Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 3

Kodi Mulungu Analenga Dziko Lapansili Chifukwa Chiyani?

Kodi Mulungu Analenga Dziko Lapansili Chifukwa Chiyani?
  • N’chifukwa chiyani Mulungu analenga anthu?

  • Kodi Satana anatsutsa bwanji ulamuliro wa Mulungu?

  • Kodi moyo padzikoli udzakhala wotani m’tsogolo?

1. Kodi Mulungu analenga dziko lapansili chifukwa chiyani?

PAMENE Mulungu ankalenga dzikoli anali ndi cholinga chabwino kwambiri. Yehova ankafuna kuti padziko lapansili pazikhala anthu athanzi komanso osangalala. Baibulo limanena kuti “Yehova Mulungu . . . anakonza munda ku Edeni” ndipo “anameretsa . . . mtengo wamtundu uliwonse wooneka bwino ndi wa zipatso zabwino kudya.” Ndiyeno Mulungu atalenga mwamuna ndi mkazi oyambirira, Adamu ndi Hava, anawaika m’munda wokongola kwambiri umenewu kuti azikhalamo ndipo anawauza kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anire.” (Genesis 1:28; 2:8, 9, 15) Choncho Mulungu ankafuna kuti anthu azibereka ana, akulitse munda wa Edeni mpaka ufike dziko lonse lapansi, ndiponso kuti azisamalira nyama.

2. (a) Kodi timadziwa bwanji kuti zimene Mulungu ankafuna polenga dziko lapansi zidzachitikadi? (b) Malinga ndi zimene Baibulo limanena, kodi ndi anthu otani amene adzakhale ndi moyo wosatha?

2 Kodi inuyo mumaona kuti zimene Yehova Mulungu ankafunazi, zoti anthu azikhala m’paradaiso, zidzachitikadi? Mulungu ananena kuti: “Ineyo ndalankhula . . . ndipo ndidzazichitadi.” (Yesaya 46:9-11; 55:11) Izi zikusonyeza kuti chilichonse chimene Mulungu wafuna kuchita sichilephereka. Iye ananena kuti dziko lapansi “sanalilenge popanda cholinga, [koma] analiumba kuti anthu akhalemo.” (Yesaya 45:18) Koma kodi Mulungu ankafuna kuti padzikoli pazikhala anthu otani? Nanga ankafuna kuti anthuwo azikhalapo kwa nthawi yaitali bwanji? Baibulo limayankha kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29; Chivumbulutso 21:3, 4.

3. Kodi padziko lapansi pali mavuto otani, nanga zimenezi zimachititsa anthu kukhala ndi mafunso ati?

3 N’zachidziwikire kuti zimenezi sizinachitikebe. Panopa anthu amamwalira chifukwa cha matenda komanso amamenyana n’kuphana. Chinachake chiyenera kuti chinalakwika chifukwa zimene zikuchitika masiku ano si zimene Mulungu ankafuna. Kodi n’chiyani chinachitika? N’chifukwa chiyani zimene Mulungu ankafuna sizinachitikebe? Palibe buku la mbiri yakale limene lingatiuze chimene chinachitika chifukwa nkhaniyi inayambira kumwamba.

ZIMENE MNGELO WINA ANACHITA KUTI AKHALE MDANI WA MULUNGU

4, 5. (a) Kodi ndani ankalankhula ndi Hava pogwiritsa ntchito njoka? (b) Kodi n’chiyani chingachititse munthu wakhalidwe labwino kusintha n’kukhala wakuba?

4 Buku loyamba la m’Baibulo limatiuza za winawake amene anatsutsa Mulungu m’munda wa Edeni. Iye amatchedwa “njoka” koma sikuti anali njoka yeniyeni. Buku lomalizira la m’Baibulo limamutchula kuti “Mdyerekezi ndi Satana, amene akusocheretsa dziko lonse lapansi.” Amatchedwanso “njoka yakale.” (Genesis 3:1; Chivumbulutso 12:9) Mngelo ameneyu, kapena kuti mzimu wamphamvu wosaoneka, anagwiritsa ntchito njoka polankhula ndi Hava. Zimene anachitazi n’zofanana ndi zimene munthu waluso amachita kuti mawu ake azimveka ngati chikulankhula ndi chidole. Sitikukayikira kuti mngelo ameneyu analipo pamene Mulungu ankalenga dziko lapansili kuti anthu akhalemo.—Yobu 38:4, 7.

5 Koma kodi ndani analenga “Mdyerekezi,” kapena kuti “Satana” popeza Yehova analenga zinthu zabwino zokhazokha? Mwachidule tingati mwana mmodzi mwa ana auzimu amphamvu a Mulungu anadzipanga yekha kukhala Mdyerekezi. Koma kodi zimenezi zinatheka bwanji? Pajatu munthu amene poyamba anali wakhalidwe labwino komanso wokhulupirika amatha kusintha n’kukhala wakuba. Kodi n’chiyani chimam’pangitsa kuti asinthe? Munthuyo angayambe kulakalaka zinthu zinazake zolakwika. Ngati atamangoganizirabe zinthuzo, maganizo olakwikawo akhoza kukula. Ndiyeno atapeza mpata akhoza kuchita zinthu zimene wakhala akuganizazo.—Werengani Yakobo 1:13-15.

6. Kodi mngelo wa Mulungu anakhala bwanji Satana Mdyerekezi?

6 Izi ndi zimene zinachitika ndi Satana Mdyerekezi. Iye anamva Mulungu akuuza Adamu ndi Hava kuti abereke ana ndi kudzaza dziko lapansi. (Genesis 1:27, 28) Satana ayenera kuti anayamba kuganiza kuti, ‘Zingakhale bwinotu anthu onsewo atati azilambira ineyo osati Mulungu.’ Apa maganizo olakwika anayamba kukula mumtima mwake. Patapita nthawi anamuuza Hava zinthu zabodza zokhudza Mulungu n’cholinga chakuti zimene ankalakalakazo zitheke. (Werengani Genesis 3:1-5.) Zimene anachitazi zinam’pangitsa kuti akhale “Mdyerekezi,” kutanthauza “Woneneza.” Ndiponso anakhala “Satana,” kutanthauza “Wotsutsa.”

7. (a) N’chifukwa chiyani Adamu ndi Hava anafa? (b) N’chifukwa chiyani ana onse a Adamu amakalamba ndi kufa?

7 Zinthu zabodza zimene Satana Mdyerekezi ananena zinachititsa kuti Adamu ndi Hava asamvere Mulungu. (Genesis 2:17; 3:6) Kusamvera kwa Adamu ndi Hava kunachititsa kuti m’kupita kwa nthawi amwalire chifukwa ndi zimene Mulungu ananeneratu kuti zidzachitika ngati sadzamvera. (Genesis 3:17-19) Popeza Adamu atachimwa sanakhalenso wangwiro, ana ake onse anatengera uchimo wakewo. (Werengani Aroma 5:12.) Zimene zinachitikazi tingaziyerekeze ndi zimene zimachitika poumba njerwa. Ngati chikombole chili chopindika, ndiye kuti njerwa iliyonse imakhala yopindika. N’chimodzimodzinso ndi munthu aliyense. Tonse tinatengera uchimo kuchokera kwa Adamu. N’chifukwa chake anthu onse amakalamba ndi kufa.—Aroma 3:23.

8, 9. (a) Kodi Satana ankaona kuti Yehova ndi wolamulira wotani? (b) N’chifukwa chiyani Mulungu sanaphe oukirawo nthawi yomweyo?

8 Pamene Satana anachititsa Adamu ndi Hava kuti achimwire Mulungu, anayambitsa kagulu koukira ulamuliro wa Mulungu. Iye ankafuna kuti anthu aziona ngati Yehova salamulira bwino. Iye ankaona kuti Mulungu si wolamulira wabwino, amauza anthu zinthu zabodza komanso amawamana zabwino. Ankaonanso kuti anthu sakufunikira kulamuliridwa ndi Mulungu chifukwa paokha akhoza kudziwa kuti ichi ndi chabwino kapena choipa. Satana ankaonanso kuti anthu zingamawayendere bwino ngati atamalamuliridwa ndi iyeyo. Kodi Mulungu akanachita chiyani ndi kunyoza kotereku? Ena amaona kuti chidule chinali kungowapha onse oukirawo. Koma kodi kuchita zimenezi kukanasonyeza kuti Satana ankanena zabodza? Kodi zikanapangitsa anthu kutsimikizira kuti Mulungu ndi wolamulira wabwino?

9 Popeza Yehova amaweruza mwachilungamo kwambiri, sanafune kuwononga anthu oukirawo nthawi yomweyo. Anaona kuti ndi bwino kudikira kaye kuti pakhale mpata wokwanira wotsimikizira kuti zimene Satana ananena zinali zabodza. Choncho Mulungu anapereka mwayi kwa anthu woti adzilamulire okha kwa kanthawi motsogoleredwa ndi Satana. Koma kodi Yehova anachita zimenezi chifukwa chiyani, nanga n’chifukwa chiyani walola kuti padutse nthawi yaitali chonchi asanathetse nkhaniyi? Tidzakambirana mfundo zimenezi m’Mutu 11. Koma panopo tingachite bwino kuganizira mfundo yakuti: Kodi Adamu ndi Hava anachita bwino kukhulupirira zonena za Satana yemwe anali asanawachitirepo chilichonse chabwino? Kodi zinali zomveka kukhulupirira kuti Yehova, yemwe anali atawapatsa chilichonse chomwe anali nacho, anali wankhanza komanso wabodza? Kodi mukanakhala inuyo mukanatani?

10. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tili kumbali ya Yehova pamene akuyankha zimene Satana ananena?

10 Tikufunikira kuganizira mafunso amenewa mofatsa chifukwa nafenso tiyenera kusankha kukhulupirira Mulungu kapena Satana. Nanunso muli ndi mwayi wokhala kumbali ya Yehova pamene akuyankha zimene Satana ananena. Zochita zanu zingasonyeze kuti mumasangalala kulamuliridwa ndi Yehova ndipo zimenezi zingasonyeze kuti Satana ndi wabodza. (Salimo 73:28; werengani Miyambo 27:11.) N’zomvetsa chisoni kuti pa anthu ambirimbiri omwe ali m’dzikoli, ndi anthu ochepa okha amene amasankha kukhala kumbali ya Yehova. Zimenezi zikusonyeza kuti Satana ndi amene akulamulira dzikoli. Koma kodi zimenezi ndi zomwe Baibulo limaphunzitsa?

KODI AKULAMULIRA DZIKOLI NDI NDANI?

Kodi Satana akananena bwanji kuti am’patsa Yesu maufumu adziko lapansi zikanakhala kuti maufumuwo si ake?

11, 12. (a) Kodi kuyesedwa kwa Yesu kumasonyeza bwanji kuti Satana ndi amene akulamulira dzikoli? (b) Kodi pali umboni winanso uti wosonyeza kuti akulamulira dzikoli ndi Satana?

11 Yesu ankadziwa kuti Satana ndi amene akulamulira dzikoli. Pa nthawi ina Satana anaonetsa Yesu “maufumu onse a padziko ndi ulemerero wawo.” Ndiyeno anamulonjeza kuti: “Ndikupatsani zinthu zonsezi ngati mutangogwada pansi n’kundiweramira kamodzi kokha.” (Mateyu 4:8, 9; Luka 4:5, 6) Kodi pamenepa tinganene kuti Yesu anayesedwa zikanakhala kuti si Satana amene akulamulira maufumu onsewa? Yesu sanatsutse zoti maboma a dziko lapansili ndi a Satana. Iye akanatha kutsutsa zikanakhala kuti Satana mabomawa si ake.

12 N’zoona kuti Yehova ndi Mulungu Wamphamvuyonse ndipo ndi amene analenga chilengedwe chonse chochititsa chidwichi. (Chivumbulutso 4:11) Koma Yesu anafotokoza momveka bwino kuti Satana ndi “wolamulira wa dzikoli.” (Yohane 12:31; 14:30; 16:11) Baibulo limanenanso kuti Satana Mdyerekezi ndi “mulungu wa nthawi ino.” (2 Akorinto 4:3, 4) Ponena za wotsutsa ameneyu, kapena kuti Satana, mtumwi Yohane analemba kuti: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.”—1 Yohane 5:19.

MMENE DZIKO LA SATANA LIDZACHOTSEDWERE

13. N’chifukwa chiyani tikufunikira dziko latsopano?

13 Dzikoli likuwonjezeka kuipa tsiku ndi tsiku. Ladzaza ndi nkhondo, atsogoleri andale osakhulupirika, atsogoleri achipembedzo achinyengo ndi zigawenga zoopsa. Panopa dzikoli lafika poti silingakonzedwenso. Baibulo limatiuza kuti posachedwapa Mulungu achotsa dziko la Satanali pa nkhondo ya Aramagedo. Dziko loipali lidzalowedwa m’malo ndi dziko latsopano lolungama.—Chivumbulutso 16:14-16.

14. Kodi Mulungu anasankha ndani kuti akhale Wolamulira wa Ufumu wake, nanga Baibulo linaneneratu chiyani zokhudza wolamulira ameneyu?

14 Yehova Mulungu anasankha Yesu Khristu kuti akhale Wolamulira wa Ufumu wakumwamba kapena kuti boma lake. Zimenezi ndi zimene Baibulo linaneneratu kalekale kuti: “Kwa ife kwabadwa mwana. Ife tapatsidwa mwana wamwamuna, ndipo paphewa pake padzakhala ulamuliro. Iye adzapatsidwa dzina lakuti . . . Kalonga Wamtendere. Ulamuliro wake wangati wa kalonga udzafika kutali ndipo mtendere sudzatha.” (Yesaya 9:6, 7) Ponena za boma limeneli, Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:10) Monga mmene tionere m’mitu yakutsogoloku, posachedwapa Ufumu wa Mulungu udzachotsa ndi kulowa m’malo maboma onse a dzikoli. (Werengani Danieli 2:44.) Kenako Ufumuwu udzabweretsa paradaiso padziko lapansi.

DZIKO LATSOPANO LAYANDIKIRA

15. Kodi “dziko latsopano” n’chiyani?

15 Baibulo limatitsimikizira kuti: “Pali kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekezera mogwirizana ndi lonjezo lake, ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.” (2 Petulo 3:13; Yesaya 65:17) Nthawi zina Baibulo likamanena kuti “dziko,” limatanthauza anthu amene akukhala padzikoli. (Genesis 11:1) Choncho “dziko latsopano” lolungama likutanthauza anthu amene Mulungu amasangalala nawo.

16. Kodi ndi mphatso yotani imene Mulungu adzapereke kwa anthu, nanga tiyenera kuchita chiyani kuti tidzalandire mphatso imeneyi?

16 Yesu analonjeza kuti m’dziko latsopano limene likubweralo, anthu amene amachita zimene Mulungu amasangalala nazo adzalandira mphatso ya “moyo wosatha.” (Maliko 10:30) Tatsegulani Baibulo lanu pa Yohane 3:16 ndi pa Yohane 17:3, muone zimene Yesu ananena kuti tiyenera kuchita kuti tidzapeze moyo wosatha. Tsopano tiyeni tione madalitso otchulidwa m’Baibulo omwe anthu amene Mulungu adzawapatse moyo wosatha adzasangalale nawo m’paradaiso akubwerayo.

17, 18. N’chifukwa chiyani sitikayikira zoti padziko lonse padzakhala mtendere ndi chitetezo?

17 Nkhondo, kusamvera malamulo, chiwawa ndi zinthu zonse zoipa zidzatha. “Woipa sadzakhalakonso. . . . Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi.” (Salimo 37:10, 11) Padzikoli padzakhala mtendere chifukwa Mulungu ‘adzaletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.’ (Salimo 46:9; Yesaya 2:4) Ndiyeno “wolungama adzaphuka, ndipo padzakhala mtendere wochuluka kwa nthawi yonse pamene mwezi udzakhalepo.” Zimenezi zikutanthauza kuti mtenderewo udzakhalapo mpaka kalekale.—Salimo 72:7.

18 Anthu olambira Yehova adzakhala motetezeka. Kale Aisiraeli akamvera Mulungu ankakhala mwamtendere. (Levitiko 25:18, 19) Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kukhala ndi mtendere ngati umenewo m’Paradaiso.—Werengani Yesaya 32:18; Mika 4:4.

19. Kodi tikudziwa bwanji kuti m’dziko latsopano mudzakhala chakudya chochuluka?

19 Sikudzakhala njala. Wamasalimo anaimba kuti: “Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.” (Salimo 72:16) Yehova Mulungu adzadalitsa anthu ake olungama ndipo “dziko lapansi lidzapereka zipatso zake.”—Salimo 67:6.

20. Kodi n’chiyani chingatithandize kutsimikiza kuti dziko lonse lidzakhala paradaiso?

20 Dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso. Malo amene anawonongedwa ndi anthu oipa adzakonzedwa ndipo mudzamangidwa nyumba zabwino zatsopano komanso mudzakhala minda yokongola. (Werengani Yesaya 65:21-24; Chivumbulutso 11:18) M’kupita kwa nthawi, malo okhala anthu adzawonjezeka mpaka dziko lonse lidzakhala lokongola komanso mudzakhala zinthu zambiri ngati mmene unalili munda wa Edeni. Mulungu sadzalephera ‘kutambasula dzanja lake ndi kukhutiritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.’—Salimo 145:16.

21. N’chiyani chikusonyeza kuti anthu adzakhala mwamtendere ndi zinyama?

21 Anthu azidzakhala mwamtendere ndi zinyama. Nyama zakutchire ndi zoweta zidzadyera pamodzi. Ngakhale mwana wamng’ono sadzaopa nyama zimene panopa ndi zoopsa.—Werengani Yesaya 11:6-9; 65:25.

22. Kodi matenda adzapitirirabe mpaka kalekale?

22 Matenda adzatha. Yesu monga Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu, adzachiritsa anthu ambiri kuposa amene anawachiritsa ali padziko lapansi pano. (Mateyu 9:35; Maliko 1:40-42; Yohane 5:5-9) Pa nthawi imeneyo “palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”—Yesaya 33:24; 35:5, 6.

23. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kuuka kwa anthu idzakhala nkhani yosangalatsa kwambiri?

23 Achibale komanso anzathu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo. Anthu onse amene anamwalira omwe Mulungu adzasankhe kuwakumbukira, adzaukitsidwa. Ndipotu Baibulo limanena kuti “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.”—Machitidwe 24:15; werengani Yohane 5:28, 29.

24. Kodi mumamva bwanji mukaganiza zodzakhala m’Paradaiso padziko lapansi?

24 Zimene takambiranazi zikusonyeza kuti anthu amene amasankha kuphunzira za Mlengi wathu wamkulu, Yehova Mulungu, ndiponso kumutumikira adzasangalala ndi madalitso ambiri. Yesu ankanena za dziko lapansi la Paradaiso pamene ankauza chigawenga chimene chinapachikidwa pambali pake kuti: “Iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (Luka 23:43) Kuphunzira za Yesu Khristu n’kofunika kwambiri chifukwa madalitso onsewa adzatheka kudzera mwa iyeyo.