Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Thandizo Lapanthawi Yake ku Macedonia

Thandizo Lapanthawi Yake ku Macedonia

 Thandizo Lapanthawi Yake ku Macedonia

“MUWOLOKERE ku Makedoniya kuno, mudzatithangate ife.” (Machitidwe 16:9) Mawu amenewa a munthu amene anaonekera mtumwi Paulo m’masomphenya, akusonyeza kuti panafunika kuti uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ulalikidwe m’gawo latsopano, m’mizinda imene masiku ano ili m’dziko la Greece.

Pa anthu 1,840 alionse mwa anthu onse a m’dziko la Macedonia, pamapezeka munthu mmodzi yekha wa Mboni za Yehova. Anthu ambiri sanamvepo za Yehova Mulungu. Inde, anthu a m’dziko limeneli akufunikiradi kumva uthenga wa mtendere.​—Mateyu 24:14.

Mulungu watsegula njira kuti thandizo la mtunduwu liperekedwe. Tsiku lina mu November 2003, ofesi ya Mboni za Yehova ku Skopje m’dziko la Macedonia inalandira telefoni yadzidzidzi. Telefoni imeneyo inachokera ku bungwe lothandiza pa ntchito yotukula miyoyo ya anthu m’dziko la Macedonia lotchedwa Macedonian Center for International Cooperation. Bungweli linapempha Mboni kuti zikakonze malo oonetsera mabuku awo ndi kufotokoza zikhulupiriro zawo pa chionetsero cha masiku atatu chomwe chinali kuyembekezeka kuyamba pa November 20. Umenewu unali mwayi waukulu wofikira anthu ambirimbiri omwe anali asanamvepo uthenga wabwino wa Ufumu.

Antchito odzipereka anagwira ntchito mwakhama kukonza malo amenewa ndi kuikapo mabuku osiyanasiyana a Mboni za Yehova m’chinenero cha Chimakedoniya. Mabuku ena anawaika poonekera kuti alendo ofika pamalo oonetsera mabukuwa azitenga ngati akufuna. Chionetsero chimenechi chinapereka mwayi kwa anthu ambiri wotenga madzi otsitsimula auzimu kwaulere.​—Chivumbulutso 22:17.

Alendo ofika pamalowo kwenikweni ankafuna mabuku ankhani zimene zikukhudza moyo wawo, monga buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa​—Mayankho Amene Amathandiza ndi Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. * Anthu 98 anasiya maadiresi awo, ndi kupempha kuti Mboni za Yehova ziwayendere. Ambiri anayamikira kwambiri ntchito yabwino imene Mboni za Yehova zikugwira komanso anayamikira mabuku awo apamwamba.

Bambo wina anafika pamalo oonetsera mabukuwa ndi mwana wake wamng’ono wamwamuna atam’gwira padzanja. Bamboyo anafunsa ngati pali mabuku a ana. Mbonizo zinamuonetsa buku lakuti  Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. * Analiona m’kati mwake patalipatali, kenako mwachidwi anafunsa mtengo wake. Atamva kuti ntchito yophunzitsa ya Mboni za Yehova imayendetsedwa ndi zopereka zaufulu, chidwi chakecho chinawonjezeka. (Mateyu 10:8) Anaonetsa mwanayo bukulo ndi kunena kuti: “Ona! buku labwino kwabasi. Ndizikakuwerengera nkhani imodzi tsiku lililonse.”

Pamalowo panafika pulofesa wina wa maphunziro ofufuza nzeru zapamwamba. Iye chidwi chake chinali pa zipembedzo, ndipo kwenikweni ankafuna kudziwa zikhulupiriro za Mboni za Yehova. Pamene anali kuona buku lakuti Mankind’s Search for God, * pulofesayo anati: “Nkhani zake azilemba momveka bwino kwambiri! Mmene azilemberamu ndi mmenenso ine ndimaganizira kuti nkhani ziyenera kulembedwera.” Patapita nthawi, panafika ophunzira ochokera kusukulu imene pulofesa ameneyu akuphunzitsa ndipo anapempha buku limene pulofesayo anatenga. Iwo ankafuna kuphunzira buku limodzimodzilo. Iwo anali kuganiza kuti mphunzitsi wawoyo akagwiritsa ntchito buku limeneli powaphunzitsa.

Chionetserochi chinapatsa anthu ena mwayi wowerenga ndi kumva choonadi cha m’Malemba kwa nthawi yoyamba. Pamalo amenewa panafika kagulu ka achinyamata ogontha kudzaona zimene zingawasangalatse. Mboni ina inakambirana nawo mwachidule, ndipo mtsikana wina ankamasulira m’chinenero chamanja. Pogwiritsa ntchito zithunzi za m’buku lakuti Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, * mbaleyo anafotokoza kuti Yesu ankachiritsa odwala, kuphatikizapo ogontha. Achinyamatawo anasangalala “kumva” kuti Baibulo likulonjeza kuti posachedwapa Yesu adzachitanso chimodzimodzi kwa anthu amene ali padziko lapansi masiku ano. Ambiri a iwo anatenga mabuku ofotokoza za m’Baibulo, ndipo anakonza zoti Mboni yodziwa chinenero chamanja ikawachezere.

Kuwonjezera pa chinenero cha Chimakedoniya, panalinso mabuku a zinenero za Chialubaniya, Chingelezi ndi Chiteki. Munthu wina amene sankatha kulankhula Chimakedoniya anapempha mabuku a Chingelezi. Atalandira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, iye anati amalankhula Chiteki. Pamene anamuonetsa mabuku a m’chinenero chakecho, anadabwa kwambiri. Anazindikira kuti Mboni za Yehova zikufunadi kuthandiza wina aliyense.

Kunena zoona chionetsero chimenechi chinapereka mpata wabwino kwambiri wochitira umboni, ndipotu zinali zolimbikitsa kwambiri kuona anthu ambiri akuchita chidwi ndi choonadi cha m’Baibulo. Inde, Yehova anatsegula njira kuti anthu ambiri ku Macedonia amve uthenga wabwino wa Ufumu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Mabuku onsewa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 7 Mabuku onsewa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 8 Mabuku onsewa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 9 Mabuku onsewa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 9]

MWAMBO WAPADERA!

Pa May 17, 2003, panachitika mwambo wofunika kwambiri, womwe unasonyeza kuti ntchito yofalitsa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ikupita patsogolo ku Macedonia. Mu mzinda wa Skopje, munachitika mwambo wotsegulira ofesi yatsopano ya Mboni za Yehova. Ntchito yomanga ofesi imeneyi inatenga zaka ziwiri, ndipo tsopano maofesi amenewa ndi aakulu kuwirikiza kanayi maofesi amene analipo kale.

Pamalopa pali nyumba zitatu mmene muli maofesi oyendetsa ntchito ya Mboni za Yehova m’dzikomo, maofesi omasulira mabuku, zipinda zogona, khitchini, ndi kochapira zovala. Guy Pierce, wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ndi amene anakamba nkhani yotsegulira ofesi yatsopanoyo. Pamwambo umenewu panafika alendo ochokera m’mayiko khumi. Onse anali osangalala kuona nyumba zatsopano zokongolazi.

[Mapu pamasamba 8, 9]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

BULGARIA

MACEDONIA

Skopje

ALBANIA

GREECE

[Chithunzi patsamba 8]

Skopje, Macedonia