Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 6

Kodi Munthu Akafa Amapita Kuti?

Kodi Munthu Akafa Amapita Kuti?
  • Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?

  • Kodi n’chifukwa chiyani anthufe timamwalira?

  • Kodi kudziwa zenizeni zimene zimachitika munthu akamwalira kuli ndi phindu lotani?

1-3. Kodi anthu amakhala ndi mafunso otani okhudza imfa, ndipo zipembedzo zosiyanasiyana zimapereka mayankho otani?

ANTHU akhala akudzifunsa mafunso amenewa kwa zaka zambiri ndipotu mafunsowa ndi ofunika kwambiri. Mayankho ake ndi ofunika kwa tonse, kaya ndife ndani ndipo timakhala kuti.

2 M’mutu wapitawu, tinakambirana mmene dipo la Yesu linatithandizira kuti tikhale ndi mwayi wodzapeza moyo wosatha. Tinaphunziranso kuti Baibulo linaneneratu za nthawi imene “imfa sidzakhalaponso.” (Chivumbulutso 21:4) Komabe panopa, timamwalira. Mfumu yanzeru Solomo inanena kuti: “Amoyo amadziwa kuti adzafa.” (Mlaliki 9:5) Timayesetsa kudzisamalira kuti tikhale ndi moyo wautali, komabe timakhala ndi nkhawa yoti kodi chidzatichitikire n’chiyani tikadzamwalira.

3 M’bale wathu kapena mnzathu akamwalira, timakhala ndi chisoni ndipo timadzifunsa kuti ‘Ndiye kuti wapita kuti? Kodi akuvutika? Kodi akutiona? Kodi tingachite chilichonse kuti timuthandize? Nanga kodi tidzamuonanso?’ Zipembedzo zimapereka mayankho osiyanasiyana pa mafunso amenewa. Zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti ngati munthu ankachita zabwino, akamwalira amapita kumwamba koma ngati ankachita zoipa, amapita kukaotchedwa kumalo ozunzirako anthu. Zina zimaphunzitsa kuti munthu akamwalira, amapita kudziko la mizimu kumene amakakhala ndi makolo ake amene anamwalira. Pamene zinanso zimaphunzitsa kuti munthu akafa amapita kumalo enaake komwe amakaweruzidwa kenako n’kubadwanso ngati munthu wina kapena nyama.

4. Kodi zipembedzo zambiri zimagwirizana pa mfundo iti yokhudza imfa?

4 Zipembedzo zimenezi zimagwirizana pa mfundo imodzi, yonena kuti munthu akafa, pali chinachake m’thupi lake chimene sichifa. Kuyambira kale komanso ngakhale masiku ano, pafupifupi zipembedzo zonse zimaphunzitsa kuti anthufe timapitirizabe kukhala ndi moyo kwinakwake tikamwalira ndipo zimene amanena zimasonyeza kuti timatha kuona, kumva komanso kuganiza. Koma kodi zimenezi zingatheke? Timatha kuona, kumva komanso kuganiza chifukwa chakuti ubongo wathu ukugwira ntchito. Koma munthu akafa, ubongo umasiya kugwira ntchito. Choncho ubongo ukasiya kugwira ntchito, sitingathe kukumbukira zinthu, kuganiza kapena kumva chilichonse. Zonsezi n’zosatheka ngati ubongo wa munthu wasiya kugwira ntchito.

KODI KWENIKWENI CHIMACHITIKA N’CHIYANI MUNTHU AKAMWALIRA?

5, 6. Kodi Baibulo limanena kuti chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?

5 Yehova amadziwa bwino zimene zimachitika munthu akamwalira chifukwa iyeyo ndi amene analenga ubongo wa munthu. Zimene iye amadziwa ndi zomwe zili zolondola ndipo Baibulo, lomwe ndi Mawu ake, limafotokoza zimene zimachitika munthu akamwalira. Mfundo yomveka bwino imene Baibulo limaphunzitsa, ndi yakuti: Munthu akafa, sakhalanso ndi moyo kulikonse. Zimangokhala ngati mmene zinalili asanabadwe. Munthu womwalira saona, kumva kapena kuganiza. Tikamwalira palibe chinthu chilichonse m’thupi mwathu chomwe chimapitirizabe kukhala ndi moyo. Si kuti tili ndi moyo kapena mzimu womwe sungafe. *

Kodi moto wa kanduloyi wapita kuti?

6 Solomo atanena kuti amoyo amadziwa kuti adzafa, analembanso kuti: “Koma akufa sadziwa chilichonse.” Kenako anawonjezera mfundo zina pa mawu amenewa, pamene ananena kuti munthu womwalira sangakhale ndi chikondi kapena chidani ndipo “kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu, kapena nzeru, ku Manda.” (Werengani Mlaliki 9:5, 6, 10.) Nalonso lemba la Salimo 146:4 limafotokoza kuti munthu akamwalira, “zonse zimene anali kuganiza zimatheratu.” Tikamwalira palibe chilichonse m’thupi lathu chimene chimapitiriza kukhalabe ndi moyo. Moyo umene tili nawowu tingauyerekezere ndi moto wa kandulo. Motowo ukazimitsidwa supitanso kulikonse, umangothera pompo.

ZIMENE YESU ANANENA PA NKHANI YA IMFA

7. Kodi Yesu anayerekezera imfa ndi chiyani?

7 Yesu Khristu anafotokozapo zimene zimachitika munthu akamwalira. Anafotokoza zimenezi pamene ankanena za mnzake dzina lake Lazaro, yemwe anali atamwalira. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Bwenzi lathu Lazaro ali m’tulo akupumula.” Ophunzira akewo ankaganiza kuti Yesu ankatanthauza kuti Lazaro akugona zenizeni chifukwa choti akudwala. Koma sizimene Yesu ankatanthauza chifukwa kenako anafotokoza momveka bwino kuti: “Lazaro wamwalira.” (Werengani Yohane 11:11-14.) Apa Yesu anayerekezera imfa ndi tulo. Choncho Lazaro sanapite kumwamba kapena kumoto. Sanapite kukakhala ndi angelo kapena makolo ake amene anamwalira. Ndiponso Lazaro sanabadwenso ngati munthu wina. Pamene anafa, sankadziwa chilichonse ngati mmene zimakhalira munthu akagona tulo tofa nato. Palinso malemba ena omwe amayerekezera imfa ndi tulo. Mwachitsanzo, Sitefano ataphedwa, Baibulo limanena kuti “anagona tulo ta imfa.” (Machitidwe 7:60) Nayenso mtumwi Paulo analemba za anthu ena a mu nthawi yake omwe anali ‘atagona mu imfa.’—1 Akorinto 15:6.

Yehova analenga anthu kuti azikhala ndi moyo padziko lapansi mpaka kalekale

8. N’chiyani chimatichititsa kuona kuti Mulungu sankafuna zoti anthu azimwalira?

8 Koma kodi zoti anthu azifa ndi zimene Mulungu ankafuna? Ayi, Yehova analenga anthu kuti azikhala ndi moyo padziko lapansi mpaka kalekale. Monga mmene tinaphunzirira m’mitu yoyambirira, Mulungu atalenga anthu awiri oyambirira anawaika m’paradaiso wokongola. Anawalenga angwiro moti sankadwala. Yehova ankafuna kuti zinthu ziziwayendera bwino. Kodi pali makolo amene angafune kuti ana awo azivutika ndi ukalamba komanso imfa? Ayi, palibe. Yehova ankakonda kwambiri ana akewa ndipo ankafuna kuti azisangalala mpaka kalekale. Pofotokoza za anthu Baibulo limati: “[Yehova] anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.” (Mlaliki 3:11) Mulungu anatilenga ndi mtima wofuna kukhala ndi moyo wosatha. Ndipo anakonza kale njira yothandiza kuti zimenezi zidzatheke.

KODI N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHUFE TIMAFA?

9. Kodi Yehova anapereka lamulo lotani kwa Adamu, nanga n’chifukwa chiyani lamuloli linali losavuta kulitsatira?

9 Ndiyeno n’chifukwa chiyani timafa? Kuti tipeze yankho, choyamba tiyenera kukumbukira zimene zinachitika pa nthawi imene padziko lapansili panali anthu awiri okha. Baibulo limati: “Yehova Mulungu anameretsa m’nthaka mtengo wamtundu uliwonse wooneka bwino ndi wa zipatso zabwino kudya.” (Genesis 2:9) Koma panali lamulo limodzi limene anthuwo ankafunika kutsatira. Yehova anauza Adamu kuti: “Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya ndithu. Koma usadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. Chifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.” (Genesis 2:16, 17) Limeneli silinali lamulo lovuta kulitsatira chifukwa m’mundamo munali mitengo ina yambiri imene akanatha kudya zipatso zake. Lamuloli linkangowapatsa mwayi wosonyeza kuti amayamikira Mulungu yemwe anawapatsa zinthu zambirimbiri, kuphatikizapo moyo wangwiro. Kumvera lamuloli kukanasonyezanso kuti ankaona kuti Atate awo akumwamba anali woyenera kuwatsogolera ndipo iwowo anali ofunitsitsa kutsogoleredwa.

10, 11. (a) Kodi chinachitika n’chiyani kuti anthu awiri oyambirira asamvere Mulungu? (b) N’chifukwa chiyani kusamvera kwa Adamu ndi Hava kunali nkhani yaikulu?

10 N’zomvetsa chisoni kuti banja loyambirirali linasankha kusamvera Yehova. Pogwiritsa ntchito njoka, Satana anafunsa Hava kuti: “Eti n’zoona kuti Mulungu anati musadye zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu?” Hava anayankha kuti: “Zipatso za mitengo yonse ya m’mundamu anatiuza kuti tizidya. Koma zipatso za mtengo umene uli pakati pa munda, Mulungu anati, ‘Musadye zipatso zake ayi, musaukhudze kuti mungafe.’”—Genesis 3:1-3.

11 Satana anati: “Kufa simudzafa ayi. Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye chipatso cha mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.” (Genesis 3:4, 5) Satana ankafuna Hava aziganiza kuti zinthu zingamuyendere bwino ngati atadya chipatso chimene analetsedwacho. Malinga ndi mawu akewa, Satana ankatanthauza kuti Hava anali ndi ufulu wosankha yekha zabwino kapena zoipa komanso wochita zilizonse zimene akufuna. Satana ankatanthauzanso kuti Yehova anawanamiza powauza kuti adzafa ngati atadya zipatso za mtengo woletsedwawo. Hava anakhulupirira zimene Satana anamuuza moti anathyola zipatso za mtengowo n’kudya. Kenako anatenga zipatso zina n’kukamupatsa mwamuna wake, ndipo nayenso anadya. Si kuti Adamu ndi Hava sankadziwa zimene ankachita. Ankadziwa kuti zimene akuchitazo ndi zimene Mulungu anawauza kuti asachite. Kudya chipatsochi, kunali kusamvera mwadala lamulo losavuta komanso lomveka bwino limene anawapatsa. Anasonyeza kusalemekeza Mulungu komanso ulamuliro wake. Zimene anachitazi zinali tchimo lalikulu chifukwa zinasonyeza kusalemekeza Mlengi wawo wachikondi.

12. Kodi n’chiyani chingatithandize kumvetsa mmene Yehova anamvera pamene Adamu ndi Hava anachita zinthu zotsutsana naye?

12 Mwachitsanzo, kodi mungamve bwanji ngati mwana wanu atayamba kuchita zinthu zosonyeza kuti samakulemekezani komanso samakukondani? Ziyenera kuti zingakukhumudwitseni kwambiri. Ndiye taganizirani mmene zinam’pwetekera Yehova Adamu ndi Hava atayamba kuchita zinthu zotsutsana naye.

Adamu anachokera kufumbi ndipo anabwereranso kufumbi komweko

13. Kodi Yehova ananena kuti n’chiyani chidzachitikire Adamu akadzafa, nanga zimenezi zikutanthauza chiyani?

13 Yehova analibe chifukwa chopitirizira kusunga Adamu ndi Hava mpaka kalekale. Iwo anafa mogwirizana ndi zimene anawauza. Atamwalira moyo wawo unathera pompo, sanapite kudziko la mizimu. Tikudziwa zimenezi chifukwa cha zimene Yehova anamuuza Adamu pa nthawi imene ankamufunsa za tchimo limene wachita. Anamuuza kuti: ‘Udzabwerera kunthaka, pakuti n’kumene unatengedwa. Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.’ (Genesis 3:19) Mulungu analenga Adamu pogwiritsa ntchito fumbi lapansi. (Genesis 2:7) Koma poyamba iye kunalibe. Choncho pamene Yehova ananena kuti Adamu adzabwerera kufumbi ankatanthauza kuti kudzakhala kulibe ngati mmene zinalili asanalengedwe. Ankatanthauza kuti sadzakhala ndi moyo ndipo sadzatha kuchita chilichonse ngati mmene dothi limakhalira.

14. N’chifukwa chiyani anthufe timafa?

14 Adamu ndi Hava akanapanda kuchimwa, akanakhala alipobe mpaka pano. Nafenso timamwalira chifukwa tinatengera uchimo kwa Adamu. (Werengani Aroma 5:12.) Uchimo uli ngati matenda oopsa obadwa nawo amene makolo amapatsira ana awo onse. Uchimo umenewu umabweretsa imfa yomwe ndi mdani wathu. (1 Akorinto 15:26) Tiyenera kuyamikira kwambiri Yehova chifukwa chotipatsa dipo limene lingatipulumutse kwa mdani woopsa ameneyu.

KUDZIWA ZENIZENI ZIMENE ZIMACHITIKA MUNTHU AKAMWALIRA N’KOTHANDIZA

15. Kodi kudziwa zenizeni zimene zimachitika munthu akamwalira n’kothandiza bwanji?

15 Zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani ya mmene akufa alili n’zothandiza kwambiri. Monga taonera, munthu akamwalira samamva kupweteka kulikonse komanso sangathe kudana ndi wina aliyense. Choncho sitiyenera kuwaopa chifukwa sangativulaze. Komanso sangatithandize kapena kufuna thandizo lathu. Sitingathe kulankhula nawo ndipo iwonso sangalankhule nafe. Atsogoleri ambiri achipembedzo amanama kuti angathe kuthandiza anthu amene anamwalira ndipo anthu amene amakhulupirira zonena zawozo amawapatsa ndalama. Koma kudziwa zenizeni zimene zimachitika munthu akamwalira kumatiteteza kuti tisapusitsidwe ndi mabodza amenewa.

16. Kodi zimene zipembedzo zambiri zimaphunzitsa zimachokera kwa ndani, nanga amaphunzitsa zotani?

16 Kodi zimene amaphunzitsa kutchalitchi kwanu zimagwirizana ndi zimene Baibulo limanena pa nkhani ya akufa? Zimene zipembedzo zambiri zimaphunzitsa sizigwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Izi zili choncho chifukwa zimene matchalitchi amenewa amaphunzitsa zimachokera kwa Satana. Iye amagwiritsa ntchito zipembedzo zonyenga pofuna kupusitsa anthu kuti azikhulupirira zoti akadzamwalira mzimu wawo udzapitirizabe kukhala ndi moyo kwinakwake. Limeneli ndi limodzi mwa mabodza amene Satana amagwiritsa ntchito pofuna kusokoneza anthu kuti asiye kutsatira Yehova Mulungu. Kodi bodza limeneli lingapangitse bwanji munthu kusiya kutsatira Mulungu?

17. N’chifukwa chiyani tinganene kuti mfundo yoti Mulungu amazunza anthu kumoto imachititsa kuti Mulungu azioneka ngati woipa?

17 Monga taonera kale, zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti munthu amene amachita zoipa akamwalira amapita kumoto kumene amakazunzika mpaka kalekale. Mfundo imeneyi imachititsa kuti Mulungu azioneka ngati woipa. Yehova ndi Mulungu wachikondi ndipo sangazunze anthu mwa njira imeneyi. (Werengani 1 Yohane 4:8.) Kodi mungamuone bwanji munthu amene angawotche mwana wake manja chifukwa choti ndi wosamvera? Kodi mungamuone kuti ndi munthu wabwino? Kodi mungalakelake atakhala mnzanu? Tikukhulupirira kuti simungatero. Mukhoza kumuona kuti ndi munthu wankhanza kwambiri. Komatu zimene Satana amafuna kuti tizikhulupirira n’zoti Mulungu amazunza anthu pamoto kwamuyaya.

18. Kodi n’chifukwa chiyani anthu ena amalambira akufa, nanga Baibulo limaphunzitsa chiyani pa nkhani imeneyi?

18 Satana amagwiritsanso ntchito zipembedzo kuti ziziphunzitsa zoti munthu akamwalira amasanduka mzimu womwe umafunika kulemekezedwa. Malinga ndi zimenezi, anthu amaona kuti mzimu wa munthu womwalira ukhoza kukhala mnzathu kapena mdani wathu. Anthu ambiri amakhulupirira bodza limeneli. Amaopa anthu akufa, kuwalemekeza ndiponso kuwalambira. Mosiyana ndi zimenezi Baibulo limaphunzitsa kuti anthu akufa ali mtulo ndipo tiyenera kulambira Mulungu woona yekha, Yehova, yemwe anatilenga ndiponso ndi amene amatisamalira.—Chivumbulutso 4:11.

19. Kodi kudziwa zenizeni zimene zimachitika munthu akamwalira kungatithandize kumvetsa mfundo ina iti imene Baibulo limaphunzitsa?

19 Kudziwa zenizeni zimene zimachitika munthu akamwalira kungakutetezeni kuti musapusitsidwe ndi bodza limene zipembedzo zimaphunzitsa. Kungakuthandizeninso kumvetsa mfundo zina za m’Baibulo. Mwachitsanzo, mukazindikira kuti anthu akamwalira samapita kudziko la mizimu, mungaone kuti zimene Mulungu analonjeza zoti anthu adzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi ndi zomveka.

20. Kodi tidzakambirana funso lotani m’mutu wotsatira?

20 Kalekale, Yobu anafunsa funso lakuti: “Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo?” (Yobu 14:14) Kodi munthu amene wafa ndipo sakudziwa chilichonse angadzakhalenso ndi moyo? Zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani imeneyi n’zolimbikitsa kwambiri ndipo mutu wotsatira udzafotokoza zimenezi.

^ ndime 5 Kuti mumve zambiri pa mawu akuti “mzimu,” onani Zakumapeto, patsamba 208-211.