Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ZAKUMAPETO

Kodi Mawu Akuti Sheoli ndi Hade Amatanthauza Chiyani?

Kodi Mawu Akuti Sheoli ndi Hade Amatanthauza Chiyani?

MUZINENERO zoyambirira, Baibulo limatchula mawu achiheberi akuti sheʼohlʹ ndi ofanana nawo achigiriki akuti haiʹdes maulendo oposa 70. Mawu awiri onsewa amatanthauza kumalo kumene anthu amapita akafa. Mabaibulo ena amamasulira mawuwa kuti “manda” kapena “dzenje.” Tiyeni tione mmene mawu amenewa awagwiritsira ntchito m’malo osiyanasiyana m’Baibulo.

Lemba la Mlaliki 9:10 limati: “Kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu, kapena nzeru, ku Manda [Sheoli] kumene ukupitako.” Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Sheoli amaimira dzenje limodzi limene tingaikemo munthu wakufa? Ayi. Baibulo likamanena za manda amodzi limagwiritsa ntchito mawu ena achiheberi ndi achigiriki, osati akuti sheʼohlʹ ndi haiʹdes. (Genesis 23:7-9; Mateyu 28:1) Kuwonjezera pamenepa, Baibulo silimagwiritsa ntchito mawu akuti “Sheoli” ponena za dzenje limodzi limene mwaikidwa mitembo ya anthu ambirimbiri.—Genesis 49:30, 31.

Ndiye kodi mawu akuti “Sheoli” amatanthauza chiyani kwenikweni? Mawu a Mulungu amasonyeza kuti mawu akuti “Sheoli” ndi akuti “Hade” amatanthauza zinthu zina, osati manda amodzi, ngakhale mutakhala kuti mwaikidwa anthu ambiri. Mwachitsanzo, pofotokoza za manda, kapena kuti Sheoli, lemba la Yesaya 5:14 limanena kuti: “Akulitsa malo ake ndipo atsegula kwambiri pakamwa pake kupitirira malire.” Ngakhale kuti Sheoli yameza kale anthu ambirimbiri, nthawi zonse imakhalabe ndi njala yofuna kumeza anthu ena. (Miyambo 30:15, 16) Mosiyana ndi dzenje limodzi lomwe likhoza kudzaza, “Manda . . . sakhuta.” (Miyambo 27:20) Zimenezi zikutanthauza kuti Sheoli singadzaze. Ndiye kuti Sheoli, kapena kuti Hade, si malo enieni amene ali kwinakwake, koma ndi manda a anthu onse.

Zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani ya kuukitsidwa kwa akufa, zingatithandize kumvetsa bwino tanthauzo la mawu akuti “Sheoli” komanso “Hade.” Mawu a Mulungu amasonyeza kuti mawu akuti Sheoli ndi Hade amanena za manda amene kuli anthu omwe adzaukitsidwe. * (Yobu 14:13; Machitidwe 2:31; Chivumbulutso 20:13) Mawu a Mulungu amasonyezanso kuti ku Sheoli, kapena kuti Hade, kuli anthu amene ankatumikira Mulungu ndiponso anthu ena ambiri amene sanatumikirepo Mulungu. (Genesis 37:35; Salimo 55:15) N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.”—Machitidwe 24:15.

^ ndime 1 Koma akufa amene sadzaukitsidwa amafotokozedwa kuti ali ku “Gehena,” osati ku Sheoli kapena ku Hade. (Mateyu 5:30; 10:28; 23:33) Mofanana ndi Sheoli ndi Hade, Gehena si malo enieni.