MUTU 16

Yesetsani Kuti Muzilambira Mulungu M’njira Yovomerezeka

Yesetsani Kuti Muzilambira Mulungu M’njira Yovomerezeka
  • Kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani pa nkhani yogwiritsa ntchito mafano ndi kulambira mizimu ya makolo?

  • Kodi Akhristu amawaona bwanji maholide achipembedzo?

  • Kodi mungafotokozere bwanji anthu ena zimene mumakhulupirira popanda kuwakhumudwitsa?

1, 2. Kodi ndi funso liti limene muyenera kudzifunsa pamene mwatuluka m’chipembedzo chonyenga, ndipo n’chifukwa chiyani funso limeneli lili lofunika?

TIYEREKEZE kuti mwadziwa zoti moyo wanu uli pangozi chifukwa munthu wina wathira poizoni pachitsime chimene mumatungapo madzi. Kodi mungachite chiyani? Mungayesetse nthawi yomweyo kuti mupeze chitsime china cha madzi abwino. Koma ngakhale mutachita zimenezi mungamadzifunsebe kuti, ‘Kodi sindinamwe kale madzi apoizoniwo?’

2 Zimenezi ndi zofanana ndi zomwe zimachitika pa nkhani ya chipembedzo chonyenga. Baibulo limaphunzitsa kuti kulambira konyenga ndi koipitsidwa ndi zinthu zabodza zimene zipembedzo zonyenga zimaphunzitsa komanso miyambo yake. (2 Akorinto 6:17) N’chifukwa chake muyenera kutulukamo mu “Babulo Wamkulu,” yemwe ndi zipembedzo zonse zonyenga. (Chivumbulutso 18:2, 4) Kodi ndi zimene inuyo mwachita? Ngati mwatero, mwachita bwino kwambiri. Komabe kungotuluka m’chipembedzo chonyenga sikokwanira. Pambuyo potuluka, mungachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi pali zinthu zina zokhudzana ndi kulambira konyenga zimene ndimachitabe?’ Tiyeni tikambirane zitsanzo zingapo.

KULAMBIRA MAFANO KOMANSO MIZIMU YA MAKOLO

3. (a) Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani yogwiritsa ntchito mafano polambira, ndipo n’chifukwa chiyani ena angavutike kuti ayambe kuona zinthu zimenezi mmene Mulungu amazionera? (b) Kodi muyenera kuchita chiyani ndi chinthu chilichonse chomwe muli nacho chokhudzana ndi kulambira konyenga?

3 Anthu ena akhala ali ndi mafano kapena tiakachisi m’nyumba zawo kwa zaka zambiri. Kodi inunso munali ndi zinthu ngati zimenezi? Ngati munali nazo, n’kutheka kuti panopa mukuona kuti ndi chinthu chachilendo komanso chovuta kupemphera kwa Mulungu popanda kugwiritsira ntchito zimenezo. Mwinanso munkazikonda kwambiri. Komatu Mulungu ndi amene amatiuza njira yoyenera yomulambirira ndipo Baibulo limati Mulungu samafuna kuti tizigwiritsa ntchito mafano pomulambira. (Werengani Ekisodo 20:4, 5; Salimo 115:4-8; Yesaya 42:8; 1 Yohane 5:21) Mungasonyeze kuti mwatsimikiza kuyamba kutumikira Mulungu m’njira yovomerezeka ngati mutawononga zinthu zonse zimene muli nazo zomwe zimagwirizana ndi kulambira konyenga. Muyenera kuyamba kuziona kuti ndi ‘zonyansa’ ngati mmene Yehova amazionera.—Deuteronomo 27:15.

4. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti kulambira mizimu ya makolo n’kosathandiza? (b) N’chifukwa chiyani Yehova analetsa anthu ake kuti asamachite zilizonse zokhudzana ndi kukhulupirira mizimu?

4 Kulambira mizimu ya makolo n’kofala m’zipembedzo zonyenga. Ena asanaphunzire Baibulo, ankakhulupirira kuti akufa amakakhala kudziko la mizimu ndipo angathe kuthandiza anthu amoyo kapena kuwavulaza. N’kutheka kuti mwina inunso munkachita nawo zinthu zosangalatsa mizimu ya akufa. Koma monga mmene munaphunzirira m’Mutu 6, akufa sakhala ndi moyo kwinakwake. Choncho kuyesa kulankhulana nawo n’kosathandiza. Mauthenga alionse amene amaoneka ngati ndi ochokera kwa anthu amene anamwalira amakhala akuchokera kwa ziwanda. N’chifukwa chake Yehova analetsa Aisiraeli kuti asamayese kulankhula ndi anthu akufa kapena kuchita zinthu zilizonse zokhudzana ndi kukhulupirira mizimu.—Werengani Deuteronomo 18:10-12.

5. Kodi muyenera kuchita chiyani ngati m’mbuyomu munkagwiritsa ntchito mafano kapena kulambira mizimu ya makolo?

5 Kodi muyenera kuchita chiyani ngati m’mbuyomu munkagwiritsa ntchito mafano kapena kulambira mizimu ya makolo? Muyenera kuwerenga ndi kuganizira mozama nkhani za m’Baibulo zimene zimasonyeza mmene Mulungu amaonera zinthu zimenezi. Muyeneranso kupemphera kwa Yehova tsiku lililonse kuti akuthandizeni kumulambira m’njira yovomerezeka komanso kuti muziona zinthu mmene iyeyo amazionera.—Yesaya 55:9.

AKHRISTU OYAMBIRIRA SANKAKONDWERERA KHIRISIMASI

6, 7. (a) Kodi pa Khirisimasi anthu amati amakumbukira chiyani, nanga Akhristu oyambirira ankakondwerera nawo Khirisimasi? (b) M’nthawi ya Akhristu oyambirira, kodi ndi anthu ati amene ankachita zikondwerero zokumbukira tsiku lobadwa?

6 Kulambira kwathu kungaipitsidwe ndi chipembedzo chonyenga ngati timachita nawo maholide otchuka. Mwachitsanzo, taganizirani za Khirisimasi. Pafupifupi zipembedzo zonse zomwe zimati ndi zachikhristu zimanena kuti Khirisimasi ndi chikondwerero chokumbukira kubadwa kwa Yesu Khristu. Koma palibe umboni uliwonse umene umasonyeza kuti ophunzira a Yesu ankachita Khirisimasi. Buku lina linati: “Kwa zaka 200 kuchokera pamene Yesu anabadwa, palibe munthu amene ankadziwa tsiku lenileni limene Yesuyo anabadwa ndipo ndi anthu ochepa kwambiri amene ankafuna kulidziwa.”—Sacred Origins of Profound Things.

7 N’kutheka kuti ophunzira a Yesu ankadziwa tsiku lenileni limene iye anabadwa, komabe iwo sakanachita mwambo uliwonse wokumbukira tsikuli. Chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa malinga ndi zimene buku lina linanena, “Akhristu oyambirira ankaona kuti kukondwerera tsiku limene munthu anabadwa unali mwambo wachikunja.” (The World Book Encyclopedia) Zikondwerero zokumbukira tsiku lobadwa zimene zimatchulidwa m’Baibulo ndi za mafumu awiri omwe sankalambira Yehova. (Genesis 40:20; Maliko 6:21) Kale anthu akunja ankasangalaliranso masiku amene milungu yawo inabadwa. Mwachitsanzo, pa 24 May, anthu aku Roma ankakumbukira kubadwa kwa mulungu wawo wamkazi dzina lake Diana. Tsiku lotsatira, ankakumbukira kubadwa kwa dzuwa limene ankalilambira ngati mulungu ndipo ankamutchula kuti Apollo. Choncho zikondwerero za tsiku lobadwa zinkachitika ndi anthu achikunja osati Akhristu.

8. Kodi zikondwerero za tsiku lobadwa zikugwirizana bwanji ndi kukhulupirira mizimu? Fotokozani.

8 Palinso chifukwa china chomwe chinkachititsa kuti Akhristu oyambirira asamachite mwambo wokumbukira tsiku limene Yesu anabadwa. Ophunzirawo ayenera kuti ankadziwa zoti kukumbukira tsiku lobadwa n’kogwirizana ndi kukhulupirira mizimu. Mwachitsanzo, Agiriki komanso Aroma ambiri ankakhulupirira kuti pa nthawi imene munthu aliyense akubadwa pankabwera mzimu winawake ndipo mzimuwo unkamuteteza moyo wake wonse. Buku lina linati: “Mzimu umenewu unkakhala pachibale ndi mulungu amene anabadwanso pa tsiku ngati lomwelo.” (The Lore of Birthdays) Yehova sangasangalale ndi mwambo uliwonse umene ungasonyeze ngati kuti pali mgwirizano pakati pa Yesu ndi zokhulupirira mizimu. (Yesaya 65:11, 12) Ndiye kodi anthu anayamba bwanji kukondwerera Khirisimasi?

KODI KHRISIMASI INAYAMBA BWANJI?

9. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti anthu ayambe kunena kuti Yesu anabadwa pa 25 December?

9 Anthu anayamba kukumbukira tsiku la kubadwa kwa Yesu pa 25 December patadutsa zaka mahandiredi ambiri iye atabwerera kumwamba. Koma limeneli si tsiku limene Yesu anabadwa. * Ndiye kodi anthu anasankha bwanji tsiku la 25 December? Anthu ena amene ankati ndi Akhristu anayamba kuona kuti “zingakhale bwino tsiku lobadwa la Yesu litafanana ndi tsiku limene Aroma ankachita mwambo wachikunja” wokumbukira kubadwa kwa dzuwa. (The New Encyclopædia Britannica) Nthawi yozizira, pamene dzuwa silinkatentha kwenikweni, anthu achikunja ankachita zikondwerero zosiyanasiyana n’cholinga choti dzuwa libwerere kumene lapita. Iwo ankakhulupirira kuti pa 25 December m’pamene dzuwa linkayamba ulendo wake wobwerera. Pofuna kukopa anthu achikunjawo kuti alowe Chikhristu, atsogoleri achipembedzo anasintha chikondwerero chimenechi kuti chizioneka ngati chachikhristu. *

10. N’chifukwa chiyani kale anthu ena sankachita nawo Khirisimasi?

10 Anthu anazindikira kalekale kuti Khirisimasi inachokera ku miyambo yachikunja. Pozindikira zimenezi, dziko la England komanso mayiko ena a ku America anakhazikitsa lamulo loletsa mwambowu m’zaka za m’ma 1600. Aliyense amene sankapita kuntchito pa tsiku la Khirisimasi ankamulipilitsa. Koma pasanapite nthawi, mwambowu unayambiranso ndipo panawonjezereka miyambo ina. Khirisimasi inayambiranso kukhala mwambo wotchuka, ndipo zidakali choncho m’mayiko ambiri mpaka pano. Komabe, anthu amene amafuna kusangalatsa Mulungu samakondwerera Khirisimasi kapena mwambo wina uliwonse umene unachokera ku miyambo yachikunja. *

KODI PALI VUTO NDI MMENE ZINAYAMBIRA?

11. N’chifukwa chiyani anthu ena amaona kuti kuchita nawo maholide ena kulibe vuto, koma kodi n’chiyani chimene tiyenera kuganizira kwambiri?

11 Ena amavomereza kuti Khirisimasi ndiponso maholide ena zinayambira ku miyambo yachikunja koma amaonabe kuti palibe vuto kuchita maholide amenewa. Ndipotu anthu ambiri akamachita maholidewa samaganizira n’komwe kuti zimene akuchitazo n’zogwirizana ndi kulambira konyenga. Iwo amaona kuti maholide amenewa amawapatsa mpata wocheza ndi mabanja awo. Kodi nanunso mumaona kuti maholide amenewa ndi abwino chifukwa amakupatsani mpata wocheza ndi banja lanu? Ngati ndi choncho, ndiye kuti mumavutika kutsatira zimene kulambira koona kumafuna chifukwa chokonda banja lanu, osati chifukwa chokonda kulambira konyenga. Dziwani kuti Yehova, amene anayambitsa banja, amafuna kuti muzisangalala ndi achibale anu. (Aefeso 3:14, 15) Koma ndi bwino kucheza ndi banja lanu mukuchita zinthu zimene Mulungu amasangalala nazo. Mtumwi Paulo anafotokoza za chinthu chimene tiyenera kuganizira kwambiri tikamapanga zinthu. Iye anati: “Nthawi zonse muzitsimikiza kuti chovomerezeka kwa Ambuye n’chiti.”—Aefeso 5:10.

Kodi mungatole n’kudya switi woti anagwera m’ngalande ya madzi oipa?

12. Fotokozani chitsanzo chosonyeza chifukwa chake tiyenera kupewa kuchita nawo zinthu zochokera ku miyambo yachikunja.

12 Mwina mumaona kuti zifukwa zimene anthu amachitira maholidewa masiku ano, si zofanana ndi zomwe ankachitira poyamba. Ndiye kodi pali vuto ndi mmene maholidewa anayambira? Inde lilipo. Tiyerekeze kuti mwaona switi m’ngalande ya madzi oipa. Kodi mungatole n’kudya? N’zokayikitsa ngati mungatero chifukwa switiyo ndi woipa. Mofanana ndi switiyo, maholidewa ngakhale atakhala osangalatsa koma anachokera ku miyambo yachikunja. Kuti tipitirizebe kulambira Mulungu m’njira yovomerezeka, tiyenera kuona zinthu mmene Yesaya ankaonera. Iye anauza atumiki a Mulungu anzake kuti: “Musakhudze chinthu chilichonse chodetsedwa.”—Yesaya 52:11.

MUZICHITA ZINTHU MOSAMALA

13. Kodi pangakhale mavuto otani ngati mutasiya kuchita nawo maholide?

13 Nthawi zina mukhoza kukumana ndi mavuto chifukwa chosachita nawo maholide. Mwachitsanzo, anzanu amene mumagwira nawo ntchito akhoza kudabwa kuti n’chifukwa chiyani simuchita nawo zikondwerero zinazake zomwe zimachitika kuntchito kwanu. Kodi mungatani ngati munthu winawake atakupatsani mphatso ya Khirisimasi? Komanso kodi pangakhale vuto lililonse kulandira mphatsoyo? Nanga bwanji ngati mwamuna kapena mkazi wanu ndi wa mpingo wina ndipo amaona kuti palibe vuto kuchita maholide amenewa? Kodi mungatani kuti ana anu asamaone kuti akumanidwa zinthu zinazake chifukwa choti samachita nawo maholide?

14, 15. Kodi mungatani ngati munthu wina wakupatsani mafuno abwino a chikondwerero chinachake, kapena ngati akufuna kukupatsani mphatso?

14 Muyenera kuchita zinthu mosamala nthawi zonse. Mwachitsanzo, ngati munthu wina amene mwangokumana naye wanena mawu okufunirani mafuno abwino a holide inayake, mukhoza kungothokoza. Komano ngati munthuyo mumakumana naye kawirikawiri kapena ndi mnzanu wakuntchito, mungafunike kumufotokozera momveka bwino. Komabe nthawi zonse muyenera kuchita zinthu mosamala. Baibulo limatilangiza kuti: “Nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo, okoma ngati kuti mwawathira mchere, kuti mudziwe mmene mungayankhire wina aliyense.” (Akolose 4:6) Muyenera kufotokoza bwino zimene mumakhulupirira kuti musaoneke ngati wachipongwe. Afotokozereni bwino kuti si kuti mukudana ndi zopatsana mphatsozo kapena kusangalala limodzi ndi anzanu, kungoti mungakonde kupanga zinthu zimenezi pa nthawi ina.

15 Nanga bwanji ngati munthu wina akufuna kukupatsani mphatso? Zimene mungachite zingatengere mmene zinthu zilili pa nthawiyo. Mwina amene akufuna kukupatsani mphatsoyo anganene kuti: “Ndikudziwa kuti simukondwerera holideyi, komabe ndangofuna kukupatsani mphatsoyi.” Pamenepo mwina mungaone kuti kulandira mphatsoyo sikukutanthauza kuti mwachita nawo chikondwererocho. Koma ngati munthuyo sakudziwa zimene mumakhulupirira pa nkhaniyi, mungamufotokozere bwinobwino chifukwa chimene simuchitira chikondwererocho. Zimenezi zingam’thandize kumvetsa chifukwa chomwe mwalandirira mphatso yakeyo koma osam’patsa yanu. Koma zingakhale bwino kukana ngati mphatsoyo ikuperekedwa n’cholinga chongofuna kuona ngati mumatsatiradi zimene mumakhulupirira.

NANGA BWANJI AKAKHALA ACHIBALE?

16. Kodi tingatani kuti tisamakhumudwitse achibale athu pa nkhani ya zikondwerero zimene amachita?

16 Bwanji ngati achibale anu amakhulupirira zosiyana ndi zimene mumakhulupirira? Apanso mufunika kuchita zinthu mosamala. Simuyenera kutsutsana nawo pa mwambo uliwonse kapena chikondwerero chilichonse chimene amapanga. M’malomwake, muzilemekeza zimene amakhulupirira mofanana ndi mmene mungafunire kuti nawonso azilemekeza zimene inuyo mumakhulupirira. (Werengani Mateyu 7:12.) Muzipewa kuchita zinthu zimene zingaoneke ngati mukuchita nawo miyamboyo. Komabe dziwani kuti pali zinthu zina zimene munthu atachita sizingatanthauze kuti wachita nawo mwambowo. Nthawi zonse muzionetsetsa kuti zimene mukuchita sizipangitsa kuti muzidziimba mlandu kuti mwalakwitsa zinazake.—Werengani 1 Timoteyo 1:18, 19.

17. Kodi muyenera kuchita chiyani kuti ana anu asamaone ngati akumanidwa zinthu zina chifukwa choti sapanga nawo zikondwerero zosiyanasiyana?

17 Kodi mungatani kuti ana anu asamaone kuti akumanidwa zinthu zinazake chifukwa choti samachita nawo maholide? Ana angaone kuti akumanidwa zinazake kapena ayi malinga ndi zimene mumachita masiku ena. Makolo ena amakonza zopereka mphatso kwa ana awo nthawi ina iliyonse. Mphatso ya mtengo wapatali kwambiri imene makolo angapereke kwa ana awo ndi kupatula nthawi yocheza nawo komanso kuwasonyeza chikondi.

MUZICHITA ZIMENE AKHRISTU OONA AMAFUNIKA KUCHITA

Kulambira Mulungu m’njira yovomerezeka kumachititsa kuti munthu akhale wosangalala

18. Kodi misonkhano yachikhristu ingakuthandizeni bwanji kuti muzilambira Mulungu m’njira yovomerezeka?

18 Kuti musangalatse Mulungu, muyenera kusiya kuchita zinthu zimene zimagwirizana ndi kulambira konyenga n’kumachita zimene Akhristu oona amafunika kuchita. Kodi zina mwa zinthu zimenezi ndi ziti? Baibulo limati: “Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezere kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.” (Aheberi 10:24, 25) Misonkhano yachikhristu ndi nthawi yosangalatsa imene ingakuthandizeni kuti muzilambira Mulungu m’njira yovomerezeka. (Salimo 22:22; 122:1) Kumisonkhanoyi, Akhristu okhulupirika ‘amalimbikitsana.’—Aroma 1:12.

19. Kodi kuuza ena zinthu zimene mumaphunzira kuchokera m’Baibulo n’kofunika bwanji?

19 Njira inanso imene ingakuthandizeni kuti muzilambira Mulungu m’njira yovomerezeka ndi kuuza ena zimene mwadziwa pa nthawi imene mwakhala mukuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Masiku ano, anthu ambiri “akuusa moyo ndi kubuula” chifukwa cha zinthu zoipa zimene zikuchitika padziko lapansili. (Ezekieli 9:4) Mwina mukudziwa anthu ena amene akuvutika m’njira zosiyanasiyana. Bwanji osawauzako zimene mukuyembekezera m’tsogolo zomwe Baibulo limaphunzitsa? Kupita kumisonkhano komanso kuuza ena zimene mumaphunzira m’Baibulo, zingakuthandizeni kuti pang’ono ndi pang’ono musamafunenso kuchita nawo miyambo iliyonse yachipembedzo chonyenga. Dziwani kuti mukamayesetsa kulambira Mulungu m’njira yovomerezeka, mudzakhala wosangalala komanso mudzapeza madalitso ambiri.—Malaki 3:10.

^ ndime 9 Chinthu chinanso chimene chinapangitsa kuti asankhe tsiku la 25 December ndi chikondwerero cha Saturnalia. Anthu ankachita chikondwerero chimenechi kuyambira pa 17 mpaka pa 24 December polemekeza mulungu wachiroma wa zaulimi. Pamwambo umenewu pankakhala zakudya zambirimbiri, kusangalala komanso kupatsana mphatso.

^ ndime 10 Kuti mudziwe mmene Akhristu oona amaonera maholide ena otchuka, onani Zakumapeto, tsamba 222-223.