Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuphunzira Panopa Mpaka Muyaya

Kuphunzira Panopa Mpaka Muyaya

 Kuphunzira Panopa Mpaka Muyaya

ULRICH Strunz, yemwe ndi dokotala wachijeremani analemba mabuku angapo a mutu wakuti Forever Young (Kukhalabe Wamng’ono Mpaka Muyaya). M’mabuku amenewa iye anati, kuchita masewera olimbitsa thupi, kudya chakudya chabwino ndiponso kukhala ndi khalidwe labwino zingathandize munthu kukhala ndi thanzi labwino ngakhalenso kutalikitsa moyo kumene. Komabe, iye sanalonjeze anthu owerenga mabuku ake kuti angakhale moyo kwamuyaya mwa kutsatira malangizo akewo.

Komabe, alipo maphunziro amene angathandizedi munthu kupeza moyo wosatha. Ndipotu, ngati mutakhala ndi moyo kwamuyaya, mungaphunzire mpaka kalekale zinthu zopindulitsa. Popemphera kwa Mulungu, Yesu anati: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Choyamba tiyeni tikambirane tanthauzo la mawu akuti “moyo wosatha.” Kenako, tikambirane kuti kudziwa Mulungu ndi Yesu Kristu kumeneku kumaphatikizapo chiyani, ndipo tingawadziwe motani.

Malinga ndi zimene Baibulo limanena, posachedwapa Mlengi adzasandutsa dziko lapansili kukhala paradaiso, mmene anthu azidzatha kukhala ndi moyo wautali. Pokhazikitsa Paradaiso ameneyu, padzachitika zinthu zoopsa zofanana ndi Chigumula cha m’tsiku la Nowa. Lemba la Mateyu chaputala 24, vesi 37 mpaka 39, likusonyeza kuti Yesu anayerekezera nthawi yathu ino ndi ‘masiku a Nowa.’ M’masiku amenewo, anthu ‘sanadziwe’ kuti anali m’nthawi yamapeto. Iwo ananyalanyazanso uthenga umene Nowa anali kulalikira. Kenako linafika ‘tsiku limene Nowa  analowa m’chingalawa’ ndipo Chigumula chinawononga onse amene sanamvere uthenga wake. Nowa ndi onse amene anali nawo m’chingalawamo anapulumuka.

Yesu anasonyeza kuti “tsiku” lofanana ndi limeneli likubwera m’nthawi yathu ino. Anthu amene akuphunzira ndi kumvera uthenga wokhudza tsiku loopsa limeneli adzakhala ndi chiyembekezo chopulumuka komanso chokhala ndi moyo wosatha. Kuwonjezera pamenepo, anthu amene anamwalira omwe Mulungu akuwakumbukira adzauka kwa akufa ndi chiyembekezo chakuti sadzafanso. (Yohane 5:28, 29) Onani mmene Yesu anafotokozera mfundo ziwiri zimenezi. Polankhula ndi Marita za kuuka kwa akufa, iye anati: “Wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo; ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthawi yonse.” Umboni ukusonyeza kuti “tsiku” limeneli lili pafupi kwambiri, kutanthauza kuti n’kutheka kuti inuyo ‘simudzamwalira nthawi yonse.’​—Yohane 11:25-27.

Kenako Yesu anafunsa Marita kuti: “Kodi ukhulupirira ichi?” Iye anayankha kuti: “Inde Ambuye.” Kodi Yesu akanakufunsani funso lomweli lero, mukanayankha kuti chiyani? Mwina zikanakuvutani kukhulupirira kuti munthu angakhale ndi moyo osamwalira konse. Komabe, ngakhale kuti mungaganize choncho, mosakayikira mungakonde kukhulupirira zimenezi. Taganizirani zimene mungaphunzire mutati ‘musamwalire nthawi yonse.’ Yerekezerani mukusangalala ndi zinthu zonse zimene mumalakalaka mutaphunzira ndi kuchita panopa koma simukwanitsa chifukwa chosowa nthawi. Ndipo tangoyerekezerani mukuonananso ndi okondedwa anu amene anamwalira. Kodi ndi maphunziro ati amene angatheketse zimenezi, nanga mungawapeze bwanji?

N’zotheka Kuphunzira Zinthu Zopatsa Moyo

Kodi anthufe tingakwanitse kuphunzira za Mulungu ndi Kristu? Inde, tingatero. N’zoona kuti sitingakwanitse kuphunzira zinthu zonse zomwe Mlengi analenga. Koma pamene Yesu anagwirizanitsa kuphunzira kapena kuti ‘kudziwa’ ndi “moyo wosatha,” sikuti ankanena za sayansi ya zakuthambo kapena masayansi ena. Lemba la Miyambo chaputala 2, vesi 1 ndi 5, limasonyeza kuti “mawu” komanso “malamulo” opezeka m’Baibulo n’ngofunika kwambiri kuti ‘tim’dziwedi Mulungu.’ Ndipo lemba la Yohane 20:30, 31 limasonyeza kuti zinthu zolembedwa m’Baibulo, n’zokwanira kuti tim’dziwe Yesu ndi ‘kukhala nawo moyo.’

Choncho kuphunzira za Yehova ndi Yesu Kristu m’Baibulo n’kokwanira ngati mukufuna kudziwa mmene mungapezere moyo wosatha. Baibulo ndi buku lapadera kwambiri. Mokoma mtima, Mlengi anauzira amuna olemba buku limeneli kuti alilembe m’njira yakuti munthu amene sanaphunzire mokwanira azitha kuliphunzira kuti adzapeze moyo wosatha. Mofananamo, munthu amene sachedwa kumvetsa zinthu ndipo ali ndi nthawi komanso zipangizo zokwanira, angathe kupezabe zinthu zatsopano zoti aphunzire m’Malemba ouziridwawo. Popeza mukutha kuwerenga nkhani ino monga mmene mukuchitiramu, ndi umboni wakuti mungathe kuphunzira, koma kodi muyenera kuugwiritsa ntchito motani mwayi umenewu?

Padziko lonse lapansi, zitsanzo zambiri zasonyeza kuti njira yabwino yokwaniritsira zimenezi ndiyo kuphunzira Baibulo mothandizidwa ndi munthu amene anaphunzira kale nkhani imene mukuphunzirayo. Monga mmene Nowa anayesetsera kuphunzitsa anthu a m’nthawi yake, Mboni za Yehova n’zofunitsitsa kubwera kunyumba kwanu kudzaphunzira nanu Baibulo. Iwo angagwiritse ntchito kabuku kakuti Kodi  Mulungu Amafunanji kwa Ife? kapena buku la mutu woyenerera wakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. * Ngati zimakuvutani kukhulupirira kuti m’dziko lapansi la Paradaiso, anthu okhulupirika “sadzamwalira nthawi yonse,” kukambirana zinthu za m’Baibulo kumeneku kungakuthandizeni kukhulupirira lonjezo limeneli. Choncho, ngati mukufuna moyo wosatha, kapena mukufuna kungodziwa chabe ngati ndi chinthu chanzeru kukhulupirira kuti mungakhale ndi moyo wosatha, kodi muyenera kuchita chiyani? Muyenera kugwiritsa ntchito mwayi umenewu wophunzira Baibulo.

Kodi mudzatenga nthawi yaitali bwanji mukuphunzira? Kabuku kamasamba 32 kamene tatchula kaja, kakupezeka m’zinenero zambiri ndipo kali ndi mitu ifupiifupi 16 yokha yophunzira. Kapena ngati mutapatula ola limodzi pamlungu, m’miyezi yowerengeka mudzaphunzira nkhani zofunika kwambiri za m’Baibulo, m’buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Zofalitsa zimenezi zathandiza anthu ambiri kuphunzira zinthu zochuluka ndi kuyamba kukonda kwambiri Mulungu. Mlengi adzapereka mphoto kwa anthu amene akum’kondadi, ndipo adzawathandiza kupeza moyo wosatha.

N’zothekadi kuphunzira zinthu zimene zingatithandize kupeza moyo wosatha, ndipo maphunziro amenewa n’ngosasowa. Baibulo lonse kapena zigawo zake lamasuliridwa m’zinenero zoposa 2,000. M’mayiko 235, Mboni za Yehova n’zokonzeka kuthandiza munthu aliyense payekha ndipo zikufalitsa mabuku ofotokoza za m’Baibulo kuti anthu aphunzire zambiri.

Kuphunzira Panokha

Ubwenzi wanu ndi Mulungu ndi nkhani yapakati pa inuyo ndi Mlengi basi. Ndinu nokha amene mungasamale ubwenzi umenewu ndi kuulimbitsa, ndipo ndi Mulungu yekha amene angakupatseni moyo wosatha. Choncho muyenera kupitiriza kuphunzira panokha Mawu ake olembedwa. Zingakhale zosavuta kwa inu kupatula nthawi yophunzira ngati munthu wina atamabwera kwanuko nthawi ndi nthawi kudzaphunzira nanu.

Popeza kuti Baibulo komanso mabuku ofotokoza za m’Baibulo angatithandize “kum’dziwadi Mulungu,” m’pofunika kuwasamalira kwambiri. (Miyambo 2:5) Mukatero mudzatha kuwagwiritsa ntchito kwa zaka zambiri. Ngati mukukhala m’dziko losauka, n’kutheka kuti simunagwiritse ntchito mabuku ambiri kusukulu. Mwina munaphunzira mwa kungomvetsera ndiponso kuonerera. Mwachitsanzo, ku Benin kuli zinenero zoposa 50. Choncho m’dziko limenelo si zachilendo munthu kulankhula bwinobwino zinenero zinayi kapena zisanu, ngakhale kuti sanawerengepo buku lililonse pophunzira zinenero zimenezo. Kutha kuphunzira mwa kungomvetsera, kuonerera, ndi kutchera khutu ndi dalitso lalikulu. Komabe, mudzaona kuti mabuku angakuthandizeni kwambiri pophunzira.

Ngati m’nyumba mwanu mulibe malo okwanira, yesetsani kupeza malo abwino oti muzisunga Baibulo lanu ndi mabuku othandiza pophunzira Baibulo. Asungeni pamalo osavuta kuwapeza komanso pamene sangawonongeke.

Kuphunzira ndi Banja Lanu

Ngati ndinu kholo, muyenera kukhala ndi chidwi chofuna kuthandiza ana anu kuphunzira zimene inuyo mukuphunzira. M’mayiko osauka, makolo nthawi zambiri amaphunzitsa ana awo ntchito zosiyanasiyana zothandiza pamoyo. Ntchito zimenezi ndi monga kuphika, kufuna nkhuni, kutunga madzi, kulima, kupha nsomba, kugula ndi kugulitsa zinthu kumsika. Amenewa ndi maphunziro othandizadi pamoyo. Komabe pa maphunziro amenewa, makolo ambiri saphatikizapo maphunziro othandiza ana kudzapeza moyo wosatha.

Mulimonse mmene zinthu zingakhalire pamoyo wanu, mwina mukuona kuti mulibe nthawi yokwanira. Mlengi akudziwanso zimenezo. Pankhani ya kuphunzitsa ana njira zake, onani zimene Mulungu ananena zaka zambiri zapitazo: “Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.” (Deuteronomo 6:7) Mogwirizana ndi mfundo zimenezi, bwanji osayesa kupanga ndandanda yanu yophunzitsira ana anu ngati yotsatirayi:

 1. “Pokhala pansi m’nyumba zanu”: Yesetsani kukambirana nkhani za m’Baibulo nthawi zonse ndi ana anu panyumba, mwinamwake mlungu uliwonse, monga momwe winawake ankachitira pophunzira ndi inuyo. Mboni za Yehova zimafalitsa mabuku ofotokoza za m’Baibulo othandiza pophunzitsa ana amisinkhu yonse.

2. “Poyenda inu panjira”: Kambiranani za Yehova ndi ana anu nthawi iliyonse, monga momwe mumachitira powaphunzitsa zofunika pamoyo kapena kuwapatsa malangizo alionse.

3. “Pogona inu pansi”: Pempherani ndi ana anu usiku uliwonse.

4. “Pouka inu”: Mabanja ambiri apindula mwa kukambirana lemba limodzi la m’Baibulo m’mawa uliwonse. Mboni za Yehova zimagwiritsa ntchito kabuku kakuti Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku * pochita zimenezi.

M’mayiko osauka, makolo ambiri amayesetsa kuti mmodzi mwa ana awo akhale wophunzira bwino. Amachita izi kuti makolowo akadzakalamba, mwanayo adzawathandize. Koma mukaphunzira Baibulo ndi kulimbikitsa ana anu kuphunziranso Baibulo, inuyo limodzi ndi banja lanu lonse mudzaphunzira zinthu zimene zidzakuthandizani kupeza moyo wamuyaya.

Kodi tsiku lidzafika pamene tidzadziwa chilichonse? Ayi. Pamene dziko lathuli likupitirizabe kuzungulira m’chilengedwe chonse chopanda malirechi, tidzapitiriza kuphunzira. Inde, lemba la Mlaliki 3:11 limati: “Chinthu chilichonse [Mulungu] anachikongoletsa pa mphindi yake; ndipo waika zamuyaya m’mitima yawo ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.” Kuphunzira ndi chinthu chosangalatsa chomwe sichidzatha.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Onsewa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 23 Kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

“Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu . . . ”

[Zithunzi patsamba 7]

Thandizani banja lanu kuphunzira panopa mpaka muyaya