:10.

Mungakhulupirire Baibulo limene likufotokoza kuti Yehova ndi “Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo,” komanso ndi “wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.” (Deuteronomo 32:4; Ahebri 11:6) Mwachitsanzo, mayi wina ku California, ku United States anati: “Bambo anga anachita utumiki wanthawi zonse kwa zaka khumi asanakhale ndi ana. Ndinkasangalala akamandiuza nkhani za mmene Yehova anawathandizira mu utumikiwo. Nthawi zambiri ankagwiritsa ntchito ndalama yonse imene anali nayo, kugulira mafuta a galimoto kuti athe kupita mu utumiki. Akabwerera kunyumba kuchokera ku utumikiko, nthawi zambiri ankadabwa kupeza wina ataika zakudya pakhomo pawo.”

Kuwonjezera pa kutithandiza ndi zithu zofunika, “Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse,” amatilimbikitsa mwamaganizo ndi mwauzimu. (2 Akorinto 1:3) Mboni ina imene yapirira ziyeso zambiri kwa zaka zambiri inati: “Ukamadalira Yehova sudandaula chilichonse. Umenewu umakhala mpata wabwino wokhulupirira Yehova ndi kuona akukuthandiza.” Modzichepetsa, mungalankhule ndi “Wakumva pemphero,” muli wotsimikiza kuti adzamvetsera madandaulo anu.​—Salmo 65:2.

Okolola auzimu amalandira madalitso ochuluka. (Mateyu 9:37, 38) Kuchita utumiki kwathandiza anthu ambiri kukhala ndi moyo wathanzi, ndipo inunso kungakuthandizeni m’njira yomweyo. Koma chofunika kwambiri n’chakuti, kulalikira kwa ena kumatithandiza kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Mulungu.​—Yakobo 2:23.

Pitirizani Kuchita Zabwino

Mtumiki wa Mulungu angalakwitse kwambiri ngati ataganiza kuti Yehova wakhumudwa naye chifukwa akulephera kuchita zonse zimene akufuna mu utumiki chifukwa cha matenda kapena ukalamba. N’chimodzimodzinso kwa amene akulephera kukwaniritsa utumuki mmene iwo akufunira chifukwa chodwaladwala, maudindo a m’banja, kapena mavuto ena.

Kumbukirani kuti mtumwi Paulo ataona kuti sakukwanitsa zimene amafuna chifukwa cha matenda kapena vuto linalake, ‘anapempha Ambuye katatu kuti chichoke kwa iye.’ M’malo mochiritsa Paulo kuti achite zambiri potumikira Yehova, Mulungu anati: “Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa m’ufoko.” (2 Akorinto 12:7-10) Choncho khalani otsimikiza kuti ngakhale kuti mukupirira vuto linalake, Atate wanu wakumwamba amayamikira chilichonse chimene mungachite popititsa patsogolo zofuna zake.​—Ahebri 13:15, 16.

Mlengi wathu wachikondi safuna zochuluka kwa ife kuposa zimene tingakwanitse. Iye akungofuna kuti tikhale ndi chikhulupiriro chimene chimatilimbikitsa kuchitapo kanthu.

[Chithunzi patsamba 26]

Kodi kuphunzira Chilamulo kokha kunali kokwanira?

[Zithunzi patsamba 29]

Chikhulupiriro chathu chiyenera kukhala ndi ntchito zake