Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 1

Kodi Zoona Zenizeni za Mulungu N’zotani?

Kodi Zoona Zenizeni za Mulungu N’zotani?
  • Kodi Mulungu amakuganiziranidi?

  • Kodi Mulungu ali ndi dzina? Nanga ali ndi makhalidwe otani?

  • Kodi n’zotheka kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu?

1, 2. N’chifukwa chiyani nthawi zambiri ndi bwino kufunsa mafunso?

KODI munayamba mwadabwapo ndi mmene ana amafunsira mafunso? Ana ambiri amakonda kufunsa mafunso akangoyamba kulankhula. Amachita chidwi kwambiri ndi zinthu ndipo nthawi zina amakuyang’anitsitsani n’kukufunsani mafunso ngati akuti: N’chifukwa chiyani kumwamba kumaoneka kwa buluu? Kodi nyenyezi zilipo zingati? Kodi mbalame zimatha bwanji kuuluka? Mukhoza kuyesetsa kuti muyankhe mafunsowa koma nthawi zambiri zimakhala zovuta kuti mumuyankhe mogwira mtima. Ngakhale mutayesetsa kumuyankha mogwira mtima, mwina angakufunseninso kuti: Chifukwa chiyani?

2 Si ana okha amene amafunsa mafunso. Ngakhale akuluakulu amafunsanso mafunso. Timafunsa kuti tisasochere, kuti tidziwe zinthu zoopsa zimene tiyenera kuzipewa kapena kuti tidziwe zinthu zomwe timachita nazo chidwi. Koma zikuoneka kuti anthu ambiri akamakula amasiya kufunsa mafunso, makamaka mafunso ofunika kwambiri ndipo samafufuza n’komwe kuti apeze mayankho.

3. N’chifukwa chiyani anthu ambiri safufuza mayankho a mafunso ofunika kwambiri?

3 Taonaninso funso lomwe lili pachikuto cha bukuli, mafunso amene ali kumayambiriro kwa bukuli kapena amene ali kumayambiriro kwa mutuwu. Amenewa ndi ena mwa mafunso ofunika kwambiri amene muyenera kudzifunsa. Komatu anthu ambiri safuna kufufuza mayankho ake. N’chifukwa chiyani anthu safufuza mayankho a mafunsowa? Kodi m’Baibulo muli mayankho a mafunso amenewa? Anthu ena amaona kuti zimene Baibulo limanena poyankha mafunso amenewa ndi zovuta kuzimvetsa. Ena amada nkhawa kuti akafunsa achita manyazi, pomwe ena amaona kuti amene angayankhe mafunso ngati amenewa ndi atsogoleri azipembedzo. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

4, 5. Kodi ndi mafunso ofunika ati amene tiyenera kudzifunsa, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kufufuza mayankho ake?

4 Mwina nanunso mumafuna mutapeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri pa moyo wanu. Sitikukayikira kuti nthawi zina mumadzifunsa kuti: ‘Kodi cholinga cha moyo n’chiyani? Kodi n’choti anthu azibadwa, kukula, kukalamba kenako n’kufa? Kodi Mulungu ali ndi makhalidwe otani?’ Mungachite bwino kudzifunsa mafunso amenewa komanso kupitirizabe kufufuza mpaka mutapeza mayankho ogwira mtima komanso odalirika. Yesu Khristu, yemwe ndi mphunzitsi wotchuka, ananena kuti: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna, ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulirani.”—Mateyu 7:7.

5 Ngati ‘mutapitiriza kufunafuna’ mayankho a mafunso ofunika kwambiri amenewa mudzapindula chifukwa cha khama lanulo. (Miyambo 2:1-5) Kaya munauzidwa zotani koma choti mudziwe n’choti mayankho alipo ndipo mukhoza kuwapeza. Mayankho ake mungawapeze m’Baibulo ndipo ndi osavuta kuwamvetsa. Chosangalatsa n’chakuti mayankhowo amatithandiza kuti tizikhala osangalala komanso amatipatsa chiyembekezo. Amatithandizanso kuti tikhale ndi moyo wabwino ngakhale panopo. Koma choyamba, tiyeni tiyankhe funso limene limasokoneza maganizo a anthu ambiri.

KODI MULUNGU SATIGANIZIRA KOMANSO NDI WOPANDA CHISONI?

6. N’chifukwa chiyani anthu ambiri amaganiza kuti Mulungu sawaganizira?

6 Anthu ambiri amaona kuti Mulungu satiganizira ndipo ndi wopanda chisoni. Amaganiza kuti akanakhala kuti Mulungu amatiganizira bwenzi zinthu zikuyenda bwino padzikoli. Kulikonse kukuchitika zinthu zomvetsa chisoni, nkhondo komanso anthu akudana kwambiri. Anthufe timadwala, timavutika ndipo anthu amene timawakonda amamwalira. Choncho anthu ambiri amaganiza kuti, ‘Akanakhala kuti Mulungu amatiganizira, kodi sakanachititsa kuti zoipa zonsezi zisamachitike?’

7. (a) Kodi atsogoleri achipembedzo amachititsa bwanji anthu kuganiza kuti Mulungu ndi wopanda chisoni? (b) Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya mayesero amene tingakumane nawo?

7 Chomvetsa chisoni n’chakuti, nthawi zina atsogoleri azipembedzo ndi amene amachititsa anthu kuganiza kuti Mulungu ndi wopanda chisoni. Kodi amachita bwanji zimenezi? Anthu akakumana ndi mavuto enaake mwadzidzidzi, atsogoleriwa amanena kuti zimene zachitikazo ndi chifuniro cha Mulungu. Akamanena mawu amenewa amakhala akuimba mlandu Mulungu kuti ndi amene wachititsa zoipazo. Koma kodi n’zoona kuti Mulungu ndi amene amachititsa zinthu zoipa? Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani imeneyi? Lemba la Yakobo 1:13 limanena kuti: “Munthu akakhala pa mayesero asamanene kuti: ‘Mulungu akundiyesa.’ Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” Choncho sikuti Mulungu ndi amene amachititsa zinthu zoipa zimene mumaona m’dzikoli. (Werengani Yobu 34:10-12.) N’zoona kuti amalola kuti zinthu zoipa zizichitika. Koma pali kusiyana pakati pa kulola kuti chinachake chichitike ndi kuchichititsa kuti chichitike.

8, 9 (a) Fotokozani fanizo lotithandiza kumvetsa kuti kulola kuti zinthu zoipa zichitike n’kosiyana ndi kuchititsa kuti zichitike. (b) N’chifukwa chiyani n’kulakwa kuimba Mulungu mlandu chifukwa cholola anthu kusankha kuchita zinthu zoipa?

8 Mwachitsanzo, taganizirani za bambo wachikondi komanso wanzeru yemwe ali ndi mwana wamkulu amene akukhala naye pakhomo. Ndiyeno mwanayo akuyamba kuchita zinthu zosamvera bambo akewo kenako akusankha kuchoka pakhomopo ndipo bambo ake sakumuletsa. Mwanayo akupitiriza kuchita makhalidwe oipa kenako akukumana ndi mavuto aakulu. Kodi pamenepa tinganene kuti bambo a mwanayo ndi amene achititsa mavutowo? Ayi. (Luka 15:11-13) Mofanana ndi zimenezi, Mulungu saletsa anthu kusankha kuchita zimene akufuna ngakhale zinthuzo zitakhala zoipa koma si amene amachititsa mavuto amene anthuwo amakumana nawo. Choncho n’kulakwa kuimba Mulungu mlandu kuti ndi amene amachititsa mavuto amene anthu onse akukumana nawo.

9 Mulungu ali ndi zifukwa zomveka zimene zimamuchititsa kuti azilola anthu kusankha kuchita zinthu zoipa. Koma popeza Mulungu ndi Mlengi wamphamvu komanso wanzeru akanatha kungokhala osatiuza zifukwazo. Koma chifukwa chakuti amatikonda watiuza zimene zimamuchititsa kuti azilola anthu kusankha kuchita zinthu zoipa. Mudzaphunzira zambiri pa nkhaniyi m’Mutu 11. Choti mudziwe n’chakuti Mulungu si amene amachititsa mavuto omwe timakumana nawo koma ndi amene amatithandiza tikakumana ndi mavutowo.—Yesaya 33:2.

10. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira kuti Mulungu adzathetsa zoipa zonse?

10 Tizikhulupirira kwambiri Mulungu chifukwa ndi woyera. (Yesaya 6:3) Zimenezi zikutanthauza kuti iye sangachite zoipa ngakhale pang’ono. Koma anthu sitingawakhulupirire choncho chifukwa nthawi zina amachita zachinyengo. Ngakhale munthu wokhulupirika amene ali ndi udindo nthawi zambiri sakhala ndi mphamvu zokonza zinthu zimene anthu oipa awononga. Koma Mulungu ali ndi mphamvu zonse. Akhoza kuthetsa mavuto onse amene anthu akukumana nawo ndipo ndi zimene achite posachedwapa. Mulungu akamadzathetsa mavutowa adzachotseratu zoipa zonse.—Werengani Salimo 37:9-11.

KODI MULUNGU AMAMVA BWANJI TIKAMAKUMANA NDI ZINTHU ZOPANDA CHILUNGAMO?

11. (a) Kodi Mulungu amamva bwanji akamaona anthu akuchita zinthu zopanda chilungamo? (b) Kodi Mulungu amamva bwanji akamaona inuyo mukuvutika?

11 Kodi mukuganiza kuti Mulungu amamva bwanji akamaona zimene zikuchitika m’dzikoli komanso zimene inuyo mukukumana nazo pa moyo wanu? Baibulo limanena kuti Mulungu “amakonda chilungamo.” (Salimo 37:28) Chifukwa cha zimenezi amasangalala akamaona anthu akuchita zabwino koma amadana ndi zinthu zonse zopanda chilungamo. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti nthawi ina m’mbuyomu Mulungu anamva ‘kupweteka kwambiri mumtima’ chifukwa anthu ambiri ankachita zinthu zoipa. (Genesis 6:5, 6) Mulungu sanasinthe mmene amaonera zinthu. (Malaki 3:6) Sasangalala akamaona zinthu zoipa zomwe zikuchitika m’dzikoli komanso akamaona anthu akuvutika. Ndipotu Baibulo limati: “Amakuderani nkhawa.”—Werengani 1 Petulo 5:7.

Baibulo limatiphunzitsa kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi

12, 13. (a) N’chifukwa chiyani anthufe tili ndi chikondi komanso makhalidwe ena abwino, nanga timamva bwanji tikaona zinthu zoipa zikuchitika? (b) Kodi mukudziwa bwanji kuti Mulungu adzathetsa mavuto omwe akuchitika padzikoli?

12 Kodi tingatsimikize bwanji kuti Mulungu amadana ndi zinthu zoipa? Baibulo limanena kuti munthu analengedwa m’chifaniziro cha Mulungu. (Genesis 1:26) Choncho ifeyo tili ndi makhalidwe abwino chifukwa tinatengera makhalidwe abwino a Mulunguyo. Mwachitsanzo, kodi inuyo mumakhumudwa mukaona anthu osalakwa akuvutika? Ngati inuyo mumakhumudwa ndi zinthu zopanda chilungamo ngati zimenezi, dziwani kuti Mulungu ndi amene amakhumudwa kwambiri.

13 Chimodzi mwa zinthu zosangalatsa n’chakuti anthufe timatha kukondana ndipo khalidwe limenelinso tinatengera kwa Mulungu. Baibulo limanena kuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Choncho anthufe timakondana chifukwa tinatengera khalidwe la Mulungu la chikondi. Kodi chikondi chimakuchititsani kukhala ndi mtima wofuna kuthetsa zoipa zonse komanso zinthu zonse zopanda chilungamo zomwe mumaziona m’dzikoli? Kodi mukanakhala ndi mphamvu mukanathetsa zoipa zonse komanso mavuto amene anthu akukumana nawo? Tikukhulupirira kuti ndi zimene mukanachita. Choncho musamakayikirenso zoti Mulungu adzathetsa zoipa zonse komanso zinthu zonse zopanda chilungamo. Sikuti zimene talonjezedwa kumayambiriro kwa bukuli ndi zinthu zosatheka ayi. Zimene Mulungu watilonjeza zidzachitikadi. Koma kuti tizikhulupirira kuti zinthu zimenezi zidzachitikadi tiyenera kuphunzira za Mulungu amene anatilonjeza zinthu zimenezi.

MULUNGU AMAFUNA KUTI INUYO MUMUDZIWE

Ngati mukufuna kuti munthu wina akudziweni mumamuuza dzina lanu. Mulungu anaika dzina lake m’Baibulo pofuna kutithandiza kuti timudziwe

14. Kodi dzina la Mulungu ndi ndani, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuligwiritsa ntchito?

14 Kodi mumatani ngati mukufuna kuti munthu wina akudziweni? Mumamuuza dzina lanu. Ndiye kodi Mulungu ali ndi dzina? Zipembedzo zambiri zimanena kuti dzina lake ndi “Mulungu” kapena “Ambuye,” koma amenewa si mayina ake enieni. Mayina amenewa ndi audindo ndipo ndi ofanana ndi mayina ena audindo ngati “mfumu” ndiponso “pulezidenti.” Baibulo limanena kuti Mulungu ali ndi mayina ambiri audindo ndipo ena mwa mayinawa ndi “Mulungu” komanso “Ambuye.” Koma limanenanso kuti Mulungu ali ndi dzina lake lenileni lomwe ndi Yehova. Lemba la Salimo 83:18 limanena kuti: “Inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.” Ngati m’Baibulo lanu mulibe dzina limeneli, werengani Zakumapeto tsamba 195-197 m’bukuli kuti mudziwe chifukwa chake. Koma choti mudziwe n’chakuti dzina la Mulungu limapezeka m’malo ambiri m’mipukutu yakale ya Baibulo. Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amafuna kuti mudziwe dzina lake komanso muziligwiritsa ntchito. Ndipo tinganene kuti akugwiritsa ntchito Baibulo pofuna kukuthandizani kuti mumudziwe.

15. Kodi dzina lakuti Yehova limatanthauza chiyani?

15 Mulungu anadzipatsa dzina limene lili ndi tanthauzo lofunika kwambiri. Dzina lakuti Yehova limatanthauza kuti iye akhoza kukwaniritsa lonjezo lililonse komanso akhoza kukwaniritsa cholinga chilichonse chomwe angakhale nacho. * Dzina la Mulungu limeneli ndi losiyana kwambiri ndi dzina lililonse chifukwa ndi lapadera kwambiri. Palibenso wina amene amadziwika ndi dzina limeneli. Koma pali zinthu zinanso zomwe zimachititsa Yehova kukhala wapadera kwambiri. Kodi zinthu zake ndi ziti?

16, 17. Kodi mayina audindo otsatirawa akutiphunzitsa chiyani za Yehova: (a) “Wamphamvuyonse”? (b) “Mfumu yamuyaya”? (c) “Mlengi”?

16 Pofotokoza za Yehova, lemba la Salimo 83:18 limati: “Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba.” Komanso ndi Yehova yekha amene amadziwika kuti “Wamphamvuyonse.” Lemba la Chivumbulutso 15:3 limati: “Ntchito zanu n’zazikulu ndi zodabwitsa, inu Yehova Mulungu Wamphamvuyonse. Njira zanu ndi zolungama ndi zoona, inu Mfumu yamuyaya.” Dzina laudindo lakuti “Wamphamvuyonse” limatithandiza kudziwa kuti Yehova ali ndi mphamvu zambiri kuposa wina aliyense. Ali ndi mphamvu zoti sitingaziyerekezere ndi chilichonse ndipo ndi iye yekha amene ali ndi mphamvu zoterozo. Dzina laudindo lakuti “Mfumu yamuyaya” limatiphunzitsanso kuti Yehova ndi wosiyana kwambiri ndi aliyense. Lemba la Salimo 90:2 limati: “Inu ndinu Mulungu kuyambira kalekale mpaka kalekale.” Mfundo imeneyi ndi yochititsa chidwi komanso yolimbikitsa kwambiri.

17 Komanso Yehova ndi wosiyana ndi aliyense chifukwa ndi Mlengi. Lemba la Chivumbulutso 4:11 limanena kuti: “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandira ulemerero ndi ulemu, chifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.” Chilichonse chimene mungachiganizire, kaya ndi angelo akumwamba, nyenyezi zambiri zimene zimawala usiku, zipatso, nsomba zimene zimapezeka m’nyanja komanso m’mitsinje, zonsezo zinakhalako chifukwa zinachita kulengedwa ndi Yehova.

KODI N’ZOTHEKA KUTI INUYO MUMUYANDIKIRE YEHOVA?

18. N’chifukwa chiyani anthu ena amaganiza kuti n’zosatheka kumuyandikira Mulungu, koma kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani pa nkhani imeneyi?

18 Anthu ena akadziwa makhalidwe odabwitsa a Yehova amachita mantha. Amaganiza kuti Mulungu ndi wapamwamba kwambiri moti sangamuyandikire kapena kuti Mulunguyo sangawaone kuti ndi ofunika. Kodi maganizo amenewa ndi olondola? Baibulo limaphunzitsa zosiyana ndi zimenezi chifukwa ponena za Yehova limati: “Kwenikweni, iye sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Machitidwe 17:27) Ndipotu Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”—Yakobo 4:8.

19. (a) Kodi tingatani kuti tiyambe kuyandikira Mulungu, ndipo tikhoza kupeza madalitso otani? (b) Kodi ndi makhalidwe a Mulungu ati amene akusangalatsani?

19 Kodi mungatani kuti muyandikire Mulungu? Choyamba, pitirizani kuphunzira za Mulungu. Yesu ananena kuti: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.” (Yohane 17:3) Baibulo limaphunzitsa kuti anthu adzapeza “moyo wosatha” akamaphunzira za Yehova komanso za Yesu. Taona kale kuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:16) Koma Yehova ali ndi makhalidwe enanso abwino ndiponso ochititsa chidwi. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti Yehova ndi “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi choonadi.” (Ekisodo 34:6) Iye ndi “wabwino” komanso “wokonzeka kukhululuka.” (Salimo 86:5) Mulungu ndi woleza mtima. (2 Petulo 3:9) Komanso ndi wokhulupirika. (Chivumbulutso 15:4) Pamene mukupitiriza kuphunzira Baibulo muona mmene Yehova wasonyezera makhalidwe amenewa komanso ena ochititsa chidwi.

20-22. (a) Kodi anthufe sitingathe kukhala mabwenzi a Mulungu chifukwa chakuti sitingathe kumuona? Fotokozani. (b) Kodi anthu ena amene amakuganizirani angakuuzeni kuti muchite chiyani, koma inuyo muyenera kuchita chiyani?

20 N’zoona kuti simungathe kumuona Mulungu chifukwa ndi mzimu. (Yohane 1:18; 4:24; 1 Timoteyo 1:17) Koma kuphunzira Baibulo kungakuthandizeni kuti mumudziwe ngati mmene mungadziwirane ndi munthu mnzanu. Mofanana ndi zimene wamasalimo ananena, inunso mukhoza ‘kuona ubwino wa Yehova.’ (Salimo 27:4; Aroma 1:20) Mukapitiriza kuphunzira za Yehova mudzamvetsa kuti ndi weniweni, mudzayamba kumukonda komanso mudzayamba kumuyandikira.

Bambo akamakonda ana ake zimasonyeza kuti anatengera chikondi chimene Atate wathu wakumwamba ali nacho

21 Mudzamvetsanso chifukwa chake Baibulo limatilimbikitsa kuti tizimuona Yehova ngati Atate wathu. (Mateyu 6:9) Mulungu anatipatsa moyo, koma mofanana ndi bambo amene amakonda ana ake, amafunanso kuti tikhale ndi moyo wabwino kwambiri. (Salimo 36:9) Baibulo limatiphunzitsanso kuti anthu akhoza kukhala mabwenzi a Yehova. (Yakobo 2:23) N’zosangalatsa kwambiri kudziwa kuti mukhoza kukhala bwenzi la Mulungu, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi.

22 Pamene mukupitiriza kuphunzira Baibulo anthu ena amene amakuganizirani akhoza kukuuzani kuti musiye kuphunzira. Iwo angakuuzeni zimenezi poopa kuti musiya kukhulupirira zimene munkakhulupirira poyamba. Koma musalole kuti munthu aliyense akulepheretseni kukhala pa ubwenzi ndi Yehova chifukwa kuchita zimenezi ndi chinthu chamtengo wapatali kuposa china chilichonse.

23, 24. (a) N’chifukwa chiyani muyenera kupitiriza kufunsa mafunso pa zimene mukuphunzira? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’mutu wotsatira?

23 N’zoona kuti zinthu zina zidzakhala zovuta kuti muzimvetse poyamba. Choncho muyenera kukhala wodzichepetsa kuti muzifunsa pamene simunamvetse koma musalephere kufunsa chifukwa cha manyazi. Yesu ananena kuti ndi bwino kukhala wodzichepetsa ngati kamwana. (Mateyu 18:2-4) Ndipotu ana amafunsa mafunso ambiri. Mulungu akufuna kuti mupeze mayankho a mafunso ofunika kwambiri. Baibulo limanenanso za anthu ena amene ankafunitsitsa kuphunzira za Mulungu. Anthu amenewa ankafufuza mosamala m’Malemba pofuna kutsimikizira kuti zimene aphunzira ndi zoona.—Werengani Machitidwe 17:11.

24 Kuti mudziwe zambiri za Yehova muyenera kuphunzira Baibulo. Baibulo ndi buku losiyana kwambiri ndi mabuku ena onse. Mutu wotsatira udzafotokoza zambiri pa nkhani imeneyi.

^ ndime 15 Kuti mudziwe zambiri pa katchulidwe komanso tanthauzo la dzina la Mulungu, werengani Zakumapeto tsamba 195-197.