Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Buku Lothandiza Pantchito Yomasulira Mabuku

Buku Lothandiza Pantchito Yomasulira Mabuku

 Buku Lothandiza Pantchito Yomasulira Mabuku

MLEMBI wamkulu wa Baibulo, Yehova Mulungu, akufuna kuti uthenga wabwino wa Ufumu wake ulalikidwe “kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu.” (Chivumbulutso 14:6) Akufuna kuti Mawu ake olembedwa azipezeka mosavuta kwa munthu aliyense. Kuti zimenezo zitheke, Baibulo lamasuliridwa m’zinenero zambiri kuposa buku lina lililonse padziko lapansi. Omasulira ambirimbiri ayesetsa mwakhama kulemba maganizo a Mulungu m’chinenero china.

Komabe, sikuti omasulirawa angomasulira chabe Baibulo n’kuimira pomwepo ayi. Mobwerezabwereza, agwiritsa ntchito Baibulo lenilenilo pomasulira mabuku ena. Omasulira ambiri ayerekezera mmene mawu enaake a m’Baibulo anawamasulira m’zinenero zosiyanasiyana kuti athe kumasulira mawuwo molondola. Popeza kuti Baibulo ndi lothandiza kwambiri pa ntchito yomasulira, tsopano akuligwiritsa ntchito m’makompyuta amene amatha kumasulira paokha.

N’zovuta kuti kompyuta payokha imasulire nkhani momveka bwino. Akatswiri ena afika poganiza kuti kompyuta payokha singathe kumasulira. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti mawu paokha sapanga chinenero. Chinenero chilichonse chili ndi njira yake yophatikizira mawu, malamulo ake, mawu amene satsatira malamulo amenewa, mawu ophiphiritsa ndiponso zining’a. Anthu ayesetsa kuphunzitsa kompyuta zinthu zonsezi, koma sizinathandize. Nkhani zambiri zimene makompyuta anamasulira zinali zosamveka.

Koma malinga ndi zimene ananena Franz Jesef Och, katswiri wotchuka pantchito yophunzitsa makompyuta kuti azimasulira, tsopano akatswiri a makompyuta akufufuza njira zatsopano zoti makompyuta azitsatira pomasulira. Tiyerekeze kuti nkhani ya Chingelezi mukufuna kuimasulira m’Chichewa. Choyamba, mutenge mawu amene alipo kale m’zinenero ziwirizi. Kenako muwalowetse mu kompyuta. Kompyuta imafananiza mawu achingelezi ndi achichewawo. Mwachitsanzo, kompyuta ikapeza liwu lachingelezi m’malo osiyanasiyana, ndipo m’malo onsewa nthawi zonse mukupezeka mawu a Chichewa akuti “nyumba,” zikatero kompyutayo imangoti liwu lachingelezilo Chichewa chake ndi “nyumba.” N’kutheka kuti mawu apafupi ndi liwu limeneli angakhale ofotokoza zambiri za nyumbayo, monga akuti, “yaikulu,” “yaing’ono,” “yakale” kapena “yatsopano.” Choncho kompyuta imaika pamodzi mawu   otanthauza chinthu chimodzi m’zinenero ziwirizo, komanso mawu amene amayendera limodzi. Kompyuta ikamaliza kusanja mawu amenewa, zomwe mwinamwake zingatenge masiku kapena milungu yowerengeka, imatha kugwiritsa ntchito mawu amenewa pomasulira nkhani yatsopano. Ngakhale kuti zimene kompyuta ingamasulire m’njira imeneyi zingakhale zosatsatira bwino galamala ndi kalembedwe ka chinenerocho, kawirikawiri zimakhala zomveka powerenga moti munthu amatha kupeza mfundo zofunika.

Kuti nkhani yomasuliridwa ikhale yomveka, mbali yaikulu zimadalira kuchuluka kwa mawu amene analowetsedwa mukompyuta komanso ngati anali omasuliridwa bwino. Apa m’pamene Baibulo lathandiza kwambiri. Baibulo linamasuliridwa m’zinenero zambiri, limapezeka mosavuta, ndipo lili ndi mawu ochuluka kwambiri. Choncho buku limene ofufuza analisankha msanga pophunzitsa kompyuta kumasulira chinenero chatsopano, linali Baibulo.