Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Msonkhano Umene Unachitika mu Msasa wa Anthu Othawa Kwawo Unapatsa Chiyembekezo Anthu Otaya Mtima

Msonkhano Umene Unachitika mu Msasa wa Anthu Othawa Kwawo Unapatsa Chiyembekezo Anthu Otaya Mtima

 Msonkhano Umene Unachitika mu Msasa wa Anthu Othawa Kwawo Unapatsa Chiyembekezo Anthu Otaya Mtima

MSASA wa anthu othawa kwawo wa Kakuma uli kumpoto m’dziko la Kenya, pafupi ndi malire a dzikoli ndi la Sudan. Pamsasa umenewu pali anthu oposa 86,000. Dera limeneli ndi louma kwambiri ndiponso masana kumatentha kufika 50 digiri seshasi. Sizachilendo kuona anthu othawa kwawo amenewa akumenyana. Kwa anthu ambiri, msasawu wangokhala malo amavuto. Komabe, ena ali ndi chiyembekezo.

Ena mwa anthu othawa kwawo amene ali mumsasawu ndi Mboni za Yehova, zomwe zikulengeza mwachangu uthenga wabwino wa Ufumu. Iwo amasonkhana mu mpingo waung’ono ku Lodwar, umene uli pamtunda wa makilomita 120 kummwera kwa msasawo. Mpingo wina woyandikana ndi umenewu uli kutali, mtunda woyenda maola asanu ndi atatu pagalimoto.

Popeza kuti n’zosatheka kuti anthu othawa kwawo azituluka mumsasawo mmene akufunira, ambiri amalephera kukapezeka pa misonkhano ikuluikulu ya Mboni za Yehova. Pa chifukwa chimenechi, anakonza zoti akhale ndi tsiku la msonkhano wapadera mumsasa momwemo.

Ulendo Wopita Kumpoto

Pofuna kukathandiza pa msonkhanowu, Mboni zokwana 15 zochokera m’tauni ya Eldoret yomwe ili pamtunda wa makilomita 480 kummwera kwa msasawo, zinadzipereka kuyenda ulendo wovuta wopita kumpoto, kudera lotentha la Lodwar. Pagulu limeneli panali wophunzira Baibulo amene anathandiza paulendowu mwa kupereka minibasi yake ndi woyendetsa. Iwo anali ofunitsitsa ndi mtima wonse kukalimbikitsa abale awo.

Ananyamuka ulendo umenewu m’mawa kwambiri kukuzizira, kuchokera ku dera lamapiri kumadzulo kwa Kenya. Msewu wamabampu wopita kumeneko, unakwezeka zitunda kudutsa m’phepete mwa minda ndi nkhalango, usanayambe kutsetsereka kulowera m’chipululu chotentha. Mbuzi ndi ngamila zinali kudya udzu m’nthaka yopanda chonde. Anakumana ndi anthu a m’deralo atavala zovala zakwawoko, ambiri a iwo atanyamula zibonga, mauta ndi mivi. Atayenda kwa maola 11, Mbonizo zinafika ku Lodwar, dera lotentha ndiponso lafumbi, mmene muli anthu pafupifupi 20,000. Mboni zakumeneko zinawalonjera mosangalala, kenako apaulendowo anapita kukagona kuti apumule  ndi kukonzekera zochitika za Loweruka ndi Lamlungu.

M’mawa mwake, alendowo anapita kukaona malo ena ochititsa chidwi m’deralo. Malo omwe sanafune kuwaphonya anali Nyanja ya Turkana, yomwe ndi nyanja yaikulu m’dziko la Kenya. Nyanja imeneyi ili m’katikati mwa chipululu ndipo ili ndi ng’ona zambiri padziko lonse lapansi. Anthu ochepa amene amakhala m’phepete mwa nyanja imeneyi ntchito yawo ndi kusodza m’madzi amchere a m’nyanjayi. Madzulo ake, alendowo anasangalala kupezeka pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndi Msonkhano wa Utumiki pa mpingo wa Lodwar. Mpingo umenewu uli ndi Nyumba ya Ufumu yokongola zedi. Nyumba imeneyi anaimanga m’chaka cha 2003 kudzera m’ntchito ya Mboni yomanga Nyumba za Ufumu m’mayiko osauka.

Tsiku la Msonkhano Wapadera

Tsiku la msonkhano wapaderawu linali Lamlungu. Mpingo wa Lodwar, komanso abale ochokera kutaliwo analoledwa kulowa mumsasamo pomakwana 8 koloko m’mawa, choncho Mbonizo zinali zofunitsitsa kuyamba msonkhanowo mofulumira. Popita kumalire a dzikoli ndi dziko la Sudan, iwo anadutsa mumsewu wokhotakhota wodutsa m’dera lopanda chonde. Msewu umenewu unadutsa m’phepete mwa mapiri osongoka. Atafika pa mudzi wa Kakuma, anayamba kuona madera akutali. Anapeza kuti kunali kugwa mvula choncho msewu wafumbi wopita kumsasako unali ndi zithaphwi za madzi m’malo ambiri. Nyumba zambiri zinali za zidina zosawotcha zofolera ndi malata kapena malona. Anthu ochokera m’dziko limodzi ngati ku  Ethiopia, Somalia, Sudan ndi m’mayiko ena amakhala paokha. Anthu othawa kwawowo analandira alendowo mwansangala.

Msonkhano unachitikira mu holo yochitira maphunziro. Zithunzi zimene zinali m’makoma pamalo amenewa, zinkasonyeza mavuto omwe anthu othawa kwawo akukumana nawo, koma patsikulo aliyense mu holomo anali ndi chiyembekezo. Nkhani zonse zinakambidwa m’Chingelezi ndi m’Chiswahili. Okamba nkhani ena amene ankatha kulankhula zinenero ziwiri zonsezi ankamasulira okha nkhani zawo. Mbale wothawa kwawo ku Sudan anakamba nkhani yoyamba yakuti, “Kuyesa Mtima Wathu Wophiphiritsira.” Nkhani zina zonse zinakambidwa ndi akulu ochokera m’madera ena.

Chochitika chapadera pa msonkhano uliwonse chimakhala ubatizo. Nkhani yaubatizo ili pafupi kutha, aliyense anaponya maso kutsogolo pamene munthu mmodzi wofuna kubatizidwa anali kuimirira. Gilbert anathawa kwawo limodzi ndi bambo ake panthawi imene kunali nkhondo yopululutsa fuko mu 1994. Poyamba anathawira ku Burundi poganiza kuti kumeneko akatetezeka, koma posakhalitsa anazindikira kuti miyoyo yawo inali idakali pangozi. Gilbert anathawira ku Zaire, kenako ku Tanzania. Nthawi zina anali kubisala m’nkhalango, ndipo pamapeto pake anafika ku Kenya. Pamene wokamba nkhani anali kumulandira m’gulu la Yehova monga mbale, anthu ambiri anali kugwetsa misozi. Wokamba nkhani atafunsa mafunso awiri, Gilbert, amene anali ataimirira kutsogolo kwa gulu la anthu okwana 95, anayankha momveka bwino komanso mwachidaliro m’Chiswahili kuti “Ndiyo!” kutanthauza kuti “Inde!” Iye ndi abale ena anali atakumba dzenje ndi kuikapo lona limene kale anafolerera nyumba yake pamsasapo. Posonyeza kuti anali kufunitsitsadi kubatizidwa, m’mawa umenewo anathira madzi m’dzenje limeneli pogwiritsa ntchito ndowa, mpaka analidzazitsa yekha.

M’chigawo chamasana, imodzi mwa mbali zochititsa chidwi inali kufotokoza zokumana nazo zapadera za Mboni zothawa kwawo. Mbale wina anafotokoza mmene anayambira kukambirana ndi munthu wina amene anali kupumula pansi pa mtengo.

“Tandiuzani, kodi pansi pa mtengo m’posaopsa kukhalapo nthawi zonse?”

Munthuyo anayankha kuti “Inde.” Kenako anawonjezera kuti: “Koma usiku m’poopsa.”

Ndiyeno mbaleyo anawerenga lemba la Mika 4:3, 4 lomwe limati: “Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa.” Kenako anafotokoza kuti: “Mwaona, m’dziko latsopano la Mulungu, kukhala pansi pa mtengo kudzakhala kosaopsa nthawi zonse.” Munthuyo analandira buku lothandiza pophunzira Baibulo.

Anthu atatu a m’banja la mlongo wina yemwe anali nawo pa ulendo wopita ku Kakuma, anali atangomwalira kumene. Ponena za abale a pamsasapo, iye anati: “Zovuta pamalo ano n’zambiri; komabe, iwo alimbitsa chikhulupiriro chawo. Akukhala m’malo osasangalatsa, komabe akutumikira Yehova mwachimwemwe, ndipo ali pamtendere ndi Mulungu. Zimenezi zandilimbikitsa kukonda mtendere ndi kutumikira Yehova. Mavuto anga ndi ochepa kwabasi poyerekezera ndi abale amenewa.”

Msonkhanowo unatha ukusangalatsabe. M’nkhani yotsiriza, wokamba nkhani ananena kuti panali alendo ochokera m’mayiko eyiti. Mboni ina yothawa kwawo inati msonkhano umenewu unali umboni woti Mboni za Yehova n’zogwirizana komanso zimakondana m’dziko logawanikali. Ubale wawo wachikristu ndi weniwenidi.​—Yohane 13:35.

 [Bokosi/​Chithunzi patsamba 25]

ANYAMATA A KU SUDAN OLEKANITSIDWA NDI MABANJA AWO

Chiyambireni nkhondo yachiweniweni ku Sudan m’chaka cha 1983, anthu 5 miliyoni athawa kwawo. Ena mwa iwo ndi ana pafupifupi 26,000, amene analekanitsidwa ndi mabanja awo. Ambiri mwa ana amenewa anathawira m’misasa ya ku Ethiopia, kumene anakhalako pafupifupi zaka zitatu. Kumeneko anakakamizika kuchokako, ndipo anayenda kwa chaka chimodzi kudutsanso ku Sudan ndi kukafika kumpoto kwa dziko la Kenya. Ena mwa ana amenewa anaphedwa pa ulendo wawo wosautsawo ndi asilikali, anthu achifwamba, matenda ndi zilombo zakuthengo, mwakuti theka lokha la ana amenewa ndi amene anapulumuka. Patapita nthawi, ana opulumukawo ndi amene anadziwika kwambiri pamsasa wa Kakuma. Mabungwe opereka thandizo kwa anthu ovutika amawatcha kuti anyamata a ku Sudan olekanitsidwa ndi mabanja awo.

Tsopano mumsasa wa Kakuma muli anthu othawa m’mayiko osiyanasiyana monga Sudan, Somalia, Ethiopia ndi mayiko ena. Munthu wothawa kwawo akafika pamsasawo, amam’patsa zipangizo zofunika kuti amange nyumba komanso amam’patsa lona lofolerera nyumbayo. Kawiri pamwezi munthu aliyense wothawa kwawo amam’patsa ufa wolemera pafupifupi makilogalamu 6, nyemba kilogalamu imodzi, komanso mafuta ophikira ndi mchere pang’ono. Othawa kwawo ambiri amasinthanitsa zinthu zimenezi ndi zinthu zina zimene akufuna.

Ena mwa anyamata amenewa anapezananso ndi mabanja awo, ndipo ena anawasamutsira m’mayiko ena. Koma malinga ndi zimene inanena ofesi yopezera anthu othawa kwawo malo okhala, “ena ambirimbiri anatsalira mumsasa wa Kakuma womwe ndi wafumbi komanso muli ntchentche zosaneneka. Mmenemo amavutika kuti apeze chakudya chokwanira ndipo amafunika kugwira ntchito mwakhama kuti aphunzire sukulu.”

[Mawu a Chithunzi]

Courtesy Refugees International

[Mapu patsamba 23]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

KENYA

Msasa wa Kakuma

Nyanja ya Turkana

Lodwar

Eldoret

Nairobi

[Chithunzi patsamba 23]

Moyo wa mumsasa ndi wovuta

[Chithunzi patsamba 23]

Mumsasa wa Kakuma, madzi amachita kupatsidwa

[Chithunzi patsamba 23]

Mboni za ku Kenya zinayenda ulendo wovuta kulowera kumpoto kukalimbikitsa abale awo

[Chithunzi patsamba 24]

Mmishonale akumasulira nkhani ya mpainiya wapadera wam’dzikomo

[Chithunzi patsamba 24]

Malo aubatizo

[Mawu a Chithunzi patsamba 23]

Rationing water and Kakuma Refugee Camp: Courtesy Refugees International