Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

Bukuli lakonzedwa kuti likuthandizeni pophunzira Baibulo ndipo likufotokoza zimene Baibulo limanena pa nkhani zosiyanasiyana, monga n’chifukwa chiyani timakumana ndi mavuto, kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira, komanso tingatani kuti tikhale ndi banja losangalala.

Kodi Zimene Zikuchitikazi Ndi Zomwe Mulungu Ankafuna?

N’kutheka kuti mumadabwa kuti n’chifukwa chiyani panopa m’dzikoli muli mavuto ambiri. Kodi mukudziwa kuti Baibulo limanena kuti zimenezi zitha posachedwapa ndipo inuyo mukhoza kukhala m’gulu la anthu amene adzasangalale ndi moyo mavutowa atatha?

MUTU 1

Kodi Zoona Zenizeni za Mulungu N’zotani?

Kodi inuyo mumaona kuti Mulungu amakuganizirani? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe makhalidwe a Mulungu komanso zimene mungachite kuti mumuyandikire.

MUTU 2

Baibulo Ndi Buku Lochokera Kwa Mulungu

Kodi Baibulo lingakuthandizeni bwanji kupirira mavuto anu? N’chifukwa chiyani muyenera kukhulupirira maulosi a m’Baibulo?

MUTU 3

Kodi Mulungu Analenga Dziko Lapansili Chifukwa Chiyani?

Kodi zimene Yehova Mulungu ankafuna, zoti anthu azikhala m’paradaiso, zidzachitikadi? Ngati ndi choncho, zidzachitika liti?

MUTU 4

Kodi Yesu Khristu Ndi Ndani?

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe chifukwa chake Yesu amanenedwa kuti ndi Mesiya, kumene anachokera, ndiponso chifukwa chake ali Mwana wapadera wa Mulungu.

MUTU 5

Dipo la Yesu Ndi Mphatso ya Mulungu Yamtengo Wapatali Kuposa Zonse

Kodi dipo n’chiyani? Nanga lingakuthandizeni bwanji?

MUTU 6

Kodi Munthu Akafa Amapita Kuti?

Werengani nkhaniyi kuti mumve zimene Baibulo limanena zokhudza kumene kuli akufa komanso chifukwa chake timafa.

MUTU 7

Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso ndi Moyo

Kodi pali mnzanu kapena m’bale wanu amene anamwalira? Kodi n’zotheka kudzamuonanso? Werengani nkhaniyi kuti mumve zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kuuka kwa akufa.

MUTU 8

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Anthu ambiri amalidziwa Pemphero la Ambuye. Koma kodi mawu akuti, “Ufumu wanu udze” amatanthauza chiyani?

MUTU 9

Kodi Tilidi ‘M’masiku Otsiriza’?

Werengani nkhaniyi kuti mumve mmene zochita za anthu zikusonyezera kuti tilidi ‘m’masiku otsiriza’ omwe Baibulo linaneneratu

MUTU 10

Mmene Zochita za Angelo Komanso Ziwanda Zimakhudzira Moyo Wathu

Baibulo limanena za angelo ndi ziwanda. Koma kodi n’zoona kuti kuli angelo komanso ziwanda? Kodi zochita zawo zingakhudze moyo wanu?

MUTU 11

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola kuti Anthu Azivutika?

Anthu ambiri amaganiza kuti Mulungu ndi amene amachititsa mavuto amene anthu akukumana nawo. Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Werengani nkhaniyi kuti mumve zimene Mulungu amanena kuti ndi zomwe zikuchititsa mavutowa.

MUTU 12

Khalani ndi Makhalidwe Amene Mulungu Amasangalala Nawo

N’zotheka kukhala ndi makhalidwe amene Yehova amasangalala nawo. Mukhoza kukhala mnzake.

MUTU 13

Muziona Moyo Ngati Mmene Mulungu Amauonera

Kodi Mulungu amaiona bwanji nkhani yochotsa mimba, kuikidwa magazi, moyo wa nyama?

MUTU 14

Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Lizisangalala

Chikondi chimene Yesu anasonyeza ndi chitsanzo chabwino kwa amuna, akazi, makolo, komanso ana. Kodi tikuphunzira chiyani kuchokera kwa Yesu?

MUTU 15

Kulambira Kumene Mulungu Amavomereza

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zinthu 6 zimene zingakuthandizeni kudziwa anthu amene ali m’chipembedzo choona.

MUTU 16

Yesetsani Kuti Muzilambira Mulungu M’njira Yovomerezeka

Kodi pangakhale mavuto otani mukamauza ena zimene mumakhulupirira? Kodi mungawafotokozere bwanji m’njira yoti asakhumudwe?

MUTU 17

Pemphero Lingakuthandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu

Kodi Mulungu amamvetsera mukamapemphera? Kuti mupeze yankho la funso limeneli, muyenera kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani ya pemphero.

MUTU 18

Ubatizo Umatithandiza kuti Tikhale pa Ubwenzi ndi Mulungu

Kodi munthu ayenera kuchita chiyani kuti ayenerere kubatizidwa? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene ubatizo umatanthauza ndiponso mmene uyenera kuchitikira.

MUTU 19

Zimene Mungachite Kuti Mulungu Apitirize Kukukondani

Kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira zimene Mulungu watichitira?

ZAKUMAPETO

Tanthauzo la Dzina la Mulungu Ndiponso Mmene Tingaligwiritsire Ntchito

N’chifukwa chiyani m’Mabaibulo ambiri amene anthu ena anamasulira mulibe dzina lenileni la Mulungu? Kodi ndi bwino kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu?

ZAKUMAPETO

Mmene Ulosi wa Danieli Unasonyezera Nthawi Imene Mesiya Adzafike

Kudakali zaka zoposa 500, Mulungu anaululiratu nthawi yeniyeni imene Mesiya adzafike. Werengani nkhaniyi kuti mumve zambiri za ulosi wochititsa chidwiyi!

ZAKUMAPETO

Yesu Ndi Mesiya Amene Mulungu Ananeneratu Kuti Adzabwera

Yesu anakwaniritsa maulosi onse a m’Baibulo onena za Mesiya. Werengani m’Baibulo lanu kuti muone umboni wosonyeza kuti maulosi onse onena za Mesiya anakwaniritsidwadi.

ZAKUMAPETO

Kudziwa Zoona Zokhudza Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyera

Anthu ambiri amakhulupirira kuti Baibulo limaphunzitsa kuti pali Mulungu Atate, Mulungu Mwana ndi Mulungu Mzimu Woyera. Koma kodi zimenezi ndi zoona?

ZAKUMAPETO

N’chifukwa Chiyani Akhristu Oona Sagwiritsa Ntchito Mtanda Polambira Mulungu?

Kodi Yesu anaferadi pamtanda? Werengani nkhaniyi kuti mumve yankho la m’Baibulo la funsoli.

ZAKUMAPETO

Chakudya Chamadzulo cha Ambuye Ndi Mwambo Umene Umalemekeza Mulungu

Akhristu analamulidwa kuti azichita Chikumbutso cha imfa ya Khristu. Kodi mwambo umenewu uyenera kuchitika liti ndipo motani?

ZAKUMAPETO

Kodi Ndi Zoona Kuti Anthu Ali Ndi Mzimu Umene Sumafa?

Anthu ambiri amakhulupirira kuti munthu akafa, pali chinachake m’thupi mwake chimene chimapitirizabe kukhala ndi moyo. Koma kodi Mawu a Mulungu amati chiyani pa nkhaniyi?

ZAKUMAPETO

Kodi Mawu Akuti Sheoli ndi Hade Amatanthauza Chiyani?

Mabaibulo ena amamasulira mawu akuti Sheoli ndi Hade kuti “manda” kapena “dzenje.” Kodi mawu amenewa amatanthauza chiyani kwenikweni?

ZAKUMAPETO

Kodi Tsiku la Chiweruzo N’chiyani?

Werengani nkhaniyi kuti muone umboni woti Tsiku la Chiweruzo idzakhala nthawi yosangalatsa kwa anthu onse okhulupirika.

ZAKUMAPETO

Chaka cha 1914 Ndi Chaka Chapadera Kwambiri

Kodi ndi mfundo ziti za m’Baibulo zimene zikusonyeza kuti chaka cha 1914 chinali chapadera?

ZAKUMAPETO

Kodi Mikayeli Mkulu wa Angelo ndi Ndani?

Baibulo limatiuza kuti mngelo wamphamvu ameneyu ndi ndani. Werengani nkhaniyi kuti mumudziwe ndiponso mudziwe zimene akuchita panopa.

ZAKUMAPETO

Kodi “Babulo Wamkulu” N’chiyani?

Buku la Chivumbulutso limafotokoza za mkazi wina amene amatchulidwa kuti ‘Babulo Wamkulu.’ Kodi dzina limeneli limanena za mkazi weniweni? Kodi Baibulo limati chiyani za mkazi ameneyu?

ZAKUMAPETO

Kodi Yesu Anabadwa mu December?

Taganizirani mmene nyengo inalili pa nthawi imene Yesu anabadwa. Kodi kudziwa zimenezi kungatithandize bwanji?

ZAKUMAPETO

Kodi Akhristu Ayenera Kuchita Nawo Zikondwerero Zimene Anthu Ena Amachita?

Kodi zikondwerero zotchuka kwambiri kwanuko zinayamba bwanji? Mungadabwe kumva yankho la funso limeneli.