Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ZAKUMAPETO

Kodi Mikayeli Mkulu wa Angelo ndi Ndani?

Kodi Mikayeli Mkulu wa Angelo ndi Ndani?

MNGELO wina amene amadziwika ndi dzina lakuti Mikayeli, satchulidwa kawirikawiri m’Baibulo. Koma nthawi iliyonse imene watchulidwa ndi dzina limeneli, amakhala akugwira ntchito inayake yapadera. M’buku la Danieli, Mikayeli amatchulidwa akulimbana ndi angelo oipa. M’kalata ya Yuda, amatchulidwa akukangana ndi Satana. Ndipo m’buku la Chivumbulutso, amatchulidwa ali pa nkhondo yomenyana ndi Satana ndi ziwanda zake. Mikayeli amagwira ntchito yolimbana ndi adani a Yehova komanso yotetezera Ufumu wa Mulungu, ndipo zimenezi n’zogwirizana ndi dzina lake, chifukwa limatanthauza kuti, “Ndani Ali Ngati Mulungu?” Koma kodi Mikayeli ameneyu ndi ndani?

Anthu ena amadziwika ndi mayina angapo. Mwachitsanzo, Yakobo amadziwikanso ndi dzina lakuti Isiraeli, ndipo mtumwi Petulo amadziwikanso kuti Simoni. (Genesis 49:1, 2; Mateyu 10:2) Mofanana ndi zimenezi, Baibulo limasonyeza kuti Mikayeli ndi dzina lina la Yesu Khristu, lomwe ankadziwika nalo asanabwere padziko lapansi komanso atabwerera kumwamba. Tiyeni tikambirane malemba angapo omwe amatsimikizira zimenezi.

Mkulu wa Angelo. Mawu a Mulungu amanena kuti Mikayeli ndi “mkulu wa angelo.” (Yuda 9) Mmene dzina lakuti “mkulu wa angelo” limalembedwera zimasonyeza kuti akunena za munthu mmodzi. Zimenezi zikusonyeza pali mngelo mmodzi yekha amene ali ndi udindo umenewu. Ndipotu Baibulo limasonyeza kuti udindo umenewu ndi wa Yesu. Pofotokoza za Yesu Khristu ataukitsidwa, lemba la 1 Atesalonika 4:16 limanena kuti: “Ambuye . . . adzatsika kumwamba, ndi mfuu yolamula ya mawu a mkulu wa angelo.” Pa lemba limeneli, mawu a Yesu akufotokozedwa kuti ndi mawu a mkulu wa angelo. Choncho, Baibulo limasonyeza kuti Mikayeli mkulu wa angelo ndi Yesu.

Mtsogoleri wa Gulu Lankhondo. Baibulo limanena kuti “Mikayeli ndi angelo ake anamenyana ndi chinjoka. . . . ndi angelo ake.” (Chivumbulutso 12:7) Choncho, Mikayeli ndi Mtsogoleri wa gulu lankhondo la angelo okhulupirika. Buku la Chivumbulutso limatchulanso kuti Yesu ndi Mtsogoleri wa gulu lankhondo la angelo okhulupirika. (Chivumbulutso 19:14-16) Ndipo mtumwi Paulo anatchula za “Ambuye Yesu” ndi “angelo ake amphamvu.” (2 Atesalonika 1:7) Choncho Baibulo limanena za Mikayeli ndi “angelo ake,” ndiponso Yesu ndi “angelo ake.” (Mateyu 13:41; 16:27; 24:31; 1 Petulo 3:22) Popeza Baibulo silisonyeza zoti pali magulu awiri a angelo okhulupirika, lina lotsogoleredwa ndi Mikayeli ndipo lina lotsogoleredwa ndi Yesu, n’zomveka kunena kuti Mikayeli ndi dzina la Yesu Khristu pa udindo umene ali nawo kumwamba. *

^ ndime 1 Mfundo zina zosonyeza kuti Mikayeli ndi dzina lina la Mwana wa Mulungu zili m’buku la Samalani Ulosi wa Danieli!, tsamba 204-205, ndiponso m’buku la Chingelezi lakuti Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, tsamba 393-394. Mabukuwa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.