Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 13

Muziona Moyo Ngati Mmene Mulungu Amauonera

Muziona Moyo Ngati Mmene Mulungu Amauonera
  • Kodi Mulungu amauona bwanji moyo?

  • Kodi Mulungu amakuona bwanji kuchotsa mimba?

  • Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza moyo?

1. Kodi ndi ndani amene analenga zamoyo zonse?

MNENERI Yeremiya ananena kuti: “Yehova ndi Mulungu woonadi. Iye ndi Mulungu wamoyo.” (Yeremiya 10:10) Kuwonjezera pamenepo, Yehova Mulungu ndi amene analenga zinthu zonse zamoyo. Atumiki ake akumwamba ananena kuti: “Inu Yehova . . . munalenga zinthu zonse, ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.” (Chivumbulutso 4:11) Poimba nyimbo yotamanda Mulungu, nayenso Mfumu Davide anati: “Inu ndinu kasupe wa moyo.” (Salimo 36:9) Choncho moyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.

2. Kodi Mulungu amatisamalira bwanji kuti tikhale ndi moyo?

2 Yehova amatisamaliranso kuti tipitirizebe kukhala ndi moyo. (Machitidwe 17:28) Amatipatsa chakudya chomwe timadya, madzi amene timamwa, mpweya umene timapuma komanso dziko limene tikukhalamoli. (Werengani Machitidwe 14:15-17.) Yehova amatipatsa zinthu zonsezi n’cholinga choti tizisangalala. Koma kuti tizisangalala ndi moyo mokwanira, tiyenera kuphunzira malamulo ake n’kumawatsatira.—Yesaya 48:17, 18.

MMENE TINGASONYEZERE KUTI TIMALEMEKEZA MOYO

3. Kodi Mulungu anachita chiyani Abele ataphedwa ndi m’bale wake?

3 Mulungu amafuna kuti tizilemekeza moyo wathu komanso wa anthu ena. Mwachitsanzo, m’nthawi ya Adamu ndi Hava, mwana wawo Kaini anakwiyira kwambiri m’bale wake Abele. Yehova anachenjeza Kaini kuti mkwiyo wakewo ungamuchititse kuti achite tchimo lalikulu. Koma iye sanamvere chenjezolo. Kaini “anam’kantha Abele m’bale wake n’kumupha.” (Genesis 4:3-8) Chifukwa cha zimenezi, Yehova anamulanga Kaini.—Genesis 4:9-11.

4. M’Chilamulo cha Mose, kodi Mulungu anasonyeza bwanji kuti amaona moyo kukhala wofunika kwambiri?

4 Patadutsa zaka zoposa 2,000, Yehova anapereka malamulo kwa Aisiraeli owathandiza kuti azimutumikira m’njira yovomerezeka. Chifukwa choti malamulowo anaperekedwa kudzera mwa Mose, nthawi zina amatchedwa Chilamulo cha Mose. Limodzi mwa malamulowo linali lakuti: “Usaphe munthu.” (Deuteronomo 5:17) Lamulo limeneli linasonyeza kuti Mulungu amaona kuti moyo wa munthu ndi wofunika kwambiri, choncho anthunso ayenera kuuona chimodzimodzi.

5. Kodi tiyenera kuiona bwanji nkhani yochotsa mimba?

5 Nanga bwanji za moyo wa mwana amene sanabadwe? Malinga ndi Chilamulo cha Mose, kupha mwana amene sanabadwe kunali kulakwa. Choncho nawonso moyo wa mwana wotere ndi wamtengo wapatali kwa Yehova. (Werengani Ekisodo 21:22, 23; Salimo 127:3.) Zimenezi zikutanthauza kuti kuchotsa mimba n’kulakwa.

6. N’chifukwa chiyani sitiyenera kudana ndi munthu aliyense?

6 Kulemekeza moyo kumaphatikizapo kuona anthu anzathu moyenera. Baibulo limati: “Aliyense amene amadana ndi m’bale wake ndi wopha munthu, ndipo mukudziwa kuti aliyense wopha munthu sadzalandira moyo wosatha.” (1 Yohane 3:15) Ngati tikufuna kudzapeza moyo wosatha, tiyenera kuchotsa maganizo aliwonse odana ndi anzathu, chifukwa zinthu zambiri zachiwawa zimachitika chifukwa cha chidani. (1 Yohane 3:11, 12) Choncho tiyenera kuyesetsa kuti tizikondana.

7. Kodi ndi makhalidwe ati amene angasonyeze kuti munthu sakulemekeza moyo?

7 Nanga kodi tingalemekeze bwanji moyo wathu? Palibe munthu amene amafuna kufa, komabe ena amaika moyo wawo pangozi chifukwa chongofuna kusangalala. Mwachitsanzo, ena amasuta fodya, chamba kapena kumwa mankhwala osokoneza bongo. Zinthu zimenezi zimawononga thupi ndipo nthawi zambiri anthu amene amazigwiritsa ntchito amafa nazo. Munthu amene ali ndi chizolowezi chogwiritsa ntchito zinthu zimenezi samaona kuti moyo ndi wopatulika. Komatu Mulungu amaona kuti makhalidwe amenewa ndi onyansa. (Werengani Aroma 6:19; 12:1; 2 Akorinto 7:1.) Kuti titumikire Mulungu m’njira yovomerezeka, tiyenera kuyesetsa kusiya makhalidwe oipa amenewa ngakhale kuti kuchita zimenezi kungakhale kovuta kwambiri. Yehova angatithandize kuti tisiye makhalidwewa ndipo amayamikira akamaona kuti tikuyesetsa kusamalira moyo wathu podziwa kuti ndi mphatso yamtengo wapatali.

8. N’chifukwa chiyani nthawi zonse tiyenera kupewa zinthu zimene zingachititse ngozi?

8 Munthu amene amalemekeza moyo, nthawi zonse amaganiziranso zimene angachite kuti apewe ngozi. Choncho ngati ifeyo timalemekeza moyo, sitingachite zinthu mosasamala ndiponso sitingachite zinthu zimene zingaike moyo pa ngozi n’cholinga chongofuna kusangalala. Tidzapewa kuyendetsa galimoto kapena njinga mosasamala. Tidzapewanso masewera aliwonse achiwawa ndi oopsa. (Salimo 11:5) Lamulo lina limene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli linkanena kuti: “Ukamanga nyumba yatsopano [ya denga lafulati] uzimanganso kampanda padenga la nyumbayo kuopera kuti ungaike mlandu wa magazi panyumba yako ngati munthu atagwa kuchokera padengapo.” (Deuteronomo 22:8) Mogwirizana ndi mfundo ya m’lamulo limeneli, muyenera kusamalira masitepe komanso zinthu zina kuopera kuti wina angagwe n’kuvulala. Ngati muli ndi galimoto kapena njinga, onetsetsani kuti ili ndi zonse zofunikira poyenda pamsewu. Muziyesetsa kusamalira nyumba, galimoto kapena njinga yanu kuti zisaike moyo wanu kapena wa anthu ena pangozi.

9. Kodi moyo wa zinyama tiyenera kuuona bwanji?

9 Nanga bwanji za moyo wa zinyama? Mulungu amauonanso kuti ndi wopatulika. Iye amalola kupha nyama kuti tipeze chakudya, zovala kapena pofuna kuteteza anthu. (Genesis 3:21; 9:3; Ekisodo 21:28) Komabe kuchitira nkhanza nyama kapena kuzipha pongofuna kusewera n’kulakwa ndipo kungasonyeze kusalemekeza moyo.—Miyambo 12:10.

MMENE TINGASONYEZERE KUTI TIMALEMEKEZA MAGAZI

10. Kodi Mulungu anasonyeza bwanji kuti pali kugwirizana pakati pa moyo ndi magazi?

10 Kaini atapha m’bale wake Abele, Yehova anamuuza kuti: “Magazi a m’bale wako akundilirira munthaka.” (Genesis 4:10) Pamene Mulungu ananena kuti “magazi” ankatanthauza moyo wa Abele. Kaini ankafunika kulangidwa chifukwa choti wapha m’bale wake. Zinali ngati magazi, kapena kuti moyo wa Abele unkapempha kuti Yehova achite chilungamo. Pambuyo pa Chigumula, Mulungu anasonyezanso kugwirizana komwe kulipo pakati pa moyo ndi magazi. Chigumula chisanachitike anthu ankangodya zipatso, mtedza, masamba ndi zinthu zina zakumunda. Koma pambuyo pa Chigumula, Yehova anauza Nowa ndi ana ake kuti: “Nyama yamoyo iliyonse ikhale chakudya chanu.” Komabe Mulungu anawaletsa chinthu chimodzi. Iye anawauza kuti: “Musadye nyama pamodzi ndi magazi ake, amene ndiwo moyo wake.” (Genesis 1:29; 9:3, 4) Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amaona moyo ndi magazi kukhala zogwirizana kwambiri.

11. Kuyambira m’nthawi ya Nowa, kodi Mulungu anapereka lamulo lotani pa nkhani ya magazi?

11 Timasonyeza kuti timalemekeza magazi tikamapewa kuwadya. M’Chilamulo chimene Yehova anapereka kwa Aisiraeli, anawalamula kuti: “Munthu aliyense mwa ana a Isiraeli . . . akapita kosaka nyama, ndipo wapha nyama kapena mbalame yololeka kudya, azithira magazi ake pansi ndi kuwafotsera ndi dothi. . . . Ndauza ana a Isiraeli kuti: ‘Musamadye magazi a nyama iliyonse.’” (Levitiko 17:13, 14) Zimenezi zikusonyeza kuti lamulo la Mulungu loletsa kudya magazi, lomwe linaperekedwa kwa Nowa zaka 800 m’mbuyomo, linali likugwirabe ntchito. Zikusonyezanso bwino mmene Yehova ankaionera nkhaniyi. Iye analola kuti atumiki ake angathe kudya nyama koma osati magazi ake. Iwo ankayenera kuthira magaziwo pansi, zomwe zinali ngati kubwezera moyo wa nyamayo kwa Mulungu.

12. M’nthawi ya atumwi, kodi mzimu woyera unapereka lamulo lotani lomwe likugwirabe ntchito masiku ano?

12 Akhristu anapatsidwanso lamulo lomweli. M’nthawi ya Akhristu oyambirira, atumwi ndi amuna ena omwe ankatsogolera pakati pa otsatira a Yesu anasonkhana kuti asankhe malamulo amene anthu onse mumpingo wachikhristu ankayenera kutsatira. Atakambirana, anagwirizana mfundo iyi: “Mzimu woyera pamodzi ndi ife taona kuti ndi bwino kuti tisakusenzetseni mtolo wolemera, kupatula zinthu zofunika zokhazi zomwe ndi kupitiriza kupewa zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano, magazi, zopotola, ndi dama.” (Machitidwe 15:28, 29; 21:25) Choncho tiyenera ‘kupewa magazi.’ Mulungu amaona kuti kupewa magazi n’kofunika kwambiri mofanana ndi kupewa chiwerewere ndiponso kulambira mafano.

Dokotala atakuuzani kuti musiye mowa, kodi mukhoza kumangodziika dilipi ya mowawo?

13. Fotokozani chitsanzo chosonyeza kuti lamulo loletsa magazi likuphatikizanso nkhani yoikidwa magazi kuchipatala.

13 Kodi lamulo loti tiyenera kupewa magazi likuphatikizanso kuikidwa magazi kuchipatala? Inde. Tiyerekezere motere: Tinene kuti dokotala wakuuzani kuti musiye mowa. Kodi zimenezi zingatanthauze kuti simukuyenera kumwa mowa koma mukhoza kungodziika dilipi ya mowawo? Ayi. N’chimodzimodzinso ndi nkhani ya magazi. Kupewa magazi kumatanthauza kusalola kuti m’thupi mwathu mulowe magazi mwa njira iliyonse. Choncho lamulo loletsa magazi likutanthauza kuti sitiyenera kulola munthu aliyense kuti atiike magazi m’thupi mwathu.

14, 15. Kodi Mkhristu angatani ngati madokotala atamuuza kuti akufunika amupatse magazi, ndipo n’chifukwa chiyani angatero?

14 Koma kodi zingakhale bwanji ngati Mkhristu wavulala kwambiri kapena ngati akufunika kupangidwa opaleshoni yaikulu? Tiyerekeze kuti madokotala amuuza kuti akufunika kuikidwa magazi, apo ayi amwalira. N’zoona kuti Mkhristu sangafune kufa komabe pofuna kutetezera mphatso yamtengo wapatali ya moyo, iye angavomere kulandira thandizo lina limene silingaphatikizepo kugwiritsa ntchito magazi molakwika. Choncho iye angasankhe kulandira thandizo loterolo ngati lilipo ndiponso angalandire mankhwala ena m’malo mwa magazi.

15 Kodi Mkhristu angaphwanye lamulo la Mulungu n’cholinga chofuna kutalikitsako moyo wake m’dziko loipali? Yesu anati: “Aliyense wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya, koma aliyense wotaya moyo wake chifukwa cha ine adzaupeza.” (Mateyu 16:25) N’zoona kuti sitimafuna kufa. Koma ngati tingaphwanye lamulo la Mulungu pofuna kuyesa kupulumutsa moyo womwe tili nawowu, tingataye mwayi wodzapeza moyo wosatha. Choncho ndi bwino kukhulupirira Mulungu komanso kutsatira malamulo ake olungama. Ndipotu ngakhale titafa chifukwa cha vuto linalake, iye popeza ndi amene anatipatsa moyo, adzatikumbukira n’kutibwezera moyo wathu, womwe ndi mphatso yamtengo wapatali.—Yohane 5:28, 29; Aheberi 11:6.

16. Kodi atumiki a Mulungu amatsimikiza mtima kuchita chiyani pa nkhani ya magazi?

16 Masiku ano, atumiki a Mulungu okhulupirika amayesetsa kutsatira lamulo la Mulungu lokhudza magazi zivute zitani. Iwo samadya magazi mwa njira iliyonse komanso salola kupatsidwa magazi kuchipatala. * Iwo amakhulupirira kuti Mulungu yemwe anapanga magazi amadziwa zinthu zimene zili zabwino. Kodi inunso mumakhulupirira zimenezi?

KUGWIRITSA NTCHITO MAGAZI KOYENERA

17. M’nthawi ya Aisiraeli, kodi ndi njira iti yokha yogwiritsa ntchito magazi imene Yehova Mulungu ankavomereza?

17 Chilamulo cha Mose chinafotokoza kwambiri za njira yoyenera yogwiritsa ntchito magazi. Ponena za kulambira kumene Aisiraeli ankayenera kuchita, Yehova analamula kuti: “Moyo wa nyama uli m’magazi ndipo ine ndakuikirani magazi paguwa lansembe kuti azikuphimbirani machimo. Zili choncho popeza magazi ndiwo amaphimba machimo.” (Levitiko 17:11) Aisiraeli akachimwa ankatha kukhululukidwa ngati apereka nsembe ya nyama ndiponso kupereka magazi ake ena paguwa la nsembe. Ankapereka nsembe zimenezi kuchihema ndipo pambuyo poti kachisi wamangidwa anayamba kupereka nsembezi kumeneko. Njira yokhayi ndi yomwe inali yoyenera yogwiritsira ntchito magazi.

18. Kodi timapeza madalitso otani chifukwa cha nsembe ya magazi a Yesu?

18 Akhristu oona samapereka nsembe za nyama kapena kuika magazi a nyama paguwa la nsembe chifukwa satsatira Chilamulo cha Mose. (Aheberi 10:1) Komabe kuika magazi paguwa la nsembe komwe Aisiraeli ankachita kunkaimira nsembe yamtengo wapatali ya Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu. Monga mmene tinaphunzirira m’Mutu 5, Yesu anapereka moyo wake kuti apulumutse anthu ndipo analola kuti magazi ake akhetsedwe ngati nsembe. Kenako anapita kumwamba kumene Mulungu analandira nsembe ya moyo wangwiro imene Yesu anapereka ali padziko lapansi. Nsembe imene anaperekayi inali yokwanira ndipo sinkafunika kubwerezedwanso. (Aheberi 9:11, 12) Zimenezi zinapereka mwayi woti tizitha kukhululukidwa machimo athu ndiponso woti tidzapeze moyo wosatha. (Mateyu 20:28; Yohane 3:16) Kugwiritsa ntchito magazi mwa njira imeneyi kunali kofunika kwambiri. (1 Petulo 1:18, 19) Tingadzapeze moyo wosatha ngati timakhulupirira nsembe ya Yesu.

Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumalemekeza moyo?

19. Kodi muyenera kuchita chiyani kuti mukhale “woyera pa mlandu wa magazi a anthu onse”?

19 Tiyenera kuyamikira Yehova Mulungu chifukwa cha mphatso ya moyo imene anatipatsa. Ndipo zimenezi ziyenera kutilimbikitsa kuuza ena kuti akhoza kudzakhala ndi moyo wosatha ngati angakhulupirire nsembe ya Yesu. Kutengera chitsanzo cha Mulungu chodera nkhawa ena kuyenera kutilimbikitsa kugwira ntchito imeneyi modzipereka kwambiri. (Werengani Ezekieli 3:17-21.) Ngati titagwira ntchito imene tapatsidwayi mwakhama, tidzatha kunena mawu ngati amene mtumwi Paulo ananena akuti: “Ndine woyera pa mlandu wa magazi a anthu onse. Pakuti sindinakubisireni kanthu, koma ndinakuuzani chifuniro chonse cha Mulungu.” (Machitidwe 20:26, 27) Kuuza ena za Mulungu ndiponso zimene amafuna ndi njira yabwino yosonyezera kuti timalemekeza moyo komanso magazi.

^ ndime 16 Kuti mudziwe zambiri zokhudza thandizo limene mungalandire m’malo mwa magazi, onani tsamba 13-17 m’kabuku kakuti Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu?, kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.