Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ZAKUMAPETO

Chaka cha 1914 Ndi Chaka Chapadera Kwambiri

Chaka cha 1914 Ndi Chaka Chapadera Kwambiri

KUDAKALI zaka zambirimbiri, ophunzira Baibulo ankanena kuti m’chaka cha 1914 mudzachitika zinthu zinazake zapadera. Kodi m’chaka chimenechi munachitika zotani, nanga pali umboni wotani wosonyeza kuti chaka cha 1914 chinalidi chapadera?

Malinga ndi Luka 21:24, Yesu ananena kuti: “Anthu a mitundu ina adzapondaponda Yerusalemu, kufikira nthawi zoikidwiratu za anthu a mitundu inawo zitakwanira.” Mzinda wa Yerusalemu unali likulu la dziko la Yuda ndipo ndi kumene kunkakhala mafumu a m’banja la Davide. (Salimo 48:1, 2) Komabe mafumu amenewa anali osiyana kwambiri ndi mafumu a mitundu ina. Iwo ankakhala “pampando wachifumu wa Yehova” chifukwa ulamuliro wawo unkaimira ulamuliro wa Mulungu. (1 Mbiri 29:23) Choncho, mzinda wa Yerusalemu unkaimira ulamuliro wa Yehova.

Koma kodi anthu a mitundu ina anayamba liti ‘kupondaponda’ ulamuliro wa Mulunguwu, nanga anaupondaponda bwanji? Zimenezi zinachitika mu 607 B.C.E. pamene Yerusalemu anagonjetsedwa ndi Ababulo. Pa nthawi imeneyi, panalibe munthu aliyense amene ankalamulira “pampando wachifumu wa Yehova” ndipo dzikolo linalibe mfumu iliyonse yochokera m’banja la Davide. (2 Mafumu 25:1-26) Koma kodi ulamuliro wa Mulungu umenewu ‘adzaupondaponda’ mpaka kalekale? Ayi, chifukwa ponena za Zedekiya, yemwe anali mfumu yomaliza kulamulira ku Yerusalemu, ulosi wa Ezekieli unanena kuti: “Chotsa nduwira ndipo vula chisoti chachifumu. . . . Ufumu umenewu sudzaperekedwa kwa wina aliyense kufikira atabwera amene ali woyenerera mwalamulo kuutenga, ndipo ndidzaupereka kwa iye.” (Ezekieli 21:26, 27) “Amene ali woyenerera mwalamulo” kulowa ufumu wa Davide ndi Yesu Khristu. (Luka 1:32, 33) Izi zikutanthauza kuti ‘kupondapondaku’ kudzatha Yesu akadzayamba kulamulira monga Mfumu.

Kodi ndi liti pamene zimenezi zidzachitike? Yesu anasonyeza kuti ulamuliro wa anthu a mitundu inawu udzakhala ndi polekezera. Mu chaputala 4 cha buku la Danieli, muli nkhani yotithandiza kudziwa za kutalika kwa nthawi imeneyi komanso pamene idzathere. Nkhaniyi imafotokoza za maloto a Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo. Iye analota mtengo wautali kwambiri umene unadulidwa, ndipo chitsa chake sichinkaphukira chifukwa anali atachikulunga ndi zinthu zachitsulo. Kenako mngelo ananena kuti zikhale choncho mpaka “padutse nthawi zokwanira 7.”Danieli 4:10-16.

Nthawi zina m’Baibulo, mitengo imaimira ulamuliro. (Ezekieli 17:22-24; 31:2-5) Choncho, kudulidwa kwa mtengo umenewu kukuimira kusokonekera kwa ulamuliro wa Mulungu womwe unkaimiridwa ndi mafumu a ku Yerusalemu. Komabe masomphenyawa akutithandiza kudziwa kuti ‘kupondedwapondedwa kwa Yerusalemu’ kudzakhala kwa nthawi yochepa, yomwe ikutchulidwa kuti ndi “nthawi zokwanira 7.” Koma kodi nthawi imeneyi ndi yaitali bwanji?

Lemba la Chivumbulutso 12:6, 14, limasonyeza kuti nthawi zitatu ndi hafu, zimaimira masiku 1,260. Ndiye kuti nthawi zokwanira 7, zikuimira masiku 2,520. Komatu anthu a mitundu ina anapitirizabe ‘kupondaponda’ ulamuliro wa Mulungu masiku 2,520 atatha pambuyo pa kuwonongedwa kwa Yerusalemu. Zimenezi zikusonyeza kuti nthawi imene ikufotokozedwa mu ulosiwu ndi yaitali kwambiri, osati masiku 2,520 enieni. Tikatengera zimene malemba a Numeri 14:34 ndiponso Ezekieli 4:6 amanena, omwe amanena za “tsiku limodzi kuimira chaka chimodzi,” ndiye kuti “nthawi zokwanira 7” zikuimira zaka 2,520.

Zaka 2,520 zimenezi zikuyambira mu October 607 B.C.E., pamene mzinda wa Yerusalemu unagonjetsedwa ndi Ababulo ndipo ufumu wa banja la Davide unalandidwa. Nthawi imeneyi ikuthera mu October 1914. Apa ndi pamene ‘nthawi zoikidwiratu za anthu a mitundu ina’ zinatha, ndipo Yesu Khristu anaikidwa monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. *Salimo 2:1-6; Danieli 7:13, 14.

Yesu ananeneratu kuti nthawi ya “kukhalapo” kwake idzadziwika ndi zinthu monga nkhondo, njala, zivomezi ndi miliri, ndipo zimenezi ndi zimene zakhala zikuchitika padziko lonse kuyambira mu 1914. (Mateyu 24:3-8; Luka 21:11) Zinthu zimene zakhala zikuchitikazi ndi umboni wokwanira wosonyeza kuti Ufumu wa Mulungu unayambadi kulamulira kumwamba mu 1914 ndipo pamenepa ndi pamene “masiku otsiriza” a dziko loipali anayambira.—2 Timoteyo 3:1-5.

^ ndime 4 Kuchokera mu October 607 B.C.E. kufika mu October 1 B.C.E. panadutsa zaka 606. Kuchokera mu October 1 B.C.E. kudzafika mu October 1914 C.E. panadutsa zaka 1,914. Tikaphatikiza zaka 606 ndi zaka 1,914, timapeza zaka 2,520. Kuti mumve zambiri zokhudza kugonjetsedwa kwa Yerusalemu mu 607 B.C.E., onani buku lakuti Kukambitsirana za m’Malemba, tsamba 231-233, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.