Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

 Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi mtumwi Paulo sanakane chikhulupiriro chake chachikristu pamene anauza bungwe la Sanihedirini kuti “ine ndine Mfarisi”?

Kuti timvetse mawu a Paulo amenewa, opezeka pa Machitidwe 23:6, tifunika kuganizira mmene zinthu zinalili panthawiyo.

Ayuda achipolowe ataukira Paulo ku Yerusalemu, iye analankhula nawo. Anawauza kuti ‘anaphunzitsidwa mu mzinda [wa Yerusalemu], pa mapazi a Gamaliyeli, wolangizidwa monga mwa chitsatidwe chenicheni cha chilamulo cha makolo awo.’ Khamulo linamvetsera mawu ake odziteteza kwa kanthawi, koma kenako linakwiya naye ndipo kapitawo wamkulu amene anali kuteteza Paulo, anam’tenga ndi kulowa naye kumpanda wa asilikali. Pamene ankafuna kumukwapula, Paulo anati: “Kodi n’kuloleka kwa inu kukwapula munthu Mroma, mlandu wake wosamveka?”​—Machitidwe 21:27–22:29.

Tsiku lotsatira, kapitawo uja anatenga Paulo ndi kupita naye kubwalo lalikulu la Ayuda, la Sanihedirini. Paulo anayang’anitsitsa ndi kuona kuti m’bungwe la Sanihedirini munali Asaduki ndi Afarisi. Ndiyeno iye anati: “Amuna, abale, ine ndine Mfarisi, mwana wa Afarisi; andinenera mlandu wa chiyembekezo ndi kuuka kwa akufa.” Chifukwa cha mawu amenewa, panali kusamvana pakati pa Afarisi ndi Asaduki, “pakutitu Asaduki anena kuti kulibe kuuka kwa akufa, kapena mngelo, kapena mzimu; koma Afarisi avomereza ponse pawiri.” Ena amene anali m’gulu lampatuko la Afarisi ananena mwaukali kuti: “Sitipeza choipa chilichonse mwa munthuyu.”​—Machitidwe 23:6-10.

Popeza kuti Paulo ankadziwika monga Mkristu wachangu kwambiri, sizikanatheka kuti bungwe la Sanihedirini lim’khulupirire kuti analidi m’gulu la Afarisi. Afarisi omwe anali pamalowo sakanagwirizana ndi Mfarisi aliyense amene sakhulupirira ziphunzitso zawo zonse. Choncho mawu a Paulo akuti iye anali Mfarisi sanatanthauze kuti anali Mfarisi m’zonse. Ndipo Afarisi amene anali pamenepo anazindikira kuti Paulo sankatanthauza kuti anali Mfarisi m’zonse.

Mwa kunena kuti anali kuweruzidwa chifukwa cha chiyembekezo cha kuuka kwa akufa, mwachionekere Paulo anatanthauza kuti pankhani imeneyi anali ngati Afarisi. Pa kutsutsana kulikonse kokhudza nkhani ya kuuka kwa akufa, zikhulupiriro za Paulo zinali zofanana ndi za Afarisi osati Asaduki omwe sankakhulupirira kuuka kwa akufa.

Zimene Paulo anali kukhulupirira monga Mkristu sizinali zotsutsana ndi zikhulupiriro za Afarisi pankhani ya kuuka kwa akufa, angelo ndi mfundo zina za m’Chilamulo. (Afilipi 3:5) Choncho pamfundo zochepa zimenezi, Paulo akanatha kunena kuti anali ngati Afarisi, ndipo a m’bungwe la Sanihedirini anadziwa kuti Paulo anadzitcha Mfarisi poganizira mfundo zimenezi. Chotero anagwiritsa ntchito zomwe ankadziwa monga Myuda pofuna kugonjetsa bwalo lapamwamba la Ayuda limene linkadana naye.

Komabe, umboni waukulu wosonyeza kuti Paulo sanakane chikhulupiriro chake ndi wakuti Yehova anapitiriza kumuyanja. Usiku wa tsiku limene Paulo ananena kuti “ine ndine Mfarisi,” Yesu anamuuza kuti: “Limbika mtima; pakuti monga wandichitira umboni ku Yerusalemu, koteronso uyenera kundichitira umboni ku Roma.” Popeza kuti Paulo anali kuyanjidwa ndi Mulungu, tinganene motsimikiza kuti Paulo sanakane chikhulupiriro chake chachikristu.​—Machitidwe 23:11.