ZAKUMAPETO
Kodi Tsiku la Chiweruzo N’chiyani?
KODI mukamva za Tsiku la Chiweruzo mumaganiza za chiyani? Anthu ambiri amaganiza kuti pa tsikuli anthu ambirimbiri adzaima pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu kuti aweruzidwe. Iwo amati aliyense adzaweruzidwa payekhapayekha ndipo anthu oipa adzaweruzidwa kuti apite kukazunzidwa kwamuyaya, pomwe anthu abwino adzapita kukasangalala kumwamba. Komatu Baibulo limafotokoza zinthu zosiyana kwambiri ndi zimenezi. Mawu a Mulungu amasonyeza kuti nthawi imeneyi si yoopsa, koma yosangalatsa.
APa Chivumbulutso 20:11, 12, timawerenga mawu amene mtumwi Yohane analemba ofotokoza za Tsiku la Chiweruzo, akuti: “Ndinaona mpando wachifumu waukulu woyera, ndi amene anakhalapo. Dziko lapansi ndi kumwamba zinathawa pamaso pake, ndipo malo a zimenezi sanapezekenso. Ndiye ndinaona akufa, olemekezeka ndi onyozeka, ataimirira pamaso pa mpando wachifumuwo, ndipo mipukutu inafunyululidwa. Koma mpukutu wina unafunyululidwa, ndiwo mpukutu wa moyo. Ndipo akufa anaweruzidwa malinga ndi zolembedwa m’mipukutuyo, mogwirizana ndi ntchito zawo.” Kodi amene adzagwire ntchito yoweruzayi ndi ndani?
Woweruza wamkulu wa anthu onse ndi Yehova Mulungu. Komabe anapereka ntchito yoweruzayi kwa munthu wina. Malinga ndi Machitidwe 17:31, mtumwi Paulo ananena kuti Mulungu “wakhazikitsa tsiku limene akufuna kudzaweruza m’chilungamo dziko lapansi kumene kuli anthu, kudzera mwa munthu amene iye wamuika.” Woweruza ameneyu ndi Yesu Khristu. (Yohane 5:22) Koma kodi Tsiku la Chiweruzo limeneli lidzayamba liti? Nanga lidzakhala lalitali bwanji?
* (Chivumbulutso 16:14, 16; 19:19–20:3) Nkhondoyi ikadzatha, Satana ndi ziwanda zake adzatsekeredwa kuphompho kwa zaka 1,000. Pa nthawi imeneyi, a 144,000 adzakhala oweruza komanso adzalamulira “limodzi ndi Khristu zaka 1,000.” (Chivumbulutso 14:1-3; 20:1-4; Aroma 8:17) Tsiku la Chiweruzo si lalifupi longokwana maola 24 okha. Lidzakhala la zaka 1,000.
Buku la Chivumbulutso limasonyeza kuti Tsiku la Chiweruzo lidzayamba pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo yomwe idzawononge dziko la Satanali.Mu zaka 1,000 zimenezi, Yesu Khristu ‘adzaweruza amoyo ndi akufa.’ (2 Timoteyo 4:1) “Amoyo” akuimira “khamu lalikulu la anthu” amene adzapulumuke pa nkhondo ya Aramagedo. (Chivumbulutso 7:9-17) Koma mtumwi Yohane anaonanso “akufa . . . ataimirira pamaso pa mpando wachifumuwo” kuti aweruzidwe. Mogwirizana ndi zimene Yesu analonjeza, “onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu [a Khristu] ndipo adzatuluka,” kapena kuti adzaukitsidwa. (Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15) Koma kodi azidzayang’ana chiyani poweruza anthuwa?
Malinga ndi masomphenya amene Yohane anaona, “mipukutu inafunyululidwa” ndipo “akufa anaweruzidwa malinga ndi zolembedwa m’mipukutuyo, mogwirizana ndi ntchito zawo.” (Chivumbulutso 20:12) Kodi m’mipukutuyi munalembedwa zimene anthuwo ankachita asanamwalire? Ayi, anthuwa sadzaweruzidwa potengera zimene ankachita asanamwalire. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Chifukwa Baibulo limanena kuti: “Munthu amene wafa wamasuka ku uchimo wake.” (Aroma 6:7) Zimenezi zikusonyeza kuti anthu amene adzaukitsidwe adzakhala atakhululukidwa machimo awo onse. Ndiye kuti zimene zalembedwa m’mipukutuyi zikuimira malangizo amene Mulungu adzapereke pa nthawiyo. Kuti akhale ndi moyo kwamuyaya, anthu amene adzapulumuke Aramagedo ndiponso amene adzaukitsidwe, adzayenera kutsatira malamulo a Mulungu, kuphatikizapo malamulo atsopano amene Yehova adzapereke m’zaka 1,000 zimenezi. Choncho, anthu adzaweruzidwa potengera zimene azidzachita mkati mwa Tsiku la Chiweruzo.
Yesaya 26:9) Komabe, sikuti anthu onse adzayamba kutsatira zimene Mulungu amafuna. Lemba la Yesaya 26:10 limati: “Ngakhale munthu woipa atachitiridwa zabwino, sangaphunzire chilungamo. M’dziko lochita zowongoka, iye adzachita zinthu zopanda chilungamo ndipo sadzaona ukulu wa Yehova.” Anthu oipawa adzaphedwa m’Tsiku la Chiweruzo ndipo sadzaukitsidwanso.—Yesaya 65:20.
Pa nthawi imeneyi, kwa anthu ambiri kadzakhala koyamba kupatsidwa mwayi wophunzira ndiponso kutsatira zimene Mulungu amafuna. Izi zikutanthauza kuti padzakhala ntchito yaikulu kwambiri yophunzitsa anthu, moti “anthu okhala panthaka ya dzikolo adzaphunzira chilungamo.” (Tsiku la Chiweruzo likamadzatha, anthu amene adzakhale adakali ndi moyo adzakhala angwiro ngati mmene zinalili poyamba. (1 Akorinto 15:24-28) Kenako anthu adzayesedwa komaliza. Satana adzamasulidwa ndipo adzapatsidwa mpata woti ayesenso anthu komaliza. (Chivumbulutso 20:3, 7-10) Anthu amene sadzalola kuti Satana awasocheretse, adzaona kukwaniritsidwa kwa lonjezo la m’Baibulo lakuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Salimo 37:29) Zimene takambiranazi zikusonyeza kuti Tsiku la Chiweruzo lidzakhala nthawi yosangalatsa kwa anthu onse okhulupirika.
^ ndime 1 Kuti mumve zambiri zokhudza Aramagedo, onani buku la Kukambitsirana za m’Malemba, tsamba 37-42, ndi mutu 20 m’buku la Lambirani Mulungu Woona Yekha. Mabukuwa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.