Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zinthu Zoti Tiphunzire Zatichulukira?

Kodi Zinthu Zoti Tiphunzire Zatichulukira?

Kodi Zinthu Zoti Tiphunzire Zatichulukira?

Munthu wina ndi mkazi wake, omwe ndi amishonale, ankayang’anitsitsa mwezi atakhala pamchenga m’mphepete mwa nyanja inayake kumadzulo kwa Africa. Mwamunayo anafunsa kuti: “Kodi anthu auphunzira mwezi umenewu kufika pati, ndipo pali zinthu zochuluka motani zimene sanadziwebe?”

Mkazi wake anayankha kuti: “Bwanji zikanakhala zotheka kumaona dziko lathu lapansili likuyenda ngati mmene tikuonera mweziwu? Anthu padziko lapansi aphunziradi zinthu zambiri, koma padakali zambiri zoti aphunzire. Ndipo tangoganizani, sikuti ndi dziko lapansi lokhali limene likuzungulira dzuwa, komanso mapulaneti ena onse nawonso akutero. Zimenezi zikutanthauza kuti mwina sitidzakhalanso pa malo omwe ano popeza dziko lathuli limasinthasintha malo m’chilengedwe chonse. Ndipo anthufe timadziwa pamene dziko lathuli lili mumlengalengamu poona zinthu za kuthambo monga dzuwa ndi nyenyezi. Tikudziwa zambiri zokhudza zinthu zina, koma tikanena za pamene ifeyo tili, tingati sitikupadziwa n’komwe.”

MAWU amenewa anakhudza mfundo zinazake zoona. Zikuoneka kuti pali zambiri zoti tiphunzire. N’zoona kuti aliyense wa ife amaphunzira zinthu zatsopano tsiku lililonse. Komabe, mosasamala kanthu za kuchuluka kwa zimene timaphunzirazo, zikuoneka kuti sitikukwanitsa kuphunzira zonse zimene tingafune kuphunzira.

Kuwonjezera pa kuphunzira zinthu zambiri zatsopano, njira zosungira zinthu zomwe taphunzira zawonjezeka kwambiri. Zinthu zimene anthu onse akudziwa panopa zawonjezeka kwambiri chifukwa chakuti anthu akugwiritsa ntchito makina otsogola posunga zinthu zimene akuzidziwa kale. Makompyuta tsopano ali ndi mphamvu zambiri zosungira zinthu mwakuti panafunika mawu atsopano otchulira mphamvu zimenezi. Ma CD a mu kompyuta otchedwa ma CD-ROM angathe kusunga zinthu zambirimbiri. Ma DVD ali ndi mphamvu zochuluka kuwirikiza pafupifupi kasanu ndi kawiri mphamvu za ma CD-ROM, ndipo panopa akupanga ma DVD ena amphamvu kuposa pamenepa.

Njira zimene anthu masiku ano akugwiritsa ntchito pofalitsa nkhani n’zogometsa kwambiri. Pamene akusindikiza nyuzipepala, magazini ndi mabuku, makina osindikizirawo amathamanga pa liwiro losaneneka. Munthu amene akugwiritsa ntchito Intaneti, angaphunzire zinthu zambiri mwa kungodinikiza batani. Anthu akugwiritsa ntchito njira imeneyi komanso zina zambiri kufalitsa nkhani zochuluka zedi zoti munthu sangakwanitse kuphunzira zonsezo. Zinthu zofunika kuphunzirazi nthawi zina anthu aziyerekezera ndi nyanja yaikulu chifukwa chakuti zachuluka kwambiri. Pa chifukwa chimenechi, tiyenera kuphunzira kusambiramo, tingatero kunena kwake, koma osamwa zinthu zonse zomwe zili m’nyanjamo. Choncho, podziwa kuti zofunika kuphunzira zachuluka kwambiri timakakamizika kusankha mosamala zoti tiphunzire.

Chifukwa china chosankhira zoti tiphunzire n’chakuti zinthu zambiri zomwe tingathe kuphunzira si zothandiza kwenikweni. Kunena zoona, zina za izo n’zoipa, zosafunika n’kuzidziwa komwe. Kumbukirani kuti zimene tingaphunzire zingathe kukhala zinthu zabwino kapena zoipa, zopindulitsa kapena zosathandiza. Kuwonjezera apo, zinthu zina zimene anthu ambiri amaona ngati n’zoona zimakhala zabodza. Tamva mobwerezabwereza anthu olemekezeka akunena zinthu zomwe pambuyo pake zinadziwika kuti sizinali zoona. Mwachitsanzo, ganizirani za mlembi wa mumzinda wa Efeso, amene mosakayikira anthu anali kumuona ngati munthu wophunzira kwambiri. Iye anati: “Kodi ndani padziko lonse lapansi amene sadziwa kuti mzinda wa Efeso umayang’anira kachisi wa Mulungu wamkulu Atemi ndi fanizo lake, limene linagwa kuchokera kumwamba?” (Machitidwe 19:35, 36, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.) Ngakhale kuti aliyense ankadziwa zimenezi, ndipo ambiri ankaganiza kuti zinali zosatsutsika, komabe sizinali zoona kuti fanizo limenelo linagwa kuchokera kumwamba. Pa chifukwa chabwino, Baibulo Lopatulika limachenjeza Akristu kuti ayenera kupewa “zimene molakwa zimaoneka ngati nzeru.”​—1 Timoteo 6:20, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.

Chifukwa chachikulu chosankhira zofunika kuphunzira n’chakuti moyo wathu wamasiku anowu ndi waufupi. Kaya muli ndi zaka zingati, mosakayikira padakali zinthu zambiri zomwe mungafune kuphunzira, koma mukudziwa kuti simungakwanitse zonsezo chifukwa moyo wanu ndi waufupi.

Kodi vuto limeneli lidzatha? Kodi adzapezeka maphunziro amene angatithandize kukhala moyo wautali, kapenanso kwamuyaya? Kapena kodi maphunziro amenewo alipo kale? Ngati ndi choncho, kodi aliyense angathe kupeza maphunziro amenewo? Kodi nthawi idzafika pamene zinthu zimene tizidzaphunzira zidzakhaladi zoona monga mmene timayembekezera? Amishonale amene tinawatchula koyambirira aja apeza mayankho omveka a mafunso amenewa, ndipo inunso mungawapeze. Chonde werengani nkhani yotsatira. Nkhani imeneyi ikuthandizani kuona kuti mungathe kuphunzira mpaka muyaya.