Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 11

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola kuti Anthu Azivutika?

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola kuti Anthu Azivutika?
  • Kodi Mulungu ndi amene amachititsa mavuto padzikoli?

  • Kodi m’munda wa Edeni munayambika nkhani yotani?

  • Kodi Mulungu adzathetsa bwanji mavuto amene anthu akukumana nawo?

1, 2. Kodi masiku ano anthu akukumana ndi mavuto otani, ndipo zimenezi zimachititsa anthu ambiri kukhala ndi mafunso ati?

PA KUMENYANA koopsa kumene kunachitika m’dziko lina lomwe munali nkhondo, akazi ndi ana ambirimbiri anaphedwa ndipo anaikidwa m’manda amodzi. Pamandapo anaikapo timitanda tambirimbiri ndipo kamtanda kalikonse kanali ndi mawu akuti: “N’kupheranji anthu onsewa?” Limeneli ndi limodzi mwa mafunso amene anthu amafunsa chifukwa chosamvetsa zinthu zinazake zimene zachitika. Zinthu zina zimene zimachititsa anthu kufunsa mafunso a mtundu umenewu ndi imfa ya anzawo kapena abale awo chifukwa cha nkhondo, matenda, uchigawenga, zivomezi, kusefukira kwa madzi ndiponso zinthu zina. Akhozanso kufunsa mafunsowa ngati nyumba yawo kapena katundu zawonongeka. Amafuna kudziwa chifukwa chake zinthu zoipa ngati zimenezo zawachitikira.

2 Koma kodi n’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti anthu azivutika? Ngati Yehova Mulungu alidi ndi mphamvu zonse komanso ali ndi chikondi, nzeru ndiponso chilungamo, n’chifukwa chiyani padzikoli pamachitika zinthu zambirimbiri zopanda chilungamo? Kodi inuyo munayamba mwadzifunsapo mafunso ngati amenewa?

3, 4. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti si kulakwa kufunsa chifukwa chimene Mulungu amalolera kuti tizivutika? (b) Kodi Yehova amafuna kuti anthu azivutika?

3 Kodi n’kulakwa kufunsa chifukwa chimene Mulungu amalolera kuti anthu azikumana ndi mavuto? Ena amaopa kuti akafunsa funso ngati limeneli ndiye kuti aoneka ngati alibe chikhulupiriro kapenanso aoneka ngati salemekeza Mulungu. Koma mukamawerenga Baibulo mungaone kuti pali anthu ena okhulupirika omwe anafunsapo mafunso ngati amenewa. Mwachitsanzo, mneneri Habakuku anafunsa Yehova kuti: “N’chifukwa chiyani mukundichititsa kuona zinthu zopweteka? N’chifukwa chiyani mukupitiriza kuyang’ana khalidwe loipa? N’chifukwa chiyani kufunkha ndi chiwawa zikuchitika pamaso panga? Ndipo n’chifukwa chiyani pali mikangano ndi kumenyana?”—Habakuku 1:3.

Yehova adzathetsa mavuto onse

4 Kodi Yehova anakalipira Habakuku chifukwa chofunsa mafunso amenewa? Ayi. M’malomwake iye analola kuti mawu a Habakuku ochokera pansi pa mtimawa alembedwe m’Baibulo. Mulungu anamuthandiza kumvetsa bwino chifukwa chake zimenezo zinkachitika komanso anamuthandiza kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba. Zimenezi ndi zomwe Yehova amafunanso kukuchitirani. Kumbukirani zimene Baibulo limaphunzitsa zoti iye “amakuderani nkhawa.” (1 Petulo 5:7) Mulungu amadana ndi zinthu zoipa komanso kuona anthu akuvutika ndipo amadana ndi zimenezi kuposa mmene ifeyo timachitira. (Yesaya 55:8, 9) Nangano n’chifukwa chiyani padzikoli pali mavuto ambiri chonchi?

N’CHIFUKWA CHIYANI TIKUKUMANA NDI MAVUTO AMBIRI CHONCHI?

5. Kodi anthu ena amanena kuti timakumana ndi mavuto chifukwa chiyani, nanga Baibulo limati chiyani pa nkhaniyi?

5 Anthu a zipembedzo zosiyanasiyana amapita kwa atsogoleri awo kukafunsa chifukwa chimene chikuchititsa kuti anthu azikumana ndi mavuto ambiri. Nthawi zambiri atsogoleriwo amayankha kuti mavutowo ndi chifuniro cha Mulungu ndipo iye anakonzeratu chilichonse chimene chimachitika, kuphatikizapo zinthu zoipa. Anthu ambiri amauzidwa kuti zimene Mulungu amachita n’zosamvetsetseka kapena zoti Mulungu ndi amene amachititsa kuti anthu amwalire, ndi ana omwe, n’cholinga choti azikakhala ndi iyeyo kumwamba. Koma monga taphunzirira kale, Yehova Mulungu samachita chinthu chilichonse choipa. Baibulo limanena kuti: “Mulungu woona sangachite zoipa m’pang’ono pomwe, ndipo Wamphamvuyonse sangachite zinthu zopanda chilungamo ngakhale pang’ono.”—Yobu 34:10.

6. N’chifukwa chiyani anthu ambiri amaganiza kuti Mulungu ndi amene akuchititsa mavuto amene ali padzikoli?

6 Kodi mukudziwa chifukwa chimene chimapangitsa kuti anthu aziona ngati Mulungu ndi amene akuchititsa mavuto onsewa? Nthawi zambiri amaona choncho chifukwa amaganiza kuti Mulungu Wamphamvuyonse ndi amene akulamulira dzikoli. Anthu amenewa sadziwa mfundo yosavuta koma yofunika imene Baibulo limaphunzitsa. Mfundo imeneyi munaiphunzira m’Mutu 3. Mfundo yake ndi yakuti wolamulira weniweni wa dzikoli ndi Satana Mdyerekezi.

7, 8. (a) Kodi zimene zikuchitika m’dzikoli zikusonyeza bwanji kuti wolamulira wake ndi Satana? (b) Kodi kuchimwa kwa anthu ndiponso “zinthu zosayembekezereka” zachititsa bwanji kuti anthu azivutika?

7 Baibulo limanena momveka bwino kuti: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Kodi mfundo imeneyi si yomveka? Zimene zimachitika m’dzikoli zikugwirizana ndi khalidwe la wolamulira wake, Satana, yemwe “akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Chivumbulutso 12:9) Satana ndi woipa, wankhanza komanso wachinyengo. N’chifukwa chake m’dziko limene akulamulirali mukuchitika zinthu zambiri zoipa, zachinyengo komanso zankhanza.

8 Monga tinaonera m’Mutu 3, chifukwa china n’chakuti makhalidwe a anthu anayamba kusokonekera kungoyambira pamene Adamu anachimwa. Anthu ochimwa amakonda kulimbirana ulamuliro, ndipo zimenezi zimayambitsa nkhondo, kuponderezana ndiponso mavuto ena. (Mlaliki 4:1; 8:9) Chifukwa chachitatu chimene chimachititsa kuti anthu azivutika ndi “zinthu zosayembekezereka” zimene zimatichitikira. (Werengani Mlaliki 9:11.) Popeza panopa sitikulamulidwa ndi Yehova yemwe angatiteteze, anthu akhoza kukumana ndi mavuto chifukwa choti anali pamalo olakwika pa nthawinso yolakwika.

9. Kodi n’chiyani chikutichititsa kuona kuti Yehova ali ndi chifukwa chomveka chololera kuti mavuto azipitirira?

9 N’zolimbikitsa kudziwa kuti Mulungu si amene amachititsa kuti tizivutika. Iye sachititsa nkhondo, uchigawenga, kuponderezana, zivomezi ndiponso kusefukira kwa madzi zimene zimachititsa kuti anthu azivutika. Komabe tingafune kudziwa kuti, N’chifukwa chiyani Yehova amalola kuti tizikumana ndi mavuto onsewa? Timadziwa kuti ali ndi mphamvu yotha kuletsa kuti zimenezi zisamachitike chifukwa Baibulo limanena kuti iye ndi Wamphamvuyonse. Ndiye n’chifukwa chiyani sakuthetsa mavutowa? Popeza Mulungu ndi wachikondi, payenera kuti pali chifukwa chomveka bwino chimene wachitira zimenezi.—1 Yohane 4:8.

NKHANI IMENE INACHITIKA M’MUNDA WA EDENI

10. Kodi Satana anatsutsa chiyani, nanga anachita bwanji zimenezi?

10 Kuti tidziwe chifukwa chimene Mulungu walolera kuti anthu azivutika, tiyenera kukumbukira zimene zinachitika kuti mavutowa ayambe. Pamene Satana anachititsa kuti Adamu ndi Hava asamvere Yehova, anasonyeza kuti ankaona kuti Yehova si woyenera kulamulira anthu. Iye sanatsutse zoti Yehova ali ndi mphamvu, chifukwa amadziwa bwino kuti Yehova ali ndi mphamvu zopanda malire. Pamene ananena kuti Mulungu ndi wabodza ndiponso amawabisira anthu ake zinthu zabwino, Satana ankatanthauza kuti Mulungu ndi wolamulira woipa. (Werengani Genesis 3:2-5.) Satana anasonyeza kuti anthu angakhale ndi moyo wabwino ngati atakhala kuti sakulamulidwa ndi Mulungu. Zimene anachitazi kunali kuukira ulamuliro wa Yehova.

11. N’chifukwa chiyani Mulungu sanaphe oukirawo nthawi yomweyo?

11 Pamene Adamu ndi Hava anasiya kumvera Yehova, anakhala ngati akunena kuti: ‘Sitikufuna zoti Yehova azitilamulira. Tikhoza kumasankha tokha zoyenera kuchita.’ Kodi Yehova akanaithetsa bwanji nkhani imeneyi? Kodi akanasonyeza bwanji kuti iyeyo ndi wolamulira wabwino ndipo zimene oukirawo akunena ndi zabodza? Ena akhoza kuona kuti zikanakhala bwino Mulungu akanangowawonongeratu oukirawo nthawi yomweyo. Koma Yehova anali atanena kale kuti cholinga chake ndi choti padziko lapansi padzaze ndi ana a Adamu ndi Hava ndiponso kuti anthuwo akhale m’dziko lapansi la paradaiso mpaka kalekale. (Genesis 1:28) Yehova nthawi zonse amakwaniritsa zolinga zake. (Yesaya 55:10, 11) Kuwonjezera pamenepo, kupha oukirawo nthawi yomweyo sikukanathetsa nkhani imene Satana anayambitsa yonena kuti Yehova si woyenera kulamulira anthu.

12, 13. Fotokozani chitsanzo chosonyeza chifukwa chimene Yehova walolera kuti Satana azilamulira dzikoli ndiponso kuti anthu azidzilamulira okha.

12 Kuti timvetse nkhani imeneyi, tiyeni tiganizire chitsanzo ichi: Tiyerekezere kuti mphunzitsi akufuna kusonyeza ana a m’kalasi mwake mmene angapezere yankho la samu inayake yovuta. Ndiyeno mwana wina wokonda kutsutsa akunena kuti njira imene mphunzitsiyo akunena ndi yolakwika. Pofuna kusonyeza kuti iyeyo ndi wanzeru kuposa mphunzitsiyo, mwana wotsutsayo akukakamira kuti akudziwa njira yabwino yopezera yankho lolondola. Ana ena m’kalasimo ayamba kuganiza kuti mnzawoyo akunena zoona ndipo nawonso ayamba kutsutsa zimene mphunzitsiyo akunena. Kodi mphunzitsiyo angatani? Ngati atangowatulutsa ana otsutsawo, kodi ana amene angatsale m’kalasimo angakhale ndi maganizo otani? Kodi sangamaganize kuti mnzawoyo amanena zoona? Ana onse m’kalasimo akhoza kusiya kulemekeza mphunzitsiyo poganiza kuti watulutsa anawo chifukwa chodziwa kuti anawo amanena zoona. Koma mukuganiza bwanji ngati mphunzitsiyo atam’patsa mwana wotsutsayo mpata woti asonyeze anzakewo njira imene akunenayo?

Kodi mwana wa sukulu angadziwe zinthu kuposa mphunzitsi wake?

13 Yehova anachita zofanana ndi zimenezi. Kumbukirani kuti panali angelo enanso ambirimbiri amene ankaona zimene zinachitika m’munda wa Edeni. (Yobu 38:7; Chivumbulutso 5:11) Njira imene Yehova akanatsatira pothetsa nkhaniyi, ikanakhudza angelo onsewa ndiponso m’kupita kwa nthawi ikanadzakhudzanso anthu. Ndiye kodi Yehova anachita chiyani? Anam’patsa Satana mwayi woti asonyeze mmene iyeyo angalamulirire anthu. Yehova analolanso kuti anthu azidzilamulira okha mothandizidwa ndi Satana.

14. Kodi zimene Yehova anachita zolola kuti anthu azidzilamulira okha zili ndi ubwino wotani?

14 Mphunzitsi wa m’chitsanzo chija akudziwa zoti mwana wotsutsa uja limodzi ndi anzake sangathe kupeza yankho lolondola. Koma akudziwanso kuti kupatsa otsutsawo mpata wosonyeza njira imene akunenayo kuthandiza ana onse a m’kalasimo. Otsutsawo akalephera kupeza yankho lolondola, ana onse okhulupirika angaone kuti mphunzitsiyo ndi amene ali woyenera kuphunzitsa. Angamvetse ngati mphunzitsiyo pamapeto pake atatulutsa m’kalasi ana otsutsawo. Mofanana ndi zimenezi, Yehova anadziwa kuti angelo ndiponso anthu onse okhulupirika angaphunzirepo mfundo yofunika ngati ataona kuti Satana ndi anzake oukirawo alephera komanso ngati ataona kuti anthu sangathe kudzilamulira okha. Angaphunzire mfundo yofanana ndi imene Yeremiya ananena, yakuti: “Ine ndikudziwa bwino, inu Yehova, kuti munthu wochokera kufumbi alibe ulamuliro wowongolera njira ya moyo wake. Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.

N’CHIFUKWA CHIYANI MULUNGU SAKUTHETSABE MAVUTOWA MPAKA PANO?

15, 16. (a) N’chifukwa chiyani Yehova walola kuti anthu avutike kwa nthawi yaitali chonchi? (b) N’chifukwa chiyani Mulungu saletsa kuti zinthu zoipa zisamachitike?

15 Koma kodi n’chifukwa chiyani Yehova walola kuti anthu avutike kwa nthawi yaitali chonchi? Ndiponso n’chifukwa chiyani saletsa kuti zinthu zoipa zisamachitike? Kuti tipeze mayankho a mafunso amenewa, tiyeni tiganizire zinthu ziwiri zimene mphunzitsi wa m’chitsanzo chija sangachite. Choyamba, sangaletse mwana wotsutsayo kusonyeza njira imene akuti ndi yolondolayo. Chachiwiri, mphunzitsiyo sangathandize wotsutsayo pamene akufotokoza yankho lakelo. Mofanana ndi zimenezi, ganizirani zinthu ziwiri zimene Yehova sangachite. Choyamba, sanaletse Satana ndi onse amene ali kumbali yake kuyeserera zimene ankaona kuti ndi zolondola. Choncho panafunika kuti padutse nthawi yokwanira. Ndipo pa zaka masauzande ambiri zimene zadutsazi, anthu akhala akuyesa kudzilamulira okha pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana. Ngakhale kuti luso lawo lapita patsogolo pa nkhani za sayansi ndi ntchito zina, koma umphawi, kupanda chilungamo, uchigawenga ndiponso nkhondo zawonjezereka kuposa kale. Zimenezi zatsimikizira kuti ulamuliro wa anthu walephera.

16 Chachiwiri, Yehova sanathandize Satana kulamulira dzikoli. Mwachitsanzo, ngati Mulungu akanaletsa kuti uchigawenga usamachitike, kodi sakanakhala kuti akuthandiza oukirawo? Kodi zimenezi sizikanapangitsa anthu kuganiza kuti akhoza kudzilamulira okha popanda mavuto aliwonse? Zimenezi ndi zomwe Satana amafuna kuti anthu aziganiza koma limeneli ndi bodza. Ndipo Yehova sangathandize Satana pokwaniritsa bodza lakeli chifukwa “n’zosatheka kuti Mulungu aname.”—Aheberi 6:18.

17, 18. Kodi Yehova adzakonza bwanji zinthu zimene zawonongeka chifukwa cha ulamuliro wa anthu ndiponso zochita za Satana?

17 Komatu pali zinthu zambiri zimene zawonongeka pa nthawi imene Satana wakhala akulamulirayi. Ngakhale zili choncho, tiyenera kukumbukira kuti Yehova ali ndi mphamvu zopanda malire moti adzathetsa mavuto onse amene tikukumana nawo. Monga tinaphunzirira kale, ngakhale kuti dzikoli lawonongeka kwambiri, lidzakonzedwa n’kukhalanso Paradaiso. Anthu amene amakhulupirira nsembe ya Khristu sadzakumananso ndi mavuto amene anabwera chifukwa cha uchimo, komanso anthu adzasangalala kuona abale awo ndiponso anzawo ataukitsidwa. Izi zikusonyeza kuti Mulungu adzagwiritsa ntchito Yesu kuti “awononge ntchito za Mdyerekezi.” (1 Yohane 3:8) Yehova adzachita zinthu zonsezi pa nthawi yake yoyenera. Tiyenera kuyamikira kuti sanawononge mwamsanga anthu oipa, chifukwa zatipatsa mwayi wophunzira Baibulo ndiponso woyamba kumutumikira. (Werengani 2 Petulo 3:9, 10.) Pa zaka zonsezi, Mulungu wakhala akufufuza anthu amene akufuna kumulambira ndipo akuwathandiza kupirira mavuto onse amene akukumana nawo m’dziko lamavutoli.—Yohane 4:23; 1 Akorinto 10:13.

18 Koma ena akhoza kukhala ndi funso lakuti, ‘Kodi mavuto onsewa sakanapeweka ngati Mulungu akanalenga Adamu ndi Hava m’njira yoti asadzachimwe?’ Kuti mupeze yankho la funso limeneli, muyenera kukumbukira mphatso yamtengo wapatali imene Yehova anakupatsani.

KODI MPHATSO IMENE MULUNGU ANAKUPATSANI MUDZAIGWIRITSA NTCHITO BWANJI?

Mulungu adzakuthandizani kuti mupirire mavuto anu

19. Kodi Yehova watipatsa mphatso yamtengo wapatali iti, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira kwambiri mphatso imeneyi?

19 Monga tinaphunzirira m’Mutu 5, anthu analengedwa ndi ufulu wotha kusankha zochita. Kodi mumaona kuti imeneyi ndi mphatso yamtengo wapatali? Mulungu analenga nyama zambirimbiri, koma nyama zimenezi zimangochita zinthu mwachibadwa ndipo sizingathe kuganiza kuti ichi ndi chabwino kapena choipa. (Miyambo 30:24) Anthu apanga magalimoto omwe amatha kuyenda koma sangayende okha popanda woyendetsa. Ndiye kodi tikanasangalala ngati Mulungu akanatilenganso choncho? Ayi. Timayamikira kuti tili ndi ufulu wosankha zomwe tikufuna kuchita, anthu omwe tikufuna kuti akhale anzathu, komanso zinthu zina. Timasangalala kuti tili ndi ufulu pa zinthu zina ndipotu Yehova amafuna kuti tizisangalala ndi ufulu umenewu.

20, 21. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikugwiritsa ntchito mwanzeru ufulu wosankha umene tili nawo, ndipo n’chifukwa chiyani?

20 Yehova safuna kuti tizimutumikira mokakamizika. (2 Akorinto 9:7) Mwachitsanzo: Tiyerekeze kuti mwana wina amauza makolo ake kuti amawakonda chifukwa choti makolowo achita kumuuza kuti anene zimenezo, pamene mwana wina amangonena yekha osachita kumuuza. Kodi makolo angasangalale kwambiri ndi mwana uti? N’zodziwikiratu kuti angasangalale ndi mwana amene amangonena yekha osachita kuuzidwayo. Ndiye funso ndi lakuti, Kodi inuyo mudzagwiritsa ntchito bwanji ufulu wosankha zochita umene Yehova anakupatsani? Satana, Adamu, ndiponso Hava anagwiritsa ntchito molakwika ufulu wawo wotha kusankha zinthu. Iwo anakana kutsogoleredwa ndi Yehova Mulungu. Kodi inuyo mudzasankha chiyani?

21 Muli ndi mwayi wogwiritsa ntchito mwanzeru mphatso ya ufulu wosankha imene muli nayo. Mukhoza kukhala m’gulu la anthu ambirimbiri amene ali kumbali ya Yehova. Anthu amenewa amayesetsa kuchita zinthu zimene zimatsimikizira kuti Satana ndi wabodza ndipo walephera kulamulira anthu. Zimene anthuwa amachita zimasangalatsa Yehova. (Miyambo 27:11) Inunso mungathe kukhala m’gulu la anthu amenewa ngati mungasankhe kumachita zimene Mulungu amasangalala nazo. Tikambirana zinthu zimenezi m’mutu wotsatira.