Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 10

Mmene Zochita za Angelo Komanso Ziwanda Zimakhudzira Moyo Wathu

Mmene Zochita za Angelo Komanso Ziwanda Zimakhudzira Moyo Wathu
  • Kodi angelo amathandizadi anthu?

  • Kodi ziwanda zimachititsa anthu kupanga zinthu zotani?

  • Kodi tiyenera kuchita mantha ndi ziwanda?

1. N’chifukwa chiyani tiyenera kuphunzira za angelo?

KUTI timudziwe munthu winawake bwinobwino, nthawi zambiri zimakhala bwino kudziwanso banja limene akuchokera. Mofanana ndi zimenezi, kuti timudziwe bwino Yehova Mulungu, tiyeneranso kuwadziwa bwino angelo omwe ali ngati banja lake lakumwamba. Baibulo limanena kuti angelo ndi ‘ana a Mulungu.’ (Yobu 38:7) Koma kodi angelo amagwira ntchito zotani pokwaniritsa cholinga cha Mulungu? Kodi achitapo zotani m’mbuyomu? Kodi zochita za angelo zingakhudze moyo wanu? Ngati ndi choncho, zingakukhudzeni bwanji?

2. Kodi angelo analengedwa ndi ndani, nanga alipo angati?

2 Baibulo limatchula za angelo kambirimbiri. Tiyeni tikambirane malemba ena omwe amatchula za angelo ndipo angatithandize kuti tiwadziwe. Koma kodi angelo analengedwa ndi ndani? Lemba la Akolose 1:16 limati: “Kudzera mwa iye [Yesu Khristu] zinthu zina zonse zinalengedwa, zakumwamba ndi zapadziko lapansi.” Choncho, mngelo aliyense analengedwa ndi Yehova Mulungu pogwiritsa ntchito Mwana wake woyamba, Yesu Khristu. Koma kodi angelo alipo angati? Baibulo limasonyeza kuti Mulungu analenga angelo mamiliyoni ambiri ndipo onse ndi amphamvu kwambiri.—Salimo 103:20. *

3. Kodi lemba la Yobu 38:4-7 limatiuza chiyani za angelo?

3 Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu, limatiuza kuti Mulungu atalenga dziko lapansi, “ana onse a Mulungu anayamba kufuula ndi chisangalalo.” (Yobu 38:4-7) Zimenezi zikusonyeza kuti angelo analengedwa kalekale anthu asanalengedwe, ngakhalenso dziko lapansili n’kuti lisanalengedwe. Mawu akuti angelo ‘anafuula pamodzi mokondwera,’ omwe akupezeka m’mavesi amenewa akusonyeza kuti angelo akhoza kukhumudwa kapena kusangalala ndi zinthu zimene zachitika. Onaninso kuti “ana onse a Mulungu” anasangalalira limodzi. Pa nthawi imeneyo, angelo onse ankatumikira Yehova Mulungu mogwirizana, monga ana a banja limodzi.

ANGELO AMATITHANDIZA KOMANSO KUTITETEZA

4. Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti angelo okhulupirika amachita chidwi ndi zochita za anthu?

4 Kungoyambira pamene anaona Mulungu akulenga anthu oyambirira, angelo okhulupirika akhala akuchita chidwi ndi zochita za anthu ndiponso mmene Mulungu akukwaniritsira cholinga chake. (Miyambo 8:30, 31; 1 Petulo 1:11, 12) Koma m’kupita kwa nthawi, angelo anaona kuti anthu ambiri ayamba kusiya kutumikira Mlengi wawo wachikondi. Sitikukayikira kuti zimenezi zinakhumudwitsa angelo okhulupirikawa. Koma ngakhale munthu mmodzi yekha akayambiranso kutumikira Yehova, “kumakhala chisangalalo chochuluka kwa angelo.” (Luka 15:10) Popeza angelo amadera nkhawa kwambiri anthu amene amatumikira Mulungu, n’zosadabwitsa kuti nthawi zambiri Yehova ankatumiza angelo kuti akalimbikitse kapena kutetezera atumiki ake okhulupirika a padziko lapansi. (Werengani Aheberi 1:7, 14.) Tiyeni tione zitsanzo zingapo.

“Mulungu wanga watumiza mngelo wake kudzatseka pakamwa pa mikango”—Danieli 6:22

5. Kodi m’Baibulo muli zitsanzo ziti za anthu amene anathandizidwa ndi angelo?

5 Angelo awiri anapulumutsa Loti ndi ana ake aakazi awiri pa nthawi imene mizinda ya Sodomu ndi Gomora inkawonongedwa. (Genesis 19:15, 16) Patapita zaka zambiri, mneneri Danieli anaponyedwa m’dzenje la mikango koma mikangoyo sinamudye. Iye ananena kuti: “Mulungu wanga watumiza mngelo wake kudzatseka pakamwa pa mikango.” (Danieli 6:22) M’nthawi ya atumwi, mngelo anatulutsa mtumwi Petulo m’ndende. (Machitidwe 12:6-11) Angelo analimbikitsanso Yesu pa nthawi imene ankayamba utumiki wake wa padziko lapansi. (Maliko 1:13) Ndipo Yesu atatsala pang’ono kuphedwa, mngelo anaonekera kwa iye ndi “kumulimbikitsa.” (Luka 22:43) Zimenezi ziyenera kuti zinamulimbikitsa kwambiri Yesu pa nthawi yofunika kwambiri imeneyi.

6. (a) Kodi angelo amateteza bwanji atumiki a Mulungu masiku ano? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

6 Masiku ano angelo saonekera kwa anthu a Mulungu ngati mmene ankachitira kale. Ngakhale zili choncho, angelo amatetezabe anthu a Mulungu, makamaka ku zinthu zimene zingasokoneze moyo wawo wauzimu. Baibulo limanena kuti: “Mngelo wa Yehova amamanga msasa mozungulira onse oopa Mulungu, ndipo amawapulumutsa.” (Salimo 34:7) Mawu amenewa ndi olimbikitsa kwambiri chifukwa pali mizimu yoipa yomwe ikufuna kutiwononga. Kodi mizimu imeneyi ndi iti? Nanga inachokera kuti? Ndipo kodi imafuna kutivulaza m’njira zotani? Kuti tipeze mayankho a mafunso amenewa, tiyeni tikambirane mwachidule zimene zinachitika pachiyambi penipeni pa mbiri ya anthu.

ANGELO OIPA OMWE NDI ADANI ATHU

7. Kodi nthawi ina Satana anakwanitsa kusocheretsa anthu ochuluka bwanji?

7 Monga tinaphunzirira m’Mutu 3, mngelo wina anakhala ndi mtima wofuna kulamulira anzake ndipo anayamba kuchita zinthu zotsutsana ndi Mulungu. Pambuyo pake mngelo ameneyu anayamba kudziwika ndi dzina lakuti Satana Mdyerekezi. (Chivumbulutso 12:9) Patadutsa zaka pafupifupi 1,600 kuchokera pamene ananamiza Hava, Satana anakwanitsa kusocheretsa anthu pafupifupi onse ndipo anasiya kutumikira Mulungu. Anthu okhulupirika amene sanasocheretsedwe anali Abele, Inoki ndi Nowa.—Aheberi 11:4, 5, 7.

8. (a) Kodi chinachitika n’chiyani kuti angelo ena akhale ziwanda? (b) Kodi ziwanda zinachita chiyani kuti zipulumuke pa nthawi ya Chigumula?

8 M’nthawi ya Nowa angelo ena anasiya kutumikira Yehova. Anachoka kumwamba n’kubwera padziko lapansi pano ndipo anasintha matupi awo kuti azioneka ngati anthu. Kodi anachita zimenezi chifukwa chiyani? Lemba la Genesis 6:2 limati: “Ana a Mulungu woona anayamba kuona kuti ana aakazi a anthu anali okongola. Chotero, anayamba kudzitengera okha akazi alionse amene anawasankha.” Koma Yehova Mulungu sanalole kuti angelo amenewa apitirize kusokoneza mtundu wa anthu. Choncho anabweretsa Chigumula padziko lonse lapansi chomwe chinaseseratu anthu onse oipa. Amene anatsala ndi anthu okhulupirika okha amene ankatumikira Mulungu. (Genesis 7:17, 23) Zimenezi zinachititsa kuti angelo oipa aja, kapena kuti ziwanda, asinthenso kukhala mizimu n’kubwerera kumwamba. Zochita zawozi zinachititsa kuti akhale kumbali ya Mdyerekezi, ndipo iye anakhala “wolamulira ziwanda.”—Mateyu 9:34.

9. (a) Kodi n’chiyani chinachitikira ziwanda zitabwerera kumwamba? (b) Kodi tikambirana chiyani?

9 Mofanana ndi Satana, yemwe ndi wolamulira wawo, angelo osamverawo atabwerera kumwamba sanaloledwenso kukhala m’banja la Mulungu. (2 Petulo 2:4) Ngakhale kuti panopa sangathenso kusintha matupi awo kuti azioneka ngati anthu, adakali ndi mphamvu ndipo akusocheretsabe anthu. Satana mothandizidwa ndi angelo oipa amenewa “akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Chivumbulutso 12:9; 1 Yohane 5:19) Kodi amachita bwanji zimenezi? Ziwanda zili ndi njira zimene zimagwiritsa ntchito pofuna kusocheretsa anthu. (Werengani 2 Akorinto 2:11.) Tiyeni tikambirane zina mwa njira zimenezi.

MMENE ZIWANDA ZIMASOCHERETSERA ANTHU

10. Kodi kukhulupirira mizimu n’kutani?

10 Kuti zisocheretse anthu, ziwanda zimachititsa anthuwo kukhulupirira mizimu. Munthu amene amakhulupirira mizimu amakhala akugwirizana ndi ziwanda, kaya walankhula nazo yekha ziwandazo kapena wagwiritsa ntchito munthu wina. Baibulo limaletsa kukhulupirira mizimu ndipo limatichenjeza kuti tiyenera kupewa chilichonse chogwirizana ndi kukhulupirira mizimu. (Agalatiya 5:19-21) Ziwanda zimagwiritsa ntchito kukhulupirira mizimu ngati nyambo yawo yokolera anthu. Msodzi amagwiritsa ntchito nyambo zosiyanasiyana zogwirizana ndi mitundu ya nsomba zimene akufuna kugwira. Mofanana ndi zimenezi, mizimu yoipa nayonso imagwiritsa ntchito mitundu yosiyanasiyana ya kukhulupirira mizimu kuti izilamulira anthu.

11. Tchulani mitundu ina ya kuwombeza komanso chifukwa chake tiyenera kuipewa.

11 Nyambo imodzi imene ziwanda zimagwiritsa ntchito ndi kuwombeza kapena kufuna kudziwa zinthu zam’tsogolo. Mitundu ina ya kuwombeza ndi kukhulupirira nyenyezi, kuona pa galasi la matsenga, kutanthauzira mizere ya m’manja, kutanthauzira kulira kwa mbalame, kapena kumasulira maloto. Ngakhale kuti anthu ambiri amaganiza kuti kuwombeza kulibe vuto, Baibulo limasonyeza kuti anthu amene amalosera zam’tsogolo amachita zimenezi mothandizidwa ndi ziwanda. Mwachitsanzo, pa Machitidwe 16:16-18 amanena za “chiwanda cholosera zam’tsogolo” chimene chinkathandiza mtsikana wina kuti azilosera zinthu. Koma chiwandacho chitachoka, sankathanso kulosera zam’tsogolo.

Ziwanda zimagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana kuti zisocheretse anthu

12. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kulankhula ndi akufa n’koopsa?

12 Njira ina imene ziwanda zimagwiritsa ntchito pofuna kusocheretsa anthu ndi kuyerekezera munthu winawake amene anamwalira. Anthu amene ali ndi chisoni chifukwa cha imfa ya m’bale wawo kapena mnzawo, sachedwa kupusitsika ndi mfundo zabodza zokhudza anthu amene anamwalira. Munthu wamatsenga akhoza kuwauza uthenga winawake n’kumati wachokera kwa womwalirayo kapena akhoza kuyerekezera mawu a womwalirayo. Chifukwa cha zimenezi, anthu ambiri amakhulupirira kuti anthu akufa ali ndi moyo kwinakwake ndipo kuyesetsa kulankhula nawo kungachepetse chisoni chimene ali nacho. Koma kulankhula ndi akufa n’kosatheka ndipo kuyesa kuchita zimenezi n’kowopsa. Tikutero chifukwa ziwanda zili ndi mphamvu yotha kuyerekezera mawu a munthu amene anamwalira komanso zikhoza kumuuza munthu wamatsenga mfundo zinazake zokhudza munthu amene anamwalira. (1 Samueli 28:3-19) Komanso monga mmene tinaphunzirira m’Mutu 6, munthu akafa sakhalanso ndi moyo kwinakwake. (Salimo 115:17) Zimenezi zikusonyeza kuti “aliyense wofunsira kwa akufa” ndiye kuti wapusitsidwa ndi ziwanda ndipo akuchita zinthu zosemphana ndi zimene Mulungu amafuna. (Werengani Deuteronomo 18:10, 11; Yesaya 8:19) Choncho muyenera kupewa kuchita zimenezi chifukwa ndi nyambo imene ziwanda zimagwiritsa ntchito.

13. Kodi anthu ambiri amene poyamba ankaopa ziwanda panopa anachita chiyani?

13 Kuwonjezera pa kusocheretsa anthu, mizimu yoipa imaopsezanso anthu. Panopa Satana ndi ziwanda zake akuchita zinthu molusa kwambiri chifukwa akudziwa kuti angotsala ndi “kanthawi kochepa” kuti awonongedwe. (Chivumbulutso 12:12, 17) Komabe, anthu ambiri amene poyamba ankawopa ziwanda, anasiya kuziwopa ndipo akukhala momasuka. Kodi zimenezi zinatheka bwanji? Kodi munthu amene amavutitsidwa ndi mizimu yoipa ayenera kuchita chiyani kuti amasuke?

ZIMENE TINGACHITE KUTI MIZIMU YOIPA ISAMATILAMULIRE

14. Mofanana ndi Akhristu a ku Efeso, kodi tingatani kuti tisiye kugwirizana ndi mizimu yoipa?

14 Baibulo limatiuza mmene tingapewere mizimu yoipa komanso zimene tingachite kuti timasuke ngati tinayamba kale kuikhulupirira. Taganizirani chitsanzo cha Akhristu a m’nthawi ya atumwi omwe ankakhala mumzinda wa Efeso. Ena mwa anthu amenewa ankakhulupirira mizimu asanakhale Akhristu. Kodi anachita chiyani pa nthawi imene ankafuna kusiya kuchita zamizimu? Baibulo limati: “Ambiri ndithu amene anali kuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku awo pamodzi ndi kuwatentha pamaso pa onse.” (Machitidwe 19:19) Zimene Akhristu amenewa anachita powotcha mabuku a zamatsenga, ndi chitsanzo chabwino kwa anthu onse masiku ano amene akufuna kuti asamavutitsidwe ndi mizimu yoipa. Anthu amene akufuna kutumikira Yehova ayenera kutaya chinthu chilichonse chokhudzana ndi mizimu. Zimenezi zikuphatikizapo mabuku, magazini, mafilimu, zithunzi, ndiponso nyimbo zimene zimalimbikitsa anthu kukhulupirira mizimu kapena kuganiza kuti kukhulupirira mizimu n’kwabwino. Zinthu zina ndi monga zithumwa kapena zinthu zina zimene anthu amavala pofuna kudziteteza.—1 Akorinto 10:21.

15. Kodi n’chiyani chingatithandize kulimbana ndi mizimu yoipa?

15 Patapita zaka zingapo kuchokera pamene Akhristu a ku Efeso anawotcha mabuku awo a zamatsenga, mtumwi Paulo anawalembera kuti: “Sitikulimbana ndi anthu . . . koma . . . ndi makamu a mizimu yoipa.” (Aefeso 6:12) Zimenezi zikusonyeza kuti ziwanda zinali zikuyesetsabe kuti ziwagonjetse. Ndiye kodi Akhristu amenewa ankafunika kuchitanso chiyani? Paulo anati: “Koposa zonse, nyamulani chishango chachikulu chachikhulupiriro, chimene mudzathe kuzimitsira mivi yonse yoyaka moto ya woipayo [Satana].” (Aefeso 6:16) Tikakhala ndi chikhulupiriro cholimba m’pamene tingathe kulimbana ndi mizimu yoipa.—Mateyu 17:20.

16. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba?

16 Koma kodi tingalimbitse bwanji chikhulupiriro chathu? Tiyenera kuphunzira Baibulo. Khoma limakhala lolimba ngati maziko ake alinso olimba. Mofanana ndi khoma, nachonso chikhulupiriro chimakhala cholimba ngati maziko ake ali olimba, omwe ndi kudziwa molondola Mawu a Mulungu, Baibulo. Tikamawerenga ndi kuphunzira Baibulo tsiku lililonse, chikhulupiriro chathu chidzalimba. Mofanana ndi khoma lolimba, chikhulupiriro choterocho chidzatiteteza kuti mizimu yoipa isamativutitse.—1 Yohane 5:5.

17. Kodi ndi chinthu china chiti chofunika chomwe chingatithandize polimbana ndi mizimu yoipa?

17 Kodi Akhristu a ku Efeso anafunika kuchitanso chiyani? Popeza Akhristuwa ankakhala mumzinda womwe anthu ake ambiri ankachita zamizimu, ankafunika kutetezedwa kwambiri. N’chifukwa chake Paulo anawauza kuti: “Muzipemphera pa chochitika chilichonse mu mzimu, mwa mtundu uliwonse wa pemphero ndi pembedzero.” (Aefeso 6:18) Popeza nafenso tikukhala m’dziko limene anthu ake ambiri amachita zamizimu, kupemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima kuti atithandize n’kofunika kwambiri kuti tikwanitse kulimbana ndi mizimu yoipa. Komabe, tikamapemphera tiyenera kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu, lakuti Yehova. (Werengani Miyambo 18:10.) Choncho tiyenera kupitiriza kupemphera kwa Mulungu kuti ‘atilanditse kwa woipayo,’ yemwe ndi Satana Mdyerekezi. (Mateyu 6:13) Yehova amayankha mapemphero oona mtima ngati amenewa.—Salimo 145:19.

18, 19. (a) N’chifukwa chiyani sitikayikira zoti tingapambane pa nkhondo yolimbana ndi mizimu yoipa? (b) Kodi m’nkhani yotsatira tidzakambirana yankho la funso liti?

18 Mizimu yoipa ndi yoopsa, komabe sitiyenera kumachita nayo mantha kwambiri ngati timayesetsa kutsutsa Mdyerekezi ndiponso kuyandikira kwa Yehova. Tingamuyandikire Yehova tikamachita chifuniro chake. (Werengani Yakobo 4:7, 8.) Mphamvu za mizimu yoipa zili ndi malire, n’chifukwa chake mizimuyi inalangidwa m’nthawi ya Nowa ndipo idzalangidwanso pa tsiku lachiweruzo. (Yuda 6) Kumbukiraninso kuti timatetezedwa ndi angelo a Yehova omwe ndi amphamvu kwambiri. (2 Mafumu 6:15-17) Angelo amenewa amafuna kuti tisagonje pa nkhondo yathu yolimbana ndi mizimu yoipa. Zili ngati kuti amaonerera n’kumatichemerera tikamayesetsa kulimbana ndi mizimuyi. Choncho tiyenera kuyesetsa kukhala pa ubwenzi ndi Yehova ndiponso kugwirizana kwambiri ndi angelo okhulupirika a Mulungu. Tiyeneranso kupewa chinthu chilichonse chokhudzana ndi kukhulupirira mizimu ndiponso tiyenera kutsatira Mawu a Mulungu nthawi zonse. (1 Petulo 5:6, 7; 2 Petulo 2:9) Tikamachita zimenezi, tidzapambana pa nkhondo yathu yolimbana ndi mizimu yoipa.

19 Koma n’chifukwa chiyani Mulungu walola kuti anthu azivutika chifukwa cha mizimu yoipa ndiponso zinthu zina zoipa? Funso limeneli liyankhidwa m’mutu wotsatira.

^ ndime 2 Lemba la Chivumbulutso 5:11 limanena za angelo okhulupirika, kuti: “Chiwerengero chawo chinali miyanda kuchulukitsa ndi miyanda,” kapena kuti “10,000 kuchulukitsa ndi ma 10,000.” Choncho Baibulo limasonyeza kuti angelo alipo mamiliyoni ambirimbiri.