Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ZAKUMAPETO

Kudziwa Zoona Zokhudza Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyera

Kudziwa Zoona Zokhudza Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyera

ANTHU amene amakhulupirira kuti pali Mulungu Atate, Mulungu Mwana ndi Mulungu Mzimu Woyera amanena kuti mwa Mulungu mmodzi muli anthu atatu. Iwo amakhulupirira kuti atatu onsewa ndi ofanana mphamvu komanso onse alibe chiyambi. Malinga ndi chikhulupiriro chimenechi, ndiye kuti Atate ndi Mulungu, Mwana ndi Mulungu, Mzimu Woyeranso ndi Mulungu, komabe pali Mulungu mmodzi yekha.

Anthu ambiri amene amakhulupirira zimenezi amavomereza kuti zimene amakhulupirirazo n’zovuta kuzifotokoza. Komabe amaona kuti zimenezi ndi zomwe Baibulo limaphunzitsa. Komatu palibe vesi lililonse m’Baibulo limene limanena kuti pali Mulungu Atate, Mulungu Mwana, ndi Mulungu Mzimu Woyera. Tiyeni tikambirane vesi limene anthu okhulupirira zimenezi amanena kuti ndi lomwe limasonyeza kuti pali Mulungu Atate, Mulungu Mwana, ndi Mulungu Mzimu Woyera.

“MAWUYO ANALI MULUNGU”

Lemba la Yohane 1:1 limanena kuti: “Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali kwa Mulungu, ndipo Mawu ndiye Mulungu.” (Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Kenako m’chaputala chomwechi, mtumwi Yohane anasonyeza kuti ‘Mawuyo’ ndi Yesu. (Yohane 1:14) Komano chifukwa choti Mawuyo akunenedwa kuti ndi Mulungu, anthu ena amakhulupirira kuti Mwana ndiponso Atate ndi Mulungu mmodzi.

Kumbukirani kuti mavesi amenewa poyamba analembedwa m’Chigiriki. Patapita nthawi, anthu anamasulira malembawa kuchokera ku Chigiriki kupita m’zinenero zina. Komabe omasulira Mabaibulo ena sanagwiritse ntchito mawu akuti “Mawu ndiye Mulungu.” Iwo anachita zimenezi chifukwa ankadziwa kuti mawu Achigiriki amene anagwiritsidwa ntchito palembali ankafunika kumasuliridwa mwanjira ina. Taonani zitsanzo izi: “Logosi [Mawu] anali ngati Mulungu.” (A New Translation of the Bible) “Mawuyo anali ndi Mulungu ndipo nayenso anali ngati Mulungu.” (The Translator’s New Testament) Malinga ndi mmene Mabaibulo amenewa akusonyezera, “Mawu” ameneyu si Mulungu. * Mofanana ndi Mabaibulo amenewa, m’Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, vesili analimasulira kuti: “Mawuyo anali mulungu.” Popeza Mawu ameneyu ali ndi udindo wapamwamba kwambiri kuposa zinthu zina zonse zimene Yehova analenga, n’chifukwa chake akutchulidwa kuti anali “mulungu.” Ndipo m’Baibulo la Dziko Latsopano mawu akuti mulungu alembedwa ndi “m” wamng’ono posonyeza kuti akungofotokoza za mmene Mawuyo amachitira zinthu. Mawu akuti “mulungu” amene ali pavesili akutanthauza “wamphamvu.”

MFUNDO ZINA ZOTHANDIZA

Anthu ambiri sadziwa Chigiriki chimene chinagwiritsidwa ntchito polemba Baibulo. Ndiye kodi tingadziwe bwanji zimene Yohane ankatanthauza pavesili? Ganizirani chitsanzo ichi: Mphunzitsi akufotokoza mfundo inayake kwa ana a m’kalasi yake. Komano anawo amva zosiyanasiyana pa zimene mphunzitsiyo amafotokoza. Kodi angatani kuti adziwe zolondola? Ayenera kufunsa mphunzitsi wawoyo kuti awafotokozerenso. Kuchita zimenezi kudzawathandiza kuti amvetse bwino nkhaniyo. Mofanana ndi zimenezi, kuti timvetse tanthauzo la lemba la Yohane 1:1, ndi bwino kufufuza mfundo zina zimene Yohane analemba zokhudza udindo wa Yesu. Kuphunzira mfundo zina pa nkhaniyi kungatithandize kudziwa zolondola.

Mwachitsanzo, taganizirani mfundo ina imene Yohane analemba m’chaputala 1, vesi 18, yakuti: “Palibe munthu anaonapo Mulungu [Wamphamvuyonse] ndi kale lonse.” Komabe, anthu anamuonapo Yesu, n’chifukwa chake Yohane anati: “Mawu ameneyo anakhala ndi thupi la nyama ndi kukhala pakati pathu, ndipo tinaona ulemerero wake.” (Yohane 1:14, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Ndiye kodi zingatheke bwanji kuti Mwanayu akhalenso Mulungu Wamphamvuyonse? Yohane ananenanso kuti, “Mawuyo anali kwa Mulungu.” Ndiye zingatheke bwanji kuti munthu akhale kwa winawake, pomwe winawakeyo ndi iye yemweyo? Ndipotu zimene Yesu ananena zomwe zili pa Yohane 17:3, zimasonyeza kuti pali kusiyana pakati pa iyeyo ndi Atate wake wakumwamba. Iye anawatchula Atate wake kuti ndi “Mulungu yekhayo amene ali woona.” Chakumapeto kwa buku lake, Yohane ananena kuti: “Izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu alidi Khristu Mwana wa Mulungu.” (Yohane 20:31) Mungaone kuti Yesu akutchulidwa kuti ndi Mwana wa Mulungu, osati Mulungu. Mfundo zowonjezera zimenezi za mu Uthenga Wabwino wa Yohane zikutithandiza kumvetsa zimene lemba la Yohane 1:1 limatanthauza. Yesu ndi “mulungu” chifukwa chakuti ali ndi udindo wapamwamba, koma osati wofanana ndi wa Mulungu wamphamvuyonse.

MABUKU ENA AMATSIMIKIZIRANSO MFUNDO IMENEYI

Taganiziraninso chitsanzo cha mphunzitsi ndi ana asukulu chija. Tiyerekeze kuti ana ena akukayikirabe, ngakhale kuti mphunzitsi uja wawafotokozera mfundo zina zothandiza. Kodi angatani? Angafunse mphunzitsi wina kuti awafotokozerenso nkhaniyo. Ngati mphunzitsi winayo atafotokoza zofanana ndi zimene mphunzitsi woyamba uja anafotokoza, ana ambiri angasiye kukayikira. Mofanana ndi zimenezi, ngati simukumvetsabe zimene Yohane analemba zokhudza Yesu ndi Mulungu Wamphamvuyonse, mukhoza kuwerenga mabuku ena a m’Baibulo kuti mumvetse nkhaniyi. Mwachitsanzo, taonani zimene Mateyu analemba pofotokoza za nthawi imene Mulungu adzawononge dziko loipali. Iye anagwira mawu a Yesu akuti: “Kunena za tsikulo ndi ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo akumwamba kapenanso Mwana, koma Atate yekha.” (Mateyu 24:36) Kodi mawu amenewa akusonyeza bwanji kuti Yesu si Mulungu Wamphamvuyonse?

Yesu ananena kuti Atate wake amadziwa zambiri kuposa iyeyo. Akanakhala kuti Yesu ndi Mulungu Wamphamvuyonse, ndiye kuti nayenso akanakhala akudziwa zofanana ndi zimene Atate wake amadziwa. Choncho, Mwanayu si wofanana ndi Atate wake. Koma ena anganene kuti: ‘Yesu ankanena zimenezi ali munthu pano padziko lapansi.’ Zimenezi ndi zoona, koma nanga bwanji mzimu woyera? Ngati mzimu woyera nawonso uli Mulungu, n’chifukwa chiyani Yesu sananene kuti ukudziwa zimene Atate amadziwa?

Pamene mukupitiriza kuphunzira Baibulo, mudzadziwa malemba ena ambiri amene adzakuthandizeni kumvetsa nkhaniyi. Malemba amenewa adzakuthandizani kudziwa bwino Atate, Mwana komanso mzimu woyera.—Salimo 90:2; Machitidwe 7:55; Akolose 1:15.

^ ndime 3 Kuti mumve zambiri zokhudza lemba la Yohane 1:1, onani Nsanja ya Olonda ya November 1, 2008, tsamba 24-25, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.