Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

 Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwapindula powerenga magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

N’chifukwa chiyani anasankha tsiku la December 25 kuti likhale lokondwerera kubadwa kwa Yesu?

Mawu a Mulungu satchula tsiku limene Yesu anabadwa. Buku la Enciclopedia Hispánica limati: “Deti la December 25, pamene anthu amakondwerera Khirisimasi, sanalikhazikitse mogwirizanadi ndi tsiku limene Yesu anabadwa, koma analikhazikitsa pofuna kuti zikondwerero zachikunja za Aroma zokondwerera nthawi imene dzuwa limabwereranso pa liwombo m’nyengo ya chisanu zisanduke za Chikristu.” Aroma akale ankakondwerera kubwerera kwa dzuwa paliwombo kumeneku m’nyengo ya chisanu mwa kuchita madyerero, zisangalalo zaphokoso, ndi kupatsana mphatso.​—12/15, tsamba 4 ndi 5.

• Kodi lemba la Machitidwe 7:59 limasonyeza kuti Stefano anapemphera kwa Yesu?

Ayi. Baibulo limasonyeza kuti pemphero liyenera kupita kwa Yehova Mulungu yekha basi. Ataona Yesu m’masomphenyawo, zikuoneka kuti Stefano anaona kuti anali womasuka kumulankhula mwachindunji, ndipo anamupempha kuti: “Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.” Stefano ankadziwa kuti Yesu anali atapatsidwa udindo woukitsa akufa. (Yohane 5:27-29) Choncho Stefano anapempha Yesu kuti asunge mzimu wake, kapena kuti mphamvu ya moyo wake, kufikira tsiku limene adzamuukitse.​—1/1, tsamba 31.

• Kodi timadziwa bwanji kuti Mulungu sanakonzeretu tsogolo la munthu?

Mulungu anapatsa munthu ufulu wosankha, ndipo zimenezi zikusonyezeratu kuti chiphunzitso chakuti Mulungu anakonzeratu zam’tsogolo mwa munthu n’chabodza. Zikanasemphana ndi chikondi komanso chilungamo cha Yehova ngati Mulungu akanakonzeratu zomwe tidzachite m’tsogolo mwathu ndiyeno n’kudzatiweruza chifukwa chochita zokonzedweratuzo. (Deuteronomo 32:4; 1 Yohane 4:8)​—1/15, masamba 4 ndi 5.

• N’chifukwa chiyani kungakhale kusadzichepetsa kunena kuti zozizwitsa sizingachitike?

Asayansi ena akuvomereza kuti sanganenenso motsimikiza kuti chozizwitsa chinachake n’chosatheka, chifukwa azindikira kuti akudziwa zinthu zochepa chabe zokhudza kudabwitsa kwa sayansi ya m’chilengedwe cha Mulungu. Motero nthawi zambiri asayansiwo akapanda kumvetsetsa chozizwitsa chinachake amangoti n’chokayikitsa basi.​—2/15, masamba 5 ndi 6.

• N’chifukwa chiyani Woweruza Samsoni anauza makolo ake kuti akufuna kukwatira mwana wamkazi wa Afilisti? (Oweruza 14:2)

Kukwatira mkazi wolambira milungu yonyenga kunali kotsutsana ndi chilamulo cha Mulungu. (Eksodo 34:11-16) Komabe, mkazi wachifilisti ameneyu anali woyenera kwa Samsoni. Samsoni “analikufuna kutola chifukwa ndi Afilisti,” chotero mkazi ameneyu anali woyenera pa kukwaniritsa cholinga chimenechi. Ndipo Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu Wake kuthandiza Samsoni. (Oweruza 13:25; 14:3, 4, 6.)​—3/15, tsamba 26.

• Kodi ndibwino kuti Mkristu azipereka ndalama kapena mphatso kwa munthu wogwira ntchito m’boma pofuna kuti amugwirire ntchito inayake?

N’kulakwa kupereka chiphuphu kwa munthu wogwira ntchito m’boma pofuna kuti atichitire zinthu zoswa malamulo, apotoze chilungamo, kapena kuti achite zinthu mokondera. Koma munthu akapereka ndalama kapena mphatso kwa wogwira ntchito m’boma chifukwa chakuti wagwira ntchito yake kapena akufuna kuti amugwirire ntchito yovomerezeka mwalamulo kapenanso pofuna kupewa kuponderezedwa, sindiye kuti munthu wapereka chiphuphu ayi.​—4/1, tsamba 29.